Chilungamo Chimakuza Mtundu
MVULA itagwa kwa masiku ambiri, zimakhala zosangalatsa chotani nanga kudzuka mmaŵa ndi kuona dzuŵa likuŵala m’mwamba mopanda mitambo! Nthaka yatsitsimulidwa, ndipo tsopano zomera zingaphuke mokondwa. Nthaŵi ina Yehova Mulungu anagwiritsira ntchito zotero kufanizira madalitso a ulamuliro wolungama. Iye anati kwa Mfumu Davide: “[Pamene wolamulira anthu ali wolungama, NW]; woweruza m’kuwopa Mulungu. [Pamenepo zikhala, NW] ngati kuunika kwa mmaŵa, potuluka dzuŵa, mmaŵa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuŵala koyera, italeka mvula.”—2 Samueli 23:3, 4.
Mawu a Mulungu anakhala oona mkati mwa kulamulira kolungama kwa mwana wa Davide, Mfumu Solomo. Baibulo limati: “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.”—1 Mafumu 4:25.
Israyeli wakale anali mtundu wosankhika wa Mulungu. Iye anawapatsa malamulo ake nawauza kuti ngati adzamvera mawu ake, iye ‘adzawakulitsa koposa amitundu onse a pa dziko lapansi.’ (Deuteronomo 28:1) Si chilungamo chawo Aisrayeli chimene chinawakuza koma chinali chilungamo cha Yehova. Malamulo amene Mulungu anawapatsa anali apamwamba kwambiri kuposa malamulo a mitundu yowazinga. Monga mtundu, iwo anali opanda ungwiro mofananadi ndi mitundu yonseyo. Chifukwa chake, Chilamulo chapamwamba cha Yehova ndi kuchitsatira kwawo mosamalitsa ndizo zinawachititsa kukwezedwa pamwamba pa mitunduyo. Pamene anamvera malamulo a Yehova, iye anawayanja ndi kuwadalitsa. Mfumu Solomo inaona zimenezi mkati mwa ulamuliro wake. Iye anakhoza kunena kuti: “Chilungamo chikuza mtundu wa anthu; koma,” anachenjeza motero, “tchimo lichititsa fuko manyazi.”—Miyambo 14:34.
Mwachisoni, chifukwa cha kusamvera kwawo kobwerezabwereza, mtundu wa Israyeli unatsitsidwa. Anachititsidwa manyazi monga mtundu. Pomaliza zimenezi zinawachititsa kukanidwa kosatha ndiyeno kusankhidwa kwa mtundu watsopano wauzimu.—Mateyu 21:43.
Israyeli Wauzimu
Pamsonkhano wa bungwe lolamulira Lachikristu m’Yerusalemu, Yakobo, wobadwa Myuda, analankhula mouziridwa kuti Mulungu “anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) Mtumwi Paulo anatcha mtundu Wachikristu watsopano umenewu “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) Ponena za chifuno cha kuitanidwa kwawo, Petro analemba kuti: “Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.” (1 Petro 2:9) Monga anthu osankhika a Mulungu, iwo anayenera kuŵala monga mauniko m’dziko. Chilungamo cha Yehova chinali kudzawakweza pamwamba.—Afilipi 2:15.
Kusankhidwa kwa Aisrayeli auzimu ameneŵa kungayerekezedwe ndi kukumba diamondi. Pamene mtapo wokhala ndi diamondi wochuluka wakumbidwa, ungatulutse kokha 1 carat (200 mg) pa matani 3 a dothi. Njira imene inkagwiritsiridwa ntchito kulekanitsa diamondi ndi mtapo inali ya kusanganiza mtapowo ndi madzi ndi kuthira msanganizowo pa matebulo opaka girisi. Diamondi sifuna madzi, ndipo imakanirira m’girisi pamene mbali za mtapo zosafunikazo zinali kukokoloka ndi madziwo. Panthaŵiyi diamondi imakhala yosasalala. Komabe, ataidula ndi kuipukuta, imanyezimira kwambiri.
Mofanana ndi diamondi yokana madziyo imene simakhala mbali ya mtapo umene umaizinga, anthu a Yehova alekanitsidwa ndi dzikoli. (Yohane 17:16) Ataonetsedwa kuunika nthaŵi yoyamba, iwo angakhale asakunyezimira. Koma Mawu a Yehova ndi mzimu wake zimaumba umunthu watsopano mwa iwo, ndipo amaŵala ngati mauniko m’dzikoli. Chilungamo cha Yehova ndicho chimawakweza pamwamba ndi kuwachititsa kuŵalitsa kuunika kwamphamvu kwa choonadi cha Ufumu kulikonse, osati chilungamo chawo ayi.
Komabe, kuyambira chakumapeto kwa zaka za zana loyamba C.E., mpatuko unaloŵa m’mipingo ndi kukhudza ambiri. Otchedwa Akristu anaphatikana ndi mitundu ya dziko ndipo kunali kosatheka kuwasiyanitsa ndi dziko lowazinga.
Lerolino otsalira okhulupirika a Aisrayeli auzimu apezanso chiyanjo cha Yehova. Iwo adzilekanitsa ndi dziko ndipo adziyeretsa pa “chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Pokhala oyera ndi olungama pamaso pa Yehova, iwo amachirikiza chilungamo chake. Zimenezi zawakweza pamalo apamwamba a chiyanjo kuposa mitundu ya dzikoli. Mwa kulalikira kwawo uthenga wabwino wa Ufumu mwachangu, khamu lalikulu la padziko lonse lakokedwera kwa Yehova ndipo lakhala mbali ya anthu ake.—Chivumbulutso 7:9, 10.
Dziko Limaona Kusiyana
Akuluakulu a boma nthaŵi zina amayamikira khalidwe la atumiki a Mulungu. Kumbuyoku, mkulu wa apolisi ku Pretoria Show Grounds, South Africa, anathirira ndemanga pa khalidwe la Mboni za Yehova, zamafuko onse, zimene zimagwiritsira ntchito malowo kuchitiramo misonkhano yawo yaikulu pachaka. Pakati pa zinthu zina, iye analemba kuti: “Aliyense anali waulemu ndipo ndi waulemu, anthu omalankhulana bwinobwino, khalidwe losonyezedwa masiku angapo apitawa—zimasonyeza mtundu woposa wa anthu a gulu lanu, ndi kuti onse amakhala pamodzi monga banja limodzi lachimwemwe.”
Anthu a Yehova angachirikize chilungamo cha mtundu wake osati chabe pamisonkhano yaikulu yoteroyo komanso m’moyo wawo wa mseri. Mwachitsanzo, nthambi ya ku South Africa ya Watch Tower Society inalandira kalata kuchokera kwa mkazi wina ku Johannesburg, yakuti: “Mlungu watha ndinayendetsa galimoto chikwama changa cha ndalama chili pamwamba pake. Chinagwera mumsewu wotchedwa Jan Smuts Avenue ndipo munthu wina wa mpingo wanu, Mr. R—, anachitola ndi zonse zinali mkati mwake, kundiimbira foni, ndi kundibwezera. . . . Ndikuyamikira kwambiri kuona mtimaku kumene kuli kovuta kupeza masiku ano ndipo ndikuthokoza mpingo wanu kaamba ka kukhazikitsa miyezo imene anthu anu amatsatira.”
Inde, mwa kutsatira miyezo yolungama ya Yehova, anthu ake amakhala osiyana kwambiri ndi dziko. Chifukwa chakuti ameneŵa amasonyeza chilungamo cha Yehova, anthu oona mtima amakokedwera ku mpingo Wachikristu. Nkwachibadwa kukopeka ndi kanthu kena koyera ndi kabwino. Mwachitsanzo, munthu wina anafika pamsonkhano wa Mboni za Yehova ku Zurich, Switzerland, nanena kuti anafuna kukhala chiŵalo cha mpingowo. Anafotokoza kuti mlongo wake anachotsedwa chifukwa cha chisembwere nawonjezera kuti anafuna kuloŵa m’gulu limene “silimalekerera khalidwe loipa.” Ngakhale New Catholic Encyclopedia imavomereza kuti Mboni za Yehova zimadziŵika monga “limodzi la magulu odzisungira bwino koposa m’dziko.”
Pamene kuli kwakuti chilungamo chimakweza dzina labwino, tchimo lingadzetse chitonzo pa ilo, makamaka ngati cholakwa chachikulucho chadziŵika kwa anthu. Mpingo Wachikristu nthaŵi zina umasenza chitonzo choikidwa pa iwo pamene wina wachita tchimo lalikulu. Nchifukwa chake, anthu okhulupirika mumpingo angatetezere dzina labwino la mpingo mwa kusonyeza kuti wolakwayo walangidwa mwachifundo, kutanthauza mogwirizana ndi miyezo ya Malemba. Ngati wina achimwa ndipo salapa, amapitikitsidwa mumpingo—kuchotsedwa.—1 Akorinto 5:9-13.
Chimene Ena Amachotsedwera
Ngakhale kuti anthu zikwi zambiri amachotsedwa mumpingo Wachikristu chaka ndi chaka, iwo ali kokha chiŵerengero chochepa mwa Mboni pafupifupi mamiliyoni asanu padziko lonse. Kodi nchifukwa ninji njira yolimba imeneyi imatengedwa pa aliyense mumpingo Wachikristu? Mtundu wake wa cholakwacho uli china cha zochititsa. Koma chinthu chofunika kwambiri nchakuti kaya wolakwayo alidi wolapa pa tchimo lalikulu limene anachita kapena saali. Ngati walaswadi mtima, watembenukira kwa Yehova m’pemphero laphamphu, akumapempha chikhululukiro cha tchimo limene anachita kwa Iye, ndipo wapempha chithandizo kwa amuna athayo mumpingo, angathandizidwe kupezanso chiyanjo cha Mulungu nakhalabe mbali ya mpingo.—Miyambo 28:13; Yakobo 5:14, 15.
Ngati mwana amene ali ndi unansi wabwino ndi atate wake wachita kanthu kena kopweteka mtima wa atate wake, onse aŵiriwo ayenera kuukonza msanga unansi wamtengo wapataliwo. Momwemonso, pamene tipatulira moyo wathu kwa Yehova, timakhala naye paunansi wamtengo wapatali. Chifukwa chake, tikachita chinthu china chompweteka, tiyenera kufulumira kubwezeretsa unansiwo ndi Atate wathu Wakumwamba.
Chosangalatsa nchakuti ena amene anali ochotsedwa atsatira fanizo la mwana woloŵerera. M’fanizolo Yehova akuyerekezedwa ndi Atate wachikondi wokonzeka kulandiranso wochimwa wolapayo ngati iyeyo atembenuka mtima napempha Mulungu kumkhululukira. (Luka 15:11-24) Kulapa koona, kochokera mumtima ndi kupatuka pa choipa ndiko njira yopezera chiyanjo cha Yehova ndi kubwerera mumpingo Wachikristu. Olakwa ena olapa amene atopa nawo mtolo wa liwongo asonkhezereka kulapa ndi kutenga njira yobwerera mumpingo Wachikristu wachikondi. Motero amvetsetsa mawu a Yehova pa Yesaya 57:15.
Pofuna kuletsa anthu kulandira chisamaliro chachikondi cha Yehova, Satana amapereka chithunzi chakuti kulibe chikhululukiro cha machimo amene munthu wachita. Koma nsembe ya dipo ya Kristu Yesu ili yokwanira kukwirira machimo a yense wolapa—inde, ngakhale tchimo lacholoŵa la “dziko lonse.” (1 Yohane 2:1, 2) Tchimo lokha limene nsembeyo simakwirira ndi tchimo lochimwira mzimu woyera wa Mulungu, limene lili kupandukira dala chitsogozo cha mzimu wa Mulungu, monga machimo aakulu a Yudasi Iskariote ndi alembi ndi Afarisi ambiri.—Mateyu 12:24, 31, 32; 23:13, 33; Yohane 17:12.
Kuchirikiza Chilungamo cha Yehova
Chiyambire pamene otsalira a Aisrayeli auzimu anabwezeretsedwa m’chiyanjo cha Yehova mu 1919, iwo apitirizabe kukwezedwa pamwamba pa dziko loŵazinga. Zimenezi sizili chifukwa chakuti iwo ali abwino koma zili chifukwa cha kugonjera kwawo mwaufulu malamulo ndi miyezo ya Yehova. Chotero, mamiliyoni a “nkhosa zina” za Kristu akuyanjana ndi Israyeli wauzimu monga atsamwali awo okhulupirika. (Yohane 10:16) Anthuwa amapereka ulemerero ndi ulemu kwa Yehova m’dziko lotalikirana kwambiri ndi miyezo yolungama ya Mulungu. Zili monga momwe magazini a Personality a ku South Africa ananenera nthaŵi ina kuti: “Mboni za Yehova zikuoneka kukhala ndi mikhalidwe yabwino yochuluka ndipo zichita ngati kuti zilibe yoipa.”
Kuti asunge malo okwezeka ameneŵa m’dziko losapembedza, aliyense mumpingo Wachikristu afunikira kukhala ndi moyo woyera ndi wolungama pamaso pa Yehova. Mu Baibulo, gulu lakumwamba la Yehova limaimiridwa ndi zinthu zoyera. Limaoneka monga mkazi wokongola wovekedwa dzuŵa ndi wokhala ndi mwezi ku mapazi ake. (Chivumbulutso 12:1) Yerusalemu Watsopano akufotokozedwa monga mzinda woyera, wokongola maonekedwe ake. (Chivumbulutso 21:2) Ziŵalo zokhulupirika za mkwatibwi wa Kristu zimapatsidwa “bafuta wonyezimira woti mbu.” (Chivumbulutso 19:8) A khamu lalikulu akuonekera “atavala zovala zoyera.” (Chivumbulutso 7:9) Anthu okonda chilungamo amakopeka ndi gulu loyera. Mosiyana ndi zimenezo, gulu la Satana nlodetsedwa. Chiungwe cha zipembedzo zake chimasonyezedwa monga mkazi wachigololo, ndipo aja okhala kunja kwa mzinda woyerawo amatchedwa odetsedwa.—Chivumbulutso 17:1; 22:15.
Amene alonjezedwa moyo wosatha ndi olungama okha. Anthu osonkhanitsidwa ochirikiza chilungamo cha Yehova akuyembekezera kupulumuka mapeto a dongosolo loipali. “Wondimvera ine adzakhala wosatekeseka, nadzakhala phe osawopa zoipa,” Mulungu akulonjeza motero pa Miyambo 1:33.
Kudzakhala kosangalatsa chotani nanga pamene Solomo Wamkulu, Kristu Yesu, adzalamulira dziko latsopanolo m’chilungamo, m’kuwopa Yehova! (2 Petro 3:13) Kudzakhala ngati kuunika kwa mmaŵa pamene dzuŵa laŵala, mmaŵa mopanda mitambo. Okhala pa dziko lapansi onse adzakhala osatekeseka, aliyense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, titero kunena kwake. Anthu olungama adzakongoletsa dziko lapansi ndi kukhala m’malo ake oyenera m’chilengedwe chonse kutamanda Yehova, Mulungu wathu, kosatha.—Mika 4:3, 4; onaninso Yesaya 65:17-19, 25.
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Garo Nalbandian