Mutu 12
Mukulowetsedwa m’Nkhani Yofunika
1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji njira imene mukukhalira imakhaladi nkanthu kwa inu? (b) Kodi nkwayaninso kumene imakhala nkanthu, ndipo kodi nchifukwa ninji?
MMENE MUKUKHALIRA moyo wanu kumakhaladi nkanthu. Kudzatanthauza kwa inu mwina mtsogolo mosangalatsa kapena mwachisoni. Potsirizira pake kudzatsimikizira kaya inu mukupita ndi dziko lino kapena kupyola mapeto ake kulowa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu mmene mungakhale ndi moyo kosatha.—1 Yohane 2:17; 2 Petro 3:13.
2 Koma mmene mukukhalira moyo wanu kumayambukira ambiri koposa inu nokha. Ena akulowetsedwamo. Zimene mukuchita zimawayambukiranso. Mwa chitsanzo, ngati makolo anu ngamoyo, zimene mukuchita zingawapatse mwina ulemu kapena manyazi. Baibulo limati: “Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.” (Miyambo 10:1) Kwakukulukulu, mmene mukukhalira moyo wanu kumayambukira Yehova Mulungu. Kungampangitse mwina kukondwera kapena kungampangitse kumva chisoni. Chifukwa ninji? Chifukwa cha nkhani yofunika mu imene mukulowetsedwamo.
KODI ANTHU ADZAKHALA OKHULUPIRIKA KWA MULUNGU?
3. Kodi nchitokoso chotani chimene Satana anapereka kwa Yehova?
3 Nkhani imeneyi inadzutsidwa ndi Satana Mdyerekezi. Anaidzutsa pamene anali wokhoza kuchititsa Adamu ndi Hava kuswa lamulo la Mulungu ndipo motero kugwirizana naye m’kupandukira Mulungu. (Genesis 3:1-6) Zimenezi zinapatsa Satana zimene iye analingalira kuti zinali zifukwa zolankhulira ndi Yehova monyoza: ‘Anthu amakutumikirani kokha chifukwa cha zimene amapeza kwa inu. Ingondipatsani mpata ndipo ndingathe kuchotsa aliyense kwa inu.’ Ngakhale kuli kwakuti mawu amenewa sakupezekadi m’Baibulo, nkwachiwonekere kuti Satana ananena kanthu kena kwa Mulungu konga kameneka. Zimenezi zikusonyezedwa m’bukhu Labaibulo la Yobu.
4, 5. (a) Kodi Yobu anali yani? (b) Kodi nchiyani chimene chinachitika kumwamba m’nthawi ya Yobu?
4 Yobu anali munthu amene anakhalako zaka mazana ambiri chipanduko chitachitika m’munda wa Edene. Iye anali mtumiki wa Mulungu wolungama ndi wokhulupirika. Koma kodi zinalidi nkanthu kwa Mulungu kapena kwa Satana kuti Yobu anali wokhulupirika? Baibulo limasonyeza kuti zinaterodi. Likutiuza za kuwonekera kwa Satana pamaso pa Yehova m’bwalo la kumwamba. Wonani nkhani ya kukambitsirana kwawo:
5 “Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudziwonetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pawo. Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m’dziko ndi kuyendayenda m’mwemo. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi wawonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupewa zoipa?”—Yobu 1:6-8.
6. Kodi ndinkhani yotani imene Baibulo limasonyeza kuti inakhalako m’nthawi ya Yobu?
6 Kodi nchifukwa ninji Yehova anatchula kwa Satana kuti Yobu anali munthu wowongoka? Mwachiwonekere, panali nkhani yakuti kaya Yobu akakhalabe wokhulupirika kwa Yehova kapena ayi. Ganizirani funso la Mulungu, “Ufuma kuti?” ndi yankho la Satana, “Kupitapita m’dziko ndi kuyendayenda m’mwemo.” Funso limeneli ndi yankho la Satana zinasonyeza kuti Yehova anali kuloleza Satana mpata waufulu wa kukwaniritsa chitokoso chake chakuti iye akatha kuchotsa aliyense kwa Mulungu. Eya, kodi yankho la Satana kunali lotani ku funso la Yehova lonena za kukhulupirika kwa Yobu?
7, 8. (a) Kodi Satana ananena kuti Yobu anatumikira Mulungu kaamba ka chifukwa chotani? (b) Kodi Yehova anachitanji kuti athetse nkhaniyo?
7 “Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu awopa Mulungu pachabe? Kodi simunamchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m’dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.”—Yobu 1:9-11.
8 Mwa yankho lake Satana anali kuwiringula ponena za kukhulupirika kwa Yobu kwa Mulungu. ‘Yobu amakutumikirani,’ anatero Satana, ‘chifukwa cha zinthu zimene mumpatsa, osati chifukwa chakuti amakukondani.’ Satana anadandaulanso kuti Yehova anali kugwiritsira ntchito mphamvu yake yaikulu m’njira yosakhala bwino. ‘Mwamutetezera nthawi zonse,’ iye anatero. Motero, kuti athetse nkhaniyo, Yehova anayankha kuti: “Tawona, zonse ali nazo zikhale m’dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako!” —Yobu 1:12.
9. Kodi Satana anachititsira Yobu vuto lotani, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani?
9 Nthawi yomweyo Satana anayamba kuchititsira vuto Yobu. Iye anachititsa zifuyo zonse za Yobu mwina kuphedwa kapena kubedwa. Ndiyeno analinganiza kuti ana 10 a Yobu aphedwe. Yobu anataya pafupifupi chirichonse, komabe iye anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Iye sanatemberere Mulungu. (Yobu 1:2, 13-22) Koma amenewo sanali mapeto a nkhaniyo.
10. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Satana sanaleke?
10 Satana anawonekeranso limodzi ndi angelo ena pamaso pa Yehova. Kachiwirinso Yehova anafunsa Satana ngati iye adawona kukhulupirika kwa Yobu nati: “Naumirirabe kukhala wangwiro.” Atatero Satana anayankha kuti: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza pfupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.”—Yobu 2:1-5.
11. (a) Kodi ndiziyeso zowonjezereka zotani zimene Satana anachititsira Yobu? (b) Kodi chotulukapo chinali chiyani?
11 Mwa kuyankha Yehova anapatsa Satana chilolezo cha kuchita chirichonse chimene akatha kwa Yobu, ngakhale kuli kwakuti Mulungu anati: ‘Usamuphe.’ (Yobu 2:6) Motero Satana anakantha Yobu ndi nthenda yowopsa. Kuvutika kwa Yobu kunali kwakukulu kwambiri chakuti iye anapempha kuti afe. (Yobu 2:7; 14:13, 14) Mkazi wake weniweni anamuukira, akumati: “Chitira Mulungu mwano, ufe!” (Yobu 2:9) Koma Yobu anakana kuchita zimenezo. “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga!” iye anatero. (Yobu 27:5) Yobu anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu. Motero kunatsimikiziridwa kuti Satana analakwa m’chitokoso chake chakuti Yobu anatumikira Mulungu kokha kaamba ka phindu lakuthupi ndipo osati chifukwa cha chikondi. Kunasonyezedwanso kuti Satana sakachotsa aliyense ku kutumikira Mulungu.
12. (a) Kodi ndiyankho lotani ku chitokoso cha Satana limene Yobu anapatsa Mulungu? (b) Kodi kukhulupirika kwa Yesu kwa Mulungu kunatsimikiziranji?
12 Kodi mukuganizira kuti njira yokhulupirika ya Yobu inapangitsa Yehova kumva motani? Inampangitsa kukondwa kwambiri! Mawu a Mulungu amafulumiza kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) NdiSatana amene akutonza Yehova. Ndipo mwa njira yake yokhulupirika Yobu anakondweretsa mtima wa Mulungu. Imeneyi inapatsa Mulungu yankho ku chitonzo chonyada cha Satana kapena chitokoso chakuti anthu sakamtumikira poyesedwa. Ena ambiri apatsanso Mulungu yankho loterolo. Chitsanzo chachikulu koposa chinali munthu wangwiroyo Yesu. Iye anagwira zolimba kukhulupirika kwake kwa Mulungu mosasamala kanthu za ziyeso ndi mavuto onse amene Satana anadzetsa pa iye. Zimenezi zinatsimikizira kuti munthu wangwiroyo Adamu akadachita zimodzimodzi ngati akadafuna kutero, ndi kuti Mulungu sanali wosalungama m’kufuna kumvera kotheratu kuchokera kwa munthu.
KODI MUKUIMA PATI?
13. (a) Kodi njira imene mukukhalira moyo wanu imakhala nchiyani ndi nkhaniyo? (b) Kodi tingakondweretse Mulungu motani kapena kumumvetsa ululu?
13 Bwanji ponena za moyo wanu? Simungaganizire kuti kumakhaladi nkathu mmene inu mukukhalira ndi moyo. Koma kumaterodi. Kaya mukuzidziwa kapena ayi, kumachirikiza mwina mbali ya Mulungu ya nkhaniyo kapena mbali ya Satana. Yehova amadera nanu nkhawa, ndipo amafuna kukuwonani mukumtumikira ndi kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso. (Yohane 3:16) Pamene Aisrayeli anapandukira Mulungu, iye anapwetekedwa kapena anamva ululu. (Salmo 78:40, 41) Kodi njira yanu ya moyo ndipo ija imene ikupangitsa Mulungu kukondwa kapena kupwetekedwa nayo? Ndithudi, kuti mukondweretse Mulungu mufunikira kuphunzira malamulo ake ndi kuwamvera.
14. (a) Ponena za kugonana, kodi ndi malamulo otani amene tiyenera kumvera kuti tikondweretse Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuswa malamulo oterowo kuli tchimo?
14 Cholinga chachikulu cha Satana ndicho kuchititsa anthu kuswa malamulo a Mulungu amene amalamulira kugwiritsiridwa ntchito kwa mphamvu zawo zoberekera, ndi kakonzedwe kake ka ukwati ndi banja. Malamulo a Mulungu otetezera chimwemwe chathu amanena kuti anthu osakwatira sayenera kulowa m’kugonana, ndi kuti anthu okwatira sayenera kugonana ndi wina aliyense kuphatikiza pa mnzawo wa mu ukwati. (1 Atesolonika 4:3-8; Ahebri 13:4) Pamene lamulo la Mulungu liswedwa, kawirikawiri ana amabadwa opanda makolo amene amawakonda ndi kuwafuna. Amayi angachititsedi kutaya mimba, kupha ana iwo asanabadwe. Ndiponso, ambiri amene amachita chigololo amapeza nthenda zowopsa zakugonana zimene zingapundule ana amene iwo angabale. Ndiko kachitidwe ka kusakhulupirika, tchimo lochimwira Mulungu, kugonana ndi munthu wina amene sunakwatirane naye. Yobu anati: “Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, ngati ndalalira pa khomo la mnzanga, . . . icho ndi choipitsitsa, ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake.”—Yobu 31:1, 9, 11.
15. (a) Ngati tichita dama, kodi timakondweretsa yani? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kumvera malamulo a Mulungu?
15 Sitiyenera kudabwa kuti dziko lolamulidwa ndi Mdyerekezi lino likapangitsa kuwoneka kukhala kwabwino ndi koyenera kugonana ndi munthu amene sunakwatirane naye. Koma ngati mutero, kodi mukukondweretsa yani? Satana, osati Yehova. Kuti mukondweretse Mulungu, muyenera “kuthawa dama.” (1 Akorinto 6:18, NW) Zowona, sikofewa nthawi zonse kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Sikunali kofewanso kwa Yobu. Koma kumbukirani, nkwanzeru kumvera malamulo a Mulungu. Mudzakhala wosangalala kwambiri tsopano ngati mutero. Koma, chofunika kwambiri, mudzakhala mukuchirikiza mbali ya Mulungu ya nkhaniyo ndipo mudzamkondweretsa. Ndipo iye adzakudalitsani ndi moyo wosatha m’chimwemwe padziko lapansi.
16. (a) Kodi Yobu anadalitsidwa motani chifukwa cha kukhulupirika kwake? (b) Kodi nchiyani chimene chinganenedwe ponena za chivulazo chimene Satana amachititsa, monga ngati kuphedwa kwa ana 10 a Yobu?
16 Zowona, Satana anali wokhoza kuchititsa Yobu umphawi ndi kuchititsa imfa ya ana ake 10. Palibe kukayikira kuti kumeneku kunali kutayikiridwa kwakukulu kwa Yobu. Koma pamene Yobu anatsimikizira kukhala wokhulupirika, Mulungu anamdalitsa ndi zowirikiza kuchuluka kwa zimene adali nazo Satana asanaloledwe kumuyesa. Yobu anabalanso ana ena 10. (Yobu 42:10-17) Ndiponso, tingatsimikizire kuti ana 10 a Yobu amene anaphedwa ndi Satana adzabwezeretsedwa ku moyo m’chiukiriro cha akufa. Ndithudi, palibe chivulazo kapena vuto limene Satana akuloledwa kuchititsa limene Atate wathu wachikondi, Yehova sadzakonza m’nthawi yake yokwanira.
17. Kodi nchifukwa ninji njira imene mumakhalira imakhaladi nkanthu?
17 Motero mudzafuna nthawi zonse kukumbukira kuti mmene mukukhalira moyo wanu kumakhaladi nkanthu. Kumakhala nkanthu makamaka kwa Yehova Mulungu ndi Satana Mdyerekezi. Zimenezi ziri chifukwa chakuti mwalowetsedwa m’nkhani yakuti kaya anthu adzakhala okhulupirika kwa Mulungu kapena ayi.
[Chithunzi patsamba 106]
Yobu anayankha chitokoso cha Satana chakuti palibe aliyense akakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu poyesedwa
[Chithunzi patsamba 110]
Kugonana ndi munthu wina amene simunakwatirane naye ndiko tchimo lochimwira Mulungu
[Chithunzi patsamba 111]
Yehova anadalitsa Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake ndi zoposa kwambiri zimene adali nazo kale