NKHANI YOPHUNZIRA 2
Tizitamanda Yehova Mumpingo
“Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.”—SAL. 22:22.
NYIMBO NA. 59 Tamandani Ya Limodzi ndi Ine
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti ankakonda kwambiri Yehova?
MFUMU DAVIDE analemba kuti: “Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri.” (Sal. 145:3) Iye ankakonda kwambiri Yehova ndipo zimenezi zinamulimbikitsa kuti azimutamanda “pakati pa mpingo.” (Sal. 22:22; 40:5) N’zosachita kufunsa kuti nanunso mumakonda Yehova ndipo mumagwirizana ndi mawu a Davide akuti: “Mudalitsike [kapena kuti mutamandike] inu Yehova Mulungu wa Isiraeli atate wathu, kuyambira kalekale mpaka kalekale.”—1 Mbiri 29:10-13.
2. (a) Kodi tingatamande bwanji Yehova masiku ano? (b) Kodi anthu ena amakhala ndi vuto lotani, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Tikamayankha pamisonkhano timakhala tikutamanda Yehova. Koma abale ndi alongo ena amavutika kwambiri kuchita zimenezi. Iwo amafuna kuyankha koma amachita mantha. Kodi angatani kuti asamaope kuyankha? Nanga ndi mfundo ziti zimene zingatithandize tonsefe kuti tizipereka ndemanga zolimbikitsa? Tisanakambirane mayankho a mafunso amenewa, tiyeni tione kaye zifukwa 4 zimene zimatichititsa kuti tiziyankha pamisonkhano.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUYANKHA PAMISONKHANO?
3-5. (a) Malinga ndi Aheberi 13:15, n’chifukwa chiyani tiyenera kuyankha pamisonkhano? (b) Kodi tonsefe tiyenera kupereka ndemanga mofanana? Fotokozani.
3 Yehova watipatsa tonsefe mwayi womutamanda. (Sal. 119:108) Tikamayankha pamisonkhano timakhala kuti tikupereka ‘nsembe zotamanda Mulungu’ ndipo palibe munthu wina amene angatiperekere nsembe zimenezi. (Werengani Aheberi 13:15.) Kodi Yehova amafuna kuti tonsefe tizipereka nsembe kapena ndemanga zofanana? Ayi.
4 Yehova amadziwa kuti timasiyana maluso komanso zinthu zina. Choncho amayamikira nsembe zimene aliyense amatha kupereka. Taganizirani za nsembe zochokera kwa Aisiraeli zimene iye ankalandira. Aisiraeli ena ankakwanitsa kupereka nkhosa kapena mbuzi. Koma Aisiraeli osauka sankakwanitsa kuchita zimenezi ndipo ankaloledwa kuti apereke “njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.” Ndipo ngati anali osauka kwambiri moti sangathe kupereka zimenezi ankaloledwa kupereka “ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.” (Lev. 5:7, 11) Ufawu sunali wodula koma Yehova ankayamikira nsembe imeneyi ngati unali “ufa wosalala.”
5 Maganizo a Mulungu wathu wokoma mtima sanasinthe pa nkhaniyi. Iye sayembekezera kuti tonsefe tikamapereka ndemanga tizilankhula mwaluso ngati Apolo kapena mokopa ngati Paulo. (Mac. 18:24; 26:28) Zimene Yehova amafuna ndi zakuti tiziyesetsa kupereka ndemanga zabwino mmene tingathere. Kumbukirani chitsanzo cha mkazi wamasiye amene anapereka tindalama tiwiri tokha. Yehova anayamikira kwambiri mayiyu chifukwa anapereka zimene akanatha.—Luka 21:1-4.
6. (a) Mogwirizana ndi Aheberi 10:24, 25, kodi tingamve bwanji anthu ena akayankha pamisonkhano? (b) Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira ndemanga zimene zakulimbikitsani?
6 Tikamapereka ndemanga timalimbikitsana. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Tonsefe timasangalala tikamva ndemanga zosiyanasiyana pamisonkhano yathu. Mwachitsanzo, mawu ochepa amene mwana amayankha mochokera pansi pa mtima amatisangalatsa kwambiri. Timalimbikitsidwanso munthu akafotokoza mfundo yosangalatsa imene waphunzira. Timayamikiranso anthu amene amalimba mtima n’kuyankha ngakhale kuti ndi amanyazi kapena akuphunzira chilankhulo chathu. (1 Ates. 2:2) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene achita? Misonkhano ikatha, tikhoza kuwathokoza chifukwa cha ndemanga zawo zolimbikitsa. Tingasonyezenso kuyamikira ndemanga zawo tikamapereka ndemanga zathu. Tikutero chifukwa chakuti tikamachita zimenezi timasonyeza kuti sitikufuna kungolimbikitsidwa koma nafenso tikufuna kulimbikitsa anthu ena pamisonkhano.—Aroma 1:11, 12.
7. Kodi kupereka ndemanga kumatithandiza bwanji?
7 Kupereka ndemanga kumatithandizanso ifeyo. (Yes. 48:17) N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, ngati tikufuna kukapereka ndemanga m’pamene timakonzekera bwino misonkhano. Ndipo tikamakonzekera bwino timayamba kumvetsa bwino Mawu a Mulungu. Ndiye tikamamvetsa bwino Baibulo m’pamene timatsatira kwambiri mfundo zimene taphunzira. Chachiwiri, timasangalala kwambiri ndi misonkhano chifukwa timayankha nawo. Chachitatu, popeza pamafunika kuchita khama kuti tiyankhe, mfundo zimene tinayankhazo sitiziiwala.
8-9. (a) Malinga ndi Malaki 3:16, kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji tikamayankha pamisonkhano? (b) Kodi anthu ena angakhalebe ndi vuto liti?
8 Timasangalatsa Yehova tikamafotokoza zimene timakhulupirira. Yehova amamvetsera tikamayankha pamisonkhano ndipo amayamikira zonse zimene timachita kuti tiyankhe. (Werengani Malaki 3:16.) Tikamayesetsa kumusangalatsa amatidalitsa.—Mal. 3:10.
9 Apa zikuonekeratu kuti tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kuyankha pamisonkhano. Koma anthu ena angachitebe mantha kuti aziyankha. Ngati zili choncho ndi inuyo, musadandaule. Tiyeni tsopano tikambirane mfundo zina za m’Baibulo, zitsanzo za anthu ena ndiponso zinthu zina zimene zingatithandize kuti tiziyankha kwambiri pamisonkhano.
ZIMENE TINGACHITE KUTI TISAMAOPE KUYANKHA
10. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amachita mantha kuyankha pamisonkhano? (b) N’chifukwa chiyani simuyenera kudandaula ngati mumaopa kuyankha pamisonkhano?
10 Kodi inuyo mumachita mantha mukangoganiza zokweza dzanja lanu kuti muyankhe? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Ambirife timakhala ndi mantha tikafuna kuyankha. Koma kuti muthetse vutoli, choyamba muyenera kudziwa zimene zimakuchititsani mantha. Kodi mumaopa kuti muiwala zoti munene kapena munena zolakwika? Kapena kodi mumaganiza kuti ndemanga yanu singakhale yabwino ngati ya anthu ena? Ngati mumaopa zimenezi, musadandaule chifukwa zingasonyeze kuti ndinu wodzichepetsa komanso mumaona kuti anthu ena ndi okuposani. Yehova amakonda anthu odzichepetsa chonchi. (Sal. 138:6; Afil. 2:3) Koma iye amafunabe kuti muzimutamanda ndiponso kulimbikitsa abale ndi alongo anu kumisonkhano. (1 Ates. 5:11) Iye amakukondani ndipo angakuthandizeni kuti muzilimba mtima n’kumayankha.
11. Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zingatithandize kuti tisamaope kuyankha pamisonkhano?
11 Tsopano tiyeni tikambirane mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize. Baibulo limanena kuti tonsefe timalakwitsa nthawi zina polankhula. (Yak. 3:2) Yehova komanso abale ndi alongo athu sayembekezera kuti tizichita zabwino zokhazokha popanda kulakwitsa chilichonse. (Sal. 103:12-14) Abale ndi alongowa ali ngati achibale athu ndipo amatikonda kwambiri. (Maliko 10:29, 30; Yoh. 13:35) Amadziwanso kuti nthawi zina sitingafotokoze mfundo mmene timafunira.
12-13. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Nehemiya ndi Yona?
12 Zitsanzo za anthu ena otchulidwa m’Baibulo zingatithandizenso kuti tisamachite mantha. Mwachitsanzo, Nehemiya ankagwira ntchito m’nyumba ya mfumu yamphamvu. Pa nthawi ina, iye anakhumudwa kwambiri atamva kuti mpanda komanso mageti a ku Yerusalemu zidakali zowonongeka. (Neh. 1:1-4) Nehemiya ayenera kuti anachita mantha pamene mfumu inamufunsa zimene zamukhumudwitsa. Iye anapemphera mwamsanga kenako n’kuyankha. Mfumu itamva zimene zinachitika inathandiza kwambiri anthu a Mulungu. (Neh. 2:1-8) Chitsanzo china ndi cha Yona. Yehova atamutuma kuti akalalikire ku Nineve anachita mantha kwambiri moti anathawira kutali. (Yona 1:1-3) Koma Yehova anamuthandiza kuti agwire bwinobwino ntchitoyi. Uthenga umene Yona anapereka unathandiza kwambiri anthu a ku Nineve. (Yona 3:5-10) Nkhani ya Nehemiya ikusonyeza kuti kupemphera tisanayankhe kumathandiza kwambiri. Ndipo nkhani ya Yona ikusonyeza kuti Yehova akhoza kutithandiza kuti tizichita zimene akufuna ngakhale kuti tili ndi mantha kwambiri. Ndiye funso n’kumati, kodi pali mpingo umene anthu ake akhoza kukhala oopsa ngati a ku Nineve?
13 Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzipereka ndemanga zolimbikitsa kumisonkhano? Tiyeni tikambirane zina mwa zinthu zimenezi.
14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera bwino misonkhano, nanga tingachite zimenezi pa nthawi iti?
14 Muzikonzekera misonkhano yonse. Mukakonzekera bwino, mukhoza kulimba mtima kuti muyankhe. (Miy. 21:5) Koma sikuti tonsefe timakonzekera m’njira yofanana. Mwachitsanzo, Mlongo Eloise, yemwe ndi wamasiye komanso wazaka za m’ma 80, amayamba kukonzekera Nsanja ya Olonda chakumayambiriro kwa mlungu. Iye anati: “Ndikayambiratu kukonzekera ndimasangalala kwambiri ndi misonkhano.” Mlongo winanso dzina lake Joy, yemwe amagwira ntchito yolembedwa, amakonzekera Nsanja ya Olonda Loweruka. Iye anati: “Ndikakonzekera Loweruka zimandithandiza kuti ndikumbukire mosavuta mfundo zake.” M’bale Ike, yemwe ndi mkulu komanso mpainiya, anati: “Sindikonzekera phunziro lonse nthawi imodzi. Ndimakonda kukonzekera pang’onopang’ono mkati mwa mlungu.”
15. Kodi tingatani kuti tizikonzekera bwino misonkhano?
15 Kodi tingatani kuti tizikonzekera bwino? Musanayambe kukonzekera, muzipempha Yehova kuti akupatseni mzimu woyera. (Luka 11:13; 1 Yoh. 5:14) Kenako muziona mwachidule zimene zili munkhaniyo. Mwachitsanzo, muziona mutu, timitu ting’onoting’ono, zithunzi komanso mabokosi. Ndiyeno mukayamba kuphunzira ndime iliyonse, muziyesetsa kuwerenga malemba osagwidwa mawu. Muziganizira kwambiri nkhaniyo n’kuona mfundo zimene mungakayankhe. Mukakonzekera bwino, nkhaniyo imakufikani pamtima kwambiri ndipo zimakhala zosavuta kuti mukayankhe.—2 Akor. 9:6.
16. Kodi ndi zinthu ziti zimene muli nazo pazipangizo zamakono, nanga mumazigwiritsa ntchito bwanji?
16 Ngati n’zotheka muzigwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Gulu la Yehova latipatsa zinthu zambiri zapazipangizo zamakono zimene zingatithandize pokonzekera misonkhano. Mwachitsanzo, pulogalamu ya JW Library® imatithandiza kuti tikhale ndi mabuku komanso zinthu zina pazipangizo zathu. Izi zimathandiza kuti tizitha kuphunzira, kuwerenga kapena kumvetsera zinthuzo pa nthawi iliyonse komanso kwina kulikonse. Ena amagwiritsa ntchito zinthu zimenezi kuti aziphunzira pa nthawi yopuma kuntchito kapena kusukulu ngakhalenso poyenda. Zinthu ngati Watchtower Library komanso LAIBULALE YA PA INTANETI™ zimathandiza tikamafufuza nkhani zimene tikufuna kuziphunzira mozama.
17. (a) N’chifukwa chiyani kukonzekera ndemanga zingapo n’kothandiza? (b) Kodi mwaphunzira chiyani pa vidiyo yakuti Khalani Bwenzi La Yehova—Uzikonzekera Zimene Ukayankhe?
17 Ngati n’zotheka muzikonzekera ndemanga zingapo pa phunziro lililonse. Tikutero chifukwa chakuti nthawi zina wochititsa phunzirolo sangakutchuleni pamene mwakweza dzanja. Popeza enanso amakweza manja, wochititsa angasankhe munthu wina osati inuyo. Pofunanso kusunga nthawi, wochititsa sangalole kuti anthu ambirimbiri ayankhe pa mfundo imodzi. Ndiye musamakhumudwe ngati simunatchulidwe chakumayambiriro kwa phunziro. Koma ngati mwakonzekera ndemanga zingapo, zingakhale zosavuta kuti mupeze mwayi woyankha pa nthawi ina. Mukhozanso kukonzekera kuti mukawerenge lemba. Ngati n’zotheka, muziyesetsanso kukonzekera kuti mukayankhe m’mawu anuanu.b
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kupereka ndemanga zachidule?
18 Muzipereka ndemanga zachidule. Nthawi zambiri ndemanga zachidule komanso zosavuta kumva n’zimene zimakhala zolimbikitsa kwambiri. Choncho muziyesetsa kupereka ndemanga zachidule. Muziyesetsa kuti ndemanga yanu isapitirire masekondi 30. (Miy. 10:19; 15:23) Ngati mwakhala mukuyankha pamisonkhano kwa zaka zambiri, muyenera kupereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopereka ndemanga zachidule. Mukamapereka ndemanga zitalizitali komanso zovuta, anthu ena amaganiza kuti kuyankha kwabwino n’kumeneko ndipo iwo sangakwanitse. Chinanso n’chakuti mukamapereka ndemanga zachidule anthu ambiri amakhala ndi mpata woyankha pamisonkhano. Ngati ndinu woyamba kuyankha pa ndime, muzingopereka yankho lachindunji komanso losavuta. Musamafotokoze mfundo zonse zamundimeyo. Koma ngati munthu wina wayankha mfundo yaikulu mukhoza kufotokoza mfundo zina.—Onani bokosi lakuti “Kodi ndinganene zinthu zotani poyankha?”
19. Kodi mungatani kuti wochititsa akutchuleni pa ndime imene mukufuna kuyankha?
19 Mungauziretu wochititsa phunziro ndime imene mukufuna kuti muyankhe. Ngati mukufuna kuchita zimenezi, ndi bwino kukambirana ndi wochititsayo misonkhano isanayambe. Ndiyeno ndime imene mukufuna kuyankhayo ikafika, muzikweza dzanja m’mwamba kwambiri komanso mwamsanga kuti akuoneni.
20. Kodi misonkhano ya mpingo imafanana bwanji ndi chakudya chimene mukudya ndi anzanu?
20 Muziona kuti misonkhano ili ngati chakudya chimene mukudya ndi anzanu apamtima. Tiyerekeze kuti abale ndi alongo akuitanani kuti mukadye nawo chakudya ndipo akupemphani kuti mukonze kachakudya kenakake. Kodi mungatani? Mwina mungade nkhawa pang’ono koma mungayesetse kukonza chakudya chimene aliyense angakonde. Yehova ndi amene amatiitanira kumisonkhano ndipo amatikonzera zinthu zabwino zambiri. (Sal. 23:5; Mat. 24:45) Iye amasangalala tikamabweretsanso mphatso inayake imene tingakwanitse. Choncho tiziyesetsa kukonzekera bwino ndiponso kuyankha mmene tingathere. Tikamachita zimenezi timakhala ngati tikudya patebulo la Yehova komanso tikupereka mphatso kwa onse mumpingo.
NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndinu Yehova
a Mofanana ndi Davide, tonsefe timakonda Yehova ndipo timafuna kumutamanda. Tikapita kumisonkhano ya mpingo timakhala ndi mwayi wochita zimenezi. Koma enafe timavutika kuyankha pamisonkhano. Ngati nanunso muli ndi vuto limeneli, nkhaniyi ikuthandizani kuti mudziwe zimene mungachite kuti musamachite mantha kuyankha pamisonkhano.
b Onerani vidiyo ya pa jw.org yakuti Khalani Bwenzi la Yehova—Uzikonzekera Zimene Ukayankhe. Pitani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Anthu mumpingo akuphunzira Nsanja ya Olonda mosangalala.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Anthu amumpingo amene anali pa Phunziro la Nsanja ya Olonda aja. Moyo wa aliyense ndi wosiyana ndi wa mnzake koma onse akupeza mpata wokonzekera.