Kodi Tingatani Kuti Tikhalebe Osangalala?
“Ngakhale munthu atakhala ndi moyo zaka zambiri, m’zaka zonsezo azisangalala.”—MLAL. 11:8
1. Kodi Yehova watipatsa zinthu ziti zomwe zingatithandize kuti tizisangalala?
YEHOVA amafuna kuti tizisangalala. Iye watipatsa zinthu zambiri zotithandiza kuti tizisangalala. Mwachitsanzo, watipatsa moyo komanso watikoka kuti tizimulambira. Choncho tingagwiritse ntchito moyowu pomutamanda. (Sal. 144:15; Yoh. 6:44) Yehova amatithandizanso kuti tizipirira pamene tikumutumikira. Umenewu ndi umboni wakuti amatikonda kwambiri. (Yer. 31:3; 2 Akor. 4:16) Watipatsanso paradaiso wauzimu ndipo tikusangalala chifukwa timapezamo chakudya chauzimu chamwanaalirenji komanso abale ndi alongo amene amatikonda. Kuwonjezera pamenepo, tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolomu.
2. Kodi atumiki ena a Mulungu akulimbana ndi maganizo otani?
2 Ngakhale kuti tili ndi zinthu zosangalatsa zonsezi, atumiki ena a Mulungu sasangalala. Iwo amadziona kuti ndi achabechabe kapena amaona kuti zimene akuchita potumikira Yehova n’zopanda phindu. Amene akulimbana ndi maganizo oterewa amaona kuti n’zosatheka kuti anthu akhale ndi moyo wosangalatsa kwa “zaka zambiri.” Iwo amaona kuti moyo wangodzaza ndi mavuto okhaokha.—Mlal. 11:8.
3. Kodi n’chiyani chimene chimachititsa kuti anthu ena asamasangalale?
3 Abale kapena alongo oterewa amayamba kuganiza choncho chifukwa chokhumudwa, matenda kapena ukalamba. (Sal. 71:9; Miy. 13:12; Mlal. 7:7) Komanso tonsefe tikudziwa kuti mtima ndi wonyenga kwambiri ndipo ungatitsutse ngakhale pamene Mulungu akusangalala nafe. (Yer. 17:9; 1 Yoh. 3:20) Mdyerekezi amaimba atumiki a Mulungu milandu yabodza. Ndipo anthu amene ali ndi maganizo a Satana angatipangitse kuti tiziganiza kuti ndife opanda pake kwa Mulungu. Bodza limeneli ndi limenenso Elifazi, yemwe analibe chikhulupiriro, ananena m’nthawi ya Yobu.—Yobu 4:18, 19.
4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?
4 Malemba amanena mosapita mbali kuti Yehova sadzasiya anthu omwe ‘akuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani.’ (Sal. 23:4) Iye samatisiya chifukwa watipatsa Mawu ake. Baibulo ndi lamphamvu kwambiri ndipo ‘limatha kugwetsa zinthu zozikika molimba,’ kuphatikizapo maganizo olakwika kapena odziona ngati ndife opanda pake. (2 Akor. 10:4, 5) Choncho tiyeni tikambirane mmene Baibulo lingatithandizire kuti tizisangalala. Mfundo zimenezi zitithandiza ifeyo komanso tiona mmene tingalimbikitsire ena.
BAIBULO LINGAKUTHANDIZENI KUTI MUZIKHALABE OSANGALALA
5. N’chiyani chimene chingatithandize kukhalabe osangalala?
5 Mtumwi Paulo anafotokoza zinthu zina zimene zingatithandize kukhalabe osangalala. Iye anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro.” (2 Akor. 13:5) Palembali, mawu oti “chikhulupiriro” akutanthauza mfundo za m’Baibulo zimene Akhristu amakhulupirira. Ngati timachita zinthu mogwirizana ndi mfundo zimenezi ndiye kuti tikadali “olimba m’chikhulupiriro.” Koma tiyenera kuonanso ngati zochita zathu zikugwirizana ndi mfundo zonse zimene Akhristufe timaphunzitsidwa. Sitingasankhe kutsatira mfundo zina n’kusiya zina.—Yak. 2:10, 11.
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziyesa kuti tione “ngati tikadali m’chikhulupiriro?” (Onani chithunzi patsamba 12.)
6 Nthawi zina tingaope kudziyesa poganiza kuti mwina tingalephere mayesowo. Komatu mmene Yehova amationera n’zosiyana ndi mmene timadzionera ndipo maganizo ake ndi apamwamba kuposa athu. (Yes. 55:8, 9) Iye amayang’ana atumiki ake kuti apeze zabwino n’kuwathandiza osati kuti awapezere zifukwa. Mukamagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu podziyesa kuti muone “ngati mukadali m’chikhulupiriro,” mudzayamba kudziona mmene Mulungu amakuonerani. Popeza Baibulo limanena kuti ndinu wamtengo wapatali pamaso pa Yehova, mukamaligwiritsa ntchito mudzasiya kudziona ngati achabechabe. Mudzayamba kudziona kuti ndinu amtengo wapatali ndipo zidzakhala ngati mwatsegula makatani kuti m’nyumba mwanu musakhalenso mdima.
7. Kodi zitsanzo za anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo zingatithandize bwanji?
7 Kuganizira zitsanzo za anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo kungatithandize kwambiri kuti tidziyese ngati tikadali m’chikhulupiriro. Ndi bwino kuganizira zimene zinawachitikira n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikanakhala ineyo ndikanamva bwanji? Nanga ndikanachita zotani?’ Tiyeni tsopano tikambirane zitsanzo za anthu atatu. Zitsanzozi zikusonyeza kuti Baibulo lingatithandize kuti tidziyese ngati tikadali m’chikhulupiriro komanso kuti tizikhalabe osangalala.
MKAZI WAMASIYE WOSAUKA
8, 9. (a) Kodi zinthu zinali bwanji pa moyo wa mkazi wamasiye wosauka? (b) Kodi n’kutheka kuti mkazi wamasiyeyu anali ndi maganizo otani?
8 Pamene Yesu anali kukachisi ku Yerusalemu, anaona mkazi wamasiye wosauka. Chitsanzo cha mayiyu chingatithandize kuti tizisangalala ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. (Werengani Luka 21:1-4.) Taganizirani mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Mwamuna wake anamwalira komanso atsogoleri achipembedzo ‘ankadyerera nyumba za akazi amasiye’ m’malo mowathandiza. (Luka 20:47) Mayiyu anali wosauka kwambiri moti ndalama imene anapereka kukachisi inali yofanana ndi malipiro amene munthu ankalandira akagwira ganyu maminitsi ochepa.
9 Kodi mukuganiza kuti mayiyu ankamva bwanji pamene ankalowa m’bwalo la kachisi atatenga timakobiri tiwiri? Kodi ankayerekezera ndalama zochepazo ndi zimene ankapereka pa nthawi imene mwamuna wake anali moyo? Kodi akanachita manyazi poona anthu ena akupereka zambiri, mwina n’kumaganiza kuti chopereka chakecho n’chosathandiza? Komatu maganizo amenewa sanamulepheretse kupereka kwa Mulungu zimene akanakwanitsa.
10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti Mulungu ankaona kuti mkazi wamasiye uja anali wamtengo wapatali?
10 Yesu anasonyeza kuti Yehova ankaona kuti mayiyu ndi wamtengo wapatali komanso anayamikira ndalama imene anapereka. Ananena kuti mayiyu “waponya zochuluka kuposa [olemera] onse amene aponya.” Ndalama zimene anaperekazo zinasakanikira ndi zimene ena anapereka, koma Yesu anamuyamikira. Anthu osunga ndalamazo sakanadziwa mmene Yehova ankaonera tindalamato komanso amene anapereka. Choncho chofunika kwambiri ndi mmene Mulungu ankaonera zimene mayiyu anachita, osati mmene anthu ena kapena iyeyo ankaonera. Nkhani imeneyi ingakuthandizeni kudziyesa kuti muone ngati mukadali m’chikhulupiriro.
11. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya mkazi wamasiye?
11 Zimene mungapereke kwa Yehova zimadalira mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Ena salalikira kwambiri chifukwa cha ukalamba kapena matenda. Kodi ndi bwino kuti oterewa azikayikira kupereka malipoti? Ngakhale kuti mumachita zambiri mu utumiki, mwina mungaone ngati zimene mukuchitazo n’zochepa poyerekezera ndi maola ambirimbiri amene anthu a Mulungu amathera pomutumikira chaka chilichonse. Koma nkhani ya mkazi wamasiyeyu ikutithandiza kuona kuti Yehova amaona kuti chilichonse chimene atumiki ake akumuchitira, makamaka pa nthawi ya mavuto, n’chamtengo wapatali. Taganizirani zimene mwachita chaka chathachi polambira Yehova. Kodi munafunikira kudzimana zina zake kuti mupeze ola limodzi lomutumikira? Ngati ndi choncho, dziwani kuti Mulungu amaona kuti zimene munachita pa ola limenelo n’zamtengo wapatali kwambiri. Mukamachita zonse zimene mungathe potumikira Yehova, ngati mmene mkazi wamasiye uja anachitira, ndiye kuti “mukadali m’chikhulupiriro.”
“CHOTSANI MOYO WANGA”
12-14. (a) Kodi Eliya anamva bwanji zinthu zitavuta? (b) N’chifukwa chiyani anamva choncho?
12 Mneneri Eliya ankakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo anali wokhulupirika. Koma pa nthawi ina, iye anakhumudwa kwambiri mpaka kufika pouza Yehova kuti angomupha. Iye anati: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga.” (1 Maf. 19:4) Ngati simunakumanepo ndi mavuto okuchititsani kumva chonchi, mungaganize kuti Eliyayo ankangolankhula “zopanda pake.” (Yobu 6:3) Komatu umu ndi mmene ankamveradi pa nthawiyo. Ndipo Yehova sanamukalipire chifukwa chonena zimenezi koma anamuthandiza.
13 Kodi chinachitika n’chiyani kuti Eliya akhale ndi maganizo amenewa? Pa nthawiyi Eliya anali atangopambana kumene pa mayeso amene anasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu woona ndipo aneneri a Baala okwana 450 anaphedwa. (1 Maf. 18:37-40) Eliya ayenera kuti ankaganiza kuti anthu a Mulungu ayamba kulambira Yehova koma izi si zimene zinachitika. Yezebeli, yemwe anali mfumukazi yoipa kwambiri, anatumizira Eliya uthenga woti amupha. Eliya anachita mantha kwambiri n’kuthawa kudutsa ku Yuda mpaka kukafika kuchipululu chinachake.—1 Maf. 19:2-4.
14 Ndiyeno ali yekhayekha kumeneko anayamba kuona kuti zonse zimene wachita pa ntchito yake yauneneri n’zopanda phindu. Iye anauza Yehova kuti: “Sindine woposa makolo anga.” Apatu ankatanthauza kuti iye ndi wachabechabe ndipo ali ngati fumbi komanso mafupa a azigogo ake amene anamwalira. Zinali ngati wadziyesa n’kupeza kuti ndi wolephera komanso wopanda ntchito kwa aliyense kuphatikizapo Yehova.
15. Kodi Yehova anathandiza bwanji Eliya kudziwa kuti akumuonabe kuti ndi munthu wamtengo wapatali?
15 Komatu umu si mmene Wamphamvuyonse ankaonera Eliya. Yehova ankaona kuti Eliya ndi munthu wamtengo wapatali ndipo anamutsimikizira zimenezi. Choyamba, anatumiza mngelo kuti akamulimbikitse. Kenako anamupatsa chakudya ndi madzi kuti zimupatse mphamvu pa ulendo wake wa masiku 40 wopita kuphiri la Horebe. Komanso anamuthandiza kuti asaganize zoti palibe Mwisiraeli wokhulupirika aliyense amene watsala. Chochititsa chidwi n’chakuti Mulungu anamupatsanso ntchito ina ndipo iye anavomera. Eliya atathandizidwa ndi Yehova, analimba mtima ndipo anapitanso kukapitiriza ntchito yake yauneneri.—1 Maf. 19:5-8, 15-19.
16. Kodi Yehova wakuthandizani bwanji inuyo panokha?
16 Nkhani ya Eliyayi ingakuthandizeni kudziyesa kuti muone ngati mukadali m’chikhulupiriro ndipo ingakulimbikitseni kuti muzikhalabe wosangalala. Choyamba, taganizirani mmene Yehova wakuthandizirani inuyo. N’kutheka kuti pa nthawi ina zinthu zitavuta, Mkhristu wina kapena mkulu mumpingo anakuthandizani. (Agal. 6:2) Mwina munalimbikitsidwa mutawerenga Baibulo kapena mabuku athu, apo ayi mutapezeka pa misonkhano ya mpingo. Zoterezi zikachitika muzidziwa kuti Yehova ndi amene wakuthandizani ndipo muzimuyamikira m’pemphero.—Sal. 121:1, 2.
17. Kodi Yehova amaona kuti atumiki ake ndi amtengo wapatali akaganizira chiyani?
17 Chachiwiri, dziwani kuti nthawi zina maganizo athu olakwika akhoza kutipusitsa. Chofunika kwambiri n’chakuti Mulungu aziona kuti ndife okhulupirika. (Werengani Aroma 14:4.) Iye amaona kuti ndife amtengo wapatali akaganizira za kudzipereka kwathu komanso kukhulupirika kwathu osati chifukwa cha zimene takwanitsa kuchita. N’kutheka kuti mofanana ndi Eliya, mwachita zambiri potumikira Yehova koma simukuzindikira. Mwina pali anthu ena mumpingo amene mumawalimbikitsa kwambiri kapena pali anthu ena m’dera lanu amene adziwa choonadi chifukwa cha inuyo.
18. Kodi utumiki umene Yehova wakupatsani umasonyeza chiyani?
18 Chomaliza, muziona utumiki uliwonse umene Yehova wakupatsani ngati umboni wakuti iye ali nanu. (Yer. 20:11) Mofanana ndi Eliya, mwina mungakhumudwe poganiza kuti utumiki wanu sunaphule kanthu kapena zolinga zanu sizingatheke. Koma musaiwale kuti muli ndi mwayi wogwira ntchito yolalikira uthenga wabwino ndiponso wodziwika ndi dzina la Mulungu. Umenewutu ndi mwayi waukulu kuposa wina uliwonse. Choncho khalanibe okhulupirika. Mukatero, zidzakhala ngati mukuuzidwa mawu amene Yesu ananena mu fanizo lake lina akuti: “Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.”—Mat. 25:23.
“PEMPHERO LA MUNTHU WOSAUTSIKA”
19. Kodi zinthu zinali bwanji pa moyo wa amene analemba Salimo 102?
19 Wolemba Salimo 102 anali pa mavuto aakulu. Iye anali “wosautsika” chifukwa chovutika kwambiri ndipo anali ‘atalefuka.’ Choncho analibe mphamvu yolimbana ndi mavuto ake. (Sal. 102, timawu tapamwamba) Mawu ake akusonyeza kuti ankaganizira kwambiri za mavuto akewo ndiponso ankaona kuti ali yekhayekha. (Sal. 102:3, 4, 6, 11) Iye ankakhulupirira kuti Yehova akufuna kumutaya.—Sal. 102:10.
20. Kodi pemphero lingathandize bwanji munthu amene akungoganizira mavuto ake?
20 Koma wamasalimoyu anali adakali ndi mwayi wotamanda Yehova. (Werengani Salimo 102:19-21.) Pa Salimo 102 tikuona kuti ngakhale anthu okhulupirika angakumane ndi mavuto ndipo zingawavute kuti asiye kuganizira mavutowo. Wamasalimoyu ankadziona ngati “mbalame imene ili yokhayokha padenga” ndipo ankaganiza kuti palibe amene angamuthandize pa mavuto ake. (Sal. 102:7) Mukakhala ndi maganizo amenewa muyenera kuuza Yehova m’pemphero zakukhosi kwanu ngati mmene wamasalimoyu anachitira. Mapemphero anu, omwe angakhale ngati mapemphero a munthu wosautsika, angakuthandizeni kuti musamakhumudwe kwambiri. Yehova amalonjeza kuti “adzamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse, ndipo sadzapeputsa pemphero lawo.” (Sal. 102:17) Tisamakayikire lonjezo limeneli.
21. Kodi munthu angatani kuti ayambenso kusangalala?
21 Salimo 102 likusonyezanso zimene mungachite kuti muyambenso kusangalala. Wamasalimo uja atayamba kuganizira za ubwenzi wake ndi Yehova anayamba kusangalala. (Sal. 102:12, 27) Mtima wake unakhala m’malo atadziwa kuti Yehova sadzasiya kuthandiza anthu ake pamene ali pa mavuto. Choncho ngati pali vuto linalake limene likukulepheretsani kuchita zambiri mu utumiki, lipempherereni. Pemphani Yehova kuti akuyankheni, osati pongofuna kupeza mpumulo komanso kuti “dzina lake lilengezedwe.”—Sal. 102:20, 21.
22. Kodi tonsefe tingatani kuti tizisangalatsa Yehova?
22 Taona kuti tikhoza kugwiritsa ntchito Baibulo kuti tione ngati tikadali m’chikhulupiriro komanso kuti Yehova amationa kuti ndife amtengo wapatali. N’zoona kuti m’dzikoli sitingapeweretu kuvutika komanso kukhumudwa. Koma tonsefe tikhoza kusangalatsa Yehova n’kudzapulumuka ngati tipirirabe n’kumamutumikira mokhulupirika.—Mat. 24:13.