Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!
“Ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.”—YEREMIYA 31:3.
1. Kodi ndimotani mmene mkhalidwe wamaganizo wa Yesu kulinga kwa anthu wamba a m’tsiku lake unasiyanira ndi uja wa Afarisi?
CHIKONDICHO anatha kuchiona pankhope pake. Mwamuna ameneyu, Yesu, anali wosiyana kwambiri ndi atsogoleri awo achipembedzo; anasamala ena. Iye anamvera chisoni anthu ameneŵa chifukwa chakuti “anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Atsogoleri awo achipembedzo anayenera kukhala abusa achikondi oimira Mulungu wachikondi ndi wachifundo. M’malo mwake, anaona anthu wamba monga zinyalala—otembereredwa!a (Yohane 7:47-49; yerekezerani ndi Ezekieli 34:4.) Mwachionekere, lingaliro losakhala la malemba lopotoka limenelo linali losiyana kwambiri ndi lingaliro la Yehova ponena za anthu ake. Iye anali atauza mtundu wake, Israyeli: “Ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha.”—Yeremiya 31:3.
2. Kodi mabwenzi atatu a Yobu anayesa motani kumchititsa kukhulupirira kuti iyeyo anali wopanda pake pamaso pa Mulungu?
2 Komabe, Afarisi sanali oyamba kuyesa kuchititsa nkhosa zokondedwa za Yehova kukhulupirira kuti zinali zopanda pake. Talingalirani za nkhani ya Yobu. Kwa Yehova iye anali wolungama ndi wopanda chifukwa, koma “otonthoza” atatuwo anapereka lingaliro lakuti Yobu anali wampatuko wachigololo, woipa amene adzafa popanda kusiya chizindikiro chake. Iwo ananenetsa kuti Mulungu sangaŵerengere khalidwe lolungama la Yobu, popeza kuti Mulungu samakhulupirira ngakhale angelo ake ndipo amaona kumwamba monga kodetsedwa!—Yobu 1:8; 4:18; 15:15, 16; 18:17-19; 22:3.
3. Kodi Satana amagwiritsira ntchito njira zotani lerolino poyesa kuchititsa anthu kukhulupirira kuti ali opanda pake ndi osakondedwa?
3 Lerolino, Satana akugwiritsirabe ntchito ‘mchitidwe wamachenjera’ umenewu wa kuyesa kuchititsa anthu kukhulupirira kuti ali osakondedwa ndi opanda pake. (Aefeso 6:11, NW, mawu amtsinde) Zoonadi, iye kaŵirikaŵiri amanyenga anthu mwa kuwasonkhezera kukhala onyada mopanda pake. (2 Akorinto 11:3) Komanso iye amakondweretsedwa ndi kuwononga kudzilemekeza kwa amene ali pangoziyo. Makamaka zimenezi zili choncho mu “masiku otsiriza” oŵaŵitsa ano. Lerolino ambiri amakulira m’mabanja mmene muli ‘mopanda chikondi chachibadwidwe’; ambiri amalimbana tsiku ndi tsiku ndi awo amene ali aukali, adyera, aliuma olimbirira. (2 Timoteo 3:1-5) Zaka zambiri za kusautsidwa, tsankho la fuko, udani, kapena nkhanza zingakhale zitatsimikiziritsa maganizo a anthu otero kukhulupirira kuti ali opanda pake ndi osakondedwa. Mwamuna wina analemba kuti: “Sindimakonda munthu kapena kuona kukhala wokondedwa ndi aliyense. Ndimaona kukhala kovuta kwambiri kukhulupirira kuti Mulungu amasamala za ine.”
4, 5. (a) Kodi nchifukwa ninji lingaliro la kudziona kukhala wopanda pake lili losiyana ndi Malemba? (b) Kodi nchiti chimene chili chotulukapo china changozi ya kukhulupirira kuti palibe zoyesayesa zathu zimene zili zoŵerengeredwa?
4 Lingaliro la kukhala wopanda pake limatokosa mfundo yaikulu ya choonadi cha Mawu a Mulungu, chiphunzitso cha dipo. (Yohane 3:16) Ngati Mulungu analipirira mtengo waukulu kwambiri chotero—moyo wamtengo wapatali wa Mwana wa iye mwini—kutigulira mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha, ndithudi Iyeyo ayenera kukhala akutikonda; ndithudi tiyenera kukhala tili amtengo wina wake pamaso Pake!
5 Ndiponso, kungakhale kolefula maganizo chotani nanga kulingalira kuti tili osakondweretsa kwa Mulungu, kuti palibe zoyesayesa zathu zimene zimaŵerengeredwa! (Yerekezerani ndi Miyambo 24:10.) Ndi lingaliro losakondweretsa limeneli, ngakhale chilimbikitso chokhala ndi cholinga chabwino, cholinganizidwira kutithandiza kupitirizabe kuchita utumiki wathu kwa Mulungu pamene kuli kotheka, chingamvekere kwa ena ngati kutsutsidwa. Chingakhale chikuvomerezana ndi chikhutiro chathu chamkati chakuti chilichonse chimene timachita nchosakwanira.
6. Kodi nchiyani chimene chili mankhwala abwino koposa a malingaliro osakondweretsa omkitsa onena za ife eni?
6 Ngati muzindikira kuti muli ndi malingaliro osakondweretsa amenewo, musataye mtima. Ambiri a ife timadzisuliza mopambanitsa panthaŵi ndi nthaŵi. Ndipo kumbukirani, Mawu a Mulungu ngolinganizidwira “chikonzero” ndi “kupasula malinga.” (2 Timoteo 3:16; 2 Akorinto 10:4) Mtumwi Yohane analemba: “Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m’choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, mmene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Pamenepa, tiyenitu tilingalire njira zitatu m’zimene Baibulo limatiphunzitsira kuti tili amtengo wapatali kwa Yehova.
Yehova Amakuŵerengerani
7. Kodi Yesu anaphunzitsa motani Akristu onse ponena za kuŵerengeredwa kwawo pamaso pa Mulungu?
7 Choyamba, Baibulo limaphunzitsa mwachindunji kuti aliyense wa ife ali woŵerengeredwa pamaso pa Mulungu. Yesu anati: “Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiŵiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiŵalika pamaso pa Mulungu; komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu aŵerengedwa. Musawopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.” (Luka 12:6, 7) M’masiku amenewo, mpheta inali mbalame yotsika mtengo koposa yogulitsidwa monga chakudya, komabe panalibe ngakhale imodzi imene sinadziŵidwe ndi Mlengi wake. Chotero maziko a kusiyana kwakukulu ayalidwa: Ponena za anthu—amene ali oŵerengeredwa kwambirimbiri—Mulungu amadziŵa kanthu kawo kalikonse. Zili monga ngati kuti tsitsi lililonse lenileni la mitu yathu linaŵerengedwa!
8. Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kuganiza kuti Yehova akhoza kuŵerenga tsitsi la mitu yathu?
8 Tsitsi kuŵerengedwa? Ngati muganiza kuti mfundo imeneyi ya fanizo la Yesu ili yosatsimikizirika, talingalirani: Mulungu amakumbukira bwino lomwe atumiki ake okhulupirika kwakuti ngwokhoza kuwaukitsa—kuwalenganso monga momwe analili, kuphatikizapo dongosolo lawo la majini locholoŵana ndi zaka zawo zonse za zikumbukiro ndi zochitika. Kuŵerenga tsitsi lathu (limene avareji ya kumera kwake pa mutu wa munthu ili 100,000) kukakhala chinthu chosavuta poyerekezera ndi zimenezo!—Luka 20:37, 38.
Kodi Yehova Amaonanji mwa Ife?
9. (a) Kodi ndi mikhalidwe ina yotani imene Yehova amaŵerengera? (b) Kodi nchifukwa ninji mukuganiza kuti mikhalidwe yotero njamtengo wapatali kwa iye?
9 Chachiŵiri, Baibulo limatiphunzitsa zimene Yehova amaŵerengera mwa ife. Kunena mosavuta, iye amakondwera ndi mikhalidwe yathu yabwino ndi zoyesayesa zathu. Mfumu Davide anauza mwana wake Solomo: “Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingilira zonse za maganizo.” (1 Mbiri 28:9) Pamene Mulungu akusanthula mitima ya anthu miyandamiyanda m’dziko lino lodzala ndi chiwawa ndi udani, ayenera kukhala wokondwa chotani nanga pamene apeza mtima umene umakonda mtendere, choonadi ndi chilungamo! (Yerekezerani ndi Yohane 1:47; 1 Petro 3:4.) Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene Mulungu apeza mtima umene uli wodzala ndi kumkonda, umene umafuna kuphunzira za iye ndi kuuza ena chidziŵitsocho? Pa Malaki 3:16, Yehova akutiuza kuti amamvetsera kwa awo amene amalankhula ndi ena ponena za iye ndipo alidi ndi “buku la chikumbutso” la onse “akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” Mikhalidwe imeneyo njamtengo wapatali kwa iye!
10, 11. (a) Kodi ena angayese motani kuchepetsa umboni wakuti Yehova amaŵerengera mikhalidwe yawo yabwino? (b) Kodi chitsanzo cha Abiya chimasonyeza motani kuti Yehova amaŵerengera mikhalidwe yabwino pa milingo yonse?
10 Komabe, mtima wodzitsutsa ungakane umboni wotero wa kuŵerengeredwa kwathu pamaso pa Mulungu. Uwo unganong’one mosaletseka kuti, ‘Komatu pali ena ambiri amene amachita bwino kwambiri m’mikhalidwe imeneyo kuposa ine. Ha, Yehova ayenera kukhala wogwiritsidwa mwala chotani nanga pamene andiyerekeza nawo!’ Yehova samayerekeza anthu, ndiponso sali wosasinthika, woumirira pa ungwiro wake. (Agalatiya 6:4) Iye amasanthula mitima mwanzeru koposa, ndipo amaŵerengera mikhalidwe yabwino pa milingo yonse.
11 Mwachitsanzo, pamene Yehova anapereka lamulo lakuti nyumba yonse yaufumu yampatuko ya Mfumu Yerobiamu ipatsidwe chilango, ichotsedwe monga “ndowe,” Iye analamula kuti mwana wa mfumu mmodzi yekha, Abiya, aikidwe m’manda mwaulemu. Chifukwa? “Mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israyeli.” (1 Mafumu 14:10, 13) Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Abiya anali wolambira wokhulupirika wa Yehova? Osati kwenikweni, popeza kuti iye anafa, mofanana ndi a nyumba yake yoipayo. (Deuteronomo 24:16) Chikhalirechobe, Yehova anaŵerengera “chokoma” chimene anaona mu mtima wa Abiya ndipo anachitapo kanthu moyenerera. Matthew Henry’s Commentary on the Whole Bible limati: “Kumene kuli kanthu kena kabwino ka mtundu umenewo, kadzapezeka: Mulungu amene amakafunafuna, amakazindikira, ngakhale kochepetsetsa, ndipo amakondwera nako.” Ndipo musaiŵale kuti ngati Mulungu amapeza ngakhale mlingo waung’ono wa mkhalidwe wina wabwino mwa inu, iyeyo angaukulitse malinga ngati inu muyesayesa kumtumikira mokhulupirika.
12, 13. (a) Kodi Salmo 139:3 limasonyeza motani kuti Yehova amaŵerengera zoyesayesa zathu? (b) Kodi ndi m’lingaliro lotani mmene kunganenedwere kuti Yehova amapepeta zochita zathu?
12 Yehova amaŵerengera zoyesayesa zathu m’njira yofananayo. Pa Salmo 139:1-3, timaŵerenga: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziŵa. Inu mudziŵa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali. Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzoloŵerana nazo.” Chotero Yehova amadziŵa zochita zathu zonse. Koma iye amapitirira pa kungodziŵa. M’Chihebri mawuwo “njira zanga zonse muzoloŵerana nazo” angakhale ndi tanthauzo lakuti “musunga njira zanga zonse m’mwamba” kapena “musamalira njira zanga zonse.” (Yerekezerani ndi Mateyu 6:19, 20.) Komabe, kodi ndimotani mmene Yehova angasamalirire njira zathu pamene kuli kwakuti ndife opanda ungwiro ndi ochimwa kwambiri?
13 Mokondweretsa, malinga ndi kunena kwa akatswiri ena, pamene Davide analemba kuti Yehova ‘anayesa’ njira zake ndi nyengo za kupuma, kwenikweni Chihebri chinatanthauza “kupepeta” kapena “kuulutsa.” Buku lina la umboni linati: “Kumatanthauza . . . kuulutsa mankhusu onse, ndi kusiya maso ake onse—kusunga zonse zimene zili za mtengo wapatali. Tsono pano zimatanthauza kuti Mulungu anampepeta, titero kunena kwake. . . . Anachotsa mankhusu onse, kapena zinthu zonse zimene zinali zopanda pake, ndi kuona zimene zinatsalira zimene zinali zenizeni ndi zofunika.” Mtima wodzitsutsa ungapepete zochita zathu m’njira ina, ukumatiimba mlandu mowopsa chifukwa cha zolakwa zakale ndi kuona zipambano zathu kukhala zosanunkha kanthu. Koma Yehova amakhululukira machimo athu ngati tilapa moona mtima ndi kuyesayesa mwamphamvu kusabwerezanso zophophonya zathu. (Salmo 103:10-14; Machitidwe 3:19) Amapepeta ndi kukumbukira ntchito zathu zabwino. Kwenikweni, iye amazikumbukira kosatha malinga ngati tikhalabe okhulupirika kwa iye. Iye angaone kuziiŵala kukhala chisalungamo, ndipo sali wosalungama!—Ahebri 6:10.
14. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yehova amaŵerengera ntchito yathu mu utumiki Wachikristu?
14 Kodi ndi ntchito zina zabwino zotani zimene Mulungu amaziŵerengera? Pafupifupi chilichonse chimene timachita potsanzira Mwana wake, Yesu Kristu. (1 Petro 2:21) Pamenepo, ndithudi ntchito ina yofunika kwambiri, ndiyo ya kuwanditsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Pa Aroma 10:15, timaŵerenga: “Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.” Pamene kuli kwakuti tingakhale tisakuganiza za mapazi athu enieniwa kukhala “okometsetsa,” liwu limene Paulo anagwiritsira ntchito pano linali limodzimodzilo logwiritsiridwa ntchito m’matembenuzidwe a Septuagint Yachigiriki kufotokoza Rebeka, Rakele, ndi Yosefe—atatu onsewo amene anadziŵika ndi kukongola kwawo. (Genesis 26:7; 29:17; 39:6) Chotero kudziloŵetsa kwathu mu utumiki wa Mulungu wathu, Yehova, nkokongola ndi kwamtengo wapatali pamaso pake.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
15, 16. Kodi nchifukwa ninji Yehova amaŵerengera chipiriro chathu, ndipo kodi mawu a Mfumu Davide pa Salmo 56:8 amagogomezera motani mfundo imeneyi?
15 Mkhalidwe wina umene Mulungu amaŵerengera ndiwo chipiriro chathu. (Mateyu 24:13) Kumbukirani, Satana akufuna kuti mufulatire Yehova. Tsiku lililonse limene mumakhala wokhulupirika kwa Yehova ndilo tsiku lina limene mwathandiza kuchirikiza kupereka yankho pa chitonzo cha Satana. (Miyambo 27:11) Nthaŵi zina chipiriro chili nkhani yovuta kwambiri. Matenda, mavuto a zandalama, kupsinjika mtima, ndi zopinga zina zingapangitse tsiku lililonse limene likupyola kukhala loyesa. Kupirira poyang’anizana ndi mayesero otero nkwamtengo wapatali makamaka kwa Yehova. Nchifukwa chake Mfumu Davide anapempha Yehova kusunga misozi yake mu “nsupa” yophiphiritsira, akumafunsa mwachidaliro kuti, “Kodi siikhala m’buku mwanu?” (Salmo 56:8) Inde, Yehova amasunga mosamalitsa ndipo amakumbukira misozi yonse ndi kuvutika kumene tapirira posunga kukhulupirika kwathu kwa iye. Zimenezo nazonso nzamtengo wapatali pamaso pake.
16 Polingalira za mikhalidwe yathu yabwino kwambiri ndi zoyesayesa zathu, kumakhala kwachionekere chotani nanga kuti Yehova amaŵerengera kwambiri aliyense wa ife! Mosasamala kanthu za mmene dziko la Satana lachitira nafe, Yehova amatilingalira monga amtengo wapatali ndi mbali ya “zofunika za amitundu onse.”—Hagai 2:7.
Zimene Yehova Wachita Kusonyeza Chikondi Chake
17. Kodi nchifukwa ninji nsembe ya dipo ya Kristu iyenera kutikhutiritsa maganizo kuti Yehova ndi Yesu amatikonda monga munthu payekha?
17 Chachitatu, Yehova amachita zambiri kusonyeza chikondi chake kwa ife. Ndithudi, nsembe ya dipo ya Kristu ndiyo yankho lamphamvu koposa pa bodza lausatana lakuti tili opanda pake kapena osakondedwa. Sitiyenera kuiŵala konse kuti imfa yomvetsa ululu imene Yesu anavutika nayo pa mtengo wozunzirapo ndipo ngakhale ululu waukulu kwambiri umene Yehova anapirira nawo poona imfa ya Mwana wake wokondedwa unali umboni wa chikondi chawo kwa ife. Ndiponso, chikondi chimenecho chimayambukira ife aliyense payekha. Ndimo mmene mtumwi Paulo anaonera zimenezi, pakuti analemba: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.”—Agalatiya 2:20.
18. Kodi Yehova amatikokera kwa Kristu m’lingaliro lotani?
18 Yehova wasonyeza chikondi chake kwa ife mwa kutithandiza aliyense payekha kugwiritsira ntchito mwaŵi wa mapindu a nsembe ya Kristu. Yesu pa Yohane 6:44 anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye.” Mwa njira ya kulalikira, imene imafika kwa ife aliyense payekha, ndi mwa njira ya mzimu wake woyera, umene Yehova amagwiritsira ntchito kutithandiza kuzindikira ndi kugwiritsira ntchito choonadi chauzimu mosasamala kanthu za kupereŵera kwathu ndi kupanda ungwiro, Yehova mwiniyo amatikokera kwa Mwana wake ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Motero Yehova angathe kunena kwa ife monga momwe ananenera kwa Israyeli: “Ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.”—Yeremiya 31:3.
19. Kodi nchifukwa ninji mwaŵi wa pemphero uyenera kutikhutiritsa maganizo ponena za chikondi cha Yehova kwa ife?
19 Komabe, mwina mwake ndi kupyolera m’mwaŵi wa pemphero kuti timakondedwa ndi Yehova m’njira yoyandikana naye kwambiri. Iye amapempha aliyense wa ife ‘kupemphera kosaleka’ kwa iye. (1 Atesalonika 5:17) Iye amamvetsera! Amatchedwadi “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Iye sanapereke udindo umenewu kwa munthu wina aliyense, osatinso kwa Mwana wake. Tangoganizani: Mlengi wa chilengedwe chonse amatilimbikitsa kumfikira m’pemphero, momasuka. Mapembedzero anu angasonkhezeredi Yehova kuchita zimene mwina sakanachita.—Ahebri 4:16; Yakobo 5:16; onani Yesaya 38:1-16.
20. Kodi nchifukwa ninji chikondi cha Mulungu kwa ife sichili chodzikhululukira nacho pa kudzilingalira tokha kukhala wofunika kapena kudzikweza kwathu?
20 Palibe Mkristu wolingalira bwino amene angaone umboni wotero wa chikondi cha Mulungu ndi kuŵerengera kukhala chodzikhululukira chake pa kudzilingalira kukhala wofunika kwambiri kuposa mmenedi iye alili. Paulo analemba kuti: “Ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagaŵira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.” (Aroma 12:3) Chotero pamene kuli kwakuti timasangalala kukhala m’chikondi cha Atate wathu wakumwamba, tiyeni tikhale olama maganizo ndi kukumbukira kuti kukoma mtima kwa Mulungu sitinakuyenerere.—Yerekezerani ndi Luka 17:10.
21. Kodi ndi bodza lausatana lotani limene tiyenera kukana nthaŵi zonse, ndipo ndi choonadi chaumulungu chotani chimene tiyenera kusinkhasinkha nthaŵi zonse?
21 Aliyense wa ife achitetu zonse zimene angathe kukana malingaliro onse amene Satana amachirikiza m’dziko lino lakale lomafa. Zimenezo zimaphatikizapo kukana lingaliro lakuti tili opanda pake kapena osakondedwa. Ngati moyo m’dongosolo lino wakuphunzitsani kudziona inu eni monga chopinga chachikulu kwambiri chosakhoza kuchotsedwa ngakhale ndi chikondi chachikulu cha Mulungu, kapena kuona ntchito zanu zabwino kukhala zosanunkha kanthu kwakuti ngakhale maso ake oona zonse sangathe kuziona, kapena kuona machimo anu kukhala aakulu kambiri kwakuti sangatheke kukwiriridwa ndi imfa ya Mwana wake wamtengo wapataliyo, mwaphunzitsidwa bodza. Kanani mabodza otero ndi kunyansidwa nawo kwenikweni! Nthaŵi zonse tiyeni tikumbukire mawu a mtumwi Paulo ouziridwa a pa Aroma 8:38, 39: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”
[Mawu a M’munsi]
a Kwenikweni, iwo ananyoza osauka ndi mawu achipongwe akuti “ʽam-ha·ʼaʹrets,” kapena “anthu apansi.” Malinga ndi katsŵiri wina, Afarisi anaphunzitsa kuti munthu sayenera kuikizira chuma kwa anthu ameneŵa, kapena kukhulupirira umboni wawo, kapena kuwachereza monga alendo, kapena kukhala alendo awo, kapenanso kugula zinthu kwa iwo. Atsogoleri achipembedzo ananena kuti kukwatiwa kwa mwana wamkazi wa munthu kwa anthu ameneŵa kukakhala ngati kumpereka ku chilombo ali wonjatidwa ndi wopanda thandizo.
Kodi Mukuganiza Bwanji?
◻ Kodi nchifukwa ninji Satana amayesa kutichititsa kukhulupirira kuti ndife opanda pake ndi osakondedwa?
◻ Kodi Yesu anaphunzitsa motani kuti Yehova amaŵerengera aliyense wa ife?
◻ Kodi tikudziŵa motani kuti Yehova amaŵerengera mikhalidwe yathu yabwino?
◻ Kodi tingakhale otsimikizira motani kuti Yehova amaŵerengera zoyesayesa zathu?
◻ Kodi Yehova wasonyeza motani chikondi chake kwa ife aliyense payekha?
[Chithunzi patsamba 13]
Yehova amaona ndipo amakumbukira awo onse amene amaganiza pa dzina lake