Mphamvu ya Mawu Achifundo
“Mtima woŵerama ndi nkhaŵa, mawu achifundo angautsitsimule chotani nanga!”—Miyambo 12:25, Knox.
AKRISTU sali otetezereka ku masoka. Nthaŵi zina amakhala ndi nkhaŵa chifukwa cha kukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino.—2 Timoteo 3:1.
Poyang’anizana ndi tsoka, kumakhala dalitso chotani nanga kumva mawu achifundo a bwenzi lokhulupirika! “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka,” Baibulo limatero. (Miyambo 17:17) Mwamuna wokhulupirika Yobu anadziŵika chifukwa cha kukhala bwenzi la mtundu umenewu. Ngakhale Elifazi anati ponena za iye: “Pamene wina anakhumudwa, kufooka ndi kutopa, mawu ako anamlimbikitsa kunyamuka.”—Yobu 4:4, Today’s English Version.
Komabe, pamene Yobu mwiniyo anafunikira chilimbikitso, Elifazi ndi anzake sananene mawu achifundo. Anaimba mlandu Yobu chifukwa cha tsoka lake, akumasonyeza kuti ayenera kukhala atachita tchimo la mseri. (Yobu 4:8) The Interpreter’s Bible imati: “Chimene Yobu afunikira ndicho chifundo cha mtima wa munthu. Chimene alandira ndicho mpambo wa mawu achipembedzo ojeda ndi ndemanga za makhalidwe zimene zili ‘zoona’ ndi zabwinodi.” Yobu anavutika kwambiri atamva zokamba za Elifazi ndi anzake kwakuti anakakamizika kulira kuti: “Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti, ndi kundithyolathyola nawo mawu?”—Yobu 19:2.
Tisachititse konse mtumiki mnzathu wa Mulungu kulira mosautsidwa mtima chifukwa cha mawu athu opanda nzeru ndi opanda chifundo. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 24:15.) Mwambi wa Baibulo umachenjeza kuti: “Zimene mumalankhula zingapulumutse moyo kapena kuuwononga; chotero muyenera kulandira zotsatirapo za mawu anu.”—Miyambo 18:21, TEV.
Pozindikira mphamvu ya mawu, tiyeni titsatire chitsanzo cha mtumwi Paulo. Pamene anali ku Makedoniya, anali “kulimbikitsa awo amene anali kumeneko ndi mawu ambiri.”—Machitidwe 20:2, NW.