“Ndikudziwa Kuti Adzauka”
“Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.”—YOH. 11:11.
1. Kodi Marita ankakhulupirira zotani zokhudza mchimwene wake? (Onani chithunzi choyambirira.)
LAZARO atamwalira, Marita anali ndi chisoni kwambiri. Iye anali wophunzira wa Yesu komanso mnzake ndipo Yesuyo anamutonthoza pomuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Ngakhale kuti chisoni cha Marita sichinatheretu, anavomereza zimene Yesu ananena. Iye anati: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” (Yoh. 11:20-24) Iye sankakayikira kuti m’tsogolomu Lazaro adzauka. Kenako Yesu anachita zinthu zodabwitsa kwambiri chifukwa anaukitsa Lazaro tsiku lomwelo.
2. Kodi n’chifukwa chiyani mungafune kukhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Marita?
2 Masiku ano sitiyembekezera kuti Yesu kapena Atate wake angatichitire zomwezo. Koma kodi inuyo mumakhulupiriranso ndi mtima wonse kuti m’tsogolo akufa adzauka? Mwina munthu wina amene munkamukonda kwambiri anamwalira ndipo mukulakalaka mutamuona, kucheza naye kapena kumukumbatira. N’kutheka kuti amene anamwalira ndi mwamuna kapena mkazi wanu, mayi anu, bambo anu, agogo anu kapenanso mwana wanu. N’zosangalatsa kuti mofanana ndi Marita, muli ndi zifukwa zomveka zoti munenenso kuti: ‘Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa.’ Ndi bwino kuti Mkhristu aliyense aziganizira zifukwa zimene zingatichititse kuti tisamakayikire zoti akufa adzauka.
3, 4. Kodi zimene Yesu anali atachita ziyenera kuti zinalimbitsa bwanji chikhulupiriro cha Marita?
3 N’zokayikitsa kuti Marita, yemwe ankakhala pafupi ndi Yerusalemu, anaona Yesu akuukitsa mwana wa mkazi wamasiye pafupi ndi mzinda wa Naini ku Galileya. Koma ayenera kuti anamva zimene zinachitikazo. Yesu anaukitsanso mwana wa Yairo. Anthu amene anali kunyumba ya Yairo ‘ankadziwa kuti mwanayo wamwalira’ koma Yesu anatenga dzanja lake n’kumuuza kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!” Nthawi yomweyo mtsikanayo anadzuka. (Luka 7:11-17; 8:41, 42, 49-55) Marita ndi Mariya ankadziwa kuti Yesu amatha kuchiritsa odwala. Choncho ankaona kuti Yesu akanakhalapo, Lazaro sakanamwalira. Ndiye popeza anamwalira, kodi ankakhulupirira kuti n’chiyani chidzachitike? Kumbukirani kuti Marita ananena kuti Lazaro adzauka m’tsogolo, “m’tsiku lomaliza.” Kodi n’chifukwa chiyani ankakhulupirira zimenezi? Nanga n’chiyani chingakuthandizeni kukhulupirira kuti anzanu amene anamwalira akhoza kudzaukitsidwa m’tsogolo?
4 Pali zinthu zingapo zimene zingakuthandizeni kukhulupirira zimenezi. Munkhaniyi tikambirana mfundo zina za m’Baibulo zomwe mwina simunkaganizira kuti zingakuthandizeni pa nkhani imeneyi.
ZOCHITIKA ZIMENE ZIMATITHANDIZA KUKHALA NDI CHIYEMBEKEZO
5. N’chiyani chinathandiza Marita kuti asakayikire kuti Lazaro adzaukitsidwa?
5 Kumbukirani kuti Marita sananene kuti ‘Ndikuganiza kuti mchimwene wanga adzauka.’ M’malomwake ananena kuti: “Ndikudziwa kuti adzauka.” Iye sankakayikira zimenezi chifukwa anamva za anthu ena amene anaukitsidwa ndipo ena anaukitsidwa Yesu asanabwere padzikoli. Iye anamva zimenezi ali mtsikana, mwina kunyumba kwawo kapena kusunagoge. Mwina inunso mukukumbukira nkhani zitatu za m’Malemba zokhudza kuukitsidwa kwa anthu.
6. Kodi Marita ayenera kuti ankadziwa nkhani iti?
6 Nkhani yoyamba ya kuukitsidwa inachitika nthawi ya mneneri Eliya. Eliya atapita kutauni ya Zarefati ku Foinike, analandiridwa ndi mkazi wamasiye wosauka. Yehova anachititsa kuti ufa ndi mafuta za mkaziyo zisathe moti iye ndi mwana wake anapulumuka chilala. (1 Maf. 17:8-16) Kenako mwana wa mkazi wamasiyeyo anayamba kudwala mpaka anafa koma Eliya anamuthandiza. Iye anakumbatira mwana wakufayo n’kupemphera kuti: “Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo wa mwanayu ubwerere mwa iye.” Mulungu anayankha pemphero la Eliya moti mwanayo anaukadi. M’Baibulo, imeneyi ndi nkhani yoyamba yokhudza kuuka kwa munthu wakufa. (Werengani 1 Mafumu 17:17-24.) Marita ayenera kuti ankaidziwa bwino nkhani imeneyi.
7, 8. (a) Kodi Elisa anathandiza bwanji mkazi wamasiye amene anaferedwa? (b) Kodi zimene Elisa anachitazi zinasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu yotani?
7 Nkhani yachiwiri inachitika nthawi ya Elisa, yemwe analowa m’malo mwa Eliya. Mkazi wina wachiisiraeli, yemwe anali wodziwika ku Sunemu, analandira bwino Elisa m’nyumba yake. Yehova anadalitsa mkaziyo ndi mwamuna wake wachikulire moti anakhala ndi mwana wamwamuna. Koma patapita zaka zingapo, mwanayo anamwalira. Kodi inuyo mukuganiza kuti mayi ake anamva bwanji? Iye atakambirana ndi mwamuna wake, ananyamuka ulendo wa makilomita 30 kupita kukaonana ndi Elisa kuphiri la Karimeli. Mneneriyo anatuma Gehazi kuti atsogole popita ku Sunemu n’cholinga choti akaukitse mwanayo koma sanathe kumuukitsa. Kenako mayi a mwanayo anafika limodzi ndi Elisa kunyumbako.—2 Maf. 4:8-31.
8 Elisa anafika pafupi ndi thupi la mwanayo n’kupemphera. Mnyamatayo anauka ndipo anamupereka kwa mayi ake omwe anasangalala kwambiri. (Werengani 2 Mafumu 4:32-37.) Mayiyu ayenera kuti anakumbukira mawu amene Hana ananena m’pemphero lake popereka Samueli kuti azitumikira kuchihema. Paja ananena kuti: “Yehova ndi . . . Wotsitsira Kumanda, ndiponso Woukitsa.” (1 Sam. 2:6) Ku Sunemu, Mulungu anasonyezadi kuti ali ndi mphamvu youkitsa munthu wakufa.
9. Fotokozani nkhani ina yodabwitsa yokhudza Elisa.
9 Koma pali nkhani inanso yodabwitsa imene ikukhudza Elisa. Iye anakhala mneneri kwa zaka zoposa 50 kenako “anadwala matenda amene pamapeto pake anafa nawo.” Tsiku lina ku Isiraeli kunafika gulu la achifwamba ndipo pa nthawiyo n’kuti thupi la Elisa litangotsala mafupa okhaokha. Aisiraeli ena akupita kukaika maliro, anaona gululo ndipo pothawa anangoponya mtembo umene ananyamula m’manda amene munali mafupa a Elisa. Baibulo limati: “Mtembowo utangokhudza mafupa a Elisa, munthuyo anakhalanso wamoyo ndipo anaimirira.” (2 Maf. 13:14, 20, 21) Kodi mukuganiza kuti nkhani ngati zimenezi zinakhudza bwanji Marita? Ziyenera kuti zinamutsimikizira kuti Mulungu alidi ndi mphamvu youkitsa anthu. Nanga kodi nkhani zimenezi zingakuthandizeni bwanji inuyo? Ziyenera kukutsimikizirani kuti Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire.
ZOCHITIKA MUNTHAWI YA YESU KOMANSO YA ATUMWI
10. Kodi Petulo anathandiza bwanji mayi wina amene anamwalira?
10 M’Malemba Achigiriki mulinso nkhani zosonyeza kuti Mulungu anaukitsa anthu pogwiritsa ntchito atumiki ake. Mwachitsanzo, Yesu anaukitsa munthu pafupi ndi mzinda wa Naini ndiponso m’nyumba ya Yairo. Nayenso mtumwi Petulo anaukitsa mayi wina dzina lake Dorika (Tabita). Petulo atafika kumene kunali thupi lake anapemphera ndipo kenako ananena kuti: “Tabita, dzuka!” Nthawi yomweyo mayiyo anakhalanso moyo ndipo Petulo “anamupereka” kwa Akhristu anzake. Anthu anadabwa kwambiri moti ambiri “anakhala okhulupirira mwa Ambuye.” Zimenezi zinawalimbikitsa kuti azilalikira za Yesu komanso kuuza anthu kuti Mulungu ali ndi mphamvu youkitsa akufa.—Mac. 9:36-42.
11. Fotokozani zimene zinachitika kuti mnyamata wina aukitsidwe, nanga zimenezi zinakhudza bwanji anthu?
11 Mu nthawi ya Paulo anthu ena anaonanso munthu akuukitsidwa. Tsiku lina, mtumwi Paulo anali pamsonkhano umene unkachitika m’chipinda cham’mwamba ku Torowa, komwe panopa ndi kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Turkey. Paulo anakamba nkhani mpaka pakati pa usiku ndipo mnyamata wina dzina lake Utiko ankamvetsera atakhala pafupi ndi windo m’chipinda chachitatu m’mwamba. Kenako iye anayamba kugona ndipo anagwa kuchoka pawindopo kufika pansi. N’kutheka kuti Luka, yemwe anali dokotala, ndi amene anayamba kufika pamene mnyamatayo anagwera ndipo atamuona ananena kuti sikuti wangokomoka koma wafa. Zitatero, Paulo anatsika masitepe n’kukumbatira thupi la mnyamatayo kenako n’kunena kuti: “Ali moyo tsopano.” Zimenezi ziyenera kuti zinadabwitsa anthu. Iwo ataona kuti mnyamata amene anafayo wauka “anatonthozedwa kwambiri.”—Mac. 20:7-12.
N’ZOSAKAYIKITSA KUTI AKUFA ADZAUKA
12, 13. Malinga ndi zimene takambirana munkhaniyi, kodi tingafunse mafunso ati?
12 Nkhani zimene takambiranazi ziyenera kukuthandizani ngati mmene zinathandizira Marita. Ziyenera kukutsimikizirani kuti Mulungu amene amapereka moyo ali ndi mphamvu youkitsa akufa. Koma chochititsa chidwi n’chakuti anthu amene ankaukitsidwawo ankauka mothandizidwa ndi atumiki a Mulungu okhulupirika monga Eliya, Yesu ndi Petulo. Ndiye kodi tinganene chiyani za anthu amene anamwalira pa nthawi imene Mulungu sankaukitsa anthu? Kodi zikanakhala zomveka kuti atumiki a Mulungu okhulupirika aziyembekezera zoti m’tsogolo akufa adzauka? Kodi zikanakhala zomveka kuti azikhala ndi maganizo amene Marita anali nawo akuti: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza”? Kodi n’chiyani chinathandiza Marita kukhulupirira zimenezi, nanga n’chiyani chingakuthandizeni inuyo?
13 M’Baibulo muli malemba ambiri osonyeza kuti atumiki a Yehova okhulupirika ankadziwa kuti idzafika nthawi pamene akufa adzauka. Tiyeni tsopano tikambirane malemba angapo.
14. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Abulahamu pa nkhani ya kuuka kwa akufa?
14 Taganizirani zimene Mulungu anauza Abulahamu kuti achite. Paja anamuuza kuti: “Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo, ndipo . . . ukamupereke nsembe yopsereza.” (Gen. 22:2) Popeza Isaki anali mwana amene Abulahamu ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali, kodi mukuganiza kuti iye anamva bwanji Mulungu atamuuza zimenezi? Yehova anali atalonjeza Abulahamu kuti mbewu yake idzathandiza kuti anthu a mitundu yonse adalitsidwe. (Gen. 13:14-16; 18:18; Aroma 4:17, 18) Ananenanso kuti mbewuyo “idzachokera mwa Isaki.” (Gen. 21:12) Ndiye kodi zonsezi zikanatheka bwanji ngati Abulahamu akanapha Isaki? Paulo ananena kuti Abulahamu ankakhulupirira kuti Mulungu akhoza kuukitsa Isaki. (Werengani Aheberi 11:17-19.) Baibulo silisonyeza kuti Abulahamu ankaganiza kuti akapha Isakiyo, Mulungu adzamuukitsa patapita maola ochepa, tsiku limodzi kapena mlungu umodzi. Abulahamu sankadziwa kuti mwana wakeyo adzaukitsidwa liti koma sankakayikira kuti Yehova adzamuukitsa.
15. Kodi Yobu sankakayikira chiyani?
15 Nayenso Yobu ankadziwa kuti Mulungu adzaukitsa akufa. Iye anazindikira kuti mtengo ukadulidwa umaphukanso koma si mmene zilili ndi anthu. (Yobu 14:7-12; 19:25-27) Munthu amene wafa sangauke payekha. (2 Sam. 12:23; Sal. 89:48) Koma sikuti Yobu ankatanthauza kuti Mulungu sangaukitse anthu. Iye ankakhulupirira kuti akafa, padzakhala nthawi imene Yehova adzamukumbukire n’kumuukitsa. (Werengani Yobu 14:13-15.) Yobu sanadziwe nthawi yeniyeni imene Mulungu adzamukumbukire. Koma sankakayikira kuti amene analenga anthu akhoza kumukumbukira n’kumuukitsa.
16. Kodi mngelo analimbikitsa bwanji Danieli?
16 Munthu wina wokhulupirika amene amatchulidwa m’Malemba Achiheberi ndi Danieli. Iye anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri ndipo Yehova ankamuthandiza. Pa nthawi ina, mngelo anamuuza kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambiri.” Anamuuzanso kuti ‘mtendere ukhale naye’ komanso ‘alimbe mtima.’—Dan. 9:22, 23; 10:11, 18, 19.
17, 18. Kodi Danieli analonjezedwa za chiyani?
17 Danieli anali wachikulire kwambiri, wazaka pafupifupi 100, ndipo n’kutheka kuti ankaganizira kwambiri za tsogolo lake. Kodi Danieli anali m’gulu la anthu amene adzauke? Inde. Tikutero chifukwa chakuti chakumapeto kwa buku la Danieli timawerenga mawu olimbikitsa amene Mulungu anamuuza akuti: “Ndiyeno iwe pita ku mapeto ndipo udzapuma.” (Dan. 12:13) Danieli anazindikira kuti akufa amakhala ngati akupumula ndipo kumanda kumene ankapita kulibe “kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru.” (Mlal. 9:10) Koma amenewa sanali mapeto a zonse.
18 Uthenga umene Mulungu anauza Danieli unapitiriza kuti: “Udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.” Danieli sanauzidwe za tsiku kapena nthawi. Anangouzidwa kuti akadzafa zidzakhala ngati wapita kumapeto n’kupuma. Koma mawu oti “udzauka kuti ulandire gawo lako” anamutsimikizira kuti akadzafa, adzauka patapita nthawi yaitali. Nthawi imene adzaukeyo ndi imene anaifotokoza kuti “pa mapeto a masikuwo.” Baibulo lina linamasulira mawu amene Danieli anauzidwawa kuti: “Udzauka kuti ulandire gawo lako pa nthawi ya mapeto.”—Jerusalem Bible.
19, 20. (a) Kodi nkhani zimene takambirana zinathandiza bwanji Marita kuti asakayikire zoti mchimwene wake adzauka? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
19 Marita anali ndi zifukwa zomveka zomuchititsa kukhulupirira kuti mchimwene wake, yemwe anali wokhulupirika, “adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” Lonjezo limene Danieli anapatsidwa komanso mawu amene Marita anayankha Yesu ziyenera kutilimbikitsa masiku ano. Tikutero chifukwa zimatitsimikizira kuti akufa adzauka.
20 Zinthu zimene zinachitika m’mbuyomu zimatsimikizira kuti akufa akhoza kuuka n’kukhalanso ndi moyo. Atumiki a Mulungu akale ankakhulupirira kuti m’tsogolomu idzafika nthawi pamene anthu akufa adzauke. Koma kodi pali umboni wosonyeza kuti lonjezo loti munthu adzauka likhoza kukwaniritsidwa ngakhale patapita nthawi yaitali? Ngati umboniwo ulipo, ukhoza kutithandizanso kukhulupirira kwambiri zoti akufa adzauka. Koma kodi ndi liti pamene anthu adzauke? Tidzakambirana mafunso amenewa munkhani yotsatira.