Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Anakumana ndi Mavuto
SAMUELI anadziwa kuti anthu ku Silo ali ndi chisoni chachikulu. Zinkaoneka kuti anthu m’tawuni yonseyi ankalira maliro. Sitikudziwa kuti ndi azimayi ndi ana angati amene ankalira chifukwa cha nkhani yomvetsa chisoni ya abambo awo, amuna awo, ana awo ndi achibale amene anaphedwa kunkhondo. Chomwe tikudziwa ndi choti pa nthawiyi Aisiraeli okwanira 30,000 anali ataphedwa pa nkhondo yoopsa yomenyana ndi Afilisiti. Koma zimenezi zinachitika pasanathe nthawi yaitali kuchokera pamene Aisiraeli enanso 4,000 anaphedwa pa nkhondo ina.—1 Samueli 4:1, 2, 10.
Komatu limeneli linali vuto limodzi chabe mwa mavuto ambirimbiri amene Aisiraeli anakumana nawo. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Likasa la Yehova linalandidwa. Mkulu wa Ansembe Eli anali ndi ana aamuna awiri oipa kwambiri. Mayina awo anali Hofeni ndi Pinehasi ndipo iwo ananyamula Likasa lopatulika la pangano kuchokera ku Silo. Likasa limeneli linkakhala m’malo opatulika m’chihema chomwe chinali kachisi wooneka ngati tenti, ndipo chinali chizindikiro chakuti Mulungu ali pamalowo. Aisiraeli anatenga Likasalo n’kupita nalo kunkhondo poganiza kuti likakhala ngati chithumwa. Komatu pamenepa anthuwa sanaganize bwino chifukwa Afilisiti analanda Likasalo ndipo anapha Hofeni ndi Pinehasi.—1 Samueli 4:3-11.
Kwa zaka zambiri anthu ankalemekeza chihema chopatulika chimene chinali ku Silo chifukwa chakuti kunali Likasa. Koma tsopano Likasali linali litalandidwa. Eli, amene pa nthawiyi anali ndi zaka 98, atamva kuti Likasa lalandidwa anagwa pampando chagada ndipo anafa. Mpongozi wake, yemwenso mwamuna wake anali ataphedwa ku nkhondo tsiku lomweli, anamwaliranso akubereka. Mayiyo asanamwalire ananena kuti: “Ulemerero wachoka mu Isiraeli kupita kudziko lina.” Zimenezi zinalidi zoona chifukwa zinthu zinali zitasinthiratu ku Silo.—1 Samueli 4:12-22.
Kodi Samueli anatani kuti apirire mavuto aakulu amenewa? Kodi iye anali ndi chikhulupiriro cholimba moti akanatha kuthandiza anthu amenewa, omwe Yehova anali atasiya kuwateteza ndiponso kuwakonda? Masiku ano tonsefe nthawi zina timakumana ndi mavuto ndiponso zokhumudwitsa zimene zimaika chikhulupiriro chathu pa mayesero. Choncho tiyeni tione zimene tikuphunzira kwa Samueli.
Iye “Anachita Chilungamo”
Pambuyo pofotokoza za kulandidwa kwa Likasa lopatulika, Baibulo silipitiriza kunena za Samueli. M’malomwake limafotokoza za Likasalo ndiponso zimene Afilisti anakumana nazo chifukwa cholanda Likasa zomwe zinachititsa kuti akakamizike kukalibweza. Pamene Baibulo likunenanso za Samueli, n’kuti patapita zaka 20. (1 Samueli 7:2) Kodi Samueli anali akuchita chiyani zaka zimenezi? Baibulo limatiuza zimene ankachita.
Baibulo limasonyeza kuti nthawi imeneyi isanafike, “Samueli anapitiriza kulankhula ndi Aisiraeli onse.” (1 Samueli 4:1) Limasonyezanso kuti pambuyo pa zaka 20 zimenezi, Samueli ankayendera mizinda itatu ya Isiraeli, ndipo ankazungulira m’maderawa chaka chilichonse kuweruza Aisiraeli. Akayendera madera amenewa, iye ankabwerera kwawo ku Rama. (1 Samueli 7:15-17) Zimenezi zikusonyeza kuti Samueli anali munthu wotanganidwa kwambiri ndipo pa zaka 20 zimenezi anali ndi zochita zambiri.
Chinyengo ndiponso khalidwe lachiwerewere la ana a Eli linasokoneza chikhulupiriro cha anthu. Zikuoneka kuti zimenezi zinachititsa anthu ambiri kuyamba kulambira mafano. Komabe atatha zaka 20 akugwira ntchito mwakhama, Samueli anauza anthuwo kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu. Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti, ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina, ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”—1 Samueli 7:3.
Aisiraeli ankavutika kwambiri chifukwa chokhala “m’manja mwa Afilisiti.” Popeza kuti asilikali a Isiraeli anali atagonjetsedwa, Afilisiti ankaona kuti anali ndi ufulu wonse wozunza anthu a Mulunguwo. Koma Samueli anawatsimikizira kuti ngati atabwerera kwa Yehova zinthu zikhoza kusintha. Kodi Aisiraeli analidi okonzeka kubwerera kwa Yehova? Samueli anasangalala kwambiri kuona kuti iwo asiyadi mafano awo “n’kuyamba kutumikira Yehova yekha.” Kenako Samueli anaitanitsa msonkhano ku Mizipa, tauni ya kumapiri imene inali cha kumpoto kwa Yerusalemu. Anthuwo anasonkhanadi kumeneko ndipo anasala kudya komanso analapa machimo awo ndipo anasiya kulambira mafano.—1 Samueli 7:4-6.
Koma Afilisiti anamva kuti Aisiraeli asonkhana ku Mizipa ndipo anaona kuti umenewu unali mwayi woti akamenyane nawo. Choncho iwo anatumiza gulu lawo lankhondo ku Mizipa kuti likawononge anthu a Yehova. Aisiraeli atamva kuti Afilisiti akubwera, anachita mantha kwambiri ndipo anapempha Samueli kuti awapempherere. Samueli anachitadi zimenezi ndipo anapereka nsembe. Mwambo wapadera umenewu uli mkati, gulu lankhondo la Afilisiti linafika ku Mizipa. Koma Yehova anayankha pemphero la Samueli. Ndipo posonyeza mkwiyo wake, Yehova “anachititsa mabingu amphamvu kwambiri pa tsiku limenelo kuti asokoneze Afilisiti.”—1 Samueli 7:7-10.
Koma tisaganize kuti Afilisti anali ngati ana amene akangomva kulira kwa mabingu amathamangira kwa amayi awo kuti akabisale chifukwa cha mantha. Iwo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo. Koma mabingu amenewa anali asanawamvepo chiyambire. Kodi chinawaopsa kwambiri Afilisitiwa kunali kugunda kwamphamvu kwa mabinguwa? Kapena ndi chifukwa chakuti mabinguwa anachitika kumwamba kulibe mtambo ngakhale umodzi? Kapena chinali chifukwa chakuti phokoso la mabinguwo linkamveka kuchokera kumapiri, ndipo linali logonthetsa m’khutu? Kaya chinawachitisa mantha ndi chiyani, koma mfundo ndi yakuti Afilisiti anasokonezeka ndipo anaopa kwambiri. Chifukwa cha kusokonezekaku, zinthu zinasintha mofulumira. Afilisiti, omwe ankazunza Aisiraeli, anatheratu mphamvu. Asilikali a Isiraeli anabwera kuchokera ku Mizipa ndipo anagonjetsa Afilisiti n’kuwathamangitsa mpaka kum’mwera cha kumadzulo kwa Yerusalemu.—1 Samueli 7:11.
Nkhondo imeneyi inali chiyambi cha kusintha kwa zinthu pakati pa anthu a Mulungu. Pa nthawi yonse imene Samueli anali woweruza, Afilisiti ankaopa kumenyana ndi Aisiraeli. Pang’ono ndi pang’ono anthu a Mulungu anayamba kulandanso mizinda yawo imene inali m’manja mwa Afilisiti.—1 Samueli 7:13, 14.
Patapita zaka zambiri mtumwi Paulo anatchula Samueli pa mndandanda wa oweruza ndiponso aneneri okhulupirika amene “anachita chilungamo.” (Aheberi 11:32, 33) Samueli anathandizadi kwambiri kuti anthu achite zabwino ndiponso zoyenera pamaso pa Mulungu. Iye anatha kuchita zimenezi chifukwa chakuti anayembekezera Yehova moleza mtima ndipo anapitirizabe kugwira ntchito yake mokhulupirika ngakhale kuti panali mavuto osiyanasiyana. Samueli anali ndi mtima woyamikira moti Aisiraeli atapambana nkhondo ku Mizipa, Samueli anaimika mwala wachikumbutso kuti azikumbukira mmene Yehova anathandizira anthu ake.—1 Samueli 7:12.
Kodi nanunso mumalakalaka ‘mutamachita chilungamo’? Ngati ndi choncho, mungaphunzire zambiri pa kuleza mtima, kudzichepetsa komanso mtima woyamikira wa Samueli. Ndipo tonsefe tifunika kukhala ndi makhalidwe amenewa. Kuphunzira makhalidwe amenewa ali mwana, kunamuthandiza kwambiri Samueli chifukwa mu ukalamba wake anakumana ndi mavuto ambiri.
“Ana Ako Sakutsatira Chitsanzo Chako”
Nthawi yotsatira pamene Baibulo limanenanso za Samueli, n’kuti “atakalamba.” Pa nthawiyi Samueli anali ndi ana amuna awiri akuluakulu, Yoweli ndi Abiya ndipo anawasankha kuti azimuthandiza pa ntchito yoweruza. Koma chomvetsa chisoni ndi chakuti iye sanasankhe bwino. Ngakhale kuti Samueli anali woona mtima ndiponso wachilungamo, ana akewa anagwiritsa ntchito molakwa udindo wawo. Iwo sankaweruza mwachilungamo ndiponso ankalandira ziphuphu.—1 Samueli 8:1-3.
Tsiku lina akulu a mu Isiraeli anapita kwa mneneri wokalambayu ndipo anamudandaulira kuti: “Ana ako sakutsatira chitsanzo chako.” (1 Samueli 8:4, 5) Koma kodi Samueli ankadziwa zimene ana akewa ankachita? Baibulo silinena ngati ankadziwa kapena ayi. Koma Samueli anali wosiyana ndi Eli chifukwa sanali bambo wolekerera ana. Yehova anadzudzula komanso kulanga Eli chifukwa ankalephera kulangiza ana ake oipa ndiponso chifukwa iye ankalemekeza ana akewo kuposa Mulungu. (1 Samueli 2:27-29) Koma Yehova anaona kuti Samueli anali wosiyana ndi Eli.
Baibulo silifotokoza mmene Samueli anachitira manyazi, kuda nkhawa ndiponso kukhumudwa atamva za khalidwe loipa la ana akewa. Koma makolo ambiri angamvetse mmene iye anamvera atamva za khalidwe la ana akewa. Masiku ano m’dziko lovutali, ana ambiri samvera malangizo a makolo awo. (2 Timoteyo 3:1-5) Makolo amene akuvutika maganizo chifukwa chakuti ana awo analowerera, angalimbikitsidwe ndiponso kupeza malangizo poganizira chitsanzo cha Samueli. Iye sanalole kuti kusakhulupirika kwa ana ake kusinthe khalidwe lake labwino ngakhale pang’ono. Ndipo musaiwale kuti ngakhale mwana wanu atapanda kusintha pambuyo poti mwamulankhula kapena kum’patsa malangizo, nthawi ina iye akhoza kudzasintha chifukwa choona khalidwe lanu labwino. Komanso mofanana ndi Samueli, makolo nthawi zonse ayenera kuchita zinthu zimene zingasangalatse Atate wawo, Yehova Mulungu.
“Tikufuna Kuti Utiikire Mfumu”
Ana a Samueli sanaganizire n’komwe za mavuto amene angabwere chifukwa cha khalidwe lawo ladyera komanso lodzikondalo. Akulu a mu Isiraeli anayamba kuuza Samueli kuti: “Tikufuna kuti utiikire mfumu yoti izitiweruza ngati mitundu ina yonse.” Kodi pamenepa Samueli anaona kuti anthuwo akumukana iyeyo? Samueli anali atagwira ntchito yoweruza Aisiraeli m’malo mwa Yehova kwa zaka zambiri. Koma tsopano Aisiraeli anati akufuna mfumu yoti iziwalamulira, osati mneneri chabe ngati Samueli. Mitundu yonse yowazungulira inali ndi mafumu awo choncho Aisiraeli anafuna kuti nawonso akhale ndi mfumu. Kodi Samueli anamva bwanji ndi zimenezi? Baibulo limati: “Zimenezi zinamuipira” Samueli.—1 Samueli 8:5, 6.
Koma tamvani zimene Yehova anayankha Samueli atamuuza nkhaniyi m’pemphero. Yehova anati: “Mvera zonse zimene anthuwo akunena kwa iwe, pakuti sanakane iweyo koma akana ine kuti ndisakhale mfumu yawo.” Mawu a Yehova amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri Samueli. Komabe mawuwa anasonyeza kuti anthuwo anachitira Mulungu Wamphamvuyonse chipongwe chachikulu. Yehova anauza mneneri Samueli kuti achenjeze Aisiraeli za kuipa kokhala ndi munthu woti aziwalamulira ngati mfumu yawo. Koma Samueli atawachenjeza, iwo anaumirirabe kuti: “Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulira.” Popeza nthawi zonse Samueli ankamvera Mulungu, iye anapita kukadzoza mfumu imene Yehova anasankha.—1 Samueli 8:7-19.
Komano kodi Samueli anamvera Mulungu mochokera pansi pa mtima? Kapena kodi iye anachita zinthu moipidwa ndiponso monyinyirika? Kodi iye analola kuti mavuto amenewa aipitse mtima wake, n’kumangokhala wokhumudwa nthawi zonse? Anthu ambiri akanachita zimenezo, koma Samueli sanatero. Iye anadzoza Sauli kukhala mfumu ndipo anavomereza kuti anali munthu amene Yehova wamusankha. Anam’psompsona Sauli posonyeza kusangalala naye ndiponso kumugonjera monga mfumu yatsopano. Ndiyeno anauza anthuwo kuti: “Kodi mwaona amene Yehova wam’sankha, kuti palibe aliyense pakati pa anthu onse wofanana naye?”—1 Samueli 10:1, 24.
Samueli sanaganizire kwambiri zolakwa za Sauli, munthu amene Yehova anamusankha, koma anaganizira za makhalidwe abwino a Sauli. Ndiponso Samueli anaganizira kwambiri za kukhulupirika kwake kwa Mulungu, osati zakuti anthu osakhulupirikawo azimukonda. (1 Samueli 12:1-4) Komanso anagwira mokhulupirika ntchito imene Mulungu anamupatsa yolangiza anthu a Mulungu za mavuto amene ankakumana nawo ndipo anawalimbikitsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Anthuwo anakhudzidwa kwambiri ndi malangizowo ndipo anamupempha kuti awapempherere. Iye anawayankha mawu olimbikitsa akuti: “N’zosatheka kuti ineyo ndichimwire Yehova mwa kusiya kukupemphererani. Ndipo ndiyenera kukulangizani za njira yabwino ndi yolondola.”—1 Samueli 12:21-24.
Kodi munayamba mwakhumudwapo chifukwa chakuti munthu wina wasankhidwa kapena kupatsidwa mwayi winawake? Chitsanzo cha Samueli chikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yakuti sitiyenera kukhala ndi mkwiyo kapena maganizo ansanje mu mtima mwathu. Nthawi zonse Mulungu amadalitsa mtumiki wake aliyense ndiponso kumupatsa zochita.
“Kodi Ulirira Sauli Mpaka Liti?”
Samueli sanalakwitse kuyembekezera kuti Sauli achita zinthu zabwino chifukwa Sauli anali munthu wapadera kwambiri. Iye anali wamtali, wooneka bwino, wolimba mtima, wodziwa zambiri ndipo poyamba anasonyeza kuti anali wodzichepetsa ndiponso wosachita zinthu modzionetsera. (1 Samueli 10:22, 23, 27) Komanso anali ndi mphatso ina yapadera imene ndi ufulu wosankha. Anali ndi ufulu wosankha kuti akufuna kukhala munthu wotani ndiponso kusankha yekha zimene akufuna kuchita. (Deuteronomo 30:19) Komano kodi Sauli anagwiritsa ntchito mwanzeru ufulu umenewu?
N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amati akapatsidwa udindo waukulu, amayamba kudzikweza. Pasanapite nthawi, Sauli anayamba kudzikuza. Iye anasankha kusamvera malamulo a Yehova amene Samueli ankamupatsa. Tsiku lina Sauli analephera kudikira ndipo anapereka nsembe yomwe Samueli yekha ndi amene ankayenera kupereka. Samueli anadzudzula kwambiri Sauli ndipo anamuuziratu kuti ufumu sudzapitiriza kukhala m’banja lake. Koma m’malo moti aphunzirepo kanthu pa zimene Samueli anamuuza, Sauli anapitiriza kuchita zinthu zosamvera.—1 Samueli 13:8, 9, 13, 14.
Nthawi ina kudzera mwa Samueli, Yehova anauza Sauli kuti akagonjetse Aamaleki. Ena mwa malangizo amene Yehova anapatsa Sauli anali akuti aphe Agagi yemwe anali mfumu yoipa ya Aamaleki. Koma Sauli sanaphe Agagi ndiponso sanawononge zinthu zabwino zimene analanda kunkhondoko ngakhale kuti Yehova analamula kuti ziwonongedwe. Samueli atapita kukamuuza Sauli za kuipa kwa zimene anachitazo, Sauli anasonyezeratu kuti anali atasintha kwambiri. M’malo modzichepetsa n’kuvomereza kuti analakwa, Sauli anayamba kunena zinthu zambiri zodziikira kumbuyo, kupereka zifukwa zimene anachitira zimenezi, kudzilungamitsa, kusafuna kuti akambiranebe nkhaniyo komanso kuloza chala anthu. Sauli atayamba kupeputsa ndiponso kukana malangizo ponena kuti zina mwa zinthu zimene analanda kunkhondoko zinali zoti akazipereke nsembe kwa Yehova, Samueli anamuuza mawu amene anthu ambiri amawadziwa masiku ano akuti: “Kumvera kuposa nsembe.” Samueli anadzudzula Sauli molimba mtima ndipo anamuuza maganizo a Yehova pa nkhaniyo. Iye anamuuza kuti ufumu udzachotsedwa kwa Sauliyo n’kuperekedwa kwa munthu wina.—1 Samueli 15:1-33.
Samueli anakhumudwa kwambiri ndi machimo a Sauli. Iye anachezera usiku wonse kupemphera kwa Yehova za nkhaniyi. Samueli anafika mpaka polirira Sauli kwambiri. Poyamba Samueli ankaona kuti Sauli angathe kuchita bwino pa zinthu zambiri. Koma tsopano zonse zimene ankayembekezera mwa Sauli zinathera pompo. Munthu amene poyamba ankamudziwa kuti anali wabwino uja anali atasinthiratu. Iye anali atasiya kusonyeza makhalidwe ake abwino ndiponso kutsatira malangizo a Yehova. Chifukwa cha chisoni, Samueli anakana kuonananso ndi Sauli. Koma patapita nthawi Yehova analangiza Samueli mwachikondi kuti: “Kodi ulirira Sauli mpaka liti, pamene ine ndamukana kuti alamulire monga mfumu ya Isiraeli? Thira mafuta m’nyanga yako ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu, chifukwa ndapeza munthu pakati pa ana ake aamuna woti akhale mfumu yanga.”—1 Samueli 15:34, 35; 16:1.
Kuti Yehova akwaniritse cholinga chake sadalira anthu opanda ungwiro omwe nthawi zina amakhala osakhulupirika. Munthu wina akasiya kukhala wokhulupirika kwa iye, Yehova amagwiritsa ntchito wina kuti akwaniritsebe zolinga Zake. Choncho Samueli anasiya kulirira Sauli. Potsatira malangizo a Yehova, Samueli anapita ku Yerusalemu, kunyumba kwa Jese komwe anakapeza ana aamuna angapo a Jese ooneka bwino. Koma Yehova anali atamuuza kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake . . . Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Samueli 16:7) Kenako Samueli anaona Davide, yemwe anali wamng’ono pa ana onse a Jese, ndipo anazindikira kuti ameneyu ndi amene Yehova anamusankha.
Cha kumapeto kwa moyo wake, Samueli anaona kuti Yehova anachita bwino kusankha Davide kuti alowe m’malo mwa Sauli chifukwa Sauli anayamba nsanje kwambiri moti anafuna kupha Davide komanso anayamba mpatuko. Koma Davide anali ndi makhalidwe abwino kwambiri. Iye anali wolimba mtima, wokhulupirika komanso anali ndi chikhulupiriro cholimba. Pamene Samueli ankakalamba, chikhulupiriro chake chinkalimbanso kwambiri. Iye anaona kuti palibe mavuto omwe ndi akulu kwambiri moti Yehova sangathe kuwathetsa kapena kuwasandutsa madalitso. Kenako Samueli anamwalira ndipo anasiya mbiri yabwino yomwe inakhalapobe kwa zaka zambiri. N’chifukwa chake ndi zosadabwitsa kuti Aisiraeli onse anamulira munthu wokhulupirika ameneyu. Masiku anonso atumiki a Yehova angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikutsanzira chikhulupiriro cha Samueli?’
[Chithunzi patsamba 25]
Kodi Samueli akanathandiza bwanji Aisiraeli kupirira imfa ya abale awo komanso mavuto ena?
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi Samueli anapirira bwanji vuto la kukhala ndi ana osamvera?