Yobu
42 Kenako Yobu anayankha Yehova kuti:
2 “Tsopano ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse,
Ndiponso kuti palibe chilichonse chimene mukufuna kuchita chimene simungakwanitse.+
3 Inu munati, ‘Kodi uyu ndi ndani amene akuphimba malangizo anga nʼkumalankhula mopanda nzeruyu?’+
Choncho ndinalankhula, koma mosazindikira
Zokhudza zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine, zimene sindikuzidziwa.+
4 Inu munati, ‘Tamvera, ndikufuna ndilankhule.
Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.’+
5 Makutu anga anamva za inu,
Koma tsopano ndikukuonani ndi maso angawa.
7 Yehova atanena mawu amenewa kwa Yobu, Yehova anauza Elifazi wa ku Temani kuti:
“Mkwiyo wanga wayakira iweyo ndi anzako awiriwo,+ chifukwa simunanene zoona za ine,+ ngati mmene wachitira mtumiki wanga Yobu. 8 Tsopano utenge ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7. Upite nazo kwa mtumiki wanga Yobu, ndipo inuyo mukapereke nsembe yopsereza chifukwa cha tchimo lanu. Ndiyeno Yobu mtumiki wanga akakupemphererani.+ Ndithudi ineyo ndidzayankha pempho lake* kuti ndisakuchitireni zinthu mogwirizana ndi zopusa zimene mwachita, chifukwa simunanene zoona zokhudza ine ngati mmene wachitira mtumiki wanga Yobu.”
9 Choncho Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Shuwa ndi Zofari wa ku Naama anapita nʼkukachita zimene Yehova anawauza. Ndipo Yehova anamva pemphero la Yobu.
10 Yobu atapempherera anzake aja,+ Yehova anathetsa mavuto a Yobu+ nʼkubwezeretsa chuma chimene anali nacho.* Yehova anamupatsa zonse zimene anali nazo, kuwirikiza kawiri.+ 11 Azichimwene ndi azichemwali ake onse komanso anzake onse akale+ anapita kwa iye ndipo anadya naye limodzi chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamulimbikitsa komanso kumupepesa chifukwa cha masoka onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwo anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.
12 Yehova anadalitsa kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake+ moti iye anakhala ndi nkhosa 14,000, ngamila 6,000, ngʼombe 2,000* ndi abulu aakazi 1,000.+ 13 Anakhala ndi ana enanso aamuna 7 ndi ana aakazi atatu.+ 14 Mwana wake wamkazi woyamba anamʼpatsa dzina lakuti Yemima, wachiwiri Keziya ndipo wachitatu Kereni-hapuki. 15 Mʼdziko lonselo munalibe akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, ndipo bambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi azichimwene awo.
16 Pambuyo pa zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140 ndipo anaona ana ake ndi zidzukulu zake mpaka mʼbadwo wa 4. 17 Pomalizira pake Yobu anamwalira atakhala ndi moyo wautali komanso wosangalatsa.*