1 Samueli
6 Likasa+ la Yehova linakhala mʼdera la Afilisiti kwa miyezi 7. 2 Ndiyeno Afilisiti anaitana ansembe ndi olosera+ nʼkuwafunsa kuti: “Kodi Likasa la Yehova titani nalo? Tiuzeni zimene tingachite polibweza kwawo.” 3 Iwo anayankha kuti: “Ngati mukubweza likasa lapangano la Yehova Mulungu wa Isiraeli, musalibweze popanda kupereka nsembe. Mulimonse mmene zingakhalire, muyenera kupereka nsembe yakupalamula.+ Mukatero mudzachira ndipo mudzadziwa chifukwa chake dzanja lake silinasiye kukukhaulitsani.” 4 Ndiyeno iwo anafunsa kuti: “Kodi nsembe yakupalamula imene tiyenera kumutumizira ikhale chiyani?” Poyankha, ansembe ndi olosera aja anati: “Mutumize zifaniziro 5 zagolide za matenda a mudzi, ndi zifaniziro 5 zagolide za mbewa, mogwirizana ndi chiwerengero cha olamulira a Afilisiti.+ Muchite zimenezi chifukwa mliriwu wagwera aliyense wa inu, pamodzi ndi olamulira anu. 5 Mupange zifaniziro za matenda anu a mudzi ndi zifaniziro za mbewa+ zimene zikuwononga dziko, ndipo muyenera kulemekeza Mulungu wa Isiraeli. Mukatero, mwina adzachepetsako mphamvu ya dzanja lake kwa inuyo, mulungu wanu ndi dziko lanu.+ 6 Nʼchifukwa chiyani mukuumitsa mitima yanu ngati mmene anachitira Aiguputo ndi Farao?+ Mulungu atawakhaulitsa+ analola Aisiraeli kupita ndipo iwo anapitadi.+ 7 Mupange ngolo yatsopano ndipo mutenge ngʼombe ziwiri zimene zili ndi ana, zomwe sizinanyamulepo goli, nʼkuzimangirira kungoloyo. Koma ana a ngʼombezo muwabweze kunyumba kuti asapite nawo. 8 Mukatero, mutenge Likasa la Yehova nʼkuliika mungoloyo. Ndiyeno mutenge zinthu zagolide zimene mukuzitumiza ngati nsembe yakupalamula nʼkuizika mʼbokosi lina pambali pa Likasalo,+ kenako mulitumize lizipita. 9 Ndiyeno muzikaliyangʼana: Likasalo likakalowera njira yopita kwawo ku Beti-semesi,+ ndiye kuti iye ndi amenedi watichitira zinthu zoipa kwambirizi. Koma ngati silikalowera kumeneko, tidzadziwa kuti si dzanja lake limene latichitira zoipazi, koma zangochitika.”
10 Anthuwo anachitadi zimenezo. Anatenga ngʼombe ziwiri zimene zinali ndi ana nʼkuzimangirira kungolo, ndipo ana a ngʼombezo anawatsekera mʼkhola kunyumba. 11 Ndiyeno anaika Likasa la Yehova mungoloyo. Anaikamonso bokosi lokhala ndi mbewa zagolide komanso zifaniziro za matenda awo a mudzi. 12 Ngʼombezo zinayamba kuyenda mumsewu wopita ku Beti-semesi.+ Zinkangoyenda mumsewu waukulu zikulira ndipo sizinakhotere kumanja kapena kumanzere. Apa nʼkuti olamulira a Afilisiti akuzitsatira pambuyo mpaka kukafika mʼmalire a Beti-semesi. 13 Anthu a ku Beti-semesi ankakolola tirigu mʼchigwa. Atakweza maso nʼkuona Likasa, anasangalala kwambiri. 14 Ngolo ija inafika mʼmunda wa Yoswa, wa ku Beti-semesi, ndipo inaima pafupi ndi mwala waukulu. Ndiyeno anthuwo anawaza matabwa a ngoloyo nʼkupereka ngʼombe zija+ nsembe yopsereza kwa Yehova.
15 Alevi+ anatsitsa Likasa la Yehova komanso bokosi mmene munali zinthu zagolide zija, nʼkuziika pamwala waukulu uja. Kenako amuna a ku Beti-semesi+ anapereka nsembe zopsereza komanso nsembe zina kwa Yehova tsiku limenelo.
16 Olamulira 5 a Afilisiti aja ataona zimenezi, anabwerera ku Ekironi tsiku lomwelo. 17 Zifaniziro zagolide za matenda a mudzi zimene Afilisiti anatumiza kwa Yehova monga nsembe yakupalamula ndi izi:+ Mzinda wa Asidodi+ unapereka chifaniziro chimodzi, wa Gaza chimodzi, wa Asikeloni chimodzi, wa Gati+ chimodzi ndiponso wa Ekironi+ chimodzi. 18 Chiwerengero cha mbewa zagolide chinali chofanana ndi cha mizinda yonse ya Afilisiti yolamuliridwa ndi ndi olamulira 5 aja, kuyambira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mpaka kumidzi yopanda mipanda.
Mwala waukulu umene anaikapo Likasa la Yehova uli ngati mboni mpaka lero mʼmunda wa Yoswa, wa ku Beti-semesi. 19 Koma Mulungu anapha anthu a ku Beti-semesi chifukwa anayangʼana Likasa la Yehova. Anapha anthu 50,070* ndipo anthu anayamba kulira chifukwa Yehova anapha anthu ambiri.+ 20 Choncho amuna a ku Beti-semesi ananena kuti: “Ndi ndani angaime pamaso pa Yehova Mulungu woyera+ ndipo Mulungu apita kwa ndani akatisiya?”+ 21 Kenako anatumiza uthenga kwa anthu a ku Kiriyati-yearimu+ wakuti: “Afilisiti abweza Likasa la Yehova, bwerani mudzalitenge.”+