Kodi Mulungu Ali Weniweni kwa Inu?
KODI mumafikira Mulungu mwamsanga m’pemphero mutakumana ndi mavuto aakulu? Ngati mumatero, kodi mumadziŵa kuti mukulankhula ndi munthu weniweni?
Ponena za Atate wake wakumwamba, Yesu Kristu anati: “Iye wondituma Ine . . . ali woona [“ndi weniweni,” NW].” (Yohane 7:28) Inde, Yehova Mulungu ali weniweni, ndipo kupemphera kwa iye kuli ngati kupita kwa munthu amene ali bwenzi lako lokondedwa kaamba ka chithandizo kapena uphungu. Komabe, kuti Mulungu atimvere, mapemphero athu ayenera kukhala ogwirizana ndi zimene Malemba amanena zokhudza mapemphero amene angamvedwe. Mwachitsanzo, tiyenera kufikira “Wakumva pemphero” modzichepetsa kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu.—Salmo 65:2; 138:6; Yohane 14:6.
Ena angalingalire kuti chifukwa chakuti Mulungu saoneka, ndiye kuti si weniweni. Kwa iwo, Mulungu angakhale ngati chinthu chosafikirika. Ngakhale Akristu ena, amene aphunzira za mikhalidwe yodabwitsa ya Mulungu, nthaŵi zina angalephere kuzindikira mmene iye alili weniweni. Kodi mumamva motero? Ngati zili motero, kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kuti muziona Yehova Mulungu kukhala weniweni?
Phunzirani Malemba
Kodi mumaphunzira Malemba Oyera nthaŵi zonse? Ngati muphunzira Baibulo nthaŵi zonse ndiponso ngati muliphunzira kwambiri, Yehova Mulungu adzakhaladi weniweni kwa inu. Choncho, chikhulupiriro chanu chidzalimbitsidwa, ndipo kenaka mudzangokhala ngati ‘mukuona wosaonekayo.’ (Ahebri 11:6, 27) Mosiyana ndi zimenezo, ngati muphunzira Baibulo mwa apo ndi apo, chikhulupiriro chanu sichidzalimbitsidwa kwenikweni.
Tiyeni tifanizire kuti dokotala wanu wakupatsani mankhwala oti muzipaka kaŵiri patsiku pazotupatupa zimene zimakutulukani moŵirikiza. Kodi zotupatupazo zingasiye kutuluka ngati mupaka mankhwalawo kamodzi kapena kaŵiri pamwezi? Nzokayikitsa ngati zingasiye. Mofananamo, wamasalmo akutipatsa “uphungu” wa thanzi lauzimu. Ŵerengani Mawu a Mulungu ndi ‘kuwalingirira usana ndi usiku.’ (Salmo 1:1, 2) Kuti tipeze mapindu ochuluka, tifunikira kutsatira “uphungu”—kuphunzira Mawu a Mulungu tsiku lililonse, mothandizidwa ndi zofalitsa zachikristu.—Yoswa 1:8.
Kodi mukufuna kuti nthaŵi zanu zophunzira Baibulo zikhale zolimbitsa chikhulupiriro? Tayesani kugwiritsira ntchito lingaliro ili: Mutaŵerenga chaputala china m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures kapena m’Baibulo lina lokhala ndi malifalensi, sankhani vesi lochititsa chidwi ndipo ŵerengani malemba omwe aperekedwa monga malifalensi. Zimenezi zidzapangitsa phunziro lanu kukhala latanthauzo, ndipo mosakayika konse mudzazindikira kuti Baibulo lonse nlogwirizana. Kenaka, zimenezi zidzapangitsa Mlembi wake, Yehova Mulungu, kukhala weniweni kwa inu.
Kugwiritsira ntchito malifalensi kungakuthandizeninso kuzindikira maulosi a m’Baibulo ndi kukwaniritsidwa kwake. Mwina mumadziŵa bwino maulosi akuluakulu a m’Baibulo, monga onena za chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Ababulo. Koma Baibulo lili ndi maulosi enanso ambirimbiri ogwirizana ndi kukwaniritsidwa kwake. Ena mwa maulosi ameneŵa sadziŵika kwenikweni.
Mwachitsanzo, taŵerengani za ulosi wonena za chilango choperekedwa kwa munthu amene adzayesa kumanganso Yeriko ndipo taŵerenganinso za kukwaniritsidwa kwake. Yoswa 6:26 amati: “Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.” Ulosiwu unakwaniritsidwa patapita zaka pafupifupi 500, popeza timaŵerenga pa 1 Mafumu 16:34 kuti: “M’masiku ake [a Mfumu Ahabu] Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Zegubi mwana wake wotsiriza; monga mwa mawu a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.”a Mulungu woona yekha ndiye angauzire maulosi otere nakwaniritsidwadi.
Pamene muŵerenga Baibulo, mungachite chidwi ndi mfundo ina. Mwachitsanzo, mungafune kudziŵa kuti kodi panapita zaka zingati kuti ulosi wakutiwakuti ukwaniritsidwe. M’malo mongofunsa wina, bwanji osayesetsa kudzipezera yankho lake? Pogwiritsira ntchito matchati ndi zothandizira kuphunzira Baibulo, funani mayankho mwakhama monga momwe mungachitire pofufuza mwakhama mapu a kumene kuli chuma. (Miyambo 2:4, 5) Kupeza mayankho mwa njira imeneyi kudzalimbitsa chikhulupiriro chanu ndipo kudzapangitsa Yehova Mulungu kukhala weniweni kwa inu.
Pempherani Mobwerezabwereza Ndiponso Mwaphamphu
Musanyalanyaze kufunika kwa pemphero ndi chikhulupiriro. Ophunzira a Yesu anapempha mwachindunji kuti: “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” (Luka 17:5) Ngati Yehova sakuonekabe kukhala weniweni kwa inu, bwanji osampempha chikhulupiriro chowonjezereka? Pemphani Atate wanu wakumwamba mwachidaliro kuti akuthandizeni kumuona iye kuti ali weniweni.
Ngati muli ndi vuto lalikulu, patulani nthaŵi yabwino yofotokoza za vutolo kwa Bwenzi lanu lakumwamba mochokera pansi pa mtima. Pamene Yesu anali pafupi kufa, iye anapemphera mobwerezabwereza. Ngakhale kuti anatsutsa khalidwe la atsogoleri achipembedzo lopereka mapemphero aatali pofuna kuti anthu awaone, iye anapemphera kwayekha usiku wonse asanasankhe atumwi ake 12. (Marko 12:38-40; Luka 6:12-16) Tingatengereponso phunziro pazimene anachita Hana, amene anadzakhala amayi wake wa mneneri Samueli. Pofunitsitsa mwana wamwamuna, “iye analikupempherabe pamaso pa Yehova.”—1 Samueli 1:12.
Kodi tingatengepo phunziro lalikulu liti pazonsezi? Ngati mukufuna kulandira mayankho a mapemphero anu, muyenera kupemphera mofunitsitsa, mwaphamphu, ndiponso mosaleka—komatu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Luka 22:44; Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17; 1 Yohane 5:13-15) Ngati muchita zimenezi mudzapangitsa Mulungu kukhala weniweni kwa inu.
Yang’anani Chilengedwe
Umunthu wa mmisiri wa zojambulajambula umadziŵika ndi zinthu zomwe anajambula. Mofananamo, “mikhalidwe yosaoneka” ya Yehova, Wolinganiza ndi Mlengi wa chilengedwe chonse, imaonekera m’chilengedwe chake. (Aroma 1:20, NW) Ngati tiyang’ana mosamalitsa pazinthu zimene Yehova anazipanga ndi manja ake, timadziŵa bwino umunthu wake, ndipo iye amakhala weniweni kwa ife.
Ngati muyang’ana mwachidwi zinthu zolengedwa ndi Mulungu, mungazizwe kuona kuti iye alidi ndi mikhalidwe yapadera. Mwachitsanzo, nkhani yonena za mmene mbalame zimayendera maulendo aatali ingawonjezere chidziŵitso chanu cha nzeru za Yehova. Ngati muŵerenga nkhani zonena za kuthambo, mungadziŵe kuti mlalang’amba wa Milky Way, umene ukulu wake ngwofanana ndi mtunda umene kuŵala kumayenda pazaka pafupifupi 100,000, ndi umodzi chabe mwa milalang’amba ina zikwi mazana ambirimbiri thambo lonse. Kodi zimenezi sizikusonyeza nzeru za Mlengi?
Ndithudi, nzeru za Yehova nzakuya! Koma kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa inu? Zoonadi, iye sangazunguzike konse ndi mavuto amene aliyense wa ife angamuuze m’pemphero. Inde, ngakhale chidziŵitso chochepa cha chilengedwe chingapangitse Yehova kukhala weniweni kwa inu.
Yendani ndi Yehova
Kodi inuyo panokha mungazindikire mmene Yehova alili weniweni? Inde, mungatero ngati muli ofanana ndi kholo lokhulupirikalo Nowa. Iye anamvera Yehova nthaŵi zonse, kotero kuti anati ponena za iye: “Nowa anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:9) Nowa ankakhala monga kuti Yehova anali pambali pake. Mulungu angakhalenso weniweni motero kwa inu.
Ngati muyenda ndi Mulungu, mumakhulupirira malonjezo a m’Malemba ndipo mumachita zinthu mogwirizana ndi malonjezowo. Mwachitsanzo, mumakhulupirira mawu a Yesu akuti: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo [zosoŵa zakuthupi] zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:25-33) Zoonadi, si nthaŵi zonse pamene Yehova adzakupatsani zinthu zimene mukufuna m’njira imene mukuyembekezera. Komabe, ngati mupemphera ndipo mulandira thandizo la Mulungu, iye adzakhaladi weniweni kwa inu monga munthu wokhala pambali panu.
Unansi wathithithi umenewu ndi Yehova umakula ngati munthu apitirizabe kuyenda ndi Mulungu. Talingalirani za Manuela, Mboni yolankhula Chispanya, amene anapirira ziyeso zambiri. Iye anati: “Nthaŵi zonse ndikapeza mavuto kapena kusoŵa chinachake, ndimagwiritsira ntchito pulinsipulo la pa Miyambo 18:10. Ndimathamangira kwa Yehova kuti andithandize. Iye nthaŵi zonse wakhala ‘linga lolimba’ kwa ine.” Manuela ananena zimenezi atadalira Yehova ndi kuthandizidwa ndi iye kwazaka 36.
Kodi mwayamba kudalira Yehova? Musagwe mphwayi ngati unansi wanu suli monga momwe mumafunira. Tsiku lililonse khalani monga munthu amene akuyenda ndi Mulungu. Pamene mukulitsa moyo wachikhulupiriro, mudzakhala mabwenzi athithithi ndi Yehova.—Salmo 25:14, NW; Miyambo 3:26, 32.
Njira ina yoyendera ndi Mulungu ndiyo kudzitanganitsa ndi utumiki wake. Ngati mukugwira ntchito yolalikira Ufumu, muli antchito anzake a Yehova. (1 Akorinto 3:9) Kuzindikira zimenezi kudzapangitsa Mulungu kukhala weniweni kwa inu.
Wamasalmo anapereka chilimbikitso chakuti: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.” (Salmo 37:5) Musasiye kusenzetsa Mulungu katundu wolemera kapena nkhaŵa iliyonse yomwe mungakhale nayo. Nthaŵi zonse yang’anani kwa iye kaamba ka chithandizo ndi chitsogozo. Ngati nthaŵi zonse mudalira Yehova Mulungu mwa pemphero ndi kumkhulupirira kuchokera pansi pa mtima, mudzaona kuti muli pamtendere chifukwa chakuti mudzadziŵa kuti iye sadzalephera kukuthandizani. Kodi mumakhala ndi chidaliro chonse pamene mutula nkhaŵa zanu kwa Yehova? Mudzaterodi—ngati Mulungu ali weniweni kwa inu.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna chitsanzo china, ŵerengani za ulosi wa kutembereredwa kwa guwa la nsembe la Yerobiamu pa 1 Mafumu 13:1-3. Ndipo taonani kukwaniritsidwa kwake pa 2 Mafumu 23:16-18.
[Chithunzi patsamba 21]
Pangitsani nthaŵi yanu yaphunziro kukhala nthaŵi yolimbitsa chikhulupiriro
[Chithunzi patsamba 22]
Patulani nthaŵi yopemphera moŵirikiza, ndiponso mwaphamphu
[Zithunzi patsamba 23]
Yang’anani mmene mikhalidwe ya Mulungu imasonyezedwera m’chilengedwe
[Mawu a Chithunzi]
Hummingbird: U.S. Fish and Wildlife Service, Washington, D.C./Dean Biggins; nyenyezi: Chithunzi: Copyright IAC/RGO 1991, Dr. D. Malin et al, Isaac Newton Telescope, Roque de los Muchachos Observatory, La Palma, Canary Islands