Salimo
Pemphero la munthu woponderezedwa pamene ali pamavuto* ndipo akutula nkhawa zake kwa Yehova.+
2 Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pamavuto aakulu.+
3 Chifukwa masiku a moyo wanga akuzimiririka ngati utsi,
Ndipo mafupa anga akutentha kwambiri ngati ngʼanjo.+
6 Ndikufanana ndi mbalame yamʼchipululu yotchedwa vuwo.
Ndakhala ngati nkhwezule yamʼmabwinja.
8 Tsiku lonse adani anga amandinyoza.+
Anthu amene amanditonza amagwiritsa ntchito dzina langa potemberera ena.
9 Ndikudya phulusa ngati chakudya,+
Ndipo zakumwa zanga ndi zosakanikirana ndi misozi.+
10 Izi zili choncho chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanu,
Popeza munandikweza mʼmwamba kuti munditaye.
11 Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka,+
Ndipo ndafota ngati udzu.+
13 Ndithudi inu mudzanyamuka nʼkusonyeza Ziyoni chifundo,+
Chifukwa imeneyi ndi nthawi yoti mumusonyeze kukoma mtima kwanu.+
Nthawi yoikidwiratu yakwana.+
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina lanu, inu Yehova,
Ndipo mafumu onse apadziko lapansi adzaopa ulemerero wanu.+
19 Iye amayangʼana pansi ali pamalo ake apamwamba omwe ndi oyera,+
Yehova amayangʼana dziko lapansi ali kumwamba,
20 Kuti amve kuusa moyo kwa mkaidi,+
Komanso kuti amasule anthu amene aweruzidwa kuti akaphedwe.+
21 Wachita izi kuti dzina la Yehova lilengezedwe mʼZiyoni+
Komanso kuti atamandidwe mu Yerusalemu,
22 Pamene mitundu ya anthu komanso maufumu
Adzasonkhana pamodzi kuti atumikire Yehova.+
23 Anandilanda mphamvu zanga nthawi yake isanakwane.
Anafupikitsa masiku a moyo wanga.
24 Ine ndinati: “Inu Mulungu wanga,
Musachotse moyo wanga ndisanakalambe,
Inu amene mudzakhalapo ku mibadwo yonse.+
26 Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe.
Mofanana ndi chovala, zonsezi zidzatha.
Mofanana ndi zovala zimene zatha, mudzapezerapo zina ndipo nazonso zidzatha.