Salimo
3 Nyadirani dzina lake loyera.+
Mitima ya anthu ofunafuna Yehova isangalale.+
4 Funafunani Yehova+ ndipo muzidalira mphamvu zake.
Nthawi zonse muzimupempha kuti akuthandizeni.*
5 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,
Kumbukirani zozizwitsa zake ndi ziweruzo zimene wapereka,+
6 Inu mbadwa* za Abulahamu mtumiki wake,+
Inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.+
7 Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+
Ziweruzo zake zili padziko lonse lapansi.+
8 Amakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+
Lonjezo limene anapereka* ku mibadwo 1,000.+
9 Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+
Komanso lumbiro limene analumbira kwa Isaki,+
10 Limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,
Komanso monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,
11 Pamene anati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+
Kuti likhale cholowa chako.”+
12 Pamene ananena zimenezi, nʼkuti iwo ali ochepa.+
Nʼkuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo mʼdzikolo.+
13 Iwo ankayendayenda kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,
Komanso kuchokera mu ufumu wina kupita kwa anthu a mtundu wina.+
14 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awapondereze,+
Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+
15 Iye anati: “Musakhudze odzozedwa anga,
Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.”+
18 Kumeneko anamanga* mapazi ake mʼmatangadza,+
Khosi lake analiika mʼzitsulo
19 Mpaka nthawi imene zimene Mulungu ananena zinakwaniritsidwa,+
Mawu a Yehova ndi amene anamuyenga.
20 Mfumu inalamula kuti amutulutse mʼndende,+
Wolamulira mitundu ya anthu anatulutsa Yosefe mʼndende.
21 Anamupatsa udindo woyangʼanira banja lake
Komanso woyangʼanira chuma chake chonse.+
22 Anamupatsa mphamvu zolamulira* akalonga ake mmene akufunira
Komanso kuti akuluakulu aziwaphunzitsa zinthu za nzeru.+
24 Mulungu anachititsa kuti anthu ake aberekane kwambiri,+
Iye anawachititsa kuti akhale amphamvu kwambiri kuposa adani awo.+
25 Analola adaniwo kuti asinthe mitima yawo nʼkuyamba kudana ndi anthu ake,
Komanso kukonzera chiwembu atumiki akewo.+
27 Iwowa anachita zizindikiro za Mulungu pamaso pa Aiguputo,
Anachita zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.+
31 Analamula kuti pagwe ntchentche zoluma,
Komanso tizilombo touluka toyamwa magazi,* mʼmadera awo onse.+
33 Anawononga mitengo yawo ya mpesa ndi ya mkuyu
Ndipo anakhadzula mitengo mʼdziko lawo.
35 Dzombelo linadya zomera zonse mʼdziko lawo,
Linadyanso mbewu zonse zamʼmunda mwawo.
36 Kenako Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko lawo,+
Chiyambi cha mphamvu zawo zobereka.
37 Anatulutsa anthu ake atatenga siliva ndi golide.+
Ndipo pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira.
39 Mulungu anatumiza mtambo kuti uwateteze+
Komanso moto kuti uziwaunikira usiku.+
41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+
Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa mʼchipululu.+
42 Chifukwa iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu.+
43 Choncho Mulungu anatulutsa anthu ake mʼdzikomo anthuwo akusangalala,+
Anatulutsa osankhidwa ake akufuula mokondwera.
44 Anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,+
Anatenga zinthu zimene mitundu ina ya anthu inapeza itagwira ntchito mwakhama,+
45 Anachita zimenezi kuti asunge malangizo ake,+
Komanso kusunga malamulo ake.
Tamandani Ya!*