Kodi Mumalemekeza Ena Popereka Uphungu?
NKWABWINO ndi kopindulitsa chotani nanga kupatsidwa uphungu mwaulemu! “Uphungu woperekedwa mokoma mtima, molingalira, ndi mosamala umachititsa maunansi abwino,” akutero Edward. “Pamene uona kuti phungu akukulemekeza mwa kusonyeza kufunitsitsa kumvetsera mafotokozedwe ako, uphungu wake umakhala wosavuta kwambiri kuulandira,” akunena motero Warren. “Pamene phungu andichitira mwaulemu, ndimakhala womasuka kumfikira, kumpempha uphungu,” akutero Norman.
Kuyenera kwa Munthu Kwachibadwa kwa Kupatsidwa Ulemu
Uphungu wabwino, waubwenzi, ndi wachikondi umalandiridwadi. Kupereka uphungu kwa ena monga momwe mungafunire kuti muchitiridwe nkopindulitsa. (Mateyu 7:12) Phungu wabwino amapatula nthaŵi ya kumvetsera ndi kufunafuna kumvetsetsa munthu amene akupatsidwa uphungu—maganizo ake, mkhalidwe wake, ndi malingaliro ake amtima—mmalo mwa kusuliza ndi kutsutsa.—Miyambo 18:13.
Aphungu a lerolino, kuphatikizapo akulu Achikristu, afunikira kukhala maso kuti alemekeze ena popereka uphungu. Chifukwa ninji? Kaamba ka chifukwa chachimvekere chakuti mkhalidwe wa maganizo umene uli wofala m’chitaganya ngwakuchita ndi ena m’njira yopanda ulemu. Umenewu ngwoyambukira. Kaŵirikaŵiri anthu amene mumayembekezera kukuchitirani mwaulemu ndiwo amene amalephera kutero, kaya akhale anthu ophunzira, atsogoleri achipembedzo, kapena ena. Mwachitsanzo, pamalo antchito kuchotsedwa ntchito nkopweteka ndi kotsendereza maganizo kwa wolembedwa ntchito ndi wolemba ntchito yemwe. Kumawononga ulemu waumwini, makamaka ngati munthu wochotsedwayo achitiridwa mopanda ulemu. Akapitao amene ali mumkhalidwewu ayenera kuphunzira mmene angaperekere “uthenga wovuta kwambiri umenewu kotero kuti umveke bwino, mosavuta ndipo mwaukatswiri, ndi kusungitsa ulemu wa munthuyo,” ikutero The Vancouver Sun. Inde, anthu onse amayenerera kuchitiridwa mwaulemu.
Msonkhano Waukulu wa Mitundu Yogwirizana umati: “Anthu onse amabadwa ali aufulu ndi olingana muulemu ndi zoyenera. Amabadwa ndi nzeru ndi chikumbumtima ndipo ayenera kuchitirana zinthu ndi mzimu waubale.” Popeza kuti ulemu wa munthu ukuukiridwa, pali chifukwa chabwino chakuti Tchata cha Mitundu Yogwirizana ndi mawu oyamba a Universal Declaration of Human Rights zimavomereza mkhalidwe umenewu. Izo zimachirikiza “chikhulupiriro m’zoyenera zofunika za munthu, ulemu ndi kuŵerengeredwa kwa munthu.”
Yehova Analenga Munthu ndi Ulemu wa Choloŵa
Yehova ndi Mulungu waulemu. Mawu ake ouziridwa molondola amati, “Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu,” ndipo, “Ulemerero [wake] pathambo la kumwamba.”—1 Mbiri 16:27; Salmo 8:1.
Monga Mulungu wolemekezeka ndi Mfumu ya Chilengedwe chonse, iye amapereka ulemu pachilengedwe chake chonse, cha kumwamba ndi cha padziko lapansi. Wapadera koposa pakati pa awo amene amalemekezedwa ndiye Mwana wake wolamulira ndi wolemekezedwayo, Mfumu, Kristu Yesu. “Mumchitira iye ulemu ndi ukulu,” Davide analemba motero molosera.—Salmo 21:5; Danieli 7:14.
Mwachisoni, kuyenera kwa munthu kofunika kumeneku kwaipitsidwa kwambiri m’mbiri yonse ya anthu. Mngelo wina wamphamvu, amene mwa zochita zake anakhala Satana Mdyerekezi, anatokosa kuyenera, chilungamo, ndi kufunikira kwa ulamuliro wa Mulungu. Mwakuchita motero iye anasonyeza mnyozo kwa Yehova ndi kusalemekeza dzina Lake lolemekezeka akumatokosa kuyenera Kwake kwa kulamulira. Iye anadzipatsa ulemu wopambanitsa. Mofanana ndi Mdyerekezi, mafumu aumunthu amphamvu, onga ngati Nebukadinezara wa nthaŵi za m’Baibulo, anena modzikuza za ‘mphamvu ndi ulemerero wawo.’ Iwo anapeputsa ulemu wa Yehova, akumadzipatsa ulemu wosayenerera. (Danieli 4:30) Ulamuliro wotsendereza wa Satana, wokakamizidwa pamtundu wa anthu, waukira ndipo ukupitiriza kuukira ulemu wa munthu.
Kodi ulemu wanu unayamba wanyazitsidwapo? Popatsidwa uphungu, kodi unakuchititsani kumva kukhala waliwongo kwambiri, wamanyazi, wopeputsidwa, kapena woluluzidwa? “Sindinaone chisamaliro, chifundo, ndi ulemu. Ndinachititsidwa kudziona kukhala wosanunkha kanthu,” akutero André, nawonjezera kuti: “Zimenezi zinachititsa kugwiritsidwa mwala ndi nkhaŵa, ngakhale kupsinjika maganizo.” “Nkovuta kulandira uphungu kwa munthu amene mukumlingalira kuti sakukufunirani zabwino,” akutero Laura.
Kaamba ka chifukwa chimenechi, oyang’anira Achikristu akulangizidwa kuchitira gulu la nkhosa la Mulungu mwaulemu ndi molemekeza. (1 Petro 5:2, 3) Ngati pabuka mikhalidwe imene kupereka uphungu kwa ena kukakhala kofunika ndi kopindulitsa, kodi mungadzitetezere motani pakuganiza ndi khalidwe la anthu akudziko amene, mosazengereza, amapeputsa ulemu wa ena? Kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kusungitsa ulemu wa Akristu anzathu, ndi wanu womwe?—Miyambo 27:6; Agalatiya 6:1.
Malamulo a Mkhalidwe Amene Amasungitsa Ulemu
Mawu a Mulungu sanaleke kulankhula pankhaniyi. Phungu waluso adzadalira kotheratu uphungu wa Mawu a Mulungu, mmalo mwa kudalira nzeru ya dzikoli. Malembo Opatulika ali ndi chilangizo chamtengo wapatali. Pamene atsatiridwa, amalemekezetsa phungu ndi wolangizidwa yemwe. Motero, chilangizo cha Paulo kwa woyang’anira Wachikristu Timoteo chinali chakuti: “Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale; akazi aakulu ngati amayi; akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.” (1 Timoteo 5:1, 2) Ndichisoni chochuluka chotani nanga, malingaliro ovulazika, ndi manyazi zimene zingapeŵedwe mwa kumamatira kumiyezo imeneyi!
Onani kuti mfungulo ya kupereka uphungu wachipambano ndiyo kupereka ulemu woyenerera kwa munthu wina ndi kuyenera kwake kuchitiridwa m’njira yolemekezeka ndi yosamala. Akulu Achikristu, kuphatikizapo oyang’anira oyendayenda, ayenera kuyesayesa kutsatira uphungu umenewu, akumafunafuna kudziŵa chifukwa chimene munthu wofunikira kusintha maganizo akuganizira ndi kuchita monga momwe akuchitiramo. Iwo ayenera kufuna kumva lingaliro lake, ndi kupanga kuyesayesa kulikonse kupeŵa kuchititsa manyazi, kusambula, kapena kupeputsa munthu amene akuthandizidwa.
Monga mkulu, lolani kuti mbale wanu adziŵe kuti mumasamala za iye ndipo mukufuna kumthandiza pamavuto ake. Zimenezo nzimene dokotala wabwino amachita pamene mufika mu ofesi yake kuti akupimeni. Kulingalira zovula m’chipinda chozizira, chotetezeredwa kutizilombo kungakuchititseni manyazi. Mmene mumayamikirira nanga dokotala amene amazindikira ulemu wanu ndi kukulemekezani mwa kukupatsani chophimba pamene akuchita kupima kofunika kuti adziŵe chochititsa kudwala kwanu! Mofananamo, phungu Wachikristu amene amasonyeza ulemu woyenera kwa munthu ngwokoma mtima ndi wotsimikiza, komabe amapatsa ulemu wolandira uphungu wake. (Chivumbulutso 2:13, 14, 19, 20) Komabe, uphungu umene uli waukali, wopanda chikondi, ndi wosalingalira ngwofanana ndi kuvulidwa kophiphiritsira kumene kumakupangitsani kuchita manyazi, kusambulidwa, ndi kuchotseredwa ulemu wanu.
Makamaka oyang’anira Sukulu Yautumiki Wateokratiki amakhala osamala kupereka uphungu mwaulemu. Polangiza achikulire, amasonyeza chikondi chimodzimodzicho chimene akanasonyeza makolo awo akuthupi. Ngolingalira, aubwenzi, ndi achikondi. Kuzindikira koteroko nkofunika. Kumachititsa mkhalidwe wabwino woperekeramo uphungu moyenerera ndi kuulandira.
Akulu, kumbukirani kuti uphungu wothandiza ngwotsitsimula mtima, wolimbikitsa, womangirira, ndi wabwino. Pa Aefeso 4:29 pamati: “Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.”
Palibe chifukwa chogwiritsirira ntchito mawu, kalankhulidwe, kapena kukambitsirana mwaukali. Mmalomwake, kulemekeza munthu wina ndi chikhumbo cha kusungitsa kudziŵerengera kwake ndi ulemu zimakusonkhezerani kunena nkhaniyo m’njira yabwino ndi yomangirira. Yambani kufotokoza mawu alionse ndi chiyamikiro chenicheni, chochokera mumtima chifukwa cha zimene amachita bwino kapena mikhalidwe yake, mmalo mwa kugogomezera malingaliro amene akumpangitsa kumva kukhala wogwiritsidwa mwala ndi wopanda pake. Ngati mukutumikira monga mkulu, gwiritsirani ntchito ‘ulamuliro wanu kumangirira osati kugwetsera pansi.’—2 Akorinto 10:8.
Inde, cholinga cha uphungu uliwonse wochokera kwa oyang’angira Achikristu chiyenera kukhala cha kupereka chilimbikitso chofunika, kupereka zimene zili zabwino. Suyenera kulefula kapena ‘kuwopseza.’ (2 Akorinto 10:9) Ngakhale munthu amene wachita cholakwa chachikulu afunikira kupatsidwa mlingo wa ulemu waumwini ndi kulemekeza. Uphungu uyenera kukhala wa mawu achidzudzulo achikatikati limodzi ndi kukoma mtima, komabe wamphamvu kotero kuti umsonkhezere kufika pakulapa.—Salmo 44:15; 1 Akorinto 15:34.
Moyenerera, Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli chinaphatikizapo malamulo a mkhalidwe amodzimodziŵa. Chinaloleza kuperekedwa kwa uphungu ndipo ngakhale kumenya, pamene kuli kwakuti panthaŵi imodzimodziyo chikumasungitsa kuyenera kwa munthu kukhala ndi mlingo wa ulemu waumwini. Kukwapula ndi mkwapulo ‘koŵerengedwa mofikira pa choipa[cho]’ kunaloledwa, koma kumeneku sikunayenera kukhala kopambanitsa. Panali malire amene anaikidwa pachiŵerengero cha mikwapulo yoperekedwa kotero kuti wochita cholakwayo ‘asakapeputsidwe.’—Deuteronomo 25:2, 3.
Kusamala malingaliro a wochita cholakwa wolapa kunalinso mkhalidwe wa Yesu. Ponena za iye, Yesaya analosera kuti: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi laŵi lozirala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m’zowona.”—Yesaya 42:3; Mateyu 12:17, 20; Luka 7:37, 38, 44-50.
Ogogomezera mowonjezereka za kufunika kwa kumvera chisoni ndiwo mawu a Yesu mu Ulaliki wa pa Phiri akuti: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Lamulo la mkhalidwe limeneli nlofunika kwambiri m’kuchirikiza maunansi abwino kwakuti kaŵirikaŵiri limatchedwa Lamulo la Makhalidwe Abwino. Monga mkulu Wachikristu, kodi lingakuthandizeni motani kuchitira ena mokoma mtima ndi ulemu popereka uphungu?
Kumbukirani kuti nanunso mumaphophonya. Monga momwe Yakobo ananenera, “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Kukumbukira zimenezi kudzakuthandizani kukhala wosamala ndi mawu anu ndi kulamulira malingaliro anu pamene kuli koyenera kulankhula ndi ena za zolakwa zawo. Zindikirani malingaliro awo. Zimenezi zidzakuthandizani kupeŵa kusuliza kopambanitsa, kukulitsa zophophonya kapena zolakwa zazing’ono. Yesu anagogomezera zimenezi pamene anati: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nawo, kudzayesedwa kwa inunso.”—Mateyu 7:1, 2.
Lemekezani Ena —Tsutsani Mdyerekezi
Njira za Satana zalinganizidwira kukuchotserani ulemu, kuchititsa malingaliro a kumva kukhala wopeputsidwa, wopanda pake, ndi wothedwa nzeru. Onani mmene anagwiritsirira ntchito munthu monga cholankhulira kusonkhezera malingaliro oipa mwa Yobu wokhulupirika. Elifazi wonyengayo anati: “[Yehova] sakhulupirira atumiki ake; nawanenera amithenga ake [angelo oyera] zopusa; kopambana kotani nanga iwo [anthu ochimwa] akukhala m’nyumba zadothi, amene kuzika kwawo kuli m’fumbi, angothudzulidwa ngati gulugufe.” (Yobu 4:18, 19) Chotero malinga ndi kuganiza kwake, Yobu anali wosanunkha kanthu kwa Mulungu mofanana ndi gulugufe. Ndithudi, uphungu wa Elifazi ndi mabwenzi ake, pokhala wosamangirira nkomwe, ukanalanda Yobu ngakhale chikumbukiro cha nthaŵi zakale zosangalatsa. M’kuganiza kwawo kukhulupirika kwake kwanthaŵi yapita, kuphunzitsa banja, unansi ndi Mulungu, ndi mphatso za chifundo zinali zopanda pake.
Mofananamo lerolino, ochita zolakwa olapa amakhala paupandu wa malingaliro otero, ndipo pali ngozi ya kukhala ‘omizidwa ndi chisoni chochuluka.’ Akulu, popereka uphungu kwa anthu otero, ‘tsimikizirani amenewo chikondi chanu’ mwa kuwalola kukhalabe ndi mlingo wa ulemu wawo. (2 Akorinto 2:7, 8) “Kuchitiridwa mopanda ulemu kumachititsa uphungu kukhala wovuta kulandira,” akuvomereza motero William. Nkofunika kulimbitsa chikhulupiriro chawo chakuti ngamtengo wapatali m’maso mwa Mulungu. Akumbutseni kuti Yehova “sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito [yawo], ndi chikondicho [a]dachionetsera kudzina lake” m’zaka zawo zapitazo za utumiki wokhulupirika.—Ahebri 6:10.
Kodi ndizinthu zina ziti zimene zingakuthandizeni kulemekeza ena popereka uphungu? Zindikirani kuti anthu onse ali nako kuyenera kwachibadwa kwa kupatsidwa ulemu, popeza kuti anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. Amaŵerengeredwa ndi Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu; makonzedwe a mbali ziŵiri a dipo ndi chiukiriro amachitira umboni za chowonadi chimenechi. Yehova amawonjezera ulemu winanso kwa Akristu mwa ‘kuwaika kuutumiki,’ akumawagwiritsira ntchito kudandaulira mbadwo woipa kuti uyanjane ndi Mulungu.—1 Timoteo 1:12.
Akulu, kumbukirani kuti namtindi wa abale anu Achikristu ndiwo ziŵalo za maziko oyembekezeredwa a chitaganya chatsopano cha anthu m’dziko lapansi loyeretsedwa. Monga anthu oŵerengedwa ndi amtengo wapatali chotero, amayenerera kupatsidwa ulemu. Popereka uphungu, kumbukirani mmene Yehova ndi Yesu yemwe amawalingalilira, ndipo pitirizanibe kuchita mbali yanu kuthandiza abale anu kuti asungebe ulemu ndi kudziŵerengera moyang’anizana ndi zitokoso za Satana.—2 Petro 3:13; yerekezerani ndi 1 Petro 3:7.
[Bokosi patsamba 29]
Uphungu Umene Umapatsa Ulemu
(1) Perekani chiyamikiro chenicheni, chochokera mumtima. (Chivumbulutso 2:2, 3)
(2) Khalani womvetsera wabwino. Fotokozani bwino lomwe ndi mokoma mtima vutolo ndi chifukwa choperekera uphungu. (2 Samueli 12:1-14; Miyambo 18:13; Chivumbulutso 2:4)
(3) Tengani uphungu wanu m’Malemba. Khalani wotsimikiza, wolingalira, ndi wolimbikitsa, ndipo sonyezani kumvera chisoni. Sungitsani ulemu ndi kudziŵerengera kwa munthuyo. (2 Timoteo 3:16; Tito 3:2; Chivumbulutso 2:5, 6)
(4) Tsimikizirani munthuyo kuti madalitso amadza chifukwa cha kulandira ndi kugwiritsira ntchito uphungu. (Ahebri 12:7, 11; Chivumbulutso 2:7)
[Chithunzi patsamba 26]
Akulu Achikristu afunikira kulemekeza ena popereka uphungu