“Funani Yehova, ndi Mphamvu Yake”
“Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”—2 MBIRI 16:9.
1. Kodi mphamvu n’chiyani, ndipo anthu azigwiritsa ntchito motani?
MPHAMVU ingatanthuze zinthu zosiyanasiyana, monga udindo woyendetsa zinthu, ulamuliro, kapena chisonkhezero pa ena; ingakhale kukhoza kuchita zinthu kapena kukwaniritsa chinachake; mphamvu zakuthupi (nyonga); kapena ingakhale nzeru kapena khalidwe lapamwamba. Mbiri ya anthu ya mmene agwiritsira ntchito mphamvu si yabwino ayi. Bwana Acton, katswiri wa mbiri yakale, ponena za mphamvu imene anthu andale amakhala nayo, anati: “Mphamvu zimapangitsa munthu kukhala ndi khalidwe loipa ndipo mphamvu zambiri zimapangitsa munthu kukhala ndi khalidwe loipa kwambiri.” Mbiri ya zochitika zamakono ili ndi zitsanzo zambirimbiri zosonyeza kuti mawu a Bwana Acton amenewo kaŵirikaŵiri amakhaladi oona. M’zaka za zana la 20, “wina [w]apweteka mnzake pom’lamulira” kusiyana ndi kale lonse. (Mlaliki 8:9) Olamulira opotoka maganizo ndiponso opondereza anthu agwiritsa ntchito mphamvu zawo m’njira yolakwika kwambiri ndipo aphetsa anthu mamiliyoni ambiri. Mphamvu zopanda chikondi, nzeru, ndi chilungamo n’zoopsa.
2. Longosolani mmene mikhalidwe inanso yaumulungu imakhudzira Yehova pogwiritsa ntchito mphamvu zake.
2 Mosiyana ndi anthu ambiri, nthaŵi zonse Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti achite zinthu zabwino. “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Yehova amasonyeza mphamvu zake m’njira yolamulirika. Kuleza mtima kumapangitsa Mulungu kuti asawononge anthu oipa pofuna kuwapatsa mpata woti alape. Chikondi chima’mpangitsa kuti awalitsire dzuŵa pa anthu a mtundu uliwonse—olungama ndi osalungama. Chilungamo, pomalizira pake, chidzam’pangitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zake zopanda malirezo kuwonongera iye amene ali nayo mphamvu ya imfa, Satana Mdyerekezi.—Mateyu 5:44, 45; Ahebri 2:14; 2 Petro 3:9.
3. N’chifukwa chiyani mphamvu zazikulu koposa za Mulungu zili chifukwa chom’khulupirira?
3 Mphamvu zazikuluzo za Atate wathu wakumwamba ndi chifukwa china chokhalira ndi chikhulupiriro ndi chidaliro, ponse paŵiri m’malonjezo ake ndi m’chitetezo chake. Mwana wamng’ono akakhala pakati pa anthu achilendo amamva kukhala wotetezeka ngati wagwiritsa dzanja la atate wake, popeza amadziŵa kuti atate wakewo atha kum’teteza patakhala choopsa chilichonse. Momwemonso, Atate wathu wakumwamba, amene ali “wa mphamvu yakupulumutsa,” adzatiteteza kuti tisavulazike kwamuyaya m’njira iliyonse ngati tiyenda naye. (Yesaya 63:1; Mika 6:8) Ndiponso pokhala Atate wabwino, nthaŵi zonse Yehova amakwaniritsa malonjezo ake. Mphamvu zopanda malirezo zimatitsimikizira kuti ‘mawu ake adzakula mmene awatumizira.’—Yesaya 55:11; Tito 1:2.
4, 5. (a) Kodi n’chiyani chinatsatira pamene Mfumu Asa anakhulupirira Yehova ndi mtima wonse? (b) Kodi n’chiyani chingachitike ngati tikudalira njira za anthu?
4 N’chifukwa chiyani kuli kofunika kutsimikiza mtima kwambiri kuti sitidzaiŵala konse za chitetezo cha Atate wathu wakumwamba? Chifukwa chakuti n’zotheka kuda nkhaŵa kwambiri ndi zochitika zina ndi kuiŵala kumene kuli chitetezo chathu chenicheni. Zimenezi tikuziona m’chitsanzo cha Mfumu Asa, munthu amene nthaŵi zambiri anali kukhulupirira mwa Yehova. Pamene Asa anali kulamulira, gulu lankhondo la Kusi la asilikali miliyoni imodzi linaukira Yuda. Atadziŵa kuti gulu la adani ake n’lamphamvu kwambiri, Asa anapemphera kuti: “Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu, tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji aŵa m’dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakulakeni.” (2 Mbiri 14:11) Yehova anayankha pempho la Asa ndi kum’patsa chigonjetso chachikulu.
5 Koma atatumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri, chidaliro cha Asa m’mphamvu yopulumutsa ya Yehova chinachepa. Pofuna kupeŵa nkhondo ndi ufumu wakum’poto wa Israyeli, iye anapepha thandizo kwa Aramu. (2 Mbiri 16:1-3) Ngakhale kuti chiphuphu chake kwa Mfumu Benihadadi ya Aramu chinapangitsadi kupeŵa nkhondo yomwe Israyeli anafuna kuichita pa Yuda, pangano la Asa ndi Aramu linasonyeza kusadalira Yehova. Hanani mneneri anam’funsa mosapita m’mbali kuti: “Nanga Akusi ndi Alubi, sanakhala khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m’dzanja mwanu?” (2 Mbiri 16:7, 8) Komabe, Asa anakana chidzudzulo chimenechi. (2 Mbiri 16:9-12) Pamene takumana ndi mavuto, tisafufuze njira za anthu zothetsera mavutowo. M’malo mwake, tiyeni tidalire Mulungu, popeza kuti kudalira mphamvu za anthu n’kogwiritsa mwala nthaŵi zonse.—Salmo 146:3-5.
Funafunani Mphamvu Imene Yehova Amapereka
6. N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kufuna Yehova ndi mphamvu yake’?
6 Yehova angapatse atumiki ake mphamvu komanso n’kuwateteza. Baibulo limatilimbikitsa ‘kufuna Yehova, ndi mphamvu yake.’ (Salmo 105:4) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti pamene tikuchita zinthu m’mphamvu ya Mulungu, mphamvu yathu idzagwiritsidwa ntchito pazinthu zaphindu, m’malo mopweteka ena. Kulibenso kwina kumene timapeza chitsanzo chabwino zedi koma kwa Yesu Kristu, amene anachita zozizwitsa zambiri mu “mphamvu ya Ambuye.” (Luka 5:17) Yesu akanatha kuika maganizo ake pa kukhala wolemera, wotchuka, kapenanso ngakhale mfumu yamphamvuyonse. (Luka 4:5-7) M’malo mwake, anagwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anam’patsa polangiza ndi kuphunzitsa, pothandiza anthu ndi kuwachiritsa. (Marko 7:37; Yohane 7:46) Chitsanzotu chabwino zedi kwa ife!
7. Kodi ndi mkhalidwe wofunika kwambiri uti umene timakulitsa pamene tichita zinthu m’mphamvu ya Mulungu ndipo osati m’mphamvu yathu?
7 Komanso, pamene tichita zinthu mu “mphamvu imene Mulungu a[ti]patsa,” zimenezi zidzatithadiza kukhalabe ofatsa. (1 Petro 4:11) Anthu amene amangofuna kukhala ndi mphamvu amakhala okula mtima. Chitsanzo chabwino ndicho Esarihadoni mfumu ya Asuri, amene anadzitama kuti: “Ndine wamphamvu, ndine wamphamvuyonse, ndine ngwazi, ndine chiphona, ine ndekha m’patali.” Koma m’malo mwake, Yehova anasankha ‘zofooka za dziko lapansi kuti akachititse manyazi zamphamvu.’ Choncho, ngati Mkristu weniweni adzitama, amadzitama mwa Yehova, popeza amadziŵa kuti zimene wachita sanazichite mwa mphamvu yake. ‘Kudzichepetsa pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu’ kudzadzetsa kukwezedwa kwenikweni.—1 Akorinto 1:26-31; 1 Petro 5:6.
8. Kodi tiyenera kuchitanji kaye kuti tilandire mphamvu ya Yehova?
8 Kodi mphamvu ya Mulungu timaipeza motani? Choyamba, tiyenera kuipempha m’pemphero. Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti Atate wake adzapatsa mzimu woyera kwa amene akuupempha. (Luka 11:10-13) Talingalirani mmene zimenezi zinapatsira mphamvu ophunzira a Kristu pamene anasankha kumvera Mulungu osati atsogoleri achipembedzo amene anali atawalamula kuti aleke kuchitira umboni za Yesu. Pamene anapempherera thandizo la Yehova, pemphero lawo lochokera pansi pa mtima linayankhidwa, ndipo mzimu woyera unawapatsa mphamvu yopitirizabe kulalikira uthenga wabwino molimba mtima.—Machitidwe 4:19, 20, 29-31, 33.
9. Tchulani gwero lachiŵiri la mphamvu zauzimu, ndipo tchulani chitsanzo cha m’Malemba kuti musonyeze kugwira kwake ntchito.
9 Chachiŵiri, tingapeze mphamvu yauzimu m’Baibulo. (Ahebri 4:12) Mphamvu ya mawu a Mulungu inaonekeratu m’masiku a Mfumu Yosiya. Ngakhale kuti mfumu ya Yuda imeneyi inali itachotsa kale mafano achikunja m’dzikomo, pamene Chilamulo cha Yehova chinapezeka mosayembekezereka m’kachisi, iyo inasonkhezereka kulimbikitsabe ntchito yake yoyeretsa.a Yosiya iye mwini ataŵerengera anthu Chilamulocho, mtundu wonsewo unapanga pangano ndi Yehova, ndipo ntchito yochotsa kulambira mafano inayambikanso kachiŵiri, koma inachitidwa mwamphamvu kwambiri. Chotsatirapo chabwino cha kusintha zinthu kwa Yosiya chinali chakuti “masiku ake onse iwo sanapambuka kusam’tsata Yehova.”—2 Mbiri 34:33.
10. Kodi njira yachitatu yopezera mphamvu za Yehova ndi iti, nanga n’chifukwa chiyani ili yofunika kwambiri?
10 Chachitatu, timapeza nyonga ya Yehova kudzera m’mayanjano achikristu. Paulo analimbikitsa Akristu kuti azipezeka pamisonkhano nthaŵi zonse kuti ‘afulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino’ ndi kulimbikitsana. (Ahebri 10:24, 25) Pamene Petro anatulutsidwa m’ndende mozizwitsa, iye anafuna kukakhala ndi abale ake, chotero nthaŵi yomweyo anapita kunyumba ya amayi ake a Yohane Marko, kumene “ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera.” (Machitidwe 12:12) Inde, onse akanatha kungokhala kunyumba zawo ndi kumapemphera. Koma anasankha kusonkhana pamodzi ndi kupemphera ndi kulimbikitsana panthaŵi yovuta imeneyo. Cha kumapeto kwa ulendo wautali komanso woopsa wa Paulo wopita ku Roma, iye anakumana ndi abale ena ku Potiyolo komanso kenako ndi enanso amene anabwera kudzakumana naye. Kodi anamva bwanji? “Pamene Paulo anaona [abale odzakumana nayewo], anayamika Mulungu, nalimbika mtima.” (Machitidwe 28:13-15) Analimbikitsidwa pokhalanso ndi Akristu anzake. Ifenso timapeza nyonga mwa kuyanjana ndi Akristu anzathu. Malinga ngati tili ndi ufulu woyanjana ndi ena ndipo tingathe kutero, tisayese kuyenda tokha panjira yopapatiza yomka ku moyo wosatha.—Miyambo 18:1; Mateyu 7:14.
11. Tchulani zochitika zina zofuna kwambiri kuti tikhale ndi “ukulu woposa wamphamvu.”
11 Mwa kupemphera nthaŵi zonse, kuphunzira Mawu a Mulungu, ndi kuyanjana ndi okhulupirira anzathu, ‘timalimbika mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.’ (Aefeso 6:10) Mosakayikira, tonsefe tikufunikira ‘kulimbika mwa Ambuye.’ Ena amavutika ndi matenda owononga thupi, ena amavutika ndi mavuto odza ndi ukalamba kapena ndi kutayikidwa mnzawo wa moyo wonse. (Salmo 41:3) Ena amapirira chitsutso cha mwamuna kapena mkazi wawo wosakhulupirira. Makolo, makamaka amene sali muukwati, angapeze kuti kugwira ntchito yokhazikika uku akusamalira banja ndi ntchito yotopetsa kwabasi. Akristu achinyamata amafunikira nyonga yokana chisonkhezero cha anzawo ndi kukana mankhwala osokoneza bongo ndiponso chiwerewere. Tonsefe sitiyenera kuzengereza kupempha Yehova kuti atipatse “ukulu woposa wamphamvu” kuti tilimbane ndi zovuta zimenezi.—2 Akorinto 4:7.
“Alimbitsa Olefuka”
12. Kodi Yehova amatichirikiza motani mu utumiki wachikristu?
12 Yehova amaperekanso mphamvu kwa atumiki ake pamene iwo akuchita utumiki wawo. Timaŵerenga mu ulosi wa Yesaya kuti: “Iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. . . . Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” (Yesaya 40:29-31) Mtumwi Paulo anailandira mphamvuyi kuti achite utumiki wake. Chotsatira chake chinali chakuti utumiki wake unali wogwira mtima. Polembera Akristu a ku Tesalonika, iye anati: “Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera.” (1 Atesalonika 1:5) Kulalikira ndi kuphunzitsa kwake kunali ndi mphamvu yopangitsa anthu amene anam’mvetsera kusinthiratu miyoyo yawo.
13. Kodi n’chiyani chinalimbitsa Yeremiya kuti apitirizebe ngakhale kuti anali kutsutsidwa?
13 Tikamakumana ndi anthu opanda chidwi m’gawo lathu, gawo limene tingakhale titalalikiramo mobwerezabwereza kwa zaka zambiri koma osakhalamo ndi zipatso zenizeni, tingalefuke. Mofananamo, Yeremiya analefuka ndi chitsutso, kunyozedwa, ndi kusoŵa chidwi kwa anthu kumene anakumana nako. “Sindidzam’tchula [Mulungu], sindidzanenanso m’dzina lake,” anadziuza motero. Koma sanathe kungokhala chete. Uthenga wake “[unali] ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa [ake].” (Yeremiya 20:9) Kodi n’chiyani chinam’patsanso mphamvu ina mumkhalidwe wovuta zedi ngati umenewo? “Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa,” anatero Yeremiya. (Yeremiya 20:11) Yeremiya atazindikira kufunika kwa uthenga wake ndi kwa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu zinam’pangitsa kuchitapo kanthu atalimbikitsidwa ndi Yehova.
Mphamvu ya Kupweteka ndi Mphamvu ya Kuchiritsa
14. (a) Kodi lilime ndi chida champhamvu motani? (b) Perekani zitsanzo zosonyeza mmene lilime lingawonongetsere zinthu.
14 Si mphamvu zonse zimene tili nazo zimene zimachokera kwa Mulungu mwachindunji. Mwachitsanzo, lilime n’kachiŵalo kakang’ono, koma kali ndi mphamvu ya kupweteka komanso mphamvu ya kuchiritsa. “Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo,” anachenjeza motero Solomo. (Miyambo 18:21) Zotsatira za kucheza kwakufupi kwa Satana ndi Hava zikusonyeza ukulu wa mavuto amene mawu angachititse. (Genesis 3:1-5; Yakobo 3:5) Ifenso titha kuwononga zinthu kwambiri ndi lilime. Kusayankhula bwino ponena za kunenepa kwa mtsikana kungam’yambitse matenda odana ndi chakudya. Kutchulatchula za mjedo winawake mosaganizira ena kungawonongetse ubwenzi wakalekale. Inde, lilime liyenera kulamuliridwa.
15. Kodi tingagwiritse ntchito motani lilime lathu polimbikitsa ndi kuchiritsa?
15 Komabe, lilime lingamangirire komanso kupasula. Mwambi wa m’Baibulo umati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” (Miyambo 12:18) Akristu anzeru amagwiritsa ntchito mphamvu ya lilime potonthoza opsinjika maganizo ndi olira. Mawu achifundo angalimbikitse achinyamata amene akulimbana ndi chisonkhezero choipa cha anzawo. Lilime lanzeru lingatsimikizire abale ndi alongo achikulire kuti ndi ofunikabe ndiponso okondedwa. Mawu okoma mtima angasangalatse odwala. Chachikulu koposa, tingagwiritse ntchito lilime lathu kuti tigaŵire uthenga wamphamvu wa Ufumu kwa onse ofuna kumva. Kulengeza Mawu a Mulungu n’chinthu chomwe tikhoza kuchichita ngati mtima wathu ndi wodzipereka kwathunthu. Baibulo limati: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.”—Miyambo 3:27.
Kugwiritsa Ntchito Bwino Mphamvu
16, 17. Posonyeza ulamuliro wawo wopatsidwa ndi Mulungu, kodi akulu, makolo, amuna, ndi akazi awo angam’tsanzire motani Yehova?
16 Ngakhale kuti ndi wamphamvuyonse, Yehova amalamulira mpingo mwachikondi. (1 Yohane 4:8) Pom’tsanzira, oyang’anira achikristu amasamalira nkhosa za Mulungu mwachikondi, kugwiritsa ntchito bwino ulamuliro wawo, osati kuchita nawo ufumu. Inde, nthaŵi zina oyang’anira ayenera ‘kutsutsa, kudzudzula, kuchenjeza,’ koma zimenezi amazichita “ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.” (2 Timoteo 4:2) Chotero nthaŵi zonse akulu amasinkhasinkha pa mawu amene mtumwi Petro analemba kwa anthu okhala ndi ulamuliro mumpingo akuti: “Ŵetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.”—1 Petro 5:2, 3; 1 Atesalonika 2:7, 8.
17 Makolo ndi amuna okwatira alinso ndi ulamuliro woperekedwa ndi Yehova, ndipo mphamvu zimenezi ziyenera kugwiritsidwa ntchito pothandiza, kulangiza, ndi kusamala. (Aefeso 5:22, 28-30; 6:4) Chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti ulamuliro ungagwire ntchito bwino kwambiri mwachikondi. Ngati malangizo amaperekedwa m’njira yabwino komanso mosasinthasintha, ana sataya mtima. (Akolose 3:21) Maukwati amalimba pamene amuna achikristu amachita umutu wawo mwachikondi ndipo akazi awo amalemekeza kwambiri umutu wa amuna awo m’malo mopitirira malire a udindo wawo wopatsidwa ndi Mulungu kuti adzilamulira mwamuna kapena kuti zofuna zawo zichitike.—Aefeso 5:28, 33; 1 Petro 3:7.
18. (a) Kodi tiyenera kum’tsanzira motani Yehova poletsa mkwiyo wathu? (b) Kodi anthu okhala ndi ulamuliro ayenera kuyesa kusonkhezera chiyani m’mitima ya anthu amene akuwasamalira?
18 Amene ali ndi ulamuliro m’banja ndi mumpingo ayenera kuuletsa kwambiri mkwiyo wawo, chifukwa chakuti mkwiyo umasonkhezera mantha ndipo osati chikondi. Mneneri Nahumu anati: “Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wamphamvu yaikulu.” (Nahumu 1:3; Akolose 3:19) Kuletsa mkwiyo wathu kumasonyeza nyonga, pamene kusauletsa ndi umboni wa kufooka. (Miyambo 16:32) Ponse paŵiri m’banja ndi mumpingo, cholinga ndicho kusonkhezera chikondi, kukonda Yehova, kukondana wina ndi mnzake, ndi kukonda mfundo zabwino zachikhalidwe. Chikondi ndicho chomangira umodzi champhamvu kwambiri ndiponso n’chisonkhezero champhamvu koposa cha kuchita chabwino.—1 Akorinto 13:8, 13; Akolose 3:14.
19. Kodi Yehova akupereka chitsimikizo chotonthoza chotani, ndipo kodi tiyenera kuchita chiyani?
19 Kudziŵa Yehova ndiko kuzindikira mphamvu yake. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Kodi iwe sunadziŵe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema.” (Yesaya 40:28) Mphamvu za Yehova sizitha. Ngati timadalira iye ndipo osati mphamvu zathu, sadzatisiya. Amatitsimikizira kuti: “Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; ine, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.” (Yesaya 41:10) Kodi tiyenera kuchita motani ndi chisamaliro chake chachikondi? Monga Yesu, tiyeni nthaŵi zonse tigwiritse ntchito mphamvu ina iliyonse imene Yehova amatipatsa kuti tithandize ena ndi kuwalimbikitsa. Tiyeni tilamulire lilime lathu kuti lichiritse m’malo mopweteka. Ndipo nthaŵi zonse tikhale ogalamuka mwauzimu, ochirimika m’chikhulupiriro, ndi olimba m’mphamvu ya Mlengi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu.—1 Akorinto 16:13.
[Mawu a M’munsi]
a Zikuoneka kuti Ayuda anatulukira kope loyambirira la Chilamulo cha Mose, limene linaikidwa m’kachisi zaka mazana angapo kumbuyoko.
Kodi Mungalongosole?
• Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake motani?
• Kodi mphamvu za Yehova tingazipeze motani?
• Kodi mphamvu ya lilime tiyenera kuigwiritsa ntchito motani?
• Kodi ulamuliro woperekedwa ndi Mulungu ungakhale motani dalitso?
[Chithunzi patsamba 15]
Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu ya Yehova kuti athandize ena
[Zithunzi patsamba 17]
Kulengeza Mawu a Mulungu n’chinthu chomwe tikhoza kuchichita ngati mtima wathu ndi wodzipereka kwathunthu