“Kuyembekezera Mwachidwi”
“Chilengedwe chikuyembekezera mwachidwi kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu.”—AROMA 8:19, NW.
1. Kodi zinthu zikufanana motani pakati pa Akristu lerolino ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba?
ZINTHU kwa Akristu oona lerolino zikufanana ndi mmene zinalili kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba. Ulosi unathandiza atumiki a Yehova a m’masikuwo kudziŵa nthaŵi imene Mesiya adzafika. (Danieli 9:24-26) Ulosi umodzimodziwo unaneneratu za kuwonongedwa kwa Yerusalemu koma sunatchule kalikonse kodziŵitsa Akristu pasadakhale za nthaŵi imene mzindawo udzawonongedwa. (Danieli 9:26b, 27) Mofananamo, m’zaka za zana la 19, Mulungu anapangitsa kuti ulosi wina upatse chiyembekezo ophunzira Baibulo oona mtima. Mwa kugwirizanitsa “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” za pa Danieli 4:25 ndi “nthaŵi za Akunja,” iwo anakhala ndi chiyembekezo chakuti Kristu adzalandira mphamvu ya Ufumu mu 1914. (Luka 21:24, King James Version; Ezekieli 21:25-27) Pamene kuli kwakuti buku la Danieli lili ndi maulosi ambiri, lilibe ulosi uliwonse umene ungatheketse ophunzira Baibulo amakono kuŵerengera nthaŵi yeniyeni imene dongosolo lonse la zinthu la Satana lidzawonongedwa. (Danieli 2:31-44; 8:23-25; 11:36, 44, 45) Komabe, zimenezi zidzachitika posachedwapa, popeza tikukhala mu “nthaŵi ya chimaliziro.”—Danieli 12:4.a
Kudikira m’Nthaŵi ya Kukhalapo kwa Kristu
2, 3. (a) Kodi nchiyani chimene chili umboni waukulu wosonyeza kuti tikukhala m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu mumphamvu yachifumu? (b) Kodi nchiyani chikusonyeza kuti Akristu anayenera kukhalabe odikira m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu?
2 Zoonadi, ulosi unachititsa Akristu kukhala ndi chiyembekezo Kristu asanapatsidwe mphamvu ya Ufumu mu 1914. Koma “chizindikiro” chimene Kristu anapereka cha kukhalapo kwake ndi kutha kwa dongosolo la zinthu chinafotokoza zochitika. Ndipo zambiri mwa zimenezi zinali kudzachitika iye atakhalapo. Zochitika zimenezi—nkhondo, njala, zivomezi, miliri, kuwonjezeka kwa kusayeruzika, kuzunzidwa kwa Akristu, ndi kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi—ndizo maumboni aakulu akuti tsopano tili m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu mumphamvu yachifumu.—Mateyu 24:3-14; Luka 21:10, 11.
3 Komabe, tanthauzo lenileni la uphungu womalizira wa Yesu kwa ophunzira ake linali lakuti: “Yang’anirani, dikirani, . . . Dikirani.” (Marko 13:33, 37; Luka 21:36) Titaŵerenga bwino nkhani yonse ya uphungu umenewu wakuti akhale odikira tikupeza kuti Kristu kwenikweni sanali kunena za kuyang’anira chizindikiro cha kuyamba kwa kukhalapo kwake. M’malo mwake, iye anali kulangiza ophunzira ake oona kuti akhale odikira m’nthaŵi ya kukhalapo kwake. Kodi Akristu oona anafunikira kukhala tcheru ndi chiyani?
4. Kodi chizindikiro chimene Yesu anapereka chinali ndi ntchito yanji?
4 Yesu anapereka ulosi wake waukulu poyankha funso lakuti: “Zija zidzaoneka liti [zinthu zimene zidzachitika chiwonongeko cha dongosolo la zinthu lachiyuda chitayandikira]? Ndipo chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Chizindikiro chimene analosera sichinali kudzasonyeza kukhalapo kwa Kristu kokha, komanso zinthu zimene zidzachitika mapeto a dongosolo la zinthu loipa lilipoli atayandikira.
5. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti pamene kuli kwakuti adzakhalapo mwauzimu, iye ‘adzadzabe’?
5 Yesu anasonyeza kuti panthaŵi ya “kukhalapo” kwake (m’Chigiriki, pa·rou·siʹa) iye adzadza ndi mphamvu ndi ulemerero. Ponena za “kudza” kumeneku (kumene mawu achigiriki ofanana ndi liwu lakuti erʹkho·mai akutanthauza), iye anati: ‘Padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pamitambo yakumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti iye [Kristu] ali pafupi, inde pakhomo. Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika [“lakudza kwa,” NW] Ambuye wanu. . . . Khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.’—Mateyu 24:30, 32, 33, 42, 44.
Kodi Yesu Kristu Adzeranji?
6. Kodi kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu” kudzachitika motani?
6 Ngakhale kuti Yesu Kristu alipo monga Mfumu chiyambire 1914, iye ayenera kuweruza mabungwe ndi anthu kaye asanalange awo amene adzawapeza kukhala oipa. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 5:10.) Posachedwapa Yehova adzachititsa olamulira andale kuti aganize zowononga ‘Babulo Wamkulu,’ ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 17:4, 5, 16, 17) Mwachindunji, mtumwi Paulo ananena kuti Yesu Kristu adzawononga “munthu wosayeruzika”—atsogoleri a Dziko Lachikristu ampatukowo, chimake cha “Babulo Wamkulu.” Paulo analemba kuti: “Adzavumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wapakamwa pake, nadzamuwononga ndi maonekedwe a kudza kwake.”—2 Atesalonika 2:3, 8.
7. Pamene Mwana wa munthu adzafika muulemerero wake, kodi adzapereka chiweruzo chotani?
7 Posachedwa pompa, Kristu adzaweruza anthu amitundu pazimene akuchitira abale ake amene adakali padziko lapansi. Timaŵerenga kuti: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pachimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere. . . . Mfumuyo idzayankha nidzati kwa [nkhosa], Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono awa, munandichitira ichi Ine. . . . Ndipo [mbuzi zidzachoka] kumka kuchilango cha nthaŵi zonse; koma olungama kumoyo wa nthaŵi zonse.”—Mateyu 25:31-46.
8. Kodi Paulo akufotokoza motani za kudza kwa Kristu kudzaŵeruza anthu osaopa Mulungu?
8 Monga momwe fanizo la nkhosa ndi mbuzi limasonyezera, Yesu akupereka chiweruzo chomalizira pa anthu onse osaopa Mulungu. Paulo anatsimikizira okhulupirira anzake amene anali m’masautso za “mpumulo pamodzi ndi ife, pavumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha chowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wamphamvu yake, pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake.” (2 Atesalonika 1:7-10) Pokhala tikuyembekezera zochitika zosangalatsa zonsezi, kodi sitiyenera kusonyeza chikhulupiriro ndi kudikira mwachidwi kudza kwa Kristu?
Kuyembekezera Mwachidwi Vumbulutso la Kristu
9, 10. Kodi nchifukwa ninji odzozedwa amene adakali padziko lapansi akuyembekezera mwachidwi kuvumbulutsidwa kwa Yesu Kristu?
9 “Vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba” silidzangodzetsa chiwonongeko kwa oipa komanso lidzadzetsa mfupo kwa olungama. Otsalira a abale odzozedwa a Kristu amene adakali padziko lapansi mwina adzavutikabe Kristu asanavumbulutsidwe, koma iwo ngokondwa ndi chiyembekezo chawo chaulemerero chakumwamba. Mtumwi Petro analembera Akristu odzozedwa kuti: “Popeza mulaŵana ndi Kristu zoŵaŵa zake, kondwerani: kutinso pavumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.”—1 Petro 4:13.
10 Odzozedwa ngotsimikiza mtima za kukhalabe okhulupirika kufikira Kristu ‘awasonkhanitsa pamodzi kwa iye’ kuti chikhulupiriro chawo ‘choyesedwa chikapezedwe chochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pavumbulutso la Yesu Kristu.’ (2 Atesalonika 2:1; 1 Petro 1:7) Ponena za Akristu okhulupirika ameneŵa obadwa ndi mzimu, tinganene kuti: “Umboni wa Kristu unakhazikika mwa inu; kotero kuti sichikusoŵani inu chaufulu chilichonse; pakulindira inu vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu.”—1 Akorinto 1:6, 7.
11. Poyembekezera kuvumbulutsidwa kwa Yesu Kristu, kodi Akristu odzozedwa akutani?
11 Otsalira odzozedwa akumva monga Paulo, amene analemba kuti: “Ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.” (Aroma 8:18) Chikhulupiriro chawo sichilimbitsidwa mwa kuŵerengera nthaŵi. Iwo ngotanganidwa ndi utumiki wa Yehova, kupereka chitsanzo chabwino kwa anzawo, “nkhosa zina.” (Yohane 10:16) Odzozedwa ameneŵa amadziŵa kuti mapeto a dongosolo loipali ali pafupi, ndipo amamvera malangizo a Petro akuti: ‘Dzimangeni m’chuuno, kunena za mtima wanu [pokonzekera ntchito, NW], mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m’vumbulutso la Yesu Kristu.’—1 Petro 1:13.
‘Kuyembekezera Mwachidwi kwa Chilengedwe’
12, 13. Kodi ndi motani mmene chilengedwe cha anthu ‘chinagonjetsedwera kuutsiru,’ ndipo ankhosa zina akukhumba chiyani?
12 Kodi ankhosa zina nawonso ali ndi chinachake chimene akuyembekezera mwachidwi? Ndithudi ali nacho. Atalankhula za chiyembekezo chaulemerero cha awo amene anatengedwa ndi Yehova kukhala “ana” ake obadwa ndi mzimu ndi kukhalanso “oloŵa anzake a Kristu” mu Ufumu wakumwamba, Paulo anati: “Chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira [“Chilengedwe chikuyembekezera mwachidwi,” NW] vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa kuukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:14-21; 2 Timoteo 2:10-12.
13 Mwa tchimo la Adamu, mbadwa zake zonse ‘zinagonjetsedwa kuutsiru’ chifukwa chobadwira muukapolo wa uchimo ndi imfa. Mbadwazo sizinathe kudzimasula muukapolo umenewu. (Salmo 49:7; Aroma 5:12, 21) Ha! Mmene ankhosa zina akukhumbira ‘kumasulidwa kuukapolo wa chivundi’! Koma zisanachitike zimenezo, zinthu zina ziyenera kuchitika malinga ndi nthaŵi ndi nyengo za Yehova.
14. Kodi “kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu” kudzachitika motani, ndipo zimenezi zidzatheketsa motani ‘kumasulidwa kuukapolo wa chivundi’?
14 Otsalira a “ana a Mulungu” odzozedwawo ayenera ‘kuvumbulutsidwa’ kaye. Kodi zimenezi zidzachitika motani? Panthaŵi yoikika ya Mulungu, ankhosa zina adzatha kuona kuti odzozedwa ‘asindikizidwa chizindikiro’ pomalizira pake ndipo alandira ulemerero wokalamulira ndi Kristu. (Chivumbulutso 7:2-4) “Ana a Mulungu” oukitsidwa amenewo ‘adzavumbulutsidwanso’ pamene adzagwirizana ndi Kristu powononga dongosolo loipa la zinthu la Satana. (Chivumbulutso 2:26, 27; 19:14, 15) Kenako, mu Ulamuliro wa Kristu Wazaka Chikwi, ‘adzavumbulutsidwanso’ monga ansembe mwa amene mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu adzadzera kwa “chilengedwe,” amene ali anthu. Zimenezi zidzapangitsa kuti mtundu wa anthu ‘umasulidwe kuukapolo wa chivundi’ ndi kuloŵa mu “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu” pomalizira pake. (Aroma 8:21; Chivumbulutso 20:5; 22:1, 2) Pokhala akuyembekezera zinthu zazikulu kwambiri zimenezi, kodi nzodabwitsa kuti a nkhosa zina ‘akulindira vumbulutso la ana a Mulungu mwachidwi’?—Aroma 8:19.
Kuleza Mtima kwa Yehova Nchipulumutso
15. Kodi sitiyenera kuiwalanji ponena za nthaŵi ya zochitika yoikidwa ndi Yehova?
15 Yehova ndiye Wosunga Nthaŵi Wamkulu. Nthaŵi imene waikira zochitika idzaoneka kuti ndiyo yabwino koposa. Nthaŵi zina zinthu sizingachitike mmene tinkaziyembekezera patokha. Komabe, tiyenera kukhulupirira zolimba kuti malonjezo onse a Mulungu adzakwaniritsidwa. (Yoswa 23:14) Mwina akulola zinthu kumachitika kwa nthaŵi yaitali kuposa mmene ambiri ankayembekezerera. Koma tiyeni tiyesetse kumvetsa njira zake ndi kuzizwa nazo nzeru zake. Paulo analemba kuti: “Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka! Pakuti anadziŵitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wake ndani?”—Aroma 11:33, 34.
16. Kodi ndani amene adzapindula ndi kuleza mtima kwa Yehova?
16 Petro analemba kuti: “Okondedwa, popeza muyembekeza izi [kuwonongedwa kwa “miyamba” yakale ndi “dziko” lakale ndi kuloŵedwa kwake m’malo ndi “miyamba yatsopano” ndi “dziko latsopano” zolonjezedwa ndi Mulungu], chitani changu kuti [“pomalizira pake,” NW] mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema. Ndipo yesani kulekerera [“kuleza mtima,” NW] kwa Ambuye wathu chipulumutso.” Chifukwa cha kuleza mtima kwa Yehova, anthu enanso mamiliyoni ambiri akupatsidwa mpata wakuti apulumutsidwe pa “tsiku la Mulungu,” limene lidzadza mosayembekezereka “ngati mbala.” (2 Petro 3:9-15) Kuleza mtima kwake kukupatsanso aliyense wa ife mpata kuti ‘tigwire ntchito yake ya chipulumutso chathu ndi mantha, ndi kunthunthumira.’ (Afilipi 2:12) Yesu ananena kuti tiyenera ‘kudziyang’anira tokha’ ndi ‘kudikira’ ngati tikufuna kupeza chiyanjo ndi kulimbika pa “kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu” panthaŵi imene adzadza kudzapereka chiweruzo.—Luka 21:34-36; Mateyu 25:31-33.
Lindiliranibe ndi Chipiriro
17. Kodi ndi mawu a mtumwi Paulo ati amene tiyenera kumvera?
17 Paulo analimbikitsa abale ake auzimu kuti asasumike maso awo pa “zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka.” (2 Akorinto 4:16-18) Sanafune kalikonse kuphimba maso awo pamfupo yawo yakumwamba imene inaikidwa patsogolo pawo. Kaya ndife Akristu odzozedwa kapena ndife a nkhosa zina, tiyeni tizikumbukira chiyembekezo chochititsa kasochi choikidwa patsogolo pathu ndipo tisaleme. Tiyeni ‘tichilindirire ndi chipiriro,’ tikumasonyeza kuti “si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha kuchipulumutso cha moyo.”—Aroma 8:25; Ahebri 10:39.
18. Kodi nchifukwa ninji mwachidaliro tiyenera kusiya nthaŵi ndi nyengo m’manja mwa Yehova?
18 Mwachidaliro, tingasiye nthaŵi ndi nyengo m’manja mwa Yehova. Malonjezo ake adzakwaniritsidwa ‘mosazengereza’ malinga ndi nthaŵi yake. (Habakuku 2:3) Pakali pano, chilimbikitso cha Paulo kwa Timoteo chikutikhudzanso ifeyo. Iye anati: “Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Kristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake; lalikira mawu; chita nawo panthaŵi yake, popanda nthaŵi yake . . . Chita ntchito ya mlaliki . . . , kwaniritsa utumiki wako.”—2 Timoteo 4:1-5.
19. Kodi idakali nthaŵi yoti anthu a Yehova achite chiyani, ndipo chifukwa ninji?
19 Miyoyo ili poopsa—miyoyo yathu ndiponso ya anansi athu. Paulo analemba kuti: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Nthaŵi ya dongosolo loipali la zinthu yatsala nenene kutha. Pamene tikuyembekezera mwachidwi zochitika zapatsogolopa, tiyeni tizikumbukirabe kuti idakali nthaŵi ndi nyengo ya Yehova yoti anthu ake alalikire uthenga wabwino wa Ufumu. Ntchito imeneyo iyenera kuchitidwa momkhutiritsa. “Pomwepo,” anatero Yesu, “chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
[Mawu a M’munsi]
a Onani mitu 10 ndi 11 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kubwereza
◻ Ponena za kuŵerengera nthaŵi, kodi zinthu kwa ife zikufanana motani ndi mmene zinalili kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera ‘kudikira,’ ngakhale panthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu?
◻ Kodi nchifukwa ninji chilengedwe cha anthu chikuyembekezera mwachidwi “kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu”?
◻ Kodi nchifukwa ninji mwachidaliro tingasiye nthaŵi ndi nyengo m’manja mwa Yehova?
[Chithunzi patsamba 17]
Akristu ayenera kukhala odikira poyembekezera kudza kwa Kristu
[Chithunzi patsamba 18]
Otsalira odzozedwa ngotanganitsidwa ndi utumiki wa Yehova, ndipo sanazike chikhulupiriro chawo pa kuŵerengera nthaŵi