Kulemekeza Mulungu wa Chiyembekezo
“Atero Yehova wamakamu kuti: . . . ‘Amene andilemekeza ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa ine, adzapeputsidwa.’”—1 SAMUELI 2:30.
1. Nchifukwa chotani chimene tiri nacho cha kufunira kulemekeza Yehova? (1 Timoteo 1:17; Chivumbulutso 4:11)
M’CHIYANG’ANIRO cha ziyembekezo zimene tingakhale nazo, zozikidwa pa Baibulo, chiri choyenera ndi cholondola kotheratu kaamba ka ife kuti tilemekeze “Mulungu wa chiyembekezo,” “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.” (Aroma 15:13, King James Version; New World Translation) Nchifukwa ninji chiri tero? Ndimotani mmene ife, pamene tiri kokha madontho, anthu ochimwa, tingalemekezere Mlengi wamkulu wa chilengedwe chonse? Ndipo kodi iye adzabwezera kutilemekeza ife?
2. Kodi Yesu anadzimva motani ponena za kuperekedwa kwa ulemu kwa Mulungu?
2 Tingaphunzire kuchokera ku zimene zinachitika ndi Yesu. Palibe ndi mmodzi yense wa ife angakane kuti Yesu nthaŵi zonse anafuna kuti Atate ake alemekezedwe, ndi kupatsidwa ulemerero. (Yohane 5:23; 12:28; 15:8) M’chenicheni, Yesu anatsutsa Afarisi ndi alembi omwe ‘analemekeza Mulungu ndi milomo yawo koma mitima yawo inali kutali ndi iye.’ Chonde dziŵani kuti, kusalemekeza kwawo Mulungu kunaphatikizapo malingaliro osayenera ndi ntchito. (Mateyu 15:7-9) Kodi ife, ngakhale kuli tero, tinganene kuti m’kulemekeza Mulungu kwa Kristu, chiyembekezo chake chinaphatikizidwa? Ndipo ndimotani mmene Yehova anayankhira pa kulemekezedwako?
3. Kodi timadziŵa motani kuti Yesu anayembekeza mwa Yehova?
3 Yesu anatenga kumtima mawu a Davide pa Masalmo 16:10: “Simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.” Chifukwa chakuti anali ndi chiyembekezo chimenechi cha kuukitsidwa, Yesu Kristu anakhoza kunena mawu odzetsa mphamvu pa wochita zoipa yemwe anapachikidwa kumbali kwake kuti: “Indetu, ndinena ndi iwe [lero lino, udzakhala ndi ine NW] m’Paradaiso.” (Luka 23:39-43) Wochita zoipa ameneyo mwamsanga anafa, chotero sanali wokhoza masiku atatu pambuyo pake kuchitira umboni kutsimikizirika kwa chiyembekezo cha Yesu cha kuukitsidwa. Koma mboni yowona ndi maso inasimba kuti: “Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tiri mboni ife tonse.” (Machitidwe 2:31, 32) Iyo inali nsonga.
4. Ndi ulemu wotani umene Yesu anayenerera ndi kulandira? (Chivumbulutso 5:12)
4 Ambiri a anthu wamba kwa amene Yesu anatumikirako anadziŵa kuti iye anayenerera ulemu, kapena kulemekezedwa. (Luka 4:15; 19:36-38; 2 Petro 1:17, 18) Kenaka iye anafa monga munthu wachifwamba. Kodi chimenecho chinasintha zinthu? Ayi, popeza kuti Yesu anali ndi kuvomerezedwa kwa Mulungu mwa amene iye anayembekezera. Chotero, Yehova anambweretsa iye ku moyo. Nsonga yakuti “Mulungu wachiyembekezo” anawukitsa mwana wake ku moyo ndi kumveka moyo wosafa m’dziko la mizimu inatsimikizira kuti Atate ankapitirizabe kulemekeza mwana wake. Paulo akunena kuti: “Koma timpenya Yesu . . . chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.”—Ahebri 2:7, 9; Afilipi 2:9-11.
5. Kodi ndi m’njira yapadera yotani mu imene Yesu angalemekezedwere, kutulukapo m’kulemekezedwa kowonjezereka kotani kwa Mulungu?
5 Yesu, amene analemekeza Yehova, anatchula njira imodzi yapadera mu imene Atate anamulemekezera iye. M’kuwonekera kwake kwa atumwi okhulupirika, iye anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi dziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la mzimu woyera . . . onani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:18-20) Chotero Atate mowonjezereka analemekeza mwana mwa kumpatsa iye ulamuliro wapadera. Uwu ukafunikira kugwiritsiridwa ntchito m’malo mwa anthu omwe akachita ntchito yomwe imabweretsa ulemu kwa Uyo amene Yesu amalimbikira kulemekeza. Chotero, kodi ichi chimatanthauza kuti, ife anthu opanda ungwiro tingalemekeze Atate m’njira ina yake ndi kulemekezedwa ndi iye kachiŵirinso?
Anthu Alemekeza Mulungu
6. Kodi chiri choyenera kukhumba kulemekezedwa, koma kodi ndi ngozi yotani yomwe imakhalapo mu ichi? (Luka 14:10)
6 Anthu ambiri samaganiza nkomwe ponena za kulemekeza Mulungu choyamba, popeza kuti iwo ali okondweretsedwa kwambiri mkupeza ulemu kaamba ka iwo eni. Ena angakhoze ngakhale kunena kuti chiri chachibadwa kwa ife kufuna kulemekezedwa. Pali mlingo wa chowonadi m’chimenecho, monganso mmene kuliri kwachibadwa kukhumba dzina labwino, ndi mlingo wa ulemu mmenemo. (1 Timoteo 3:2, 13; 5:17; Machitidwe 28:10) Komabe, kukhumba kulemekezedwa kuchokera kwa anthu mopepuka kungagogomezeredwe monkitsa. Ichi chiri chowonekera kwa ambiri amene amangofuna kumveka pa mlingo uliwonse kapena omwe angachite chirichonse kaamba ka kufuna kuwonedwa.
7. Nchifukwa ninji kulemekezedwa ndi anthu kuli kwa pindulitso lokhala ndi polekezera chotero?
7 Pamene mulingalira ponena za icho, ngakhale kulemekezeka kokulira kochokera kwa anthu kuli kwachabe, popeza kuti onse amafa mwamsanga. Eya, zikumbukiro za otchuka ochepera zingalemekezedwe kokha kwa kanthaŵi, koma ambiri a akufa amaiwalidwa. Kodi ndi anthu angati omwe amadziŵa maina a agogo a agogo awo kapena omwe anali atsogoleri a mtundu wawo zaka zana limodzi zapitazo? Ndithudi, kaya ngati wina wake anakhalako kapena sanakhaleko sizimasintha zinthu. Iye ali kokha mchenga wa zinthu m’nyengo ya nthaŵi, luntha lochepa mu kasupe wa moyo. Ndipo ngakhale ngati iye akulemekezedwa mwachidule pambuyo pa imfa, iye sakuchidziŵa icho. (Yobu 14:21; 2 Mbiri 32:33; Mlaliki 9:5; Masalmo 49:12, 20) Chinthu chokha chimene chingapange kusiyana chiri kukhala ndi chiyembekezo chimene Mulungu amapereka, kumlemekeza iye, ndi kulemekezedwa pambuyo pake. Tingawone chimenechi m’miyoyo ya okhalako aŵiri mu Israyeli wakale.
8. Eli anagwera mu msampha wotani wophatikizapo kupereka kwa ulemu?
8 Eli anali m’modzi. Iye anatumikira Mulungu m’malo apadera a mkulu wansembe kwa zaka 40 ndipo anapatsidwanso thayo la kuweruza Aisrayeli. (1 Samueli 1:3, 9; 4:18) Ngakhale kuli tero, mkupita kwa nthaŵi iye anasonyeza kufooka kulinga kwa ana ake amuna Hofeni ndi Pinehasi. Ngakhale anali ansembe, iwo anagwiritsira ntchito molakwa malo awo mwa kuba zinthu zoperekedwa nsembe ndi mwa kudzilowetsa m’chisembwere chakugonana. Pamene atate wawo anangochita chochepa mwa kuwadzudzula iwo mopepuka, Mulungu analengeza kuti Eli ‘analemekeza ana ake kuposa ine.’ Yehova analonjeza kuti adzapitiriza ndi unsembe wa Aroni, koma akachotsapo nyumba ya Eli kuchoka pa udindo wa ukulu wa nsembe. Nchifukwa ninji? Mulungu analongosola kuti: “Amene andilemekeza ine, inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa ine, adzapeputsidwa.”—1 Samueli 2:12-17, 29-36; 3:12-14.
9. Kodi ndimotani mmene Samueli anapatsidwira mwaŵi wa kulemekeza Yehova?
9 Mosiyanako panali Samueli. Inu mwachidziŵikire mumadziŵa kuti makolo ake anamubweretsa iye pa msinkhu waung’ono kutumikira pa guwa la nsembe mu Silo. Usiku wina Yehova analankhula kwa mnyamatayo. Inu mungasangalale kuŵerenga cholembedwachi pa 1 Samueli 3:1-14, mukumalingalira kudzutsidwa kwa mnyamatayo, osati ndi kugunda kwa bingu, koma ndi liwu lotsika limene iye analilingalira molakwa kukhala la Eli wokalambayo. Kenaka lingalirani mmene chinakhalira chochititsa mantha kwa Samueli wachichepereyo kuuza mkulu wansembe wachikulireyo ponena za kulingalira kwa Mulungu kwakufuna kulanga nyumba ya Eli. Komabe Samueli anachichita icho; iye analemekeza Mulungu mwachimvero.—1 Samueli 3:18, 19.
10. M’kuyankha ku kulemekezedwa, ndimotani mmene Mulungu analemekezera Samueli?
10 Samueli analemekeza Yehova kwa zaka zingapo monga mneneri, ndipo Mulungu anamlemekeza iye. Tawonani ichi pa 1 Samueli 7:7-13. Yehova mwamsanga anayankha ku pemphero la Samueli kaamba ka thandizo lakugonjetsa Afilisti. Kodi inu simukanadzimva wolemekezeka kukhala ndi kuzindikiridwa kwa umulungu koteroko? Pamene ana a amuna a Samueli sanatsatire kutsogolera kwake, Mulungu sanamukane iye monga mmene anakanira Eli. Ichi mwachiwonekere chinali chifukwa chakuti Samueli anachita zonse zimene akanatha kulemekeza Mulungu. Akusonyeza ichi mowonjezereka, Samueli anakana pempho la anthu kaamba ka kukhala ndi mfumu ya umunthu. (1 Samueli 8:6, 7) Mulungu anagwiritsira ntchito Samueli kudzoza onse aŵiri Sauli ndi Davide. Pa imfa ya Samueli, Israyeli anamlemekeza iye mwa kulira. Chofunika koposa, ngakhale kuli tero, Mulungu anamlemekeza iye mwakumutchula iye m’Baibulo pakati pa anthu achikhulupiriro omwe adzadalitsidwa ndi chiukiriro ndi zinthu zabwino zimene Yehova Mulungu ali nazo kaamba ka iwo. (Masalmo 99:6; Yeremiya 15:1; Ahebri 11:6, 16, 32, 39, 40) Kodi ichi sichimasonyeza kuti kulemekeza “Mulungu wa chiyembekezo” kuli kwa phindu lalikulu?
Kodi Mudzalemekeza “Mulungu wa Chiyembekezo”?
11, 12. Nchiyani chomwe tifunikira kulingalira ponena za kulemekeza Yehova, ndipo ndi njira imodzi yotani yomwe ife tingachitire tero?
11 Nkhani za Yesu ndi Samueli, kungopereka kokha zitsanzo za m’Baibulo ziŵiri, zimakhazikitsa kuti anthu angaike kulemekeza “Mulungu wawo wa chiyembekezo” monga chinthu chapamwamba choyambirira m’moyo. Ndipo nkhani ziŵiri zimenezo zimasonyeza kuti mwakuchita kwake tero tingafune moyenerera ndi kulandira kulemekezedwa kuchokera kwa Mulungu. Koma kodi ndimotani mmene mungachitire ichi ndi chitsimikiziro choyenerera chakuti mudzakondweretsa Mulungu, mudzalemekezedwa ndi iye, ndipo mudzalandira chiyembekezo chanu chozikidwa pa Baibulo?
12 Kukhala ndi mantha enieni, olemekeza kaamba ka kusamukondweretsa Mulungu iri njira imodzi. (Malaki 1:6) Mwachidziŵikire ife timavomerezana mwamsanga ndi ndemanga imeneyo. Komabe, kumbukirani ana amuna a Eli. Ngati inu mukanawafunsa iwo kuti kaya anafuna kulemekeza Mulungu mwa kumuwopa iye mwaulemu, mwachidziŵikire kwenikweni iwo akanakhoza kunena kuti inde. Vuto limabwera pa kutembenuzira mu chenicheni cha ntchito m’moyo wa tsiku ndi tsiku chikhumbo chathu cha kulemekeza Mulungu mwa kumuwopa iye.
13. Chitirani chitsanzo mmene chikhumbo cha kulemekeza Yehova mwa kumuwopa iye chingatithandizire.
13 Ngati takumanizana ndi mkhalidwe woyesa mu umene ife tikhoza kuba kapena kudzilowetsa mu kulakwa kwina kwa kugonana popanda icho kukhala chodziŵika mwa chisawawa, kodi chikhumbo chathu cha kulemekeza Mulungu chidzayambukira ntchito yathu? Tifunikira kukulitsa lingaliro lakuti, ‘Ngakhale ngati kuchita zoipa kukhala kobisika, kugonjera kwanga kwenikweniko ku chimo loterolo kuli chosalemekeza “Mulungu wa chiyembekezo” amene ndimanyamula dzina lake.’ Ndipo nsonga iri yakuti choipa sichidzapitirizabe kukhala chobisika, monga mmene sizinachitire zinthu zimene ana amuna a Eli anachita. Ichi chikusonyezedwa m’mawu a Paulo onena za “kuweruza kolungama kwa Mulungu” kuti: “Adzabwezera munthu aliyense kulingana ndi ntchito zake: kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisawonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha; koma kwa iwo andewu, ndi osamvera chowonadi koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza.”—Aroma 2:5-8.
14. Kodi ndi m’njira ina yotani mu imene tingalemekezere Mulungu, ndipo kodi ndimotani mmene tingadzifunsire ife eni?
14 Kumbali ina, Paulo akutchula kutenga mbali “mu ntchito zokoma” zimene zimalemekeza Mulungu ndi kutulukamo “ulemerero ndi ulemu” kaamba ka iye. Ntchito yoyambirira ya mtundu umenewu lerolino iri imene Yesu anatchula pa Mateyu 28:19, 20: ‘Kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndikulamulirani inu.’ Kuzungulira pa dziko lonse lapansi, mamiliyoni a Mboni za Yehova ali okangalika mu ntchito yolemekeza Mulungu ya kulalikira ndi kuphunzitsa imeneyi. Ambiri akudzifutukula iwo eni kukhala atumiki a nthaŵi zonse monga apainiya, kaya pa maziko okhazikika kapena mkati mwa tchuthi cha ku ntchito kapena ku sukulu. Ndi ichi m’malingaliro, aliyense wa ife angalingalire mopindulitsa mmene iye akuimira ku ntchito imeneyi. Inu mungakhoze kudzifunsa, mwachitsanzo, ‘Kodi ndikulemekeza “Mulungu wa chiyembekezo” mwakukhala ndi kugawanamo kotheratu mu ntchito yolalikira?’
15. Kodi nchiyani chomwe chachitika kwa Akristu ena m’chigwirizano ndikulemekeza Yehova kudzera mu utumiki wapoyera?
15 Akristu ena amene kwa zaka zingapo akhala alaliki okangalika afooka mwapang’onopang’ono. Iwo alowa mu mkhalidwe wakungokhala kokha ndi kugawanamo kochepa kapena kosakhazikika mu ntchito yofunika ya kupanga ophunzira. Sitikutanthauza anthu amene ali ndi polekezera kaamba ka mavuto akuthupi ndipo afooka chifukwa cha zotulukapo za ukalamba. Kutalitali ndi zimenezo, kufooka kukuwoneka pakati pa Mboni zina za misinkhu yosiyanasiyana. Mosangalatsa, Paulo sanali kulozera ku gulu la msinkhu pamene anachenjeza Akristu molimbana ndi ‘kutopa’ mosiyanako, mosasamala kanthu za mmene msinkhu wa munthu ungakhalire, nsonga ya nkhani iri yakuti kugawanamo mokhazikika mu utumiki kumafunikira kuyesayesa. Monga mmene mwachiwonekere zinachitikira m’tsiku la Paulo, ena lerolino akulingalira kuti, ‘ndachita mbali yanga kwa zaka zingapo, chotero tsopano Akristu achatsopano angadzilowetsemo iwo eni.’—Agalatiya 6:9; Ahebri 12:3.
16. Kodi nchifukwa ninji tingapindule kuchokera ku kudzisanthula ife eni m’chigwirizano ndi ichi?
16 Awo omwe ayambukiridwa ndi njirayi ali ndithudi ochepa, koma inu mungafunse kuti, ‘Kodi ine ndithudi ndimazindikira chizolowezi chotero mwa ine ndekha? Kodi kugawanamo kwanga mu utumiki kumalinganizidwa motani ndi kuja kwa nthaŵi yapita?’ Ngakhale ngati kufooka kwachitika kapena ayi, tonsefe tifunikira kusunga m’malingaliro kuti “Mulungu wanthu wa chiyembekezo” walonjeza kupereka “ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino.” (Aroma 2:10) Paulo anagwiritsira ntchito liwu la Chigriki limene limatanthauza “kugwirira ntchito pa china chake, kutulutsa, kupanga.” Chiri chofunika chotani nanga kuti tipewe chimene chinagwera Afarisi ndi alembi omwe anangolemekeza Mulungu kokha ndi ntchito ya milomo! (Marko 7:6; Chivumbulutso 2:10) Mosiyanako, pamene kuchokera mu mtima tigawana mwachangu mu utumiki wapoyera, timatsimikizira kwa ife eni ndi kwa ena kuti tiri ndi chiyembekezo chenicheni. Timalemekeza Mlengi wanthu ndi Mpatsi wa moyo. Ndipo timabwera m’mzera wa kudzalemekezedwa ndi iye, tsopano ndi kosatha.—Luka 10:1, 2, 17-20.
Ndi Chuma Chathu
17, 18. Kodi ndi njira ina yotani mu imene tingalemekezere Mulungu, ndipo nchifukwa ninji kusinkhasinkha kuchita tero kuliri kolakwa?
17 Ponena za njira ina mu imene tingalemekezere “Mulungu wathu wa chiyembekezo”, Miyambo 3:9 imanena kuti: “Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha.” Spurrell amaika versili motere “Lemekezani Yehova ndi chuma chanu, ndi koposa zonse za chiwonjezeko chanu.”—A Translation of the Old Testament Scriptures from the Original Hebrew.
18 Popeza kuti atsogoleri achipembedzo ambiri adziŵika bwino lomwe kaamba ka umbombo wawo wopanda polekezera ndi kakhalidwe ka moyo kolemera, anthu ambiri amasinkhasinkha kupereka ku matchalitchi ndi magulu a zipembedzo amene cholinga chawo chimawonekera bwino lomwe kukhala kokha kukundika chuma. (Chivumbulutso 18:4-8) Kugwiritsira ntchito molakwa koteroko, ngakhale kuli tero, sikumasintha kuwona kwa Miyambo 3:9. M’chigwirizano ndi uphungu wouziridwa umenewo, kodi ndimotani mmene tingagwiritsire ntchito “chuma chathu” “kulemekeza Yehova,” “Mulungu wathu wa chiyembekezo”?
19. Chitirani chitsanzo mmene ena agwiritsira ntchito Miyambo 3:9.
19 Mboni za Yehova zapeza kuti chiŵerengero chomakulakula cha anthu omwe akuyankha ku uthenga wa Ufumu chimafunikira kukulitsa kwa Nyumba za Ufumu kapena kumanganso zatsopano. Chotero, pano, pali njira imodzi ya “kulemekeza Yehova ndi chuma chathu.” Achichepere ndi achikulire agawanamo m’kuchita chimenechi, monga ngati mwa kugamulapo mwaumwini kuthandizira ku ndalama za chimango. Kumamatira ku kugamulapo kwamseri koteroko kungafunikire kudziphunzitsa kwaumwini kapena ngakhale kudzimana kwina kwake, makamaka ngati makonzedwe ndi kutha kwa ntchito yomanga kutalikira pa nyengo yaitali ya nthaŵi. (2 Akorinto 9:6, 7) Chikhalirechobe, kugwiritsira ntchito ndalama mwanjira imeneyi kumalemekeza Yehova mowonadi, popeza kuti Nyumba za Ufumu ziri malo kumene Akristu amamlambira iye ndi kumene iwo ndi oyanjana nawo awo amapeza chidziŵitso cha Mulungu. Mawu a Yesu pa Mateyu 6:3, 4 amatipatsa chifukwa chabwino cha kukhulupirira kuti Mulungu adzalemekeza awo omwe amulemekeza iye.
20. (a) Nchifukwa ninji kudzifufuza kwaumwini kuli koyenera m’kugwiritsira ntchito Miyambo 3:9? (b) Ndi mafunso otani omwe tingadzifunse ife eni?
20 Mawu achenjezo, ngakhale kuli tero: Afarisi ndi alembi, amene Yesu ananena kuti sanali kuika patsogolo kulemekeza Mulungu, anatsimikizira kuti iwo anali oyambirira kupindula m’chuma chawo. Chotero uphungu wa pa Mateyu 15:4-8 umayamikira kuti ife tidzigonjetsere ku kudzifufuza kwaumwini ponena za ‘kulemekeza Yehova ndi chuma chathu.’ (Yeremiya 17:9, 10) Mwachitsanzo, Mkristu yemwe wakhala wolemera kupyolera mu bizinesi yake angalungamitse kupitirizabe kwake kugwira ntchito mokhazikika kotero kuti apeze zambiri zowonjezereka. Iye angalingalire kuti, ‘Ena akulowa mu utumiki wa upainiya kapena kupita kukatumikira kumene alaliki ali osowa kwenikweni, koma njira yanga yapadera ya kutumikira Mulungu iri mwa kukundika zambiri ndipo kenaka kukhalanso ndi zambiri zopereka.’ Zopereka zake zingachite ubwino wokulira. Koma iye akachita bwino kudzifunsa kuti ‘Kodi khalidwe la moyo wanga waumwini limawunikira kuti kugwiritsira ntchito ndalama kulemekeza Mulungu kuli cholinga changa choyambirira kaamba ka kukundikira zambirimbiri?’ (Luka 12:16-19; yerekezani ndi Marko 12:41-44.) Ndipo, ‘Kodi ndingakhoze kulinganiza zochita zanga kuti ndikhale ndi kugawanamo kwaumwini kokulira mu ntchito yofunika koposa kaamba ka tsiku lathu—ya kulengeza mbiri yabwino?’ M’chenicheni, mosasamala kanthu za chimene mkhalidwe wathu m’moyo ungakhale, tingasanthule zolinga zathu ndi ntchito ndi kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingalemekeze mokulira chotani Mpatsi wa moyo wanga ndi “Mulungu wa chiyembekezo”?’
21. Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene tiri nacho ngati tilemekeza Yehova tsopano?
21 Yehova sadzatigwiritsa mwala. Ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri chotani nanga chimene icho chiri kuti iye angakhoze, tsopano ndi kupitirizabe mpaka mtsogolo, kunena ponena za ife chomwe ananena kwa Aisrayeli okhulupirika kuti: “Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe”! (Yesaya 43:4) M’modzimodziyo walonjeza “moyo wosatha kwa awo omwe akufuna ulemu ndikulemekezeka.” Lonjezo limeneli iye akulilunjikitsa kwa awo omwe apirira “mu ntchito yabwino.” Ndi “Mulungu wa chiyembekezo” wotani nanga!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Ponena za kulemekeza Yehova kwa anthu, kodi nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku chitsanzo cha Yesu?
◻ Kodi ndimotani mmene Eli ndi Samueli anasiyanirana ponena za kulemekeza Mulungu?
◻ Kodi ndi njira zina ziti m’zimene mungawonjezere kulemekeza kumene mumabweretsa kwa Mulungu, ndipo kodi ndi kuyankha kotani kumene mungalandire?
◻ Kodi ndi mtsogolo motani mmene mukuyembekezera awo omwe amaika choyamba kulemekeza “Mulungu wathu wa chiyembekezo”?
[Bokosi patsamba 20]
MAKALATA ONENA ZA ZOPEREKA
Pano pali chidule cha zochokera m’makalata olandiridwa ndi ofesi ya Watch Tower Society ku Brooklyn, New York:
“Dzina langa ndine Abijah. Ndiri ndi zaka zisanu ndi zinayi zakubadwa. Ndifuna kukupatsani $4 kaamba ka abale omwe akugwira ntchito pa Nyumba za Ufumu. Iwo angaigwiritsire ntchito iyo kaamba ka zakudya zirizonse zazing’ono kapena zonzuna, ndiribe nazo kanthu.”—Oregon.
‘Mudzapeza chitatsekeredwa muno cheke chaumwini. Ndapitirira pa zaka 96 zakubadwa ndipo ndiri ndi vuto la kumvetsera, koma ndimasangalala ndi kusunga ndalama zanga kaamba ka ichi. Inde, ndimadziŵa, ndikuyendetsa galimoto lakale, ndipo sindimawonongera nyengo zanga za chisanu mu Florida kapena California. Ndingachite zochepera chotere kulinga ku kupangitsa mbiri yabwino ya Ufumu kulalikidwa mwa kugogoda pa zitseko. Koma mwa kusunga ndalama zanga ndi kutumiza zina kwa inu, ndimadzimva kuti ndikukhalabe ndi mbali mu iyo.’—Ohio.
‘Ndikuyamikani kaamba ka zirizonse zimene munachita kaamba ka Nyumba ya Ufumu. Ndalamayi [$5] iri ya kukuthandizani inu ndi mabukhu ndi Nsanja za Olonda kaamba ka ife kuti tiŵerenge. Ndalamayi yachokera ku chitini changa chosungiramo ndalama. Ndikuyamikani kaamba ka broshuwa ya School kutiwuza ife ponena za anamgoneka.’
“Chonde pezani cheke chotsekeredwa muno. Madola mazana aŵiri a iyo ali kaamba ka thumba la Ndalama Zomangira Nyumba za Ufumu. Zotsalazo zidzagwiritsiridwa ntchito m’njira iriyonse imene mukuwona kukhala yoyenera kuchirikiza ntchito yolalikira.”—Missouri.