PHUNZIRO 14
Tingatani Kuti Mulungu Azisangalala Ndi Kulambira Kwathu?
Monga mmene tinaphunzirira m’phunziro 13, si zipembedzo zonse zimene zimasangalatsa Mulungu. Komabe, tingathe kulambira Mlengi wathu m’njira imene imamusangalatsa. Ndiye kodi Mulungu amasangalala ndi chipembedzo chotani kapena kuti “kupembedza” kotani? (Yakobo 1:27) Tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi.
1. Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito chiyani polambira?
Tiyenera kugwiritsa ntchito Baibulo tikamalambira Mulungu. Pamene ankapemphera kwa Mulungu, Yesu anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Zipembedzo zina zimanyalanyaza dala mfundo za choonadi zomwe zili m’Baibulo limene ndi Mawu a Mulungu ouziridwa. M’malomwake zimaphunzitsa maganizo ndi miyambo ya anthu. Komatu Yehova samasangalala ndi anthu amene ‘amakankhira pambali malamulo a Mulungu.’ (Werengani Maliko 7:9.) Mosiyana ndi anthu amenewa, ifeyo timasangalatsa Mulungu chifukwa timagwiritsa ntchito Baibulo polambira komanso timatsatira malangizo ake.
2. Tizitani kuti Yehova azivomereza kulambira kwathu?
Yehova amafuna kuti tizilambira iye yekha chifukwa ndiye Mlengi wathu. (Chivumbulutso 4:11) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kukonda ndi kulambira iye yekha basi, popanda kugwiritsa ntchito mafano, zithunzi kapena chifaniziro china chilichonse.—Werengani Yesaya 42:8.
Yehova amafuna kuti tizimulambira m’njira “yoyera ndi yovomerezeka.” (Aroma 12:1) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kumvera malamulo ake pa moyo wathu. Mwachitsanzo, anthu amene amakonda Yehova amamvera ndi kutsatira malamulo ake pa nkhani yokhudza ukwati. Ndipo amayesetsa kupewa makhalidwe omwe amaika moyo pangozi monga kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala molakwika kapenanso kumwa mowa mwauchidakwa.a
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Yehova limodzi ndi Akhristu anzathu?
Misonkhano imene timakhala nayo mlungu uliwonse imatipatsa mwayi ‘wotamanda Yehova . . . mumpingo.’ (Salimo 111:1, 2) Njira imodzi imene timachitira zimenezi ndi kuimbira Mulungu nyimbo zomutamanda. (Werengani Salimo 104:33.) Yehova amafuna kuti tizisonkhana chifukwa chakuti amatikonda ndiponso amadziwa kuti misonkhano izitithandiza kukhala ndi moyo wosangalala mpaka kalekale. Tikapita kumisonkhano timalimbikitsa anthu ena ndipo iwonso amatilimbikitsa.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake Yehova samafuna kuti tizigwiritsa ntchito mafano polambira. Dziwani njira zofunika zomwe tingagwiritse ntchito potamanda Mulungu.
4. Tisamagwiritse ntchito mafano polambira
Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu amasangalala tikamapewa kugwiritsa ntchito mafano? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi n’chiyani chomwe chinachitikira atumiki a Mulungu ena omwe anayesapo kugwiritsa ntchito mafano polambira?
Anthu ena amagwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu chifukwa choganiza kuti mafanowo angawathandize kuti amuyandikire. Koma kodi kuchita zimenezi kungawathandizedi kuti amuyandikire? Werengani Ekisodo 20:4-6 ndi Salimo 106:35, 36, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi inuyo mwaonapo anthu akugwiritsa ntchito mafano kapena zifaniziro zotani polambira?
Kodi Yehova amamva bwanji anthu akamagwiritsa ntchito mafano?
Kodi mumaona kuti kugwiritsa ntchito mafano n’koyenera?
5. Tikamalambira Yehova yekha timakhala omasuka ku ziphunzitso zabodza
Onani mmene kulambira Yehova m’njira yovomerezeka kungatithandizire kuti timasuke ku ziphunzitso zabodza. Onerani VIDIYO.
Werengani Salimo 91:14, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yehova akutilonjeza kuti adzatichitira chiyani tikamasonyeza kuti timamukonda polambira iye yekha basi?
6. Timalambira Mulungu kumisonkhano ya mpingo
Tikamaimba ndi kuyankha pamisonkhano ya mpingo timatamanda Yehova ndiponso timalimbikitsana. Werengani Salimo 22:22, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi mumasangalala kumvetsera ndemanga kumisonkhano?
Kodi mungakonde kukonzekera zoti mukayankhe?
7. Yehova amasangalala tikamauza ena zomwe tikuphunzira
Pali njira zambiri zomwe tingagwiritse ntchito pouza ena choonadi cha m’Baibulo. Werengani Salimo 9:1 ndi 34:1, kenako mukambirane funso ili:
Kodi ndi mfundo iti yomwe mwaphunzira m’Baibulo yomwe mukufuna kuuzako munthu wina?
ZIMENE ENA AMANENA: “Ndife ochimwa kwambiri, sitingathe kusangalatsa Mulungu.”
Inuyo mukuganiza bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Timasangalatsa Mlengi wathu tikamalambira iye yekha basi, tikamamutamanda pamisonkhano ya mpingo komanso tikamauza ena zomwe taphunzira.
Kubwereza
Kodi tingatani kuti tidziwe njira yovomerezeka yolambirira Mulungu?
N’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Yehova yekha basi?
N’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Mulungu limodzi ndi anthu ena omwe amafuna kumusangalatsa?
ONANI ZINANSO
Munkhani yakuti, “Ndinasiya Kulambira Mafano,“ onani zimene mayi wina anachita kuti asiye kulambira mafano.
Onani zimene zingakuthandizeni kuti muziyankha pamisonkhano ya mpingo.
“Tizitamanda Yehova Mumpingo” (Nsanja ya Olonda, January 2019)
Onani mmene misonkhano inathandizira mnyamata wina ngakhale kuti ankapita kumisonkhano movutikira.
Anthu ambiri amakhulupirira kuti mtanda ndi chizindikiro cha Chikhristu, koma kodi tiyenera kuugwiritsa ntchito polambira?
“N’chifukwa Chiyani Simugwiritsa Ntchito Mtanda Polambira?” (Nkhani yapawebusaiti)
a Nkhani zimenezi tidzazikambirana kutsogoloku.