Kupereka Nsembe Anthu Achichepere—Osati Kochokera kwa Mulungu
KUNJA kwa malinga a Yerusalemu, kumeneko m’nthaŵi zakale kunali malo otchedwa Tofeti. Kumeneko, Aisrayeli ampatuko, kuphatikizapo Mafumu Ahazi ndi Manase, anali kuchita mwambo wowopsya wa kupereka nsembe ana. Pomalizira, mfumu yokhulupirika Yosiya inaletsa kachitidweko mwakupanga Tofeti kukhala malo osayenera kaamba ka mapwando a chipembedzo.—2 Mafumu 23:10; 2 Mbiri 28:1-4; 33:1, 6.
Nchifukwa ninji malo amenewo anatchedwa Tofeti? Chiyambi cha liwulo chiri chosatsimikiziridwa, koma chiri chosangalatsa kudziŵa chimene wophunzira wa Chiyuda David Kimḥi (c. 1160-c. 1235) ananena ponena za malowa. Akukambitsirana 2 Mafumu 23:10, kumene Tofeti akutchulidwa, iye analemba kuti: “Dzina lamalowo kumene iwo anapangitsa ana awo kupyola [m’moto] kupita kwa Moleki. Dzina la malowo linali Tofeti, ndipo iwo ananena kuti linatchedwa tero chifukwa chakuti pa nthaŵi ya kulambira iwo anali kuvina ndi kuimba zisakasa [Chihebri, tup·pimʹ] kotero kuti tateyo asamve kulira kwa mwana wake pamene iwo anali kumpangitsa iye kupyola m’moto, ndi kuti mtima wake usavutitsidwe pa iye ndi kumtenga iye kuchoka m’manja mwawo. Ndipo malo amenewa anali chigwa chomwe chinali cha munthu wotchedwa Hinomu, ndipo chinali kutchedwa ‘Chigwa cha Hinomu’ ndi ‘Chigwa cha Mwana wa Hinomu’ . . . Yosiya anaipitsa malo amenewo, kuwachepetsa iwo kukhala malo odetsedwa, kutairako mitembo ndi zonse zodetsedwa, kuti chisadzabwerenso mu mtima mwa munthu kupangitsa mwana wake wamwamuna ndi mwana wake wamkazi kudutsa moto kupita kwa Moleki.”
M’nthaŵi zamakono, mulungu Moleki ali kokha chozizwitsa cha mbiri yakale, ndipo ambiri mosakaikira amachipeza icho kukhala chovuta kumvetsetsa nchifukwa ninji anthu anapha ana awo kaamba ka iye. Komabe, akulu lerolino akuwonekerabe kukhala okonzekera kupha ana awo pamene chiwayenerera iwo. Mkati mwa zana lino, mamiliyoni a achichepere aperekedwa nsembe pa guwa lansembe la nkhondo. Chaka chirichonse, mamiliyoni osaŵerengeka a ana osabadwa amaphedwa dala mwa kuchotsa mimba, ambiri a iwo chifukwa chakuti kupangika kwawo m’mimba kunali chotulukapo cha kugonana kongoseŵera kapena chifukwa chakuti kubadwa kwawo kukasokoneza njira ya moyo ya makolo awo. Chotero, ana amenewa amakhala nsembe kwa milungu ya ufulu wa kugonana ndi kukondetsa zinthu za kuthupi.
Yehova ananena kuti kutentha kwa ana kwa Moleki kunali chonyansa. (Yeremiya 7:31) Kodi iye amakuwona mosiyanako kupha kopanda cholinga kwa anthu achichepere mu mbadwo wathu?
[Zithunzi patsamba 31]
Kupereka nsembe ana kwa mulungu wonyenga Moleki, monga mmene kunasonyezedwera zaka 75 zapita “m’Chitsanzo cha Zithunzithunzi za Chilengedwe”
Chigwa cha Hinomu chamakono, kuyang’ana cha kum’mawa