Yehova Amachita Chilungamo Nthawi Zonse
“Yehova ali wolungama m’njira zake zonse.”—SALMO 145:17.
1. Kodi mumamva bwanji wina akakuganizirani molakwa, ndipo tingatengepo phunziro lotani pamenepa?
KODI munthu anayamba wakuganizirani molakwa, mwina kukayikira zimene mwachita kapena zolinga zanu, koma asakudziwa tsatanetsatane wa nkhaniyo? Ngati zinakuchitikiranipo, ziyenera kuti zinakupwetekani mtima, ndipo m’pomveka. Tingatengepo phunziro lofunika kwambiri pamenepa: Sitiyenera kufulumira kukayikira munthu ngati tilibe chithunzi chonse cha nkhaniyo.
2, 3. Kodi ena amamva bwanji ndi nkhani za m’Baibulo zosakhala ndi mfundo zatsatanetsatane zoti n’kuyankha mafunso athu onse, koma Baibulo limatiuzanji za Yehova?
2 Tiyenera kukumbukira phunziro limeneli tikamaganizira zimene Yehova Mulungu anachita. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti m’Baibulo muli nkhani zina zimene poyamba zingaoneke ngati zosamvetsetseka. Nkhani zimenezi, kaya zokhudza zimene olambira Mulungu ena anachita, kapena ziweruzo zimene Mulungu anapereka kalelo, sizingakhale zatsatanetsatane moti n’kuyankha mafunso athu onse. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amakhumudwa ndi nkhani zimenezo, mwinanso kufika pokayikira kulungama kwa Mulungu. Komatu Baibulo limatiuza kuti “Yehova ali wolungama m’njira zake zonse.” (Salmo 145:17) Mawu ake amatitsimikiziranso kuti iye “sangachite choipa.” (Yobu 34:12; Salmo 37:28) Ndiye tangolingalirani mmene amamvera ena akamuganizira molakwa!
3 Tiyeni tikambirane zifukwa zisanu zimene tiyenera kuvomerezera ziweruzo za Yehova. Ndiye tikuganizira zifukwa zimenezo, tikambirane nkhani ziwiri za m’Baibulo zimene ena angavutike nazo maganizo.
Chifukwa Chiyani Tiyenera Kuvomereza Ziweruzo za Yehova?
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzichepetsa poganizira zochita za Mulungu? Perekani chitsanzo.
4 Choyamba, popeza kuti Yehova amadziwa mfundo zonse ndipo ife sitidziwa zonse, tiyenera kudzichepetsa tikamaganizira zochita za Mulungu. Tiyeni tiyerekeze kuti woweruza milandu amene amadziwika kwambiri kuti amaweruza mosakondera, wapereka chigamulo pa mlandu winawake m’khoti. Mungamuone bwanji munthu amene akutsutsa chigamulo chimenecho popanda kudziwa zonse zokhudza mlanduwo, kapena kumvetsa malamulo okhudza nkhaniyo? Kungakhale kupusa kutsutsa nkhani imene sukuidziwa bwino. (Miyambo 18:13) Ndiyetu n’kupusa kwakukulu zedi kuti anthu opanda pakefe titsutse ‘Woweruza wa dziko lonse lapansi.’—Genesis 18:25.
5. Kodi sitiyenera kuiwala chiyani tikamawerenga nkhani za m’Baibulo zofotokoza mmene Mulungu anaweruzira anthu ena?
5 Chifukwa chachiwiri chovomerezera ziweruzo za Mulungu n’chakuti, mosiyana ndi anthu, Mulungu amatha kudziwa za mu mtima wa munthu. (1 Samueli 16:7) Mawu ake amati: “Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa imso, kuti ndim’patse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.” (Yeremiya 17:10) N’chifukwa chake tikamawerenga nkhani za m’Baibulo zofotokoza mmene Mulungu anaweruzira anthu ena, tisaiwale kuti popeza amaona zonse, anaweruza mogwirizana ndi malingaliro ndiponso zolinga zobisika za munthuyo, zimene sizinalembedwe m’Mawu ake.—1 Mbiri 28:9.
6, 7. (a) Kodi Yehova wasonyeza motani kuti amatsatirabe miyezo yake yolungama ngakhale pamene kutero kungam’tayitse zambiri? (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikawerenga nkhani ina m’Baibulo imene yatichititsa kukayika ngati Mulungu anachita cholungama ndi choyenera?
6 Nachi chifukwa chachitatu chovomerezera ziweruzo za Yehova: Amatsatirabe miyezo yake yolungama ngakhale pamene kutero kungam’tayitse zambiri. Mwachitsanzo, popereka Mwana wake monga dipo lomasula anthu omvera ku uchimo ndi imfa, Yehova anakwaniritsa miyezo yake yolungama. (Aroma 5:18, 19) Ngakhale anatero, kuona Mwana wake akuzunzika ndi kufa pa mtengo wozunzikirapo kuyenera kuti kunam’pweteka kuposa china chilichonse. Kodi zimenezi zikutiuza chiyani za Mulungu? Baibulo, ponena za “chiwombolo cha mwa Kristu Yesu” limati, Mulungu anatero “kuti aonetse chilungamo chake.” (Aroma 3:24-26) Baibulo lina, pa Aroma 3:25 limati: “Zimenezi zimasonyeza kuti nthawi zonse Mulungu amachita cholungama ndi choyenera.” (Baibulo la New Century Version) Inde, zimene Yehova anachita mofunitsitsa kuti apereke dipo, zikusonyeza kuti amalemekeza kwambiri “cholungama ndi choyenera.”
7 Chotero, tikawerenga nkhani ina m’Baibulo imene imachititsa anthu ena kukayikira ngati Mulungu anachita cholungama ndi choyenera, tiyeni tikumbukire mfundo iyi: Chifukwa chotsatira mokhulupirika miyezo yake ya chilungamo, Yehova sanateteze ngakhale Mwana wake wa iye yekha kuti asakumane ndi imfa yopweteka kwambiri. Ndiye kodi angalephere kutsatira miyezo yakeyo pa nkhani zina? Zoona zake n’zakuti, Yehova saphwanya m’pang’ono pomwe miyezo yake yolungama. Chotero tili ndi zifukwa zokwanira zokhulupirira kuti nthawi zonse amachita cholungama ndi choyenera.—Yobu 37:23.
8. N’chifukwa chiyani zingakhale zosamveka anthu kuganiza kuti mwina Yehova alibe chilungamo?
8 Talingalirani chifukwa chachinayi ichi chimene tiyenera kuvomerezera ziweruzo za Yehova: Yehova anapanga munthu m’chifanizo Chake. (Genesis 1:27) Choncho anthu anapatsidwa mikhalidwe yofanana ndi ya Mulungu, kuphatikizapo mkhalidwe wofuna chilungamo. Sizingakhale zomveka ngati malingaliro athu ofuna chilungamo atichititsa kuganiza kuti mwina Yehova alibe mkhalidwe umenewu. Ngati tikuvutika maganizo chifukwa cha nkhani inayake ya m’Baibulo, tiyenera kukumbukira kuti uchimo wathu wobadwa nawo umachititsa kaonedwe kathu ka chilungamo kukhala kopanda ungwiro. Yehova Mulungu, amene tinalengedwa m’chifanizo chake, ndi wangwiro pochita chilungamo. (Deuteronomo 32:4) Sizingakhale zomveka kuganiza, ngakhale pang’ono, kuti anthu angakhale olungama kuposa Mulungu!—Aroma 3:4, 5; 9:14.
9, 10. N’chifukwa chiyani palibe chifukwa choti Yehova afotokozere anthu zifukwa zonse zimene wachitira zinthu zina?
9 Chifukwa chachisanu chovomerezera ziweruzo za Yehova n’chakuti iye ndiye “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Chotero, palibe chifukwa choti afotokozere anthu zifukwa zonse zimene wachitira zakutizakuti. Iye ndi Woumba Mbiya Wamkulu, ndipo ife tili ngati dothi limene waliumba kukhala ziwiya, kuti achite nafe mmene akufunira. (Aroma 9:19-21) Ife ziwiya zoumbidwa ndi iye, ndife ayani kuti titsutse zosankha kapena zochita zake? Mwamuna wakaleyo Yobu, ataganizira molakwa zimene Mulungu anachita kwa anthu, Yehova anamuwongolera pom’funsa kuti: “Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?” Pozindikira kuti analankhula asakudziwapo kalikonse, Yobu analapa. (Yobu 40:8; 42:6) Tiyesetse kusachita cholakwa chimenechi choona Mulungu ngati wolakwa.
10 Ndithudi, tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti Yehova amachita chilungamo nthawi zonse. Poganizira mfundo zimenezi zotithandiza kumvetsa njira za Yehova, tiyeni tsopano tikambirane nkhani ziwiri za m’Baibulo zimene ena amavutika nazo maganizo. Nkhani yoyamba ndi yokhudza zimene mmodzi mwa olambira Mulungu anachita, ndipo inayo ndi yokhudza chiweruzo china chimene Mulungu anapereka.
N’chifukwa Chiyani Loti Anapereka Ana Ake Aakazi kwa Anthu Ochita Chipolowe?
11, 12. (a) Tafotokozani zimene zinachitika Mulungu atatumiza angelo awiri ooneka ngati anthu ku Sodomu. (b) Nkhani imeneyi yachititsa anthu ena kukhala ndi mafunso otani?
11 Mu Genesis chaputala 19, muli nkhani ya zimene zinachitika pamene Mulungu anatumiza angelo awiri, ooneka ngati anthu, ku mzinda wa Sodomu. Loti anachonderera alendowo kuti akhale m’nyumba mwake. Koma usiku womwewo, khamu la amuna a mu mzindawo linazungulira nyumbayo, n’kumauza Loti kuti atulutse alendo aja kuti khamulo lichite nawo zachiwerewere. Loti anayesetsa kukambirana ndi khamulo, koma sizinathandize. Pofuna kuteteza alendo ake, Loti anati: “Abale anga, musachitetu koipa kotere. Taonanitu, ndili ndi ana aakazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nawo chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa chindwi langa.” Khamulo silinamve ndipo linatsala pang’ono kuthyola chitseko. Pomalizira pake, alendowo, amene anali angelo, anachititsa khungu khamu lochita chipolowe limenelo.—Genesis 19:1-11.
12 Nkhani imeneyi yachititsa anthu ena kukhala ndi mafunso ambiri, ndipo n’zomveka. Iwo amadzifunsa kuti: ‘Koma zoona Loti anafuna kuteteza alendo ake mwa kupereka ana ake aakazi kwa khamu lofuna zachiwerewere limenelo? Kodi Loti sanalakwe pamenepa, kapena kuchita zinthu mwamantha?’ Poganizira nkhani imeneyi, n’chifukwa chiyani Mulungu anauzira Petro kunena Loti kuti munthu “wolungama”? Kodi Mulungu anavomereza zimene Loti anachitazo? (2 Petro 2:7, 8) Tiyeni tiione bwinobwino nkhaniyi kuti tisamuganizire molakwa Yehova.
13, 14. (a) Kodi tiyenera kuganizira mfundo ziti pa nkhani ya m’Baibulo yokhudza zimene Loti anachita? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Loti sanangochita zinthu chifukwa cha mantha?
13 Choyamba, tiyenera kudziwa kuti Baibulo silitsutsa kapena kuvomereza zimene Loti anachita. Limangosimba zimene zinachitikazo. Baibulo silinenanso zimene Loti anali kuganiza kapena chimene chinam’chititsa kuchita zimene anachitazo. Akadzaukitsidwa pa “kuuka kwa olungama,” mwina adzafotokoza mwatsatanetsatane.—Machitidwe 24:15.
14 Loti sanali munthu wamantha. Pa chochitikachi, iye anali pavuto lalikulu. Ponena kuti alendowo anadza “pansi pa mthunzi” wa chindwi lake, Loti anasonyeza kuti unali udindo wake kuteteza alendowo. Koma kuwatetezako kunali kovuta. Wolemba mbiri wachiyuda, Josephus, analemba kuti anthu a ku Sodomu anali “opondereza anthu anzawo, ndi osaopa Mulungu . . . Anali kudana ndi alendo, ndipo anali kuchitirana khalidwe lonyansa wina ndi mnzake mu mzindamo.” Koma Loti sanaope kulankhula ndi khamu la anthu aukali amenewo. M’malo mwake, anatuluka kukalankhula nawo, “natseka chambuyo pakhomo pake.”—Genesis 19:6.
15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’kutheka kuti Loti anachita zimenezo chifukwa cha chikhulupiriro?
15 Ena angafunse kuti: ‘Ngakhale zili choncho, ndithudi Loti anafuna kupereka ana ake aakazi kwa khamulo? Chifukwa chiyani?’ M’malo moganiza kuti anali ndi zolinga zoipa, bwanji osaganizira zifukwa zina zimene mwina zinachititsa Loti kutero? Choyamba, n’kutheka kuti Loti anachita zimenezo chifukwa cha chikhulupiriro. Motani? Mosakayikira, Loti anali kudziwa mmene Yehova anatetezera Sara, mkazi wa Abrahamu, amalume ake. Kumbukirani kuti chifukwa Sara anali chiphadzuwa, Abrahamu anapempha Sara kuti azinena kuti Abrahamuyo ndi mchimwene wake, kuopera kuti ena angamuphe kuti atenge Sara.a Pambuyo pake, ena anam’tenga Sara kupita naye ku nyumba ya Farao. Koma Yehova anachitapo kanthu, kuteteza Sara kuti asaipitsidwe ndi Farao. (Genesis 12:11-20) Mwina Loti anali ndi chikhulupiriro kuti ana ake aakazi atetezedwa mofananamo. Chochititsa chidwi n’chakuti Yehova anachitapodi kanthu kudzera mwa angelo ake, ndipo atsikanawo anatetezedwa.
16, 17. (a) Kodi n’kutheka kuti Loti anali kufuna kudabwitsa kapena kusokoneza amuna a m’Sodomu motani? (b) Zili zonsezo zimene Loti anaganiza, ndife otsimikiza za chiyani?
16 Talingalirani chifukwa china. N’kuthekanso kuti Loti anali kufuna kudabwitsa kapena kusokoneza amunawo. Mwina anali kudziwa kuti amunawo sangakhumbe ana ake aakazi, chifukwa amuna a m’Sodomu anali okonda kugonana amuna okhaokha. (Yuda 7) Kuwonjezera apo, atsikanawo anali otomeredwa ndi amuna a mu mzindawo. Ndiye kuti mwina achibale, mabwenzi, kapena amene amachita malonda ndi anyamata omwe anali kudzakhala apongozi a Loti, anali m’khamulo. (Genesis 19:14) Mwina Loti anali ndi chikhulupiriro chakuti chifukwa cha maunansi amenewo, amuna ena m’khamulo ateteza ana ake aakaziwo. Khamu logawanika motero, silikanakhala loopsa kwambiri.b
17 Zili zonsezo zimene Loti anaganiza, ndi zolinga zake, ndife otsimikiza za chinthu chimodzi: Popeza kuti Yehova amachita chilungamo nthawi zonse, ayenera kuti anali ndi chifukwa chabwino choonera Loti kukhala munthu “wolungama.” Ndipo kungoona zochitika za khamu lochita chipolowe la anthu a m’Sodomu, kodi tingakayike zoti Yehova anali ndi zifukwa zabwino zoperekera chiweruzo pa anthu oipa a mzindawo?—Genesis 19:23-25.
N’chifukwa Chiyani Yehova Anapha Uza?
18. (a) Kodi chinachitika n’chiyani pamene Davide anafuna kusamutsira Likasa ku Yerusalemu? (b) Ndi funso lotani limene nkhani imeneyi imadzutsa?
18 Nkhani inanso imene ingaoneke ngati yosowetsa mtendere kwa ena, inachitika pamene Davide anafuna kusamutsira likasa la chipangano ku Yerusalemu. Likasalo analinyamulira pa ngolo imene Uza ndi mbale wake anali kutsogolera. Baibulo limati: “Pofika iwo ku dwale la Nakoni, Uza anatambasula dzanja lake, nachirikiza likasa la Mulungu; chifukwa ng’ombe zikadapulumuka. Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anam’kantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.” Patapita miyezi ingapo, zinatheka kusamutsa Likasalo atalinyamulira pa mapewa a Alevi achikohati, motsatira njira imene Mulungu analamula. (2 Samueli 6:6, 7; Numeri 4:15; 7:9; 1 Mbiri 15:1-14) Ena angafunse kuti: ‘Chifukwa chiyani Yehova anachitapo kanthu mwamphamvu choncho? Uza anali kungofuna kupulumutsa Likasa.’ Kuti tisamuganizire molakwa Yehova, tiyeni tikambirane mfundo zina zothandiza.
19. N’chifukwa chiyani n’kosatheka kwa Yehova kuchita chosalungama?
19 Tiyenera kukumbukira kuti n’zosatheka Yehova kuchita chosalungama. (Yobu 34:10) Kuti achite zimenezo kungakhale kupanda chikondi. Koma tikudziwa pa zimene taphunzira m’Baibulo lonse kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Kuwonjezera apo, Malemba amatiuza kuti “chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wachifumu [wa Mulungu].” (Salmo 89:14) Ndiye zingatheke bwanji Yehova kuchita chosalungama? Atati achite zimenezo, kungakhale kuzula maziko enieniwo a ufumu wake wa chilengedwe chonse.
20. Uza anayenera kudziwa bwino malamulo okhudza Likasa pazifukwa ziti?
20 Kumbukirani kuti Uza anayenera kuchidziwa bwino Chilamulo. Likasa linali kuimira kukhalapo kwa Yehova. Chilamulo chinaneneratu kuti munthu wamba asakhudze Likasa, ndipo chinachenjezeratu kuti ophwanya lamulo limeneli adzalangidwa mwa kuphedwa. (Numeri 4:18-20; 7:89) Motero, ntchito yosamutsa Likasa siinali ntchito wamba. Zikuonetsa kuti Uza anali Mlevi (koma osati wansembe), moti anayenera kudziwa zimene Chilamulo chimanena. Ndiponso, zaka zambiri m’mbuyomo, Likasa linasamutsidwira ku nyumba ya bambo ake kuti likasungidwe bwino. (1 Samueli 6:20–7:1) Linakhala kumeneko zaka 70, mpaka Davide ataganiza zolisamutsa. Choncho kuyambira ali mwana wamng’ono, Uza ayenera kuti anali kudziwa malamulo okhudza Likasa.
21. Pankhani ya Uza, n’chifukwa chiyani kukumbukira kuti Yehova amaona za mumtima wa munthu kuli kofunika?
21 Monga tatchula kale, Yehova amatha kudziwa za mu mtima wa munthu. Popeza Mawu ake amati zimene Uza anachitazo zinali “kusalingirira,” kapena kupanda ulemu, Yehova ayenera kuti anaona kudzikonda kwa mtundu winawake mwa iye kumene nkhaniyo sinatchule mwachindunji. Kodi kapena Uza anali wodzikuza, wokonda kupitirira malire pa zinthu zina? (Miyambo 11:2) Kapena kutsogolera poyera Likasa limene banja lake linali litasunga m’nyumba mwawo kunam’chititsa kunyada? (Miyambo 8:13) Kodi Uza mwina anali ndi chikhulupiriro chochepa zedi, moti anaganiza kuti dzanja la Yehova n’lalifupi, ndipo sangathe kuchirikiza Likasa loimira kukhalapo Kwake kuti lisagwe? Kaya chikhale chifukwa chotani, ndife otsimikiza kuti Yehova anachita chilungamo. Ayenera kuti anaona chinachake mu mtima wa Uza chimene chinam’pangitsa kupereka chiweruzo nthawi yomweyo.—Miyambo 21:2.
Chifukwa Chomveka Chodalira Yehova
22. Kodi nzeru za Yehova zimaoneka motani pa mfundo yakuti nthawi zina Mawu ake sanena mfundo zina?
22 Nzeru zosayerekezeka za Yehova zimaoneka pa mfundo yakuti, nthawi zina Mawu ake sanena mfundo zina. Mwakutero, Yehova amatipatsa mpata wosonyeza kuti timam’khulupirira. Pa zimene takambiranazi, kodi si zoonekeratu kuti tili ndi zifukwa zomveka zovomerezera ziweruzo za Yehova? Inde, tikamaphunzira Mawu a Mulungu ndi mtima wofunitsitsa kuphunzira, popanda kutsogoza maganizo okayikira mfundo zina, timaphunzira zambiri za Yehova. Tikatero, timakhulupiriradi kuti Yehova amachita cholungama ndi choyenera nthawi zonse. Ndiye chifukwa chake, ngati nkhani ina ya m’Baibulo ikudzutsa mafunso amene sitikupeza mayankho ake achindunji, tiyeni tikhale ndi chidaliro chakuti Yehova anachita chilungamo.
23. Kodi tiyenera kukhala ndi chidaliro chotani pa zimene Yehova adzachita m’tsogolo?
23 Tikhalenso ndi chidaliro chomwecho pa zimene Yehova adzachita m’tsogolo. Tikhale otsimikiza kuti akadzafika kudzapereka chiweruzo chake pa chisautso chachikulu chimene chayandikira, iye ‘sadzawononga olungama pamodzi ndi oipa.’ (Genesis 18:23) Chifukwa amakonda chilungamo sadzachita zimenezo m’pang’ono pomwe. Tikhalenso ndi chidaliro chonse kuti m’dziko latsopano likudzalo, iye adzakhutiritsa zosowa zathu zonse m’njira yabwino koposa.—Salmo 145:16.
[Mawu a M’munsi]
a Abrahamu anali ndi chifukwa chomveka chochitira mantha, chifukwa buku lina lakale, limasimba za Farao wina amene anauza asilikali ake kugwira mkazi wokongola, ndi kupha mwamuna wake.
b Ngati mukufuna malingaliro owonjezeka, onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya December 1, 1979, tsamba 31.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi tiyenera kuvomereza ziweruzo za Yehova pazifukwa ziti?
• Kodi n’chiyani chingatithandize kusamuganizira molakwa Yehova, pa zimene Loti anachita popereka ana ake aakazi awiri kwa khamu la anthu aukali?
• Ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kumvetsa chifukwa chake Yehova anapha Uza?
• Kodi tiyenera kukhala ndi chidaliro chotani pa zimene Yehova adzachita m’tsogolo?