Mutu 10
Pamene Wina m’Banja Wadwala
1, 2. Kodi Satana anagwiritsira ntchito motani tsoka ndi matenda kuyesa kuswa umphumphu wa Yobu?
NDITHUDI, Yobu ayenera kuŵerengeredwa pakati pa anthu amene anasangalala ndi moyo wa banja wachimwemwe. Baibulo limamutcha ‘woposa anthu onse a Kummaŵa.’ Anali ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu, pamodzi ana khumi. Analinso wokhoza kusamalira banja lake bwino lomwe. Chofunika koposa, anatsogolera pazinthu zauzimu ndipo anaika mtima pa kaimidwe ka ana ake pamaso pa Yehova. Zonsezi zinachititsa maunansi achimwemwe kukhalapo pabanja.—Yobu 1:1-5.
2 Satana, mdani wamkulu wa Yehova Mulungu, anaona mkhalidwe wa Yobu. Satana ameneyo, amene nthaŵi zonse amafunafuna njira zakuswa nazo umphumphu wa atumiki a Mulungu, anaukira Yobu mwa kuwononga banja lake lachimwemwe. Kenako, ‘anazunza Yobu ndi zilonda zoŵaŵa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pa mutu wake.’ Motero, Satana anagwiritsira ntchito tsoka ndi matenda kuti aswe umphumphu wa Yobu.—Yobu 2:6, 7.
3. Kodi nthenda ya Yobu inali motani?
3 Baibulo silimatchula dzina lenileni la nthenda ya Yobu. Komabe, limatiuza mmene inalili. Mnofu wake unali mphutsi zokhazokha, ndipo khungu lake linali kuola ndi kudyeka. Mpweya wa Yobu unali wochititsa nseru, ndipo thupi lake linali lonunkha kuola. Anali pa ululu wosaneneka. (Yobu 7:5; 19:17; 30:17, 30) M’kusautsika kwake, Yobu anali kukhala m’mapulusa akumadzikanda ndi phale. (Yobu 2:8) Ndithudi, anali wogwetsa misozi kumuona!
4. Kodi nchiyani chimene chimagwera banja lililonse nthaŵi ndi nthaŵi?
4 Kodi mukanachita motani mukanadwala nthenda yowopsa chotero? Lerolino, Satana samazunza atumiki a Mulungu ndi nthenda mmene anachitira kwa Yobu. Komabe, chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthu, zovuta za moyo wa tsiku ndi tsiku, ndi kuwonongeka kwa malo amene tikukhalamo, tiyenera kuyembekezera kuti ena m’banja adzadwala nthaŵi ndi nthaŵi. Mosasamala kanthu za njira zodzitetezera nazo zimene tingatenge, tonsefe tikhoza kudwala, ngakhale kuti ndi oŵerengeka chabe amene angavutike kufika pamlingo wa Yobu. Pamene matenda aloŵa m’banja, angakhale ovutitsa kwenikweni. Chotero tiyeni tione mmene Baibulo limatithandizira kulimbana ndi mdani wa anthu ameneyu wokhalapo nthaŵi zonse.—Mlaliki 9:11; 2 Timoteo 3:16.
KODI MUMAMVA MOTANI ZIKACHITIKA?
5. Kodi a m’banja amachita motani pamene kwagwa matenda osakhalitsa?
5 Kusokonezeka kwa moyo wozoloŵereka kumakhala kovutitsa nthaŵi zonse, mosasamala kanthu za chochititsa, makamaka ngati chosokonezacho ndi matenda osachira msanga. Ngakhale matenda osakhalitsa amafuna kusintha zinthu, kulolera, ndi kudzimana. Enawo m’banja amene ali bwino angafunikire kukhala chete kuti wodwalayo apeze mpumulo. Angafunikire kuleka kuchita zinthu zinazake. Chikhalirechobe, m’mabanja ambiri ngakhale ana aang’ono amachitira chifundo mwana mnzawo wodwala kapena kholo, ngakhale kuti nthaŵi zina angafunikire kuchita kuwakumbutsa za kuchita zimenezo. (Akolose 3:12) Ponena za matenda osakhalitsa, kaŵirikaŵiri banja limakhala lokonzeka kuchita zofunikira. Ndiponso, aliyense m’banja amayembekezera chisamaliro chofananacho ngati angadwale.—Mateyu 7:12.
6. Kodi nthaŵi zina pamakhala kumva motani pamene wina m’banja wadwala matenda aakulu, ndi osachira msanga?
6 Komabe, bwanji ngati matendawo ali aakulu kwambiri ndipo zosokonezeka nzazikulu ndi zotenga nthaŵi yaitali? Mwachitsanzo, bwanji ngati wina m’banja apuwala ndi stroko, kulemala ndi nthenda ya Alzheimer, kapena kudwala matenda ena ofooketsa? Kapena bwanji ngati wina m’banja wadwala msala, monga nthenda ya schizophrenia? Choyamba pamakhala kumva chifundo—chisoni chakuti wokondedwa akuvutika kwambiri. Komabe, chifundocho chingatsatiridwe ndi mikhalidwe ina. Pamene ena m’banja aona kuti akhudzidwa kwambiri ndipo ufulu wawo wachepa chifukwa cha matenda a winayo, angayambe kuipidwa. Angadandaule kuti: “Kodi ndi tsoka lanji limene laona ine?”
7. Kodi mkazi wa Yobu anachita motani pa kudwala kwa mwamuna wake, ndipo nchiyani chimene mwachionekere anali ataiŵala?
7 Lingaliro lofananalo liyenera kuti linafika m’maganizo a mkazi wa Yobu. Kumbukirani, iye anali atatayikidwa kale ana ake. Pamene masoka amenewo anali kuchitika, mosakayikira, nsautso yake inakulirakulira. Pomalizira pake, pamene anaona kuti mwamuna wake amene kale anali wokangalika ndi wanyonga akuzunzika ndi nthenda yoŵaŵa ndi yonyansa, zikuoneka kuti anaiŵala mfundo yaikulu imene inaposa masoka onsewo—unansi umene iye ndi mwamuna wake anali nawo ndi Mulungu. Baibulo limati: “Pamenepo mkazi [wa Yobu] ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.”—Yobu 2:9.
8. Pamene wina m’banja wadwala kwambiri, kodi ndi lemba liti limene lingathandize ena m’banja kukhala ndi lingaliro loyenera?
8 Ambiri amataya mtima, ngakhale kukwiya, pamene matenda a wina achititsa moyo wawo kusintha kwambiri. Komabe, Mkristu amene amalingalira bwino za mkhalidwewo potsirizira pake ayenera kuzindikira kuti zimenezi zimampatsa mwaŵi wa kusonyeza chikondi chake chenicheni. Chikondi choona “chikhala chilezere, chili chokoma mtima . . . [ndipo] sichitsata za mwini yekha . . . chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:4-7) Chifukwa chake, m’malo mwa kulola malingaliro akuipidwa kukula, nkofunika kuti tiyeseyese kuwakaniza.—Miyambo 3:21.
9. Kodi ndi mfundo ziti zotonthoza zimene zingathandize banja mwauzimu ndi mwamaganizo pamene wina m’banja wadwala kwambiri?
9 Kodi tingachitenji kuti titetezere mkhalidwe wauzimu ndi wamaganizo wa banja pamene wina wadwala kwambiri? Ndithudi, matenda alionse amafuna chisamaliro chake ndi mankhwala ake, ndipo sikungakhale koyenera kunena m’buku lino kuti njira yakutiyakuti yochiritsira kuchipatala kapena yakunyumba ndiyo yabwino. Komabe, m’lingaliro lauzimu, Yehova “awongoletsa onse oŵerama.” (Salmo 145:14) Mfumu Davide analemba kuti: “Wodala iye amene asamalira wosauka: tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa: Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, . . . Yehova adzamgwiriziza pakama wodwalira.” (Salmo 41:1-3) Yehova amasunga atumiki ake ali amoyo mwauzimu, ngakhale pamene ayesedwa mwamaganizo koposa zimene angathe kupirira. (2 Akorinto 4:7) A m’banja ambiri odwala matenda aakulu akumbukira mawu a wamasalmo akuti: “Ndazunzika kwambiri: ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mawu anu.”—Salmo 119:107.
MZIMU WOCHIRITSA
10, 11. (a) Kodi chofunika nchiyani kuti banja likhoze kulimbana ndi matenda? (b) Kodi mkazi wina anakhoza motani kulimbana ndi kudwala kwa mwamuna wake?
10 “Mzimu wa munthu ukhoza kupirira tsoka lake,” umatero mwambi wa Baibulo, “koma mzimu wosweka, ndani angaupirire?” (Miyambo 18:14, NW) Nsautso ingavutitse mzimu wa banja limodzinso ndi “mzimu wa munthu.” Komabe, “mtima wodekha ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30, NW) Kaya banja likukhoza kulimbana ndi matenda kapena ayi zimadalira kwambiri pa maganizo, kapena mzimu, wa a m’banjalo.—Yerekezerani ndi Miyambo 17:22.
11 Mkazi wina wachikristu anapirira kuona mwamuna wake akulemala ndi stroko atakhala muukwati wawo kwa zaka zisanu ndi chimodzi zokha. “Mwamuna wanga anayamba kuvutika kwambiri polankhula, ndipo kunali kovuta kwenikweni kulankhula naye,” akukumbukira motero. “Zinali kundipweteka mtima kwambiri kuyesayesa kumva zimene anali kuvutika kuti anene.” Tangoganizaninso za kusautsika mumtima ndi kuthedwa nzeru kumene mwamunayo anali nako. Kodi okwatiranawo anachitanji? Ngakhale kuti ankakhala kutali ndi mpingo wachikristu, mlongoyo anachita zonse zimene anakhoza kuti akhalebe wolimba mwauzimu mwa kuyendera pamodzi ndi chidziŵitso chatsopano chilichonse cha gulu limodzinso ndi kulandira nthaŵi zonse chakudya chauzimu m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Zimenezi zinampatsa nyonga yauzimu yosamalirira mwamuna wake wokondedwayo kufikira imfa yake zaka zinayi pambuyo pake.
12. Monga momwe taonera m’chochitika cha Yobu, kodi wodwala nthaŵi zina amathandiza motani?
12 M’chochitika cha Yobu, wovutikayo ndiye anakhala wolimba. Anafunsa mkazi wake kuti: “Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa?” (Yobu 2:10) Ndicho chifukwa chake wophunzira Yakobo anadzatchula Yobu kukhala chitsanzo chapadera cha kuleza mtima ndi chipiriro! Pa Yakobo 5:11 timaŵerenga kuti: “Mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha [Yehova, NW], kuti [Yehova] ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” Chimodzimodzi lerolino, kambiri kulimbika mtima kwa wodwala wa m’banja kwathandiza ena m’banjamo kukhala ndi maganizo abwino.
13. Kodi ndi kuyerekezera kotani kumene banja lokhala ndi matenda aakulu siliyenera kuchita?
13 Ambiri amene analimbana ndi matenda m’banja amavomereza kuti poyamba kumakhala kovuta kwa ena m’banja kuvomereza mkhalidwewo. Amanenanso kuti njira imene munthu amaonera mkhalidwewo imakhala yofunika kwambiri. Kupanga masinthidwe m’moyo wozoloŵereka wa banja kungakhale kovuta poyamba. Koma ngati munthu ayesayesa mwakhama, akhoza kuzoloŵera mkhalidwe watsopanowo. Mwakutero, tiyenera kusamala kuti tisayerekezere mkhalidwe wathu ndi wa ena amene alibe matenda m’banja lawo, tikumalingalira kuti moyo wawo uli wofeŵerapo ndi kuti ‘ife tili ndi tsoka chabe!’ Kunena zoona, palibe amene adziŵa kwenikweni zovuta zimene ena angakhale akulimbana nazo. Akristu onse amapeza chitonthozo m’mawu a Yesu akuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu.”—Mateyu 11:28.
KUIKA ZINTHU M’MALO AKE
14. Kodi zinthu zingaikidwe motani m’malo ake?
14 Polimbana ndi matenda aakulu, banja lingachite bwino kukumbukira mawu ouziridwa akuti: “Pochuluka aphungu [zolingirira] zikhazikika.” (Miyambo 15:22) Kodi a m’banjalo angakhale pansi ndi kukambitsirana za mkhalidwe umene matendawo achititsa? Kungakhale koyenera kuchita zimenezi mwa pemphero ndi kutembenukira ku Mawu a Mulungu kaamba ka chitsogozo. (Salmo 25:4) Kodi nzotani zimene ziyenera kulingaliridwa pa makambitsirano oterowo? Chabwino, pali zosankha za banja zimene ziyenera kupangidwa ponena za chithandizo cha kuchiritsa ndi ndalama. Kodi ndani amene adzapereka chisamaliro chachikulu? Kodi ndi motani mmene banja lingathandizire kuchirikiza chisamaliro chimenecho? Kodi makonzedwe opangidwawo adzakhudza motani aliyense m’banjamo? Kodi zofunika zauzimu za wopereka chisamaliro chachikuluyo zidzasamaliridwa motani?
15. Kodi Yehova amapereka chichirikizo chotani ku mabanja okhala ndi matenda aakulu?
15 Kupempherera mwakhama chitsogozo cha Yehova, kusinkhasinkha pa Mawu ake, ndi kulondola molimbika mtima njira yosonyezedwa ndi Baibulo kaŵirikaŵiri kumakhala ndi madalitso odabwitsa. Nthaŵi zina matenda a wodwalayo sangathe. Koma kudalira Yehova nthaŵi zonse kumakhala ndi zotulukapo zabwino kwambiri mumkhalidwe uliwonse. (Salmo 55:22) Wamasalmo analemba kuti: “Chifundo chanu, Mulungu, chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga mkati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.”—Salmo 94:18, 19; onaninso Salmo 63:6-8.
KUTHANDIZA ANA
16, 17. Kodi ndi mfundo zotani zimene ziyenera kutchulidwa pokambitsirana ndi ana aang’ono za kudwala kwa mwana mnzawo?
16 Matenda aakulu angachititse mavuto kwa ana m’banja. Nkofunika kuti makolo athandize anawo kudziŵa zosoŵa zimene zakhalapo ndi zimene angachite kuti athandize. Ngati mwana ndiye wadwala, muyenera kuthandiza ana enawo kudziŵa kuti pamene mupatsa wodwalayo chisamaliro chokulirapo sindiko kuti iwo simuwakonda kwambiri. Kuti pasakhale mkwiyo ndi chidani, makolo ayenera kuthandiza ana enawo kukhala ogwirizana kwambiri ndi kukondana kwenikweni pamene akuthandiza kusamalira mkhalidwe umene matenda amachititsa.
17 Ana aang’ono amamvetsetsa mwamsanga ngati makolo awachititsa kudziŵa mmene zinthu zimamvekera m’malo mwa kuwapatsa malongosoledwe aatali ndi ovuta kumva onena za matenda. Chotero akhoza kuwafotokozera mmene wodwalayo akumvera. Ngati ana osadwalawo aona mmene matenda amalepheretsera wodwala kuchita zimene iwo sanaziganizire, akhoza kukhala ndi ‘chikondi chaubale’ chokulirapo ndi ‘kuchitirana chifundo.’—1 Petro 3:8.
18. Kodi ana akuluko msinkhu angathandizidwe motani kumvetsetsa mavuto amene matenda amachititsa, ndipo zimenezi zingawathandize motani?
18 Ana akulupo msinkhu ayenera kuthandizidwa kuzindikira kuti pali mkhalidwe wovuta umene umafuna aliyense m’banja kukhala wodzimana. Chifukwa cha ndalama zoyenera kulipiridwa kwa dokotala ndi zogulira mankhwala, kungakhale kosatheka kuti makolo asamalire ana enawo mmene angafunire. Kodi anawo adzakwiya ndi zimenezi ndi kuona kuti akumanidwa? Kapena kodi adzamvetsetsa mkhalidwewo ndi kukhala ofunitsitsa kudzimana? Zimadalira kwambiri pa njira imene mumakambitsirana nkhaniyo ndi mzimu umene umakulitsidwa m’banja. Ndithudi, m’mabanja ambiri kudwala kwa mmodzi wa iwo kwathandiza kuphunzitsirapo ana kulondola uphungu wa Paulo wakuti: “Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.”—Afilipi 2:3, 4.
MMENE TIYENERA KUONERA KUCHIRITSA NDI MANKHWALA
19, 20. (a) Kodi ndi mathayo otani amene mitu ya mabanja imakhala nawo pamene wina m’banja wadwala? (b) Ngakhale kuti Baibulo silili buku la zamankhwala, kodi ndi motani mmene limaperekera chitsogozo pa kusamalira matenda?
19 Akristu ozindikira bwino samakana kuchiritsidwa ndi mankhwala malinga ngati sakuwombana ndi lamulo la Mulungu. Pamene wina m’banja adwala, amafuna chithandizo mwakhama kuti wovutikayo achire. Komabe, pangakhale malingaliro osiyana a madokotala amene ayenera kuwapenda mosamala. Ndiponso, m’zaka zaposachedwapa kwabuka matenda atsopano, ndipo ambiri alibe njira imodzi yochiritsira yovomerezedwa ndi onse. Ngakhale kupima matenda kolondola nthaŵi zina kumakhala kovuta kupeza. Pamenepo, kodi Mkristu ayenera kuchitanji?
20 Ngakhale kuti wolemba Baibulo wina anali dokotala ndipo mtumwi Paulo anapereka chilangizo cha mankhwala chothandiza kwa bwenzi lake Timoteo, Malemba ali chitsogozo chauzimu ndi cha makhalidwe abwino, sali buku la zamankhwala. (Akolose 4:14; 1 Timoteo 5:23) Chifukwa chake, pankhani zakuchiritsa, mitu ya mabanja achikristu iyenera kupanga zosankha zawo zoyenera. Mwinamwake angalingalire kuti afunikira kufunsira kwa madokotala ena m’malo mwa mmodzi yekha. (Yerekezerani ndi Miyambo 18:17.) Ndithudi, iwo amafuna chithandizo chabwino koposa chimene chingapezeke kaamba ka wodwalayo m’banja, ndipo ambiri amafuna chithandizo chimenechi kwa madokotala akuchipatala. Ena amakonda njira zochiritsira za akatswiri ena. Iyinso ndi nkhani ya chosankha chaumwini. Chikhalirechobe, pochita ndi mavuto a zamatenda, Akristu samaleka kulola ‘mawu a Mulungu kukhala nyali ya kumapazi awo, ndi kuunika kwa panjira yawo.’ (Salmo 119:105) Amalondolabe zitsogozo zoperekedwa m’Baibulo. (Yesaya 55:8, 9) Chotero, iwo amakana njira zopimira matenda zogwirizana ndi kukhulupirira mizimu, ndipo amapeŵa machiritso amene amaswa mapulinsipulo a Baibulo.—Salmo 36:9; Machitidwe 15:28, 29; Chivumbulutso 21:8.
21, 22. Kodi mkazi wina wa ku Asia analingalira motani pa pulinsipulo la Baibulo, ndipo ndi motani mmene chosankha chimene anapanga chinalili choyenera mumkhalidwe wake?
21 Talingalirani chochitika cha mkazi wachichepere wa ku Asia. Posapita nthaŵi atayamba kudziŵa za Baibulo chifukwa cha kuphunzira ndi mmodzi wa Mboni za Yehova, anabala mwana wamkazi miyezi yake isanakwane amene anali wolemera magalamu 1,470 chabe. Mkaziyo anasweka mtima pamene dokotala anamuuza kuti khandalo lidzalemala kwambiri ndipo silidzalankhula konse. Anamulangiza kupatsa mwanayo kwa osamalira olemala. Mwamuna wake sanadziŵe chochita. Kodi mkaziyo akanatembenukira kwa yani?
22 Iye akuti: “Ndikukumbukira kuphunzira m’Baibulo kuti ‘ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.’” (Salmo 127:3) Anaganiza za kupereka “cholandira” chimenechi kunyumba ndi kuchisamalira. Zinthu zinali zovutadi poyamba, koma ndi chithandizo cha mabwenzi achikristu mumpingo wake wa Mboni za Yehova, mkaziyo anakhoza kusamalira mwanayo ndi kumpatsa chichirikizo chapadera chofunikira. Zaka khumi ndi ziŵiri pambuyo pake, mwanayo anali kupita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu ndi kumaseŵera pamodzi ndi anzake kumeneko. Mayi wakeyo akuti: “Ndili woyamikira kwambiri kuti mapulinsipulo a Baibulo anandilimbikitsa kuchita choyenera. Baibulo linandithandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Yehova Mulungu ndi kusakhala ndi chisoni chimene ndikanakhala nacho moyo wanga wonse.”
23. Kodi Baibulo limapereka chitonthozo chotani kwa odwala ndi kwa owadwazika?
23 Matenda sadzakhala nafe kwamuyaya. Mneneri Yesaya ananena zamtsogolo panthaŵi imene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Lonjezo limenelo lidzakwaniritsidwa m’dziko latsopano limene likufika mofulumira. Komabe, pakali pano tidzapitirizabe kulimbana ndi matenda ndi imfa. Komabe chokondweretsa nchakuti Mawu a Mulungu amatipatsa chitsogozo ndi chithandizo. Malamulo a makhalidwe abwino amene Baibulo limatipatsa ali okhalitsa, ndipo amapambana malingaliro a anthu opanda ungwiro amene amasintha nthaŵi zonse. Chifukwa chake, munthu wanzeru amavomerezana ndi wamasalmo amene analemba kuti: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; . . . Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse. . . . M’kuzisunga izo muli mphotho yaikulu.”—Salmo 19:7, 9, 11.