Kukwaniritsa Udindo wa Kusamalira Banja
“ATATE inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Mwa mawu ouziridwa amenewo, mtumwi Paulo anaika udindo wosamalira banja pamalo ake oyenera—m’manja mwa atate.
M’mabanja ambiri si atate okha amene amasamalira ana awo. Mkazi wawo, amayi a anawo, amathandizana ntchito imeneyi mosangalala ndi mwamuna wakeyo. Nchifukwa chake Mfumu Solomo anati: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.”—Miyambo 1:8.
Chisamaliro Chakuthupi ndi Chauzimu
Makolo amene amakonda ana awo sawanyalanyaza mwadala. Ndithudi, ngati Mkristu achita zimenezo ndiye kuti akukana chikhulupiriro chake, mogwirizana ndi mawu a Paulo kwa Timoteo akuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.” (1 Timoteo 5:8) Akristu amadziŵa kuti kulera ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye” kumafuna zambiri kuposa kuwathandiza mwakuthupi chabe.
Talingalirani za malangizo a Mose kwa Aisrayeli pamene iwo anamanga msasa m’chigwa cha Moabu, atakhala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Pamenepo iye anabwereza kufotokoza malamulo a Mulungu kwa iwo ndipo anawalangiza kuti: “Muzisunga mawu anga awa mumtima mwanu ndi m’moyo mwanu.” (Deuteronomo 11:18) Poyambirira penipeni iye anawakumbutsa kuti ayenera kukonda Yehova ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi mphamvu yawo yonse, akumawonjezera kuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu.” (Deuteronomo 6:5, 6) Kunali kofunika kuti makolo achiisrayeli atenge mawu a m’Chilamulo cha Mulungu nawakhomereze mumtima mwawo. Ndi mitima yodzaza ndi chidziŵitso chauzimu, makolo achiisrayeli analabadira bwino lomwe mawu otsatira a Mose akuti: “Muziwaphunzitsa mwachangu [mawu a m’Chilamulo cha Mulungu] kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”—Deuteronomo 6:7; 11:19; yerekezerani ndi Mateyu 12:34, 35.
Onani kuti atate anayenera “kuphunzitsa mwachangu” mawu amenewo kwa ana awo ndiponso “kuwalankhula.” Dikishonale yotchedwa Merriam-Webster’s Collegiate Dictionary imati mawu akuti “kuphunzitsa mwachangu” amatanthauza “kuphunzitsa ndi kugogomezera kapena kulangiza mobwerezabwereza.” Pamene makolo analankhula za Chilamulo cha Mulungu tsiku lililonse—mmaŵa, masana, ndi usiku—zimenezi zinali zothandiza kwambiri kwa ana awo. Pamene anawo anazindikira kuti makolo awo anali kukonda Chilamulo cha Mulungu, iwonso anasonkhezeredwa kukulitsa unansi wathithithi ndi Yehova. (Deuteronomo 6:24, 25) Nzochititsa chidwi kuti Mose analangiza makamaka atate kuti aziphunzitsa ana awo ‘pokhala pansi m’nyumba zawo.’ Maphunziro amenewo anali mbali ya kusamalira banja. Koma kodi zinthu zili bwanji lerolino?
“Pokhala Pansi m’Nyumba Zanu”
“Si zapafupi,” anatero Janet, mayi wachikristu wa ana anayi.a “Pamafunikira kulimbikira,” akuvomereza motero Paul, mwamuna wake. Mofanana ndi makolo ena ambiri amene ali Mboni, Paul ndi Janet amayesetsa kuphunzira Baibulo ndi ana awo ngakhale kamodzi pamlungu. “Timayesetsa kukhala ndi makambitsirano a Baibulo a banja Lolemba lililonse madzulo panthaŵi yoikika,” akufotokoza motero Paul, navomerezanso kuti: “Koma zimenezi sizichitika nthaŵi zonse.” Monga mkulu woikidwa mumpingo mwake, iye nthaŵi zina amaitanidwa kuti akasamalire nkhani zina zofunika kwambiri. Ana ake aŵiri okulirapo amatumikira monga atumiki a nthaŵi zonse. Iwo amaona kuti madzulo ndiwo nthaŵi yabwino yofikira anthu mu utumiki. Choncho, monga banja, iwo anasintha nthaŵi yochitira phunziro lawo la banja. “Nthaŵi zina timachita phunziro lathu titangomaliza kudya chakudya chamadzulo,” akufotokoza motero Paul.
Ngakhale pamene makolo ayesetsa kulolera mwa kusintha nthaŵi ya phunziro la banja, iwo amayesetsabe kuti azichita phunzirolo nthaŵi zonse. “Ngati nthaŵi yochita phunziro lathu yasinthidwa,” akufotokoza motero mwana wamkazi Clare, “Atate nthaŵi zonse amalemba nthaŵi yatsopanoyo ndi kuiika pachitseko cha filiji, kuti tonsefe tidziŵe nthaŵi ya phunzirolo.”
Kusonkhana kaamba ka phunziro la Baibulo la banja lokhazikika kumaperekanso mpata woti ana ocheperako msinkhu a m’banjamo azifotokoza za nkhaŵa zawo ndi mavuto awo kwa makolo awo. Phunziro limenelo limakhala lothandiza pamene makolo akhala ololera osati kungogogomezera kuti ana aziyankha mafunso a m’buku lofotokoza za m’Baibulo limene akugwiritsira ntchito. “Phunziro lathu la banja lili msonkhano wa makambitsirano,” akufotokoza motero Martin amene ali ndi ana aamuna aŵiri. “Pamene musonkhana kamodzi pamlungu kukambitsirana za nkhani ina ya m’Malemba, mumakhala ndi mwayi wodziŵa mkhalidwe wauzimu wa banja lanu,” iye akutero. “Pamakambitsiranopo pamabuka nkhani zosiyanasiyana. Mumazindikira zimene zikuchitika kusukulu, ndiponso chinthu china chachikulu nchakuti mumazindikira makhalidwe amene ana anu akukulitsa.” Mkazi wake, Sandra, akuvomereza ndipo akuti nayenso amapindula kwambiri ndi phunziro la banjalo. “Pamene mwamuna wanga achititsa phunzirolo,” iye akutero, “Ndimaphunzira zambiri mwa kumvetsera mmene ana anga akuyankhira mafunso ake.” Kenaka Sandra amaperekapo ndemanga zake kuthandiza anyamata akewo. Iye amasangalala kwambiri ndi phunzirolo chifukwa chakuti amachita nawo mokangalika. Inde, nthaŵi za phunziro la banja zimathandiza makolo kuzindikira malingaliro a ana awo.—Miyambo 16:23; 20:5.
Khalani Ololera Ndipo Limbikirani
Pamene nthaŵi yochita phunziro lanu la banja ifika, mwina mungapeze kuti mwana wina ngwochangamuka ndiponso wachidwi, pamene mwana wina afunikira kumlimbikitsa kuti asumike maganizo ndi kupindulapo. Mayi wina wachikristu anati: “Umenewo ndiwo moyo wa banja! Pamafunikira kudziŵa chimene ungachite monga kholo. Choncho, pamene ulimbikirabe kuchita zimenezo, Yehova amakuthandiza ndipo amadzetsa mapindu ake.”
Kusumika maganizo kwa mwana kungadalire kwambiri pamsinkhu wake. Kholo lozindikira limalingalira za chimenechi. Mwamuna wina ndi mkazi wake ali ndi ana asanu, a zaka zoyambira pa 6 mpaka za m’ma 20. Atatewo, a Michael, anati: “Pamafunika kumpatsa mpata mwana wamng’ono kwambiri kuti ndiye ayambe kuyankha mafunso. Kenaka lolani ana okulirapo kuti awonjezerepo mwatsatanetsatane ndi kufotokoza mfundo zimene akonza.” Kuchita ndi ana awo mozindikira kumeneku kumathandiza makolo kuphunzitsa anawo kufunika kwa kulingalira ena. “Mwana wathu wina wamwamuna angamvetsetse,” akutero Martin, “koma mnyamata wina amafunikira kuthandizidwa kwambiri kuti amvetsetse mfundoyo. Ndimaona kuti nthaŵi ya phunzirolo imakhala nthaŵi yophunzira kusonyeza kuleza mtima kwachikristu ndi zipatso zina za mzimu.”—Agalatiya 5:22, 23; Afilipi 2:4.
Khalani okonzekera kuchita zinthu mogwirizana ndi maluso osiyanasiyana ndi misinkhu yosiyanasiyana ya ana anu. Simon ndi Mark, tsopano amene ali m’zaka zawo zaunyamata, anaona kuti pamene anali aang’ono kwambiri, iwo anali kusangalala kwambiri kuphunzira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako ndi makolo awo. “Atate athu anali kutiuza kuti tichitire chitsanzo mbali zosiyanasiyana ngati seŵero,” iwo akukumbukira motero. Atate awo akukumbukira kuti nthaŵi ina anagwada pansi pamene anali kuchitira chitsanzo fanizo la Msamariya wachifundo kwa ana awo. (Luka 10:30-35) “Zinali ngati zenizeni ndipo zinali zosangalatsa kwambiri.”
Ana ambiri amadana ndi phunziro la banja lokhazikika. Kodi zimenezi ziyenera kuletsa makolo kuti asamachititse phunzirolo panthaŵi imene anagwirizana? Ayi, safunikira kutero mpang’ono pomwe. “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana,” imatero Miyambo 22:15. Mayi wina wopanda mwamuna analingalira kuti anali kulephera kuchititsa phunziro la banja lake pamene, nthaŵi zambiri, zopinga zinaonetsa kuti zinali kulepheretsa phunzirolo. Koma analimbikirabe. Tsopano ana ake amamlemekeza kwambiri ndipo amayamikira chikondi ndi chisamaliro chimene iye anasonyeza mwa kulimbikira kuchititsa phunziro la banja lokhazikika.
Kuthandiza Anyamata ndi Atsikana “Amasiye”
Akulu achikristu ali ndi udindo wa ‘kuŵeta gulu la Mulungu.’ (1 Petro 5:2, 3) Pamene nthaŵi zina achezera mabanja a mumpingo mwawo, iwo amakhala ndi mwayi woyamikira makolo amene amakwaniritsa maudindo awo achikristu. Kodi udindo wophunzitsa ana a kholo lopanda mnzake wamuukwati uli m’manja mwa ndani? Musaiŵale kuti udindo wophunzitsa ana uli m’manja mwa kholo.
Kuchenjera kwachikristu kudzathandiza akulu kupeŵa mikhalidwe imene ingabuke ngati iwo ayesa kukwaniritsa udindo wa kholo limene palibe. Ngakhale kuti abale aŵiri angachezere mlongo wachikristu amene ali kholo lopanda mwamuna, iwo nthaŵi zonse adzakhala osamala ponena za zimene angalinganize pofuna kuchirikiza makonzedwe a phunziro la banja. Nthaŵi zina, kuitana anawo (ndipo, ngakhalenso kholo lopanda mwamunalo) kuti akakhale nawo paphunziro la banja la mkulu wina kungakhale kolimbikitsa ndiponso kothandiza. Komabe, tisaiwale kuti Yehova ndiye Atate wathu wamkulu wakumwamba. Iye ndithudi amakhalapo kuti atsogolere ndi kuthandiza mayiyo pamene achita phunzirolo ndi ana ake, ngakhale kuti amachititsa phunzirolo yekhayekha.
Nanga bwanji pamene mwana ali wodera nkhaŵa zinthu zauzimu, pamene makolo ake sadera nkhaŵa kwenikweni kapena sadera nkhaŵa nkomwe za maudindo awo auzimu? Atumiki okhulupirika a Yehova safunikira kutaya mtima. “Waumphaŵi adzipereka kwa Inu [Yehova Mulungu],” anaimba motero wamasalmo. “Wamasiye mumakhala mthandizi wake.” (Salmo 10:14) Ndiponso, akulu achikondi a mumpingo amayesetsa kulimbikitsa makolowo pamene asamalira ana awo. Iwo angalingalire zokhala ndi makambitsirano a banja nadzapezekapo kuti adzapereke malingaliro othandiza a mmene angamaphunzirire pamodzi. Komatu iwo sadzayesa konse kunyalanyaza udindo wa makolowo, chifukwa chakuti udindowo uli m’manja mwawo malinga nkunena kwa Malemba.
Ana amene makolo awo sanalandire chikhulupirirochi amafunikira kuchirikizidwa kwambiri. Kuwaitanira kuphunziro lanu la banja kumakhala kothandiza kwambiri ngati makolo awo awaloleza kutero. Robert, amene tsopano ali wachikulire amene ali ndi banja lake, anali kupezeka pamisonkhano yachikristu ndi makolo ake pamene iye anali ndi zaka zitatu zokha za kubadwa. Iye anakumbukira kuti misonkhano imeneyo inali yosangalatsa ngakhale pamene makolo ake anasiya kuyanjana ndi mpingo wachikristu. Pamene anali ndi zaka khumi, iye anakumana ndi mnyamata wina wa Mboni amene anali kumtenga popita kumisonkhano. Makolo a mnyamata wa Mboniyo anasamalira Robert mosangalala monga mwana wawo wamasiye mwauzimu ndipo m’kupita kwa nthaŵi anayamba kuphunzira naye. Chifukwa cha chisamaliro chawo chachikondi chimenechi, iye anapita patsogolo mofulumira ndipo tsopano akutumikira mosangalala monga mkulu mumpingo.
Ngakhale pamene makolo atsutsa kuti ana awo asapite patsogolo, anawo sasiyidwa okhaokha. Yehova amakhalabe Atate wokhulupirika wakumwamba. “Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye,” limatero Salmo 68:5. Anyamata ndi atsikana amasiye mwauzimu amadziŵa kuti angatembenukire kwa iye m’pemphero, ndipo iye adzawachirikiza. (Salmo 55:22; 146:9) Gulu la Yehova lokhala ngati amayi limakwaniritsa udindo wake mwachangu mwa kukonza chakudya chokoma chauzimu choperekedwa kudzera m’zofalitsa zake ndiponso pamisonkhano ya mipingo yachikristu yoposa 85,000 kuzungulira dziko lonse lapansi. Choncho, ndi chithandizo chauzimu chochokera kwa Atate wathu, Yehova, ndi gulu lake lokhala ngati amayi, ngakhale “ana amasiye” adzakhalabe ndi phunziro la Baibulo pamlingo winawake.
Makolo achikristu amene amachititsa maphunziro a Baibulo a banja ndi ana awo tiyenera kuwayamikira kwambiri. Makolo opanda anzawo amuukwati amene amalimbikira kuphunzitsa ana awo m’njira za Yehova ayenera kulandira chisamaliro chapadera ndiponso ayenera kutamandidwa chifukwa cha khama lawolo. (Miyambo 22:6) Onse amene amasamalira ana amasiye mwauzimu amadziŵa kuti zimenezi zimasangalatsa Atate wathu wakumwamba, Yehova. Kusamalira zosoŵa zauzimu za banja ndi udindo waukulu. Koma ‘musaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake mudzatuta mukapanda kufooka.’—Agalatiya 6:9.
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa.
[Chithunzi patsamba 23]
Phunziro la banja limapereka mpata wabwino woti ana a m’banjamo azifotokoza nkhaŵa zawo kwa makolo awo
[Mawu a Chithunzi patsamba 20]
Harper’s