Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachisanu cha Masalmo
ANTHU ena olemera amanena kuti: ‘Ana athu aamuna ali ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu aakazi ngati nsanamira za kungondya, zosema zokometsera nyumba ya mfumu. Nkhokwe zathu n’zodzala.’ Ndipo anthu olemerawo amafuula kuti: “Odala [“ndi achimwemwe,” NW] anthu akuona zotere!” Mosiyana ndi zimenezo, wamasalmo akuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Salmo 144:12-15) Inde, anthu otere amakhala odala, kapena kuti achimwemwe. Yehova ndi Mulungu wachimwemwe, ndipo anthu amene amamulambira amakhalanso ndi chimwemwe. (1 Timoteo 1:11) Mfundo imeneyi ikusonyezedwa m’chigawo chomaliza cha Masalmo 107 mpaka 150 cha nyimbo zouziridwa ndi Mulungu.
Chigawo Chachisanu cha Masalmo chimasonyezanso makhalidwe apamwamba a Yehova, monga chifundo, choonadi, ndi ubwino. Tikawadziwa bwino makhalidwe a Mulungu, m’pamene timakhala ndi mtima womukonda ndi kumuopa kwambiri. Kenako, timapeza chimwemwe. Inde, uthenga umene timapeza m’Chigawo Chachisanu cha Masalmo n’ngwaphindu zedi.—Ahebri 4:12.
ODALA CHIFUKWA CHA CHIFUNDO CHA YEHOVA
Ayuda obwerako ku ukapolo ku Babulo anaimba kuti: “[Anthu] ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwiza zake za kwa ana a anthu!” (Salmo 107:8, 15, 21, 31) Potamanda Mulungu, Davide akuimba kuti: ‘Choonadi chanu chifikira mitambo.’ (Salmo 108:4) M’nyimbo yotsatira, akupemphera kuti: “Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga: ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu.” (Salmo 109:18, 19, 26) Salmo la 110 ndi ulosi wonena za ulamuliro wa Mesiya. Lemba la Salmo 111:10 limati: “Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.” Salmo lotsatira limati, “wodala munthu wakuopa Yehova.”—Salmo 112:1.
Masalmo 113 mpaka 118 amatchedwa Masalmo a Haleluya, chifukwa chakuti amagwiritsa ntchito kwambiri mawu akuti “Haleluya,” kapena kuti “Tamandani Ya!” Buku la Mishnah, lomwe linalembedwa m’zaka za m’ma 400 pofuna kusunga ziphunzitso zimene zinali kungolankhulidwa pakamwa, limanena kuti nyimbo zimenezi zinali kuimbidwa pa Paskha ndi pamapwando atatu a pachaka amene Ayuda anali kuchita. Salmo la 119, lomwe ndilo lalitali pa masalmo onse ndiponso chaputala chachitali pa machaputala onse a m’Baibulo, limatamanda mawu a Yehova, kapena kuti uthenga umene iye anavumbulira anthu.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
109:23—Kodi Davide anatanthauza chiyani ponena kuti: “Ndamuka ngati mthunzi womka m’tali; ndiingidwa”? Apa Davide anali kulankhula mwa ndakatulo kuti iyeyo anaona ngati kuti imfa yake inali pafupi kwambiri.—Salmo 102:11.
110:1, 2—Kodi “Ambuye [wa Davide],” Yesu Kristu, anachita chiyani atakhala kudzanja lamanja la Mulungu? Yesu atauka kwa akufa, anakwera kumwamba ndipo anadikira kudzanja lamanja la Mulungu mpaka mu 1914 pamene anayamba kulamulira monga Mfumu. Nthawi imene Yesu anali kudikirayo, analamulira otsatira ake odzozedwa, powatsogolera pa ntchito yawo yolalikira ndi kupanga ophunzira ndiponso powakonzekeretsa kuti akalamulire limodzi naye mu Ufumu wake.—Mateyu 24:14; 28:18-20; Luka 22:28-30.
110:4—Kodi n’chiyani chimene akuti Yehova “walamulira [“walumbira,” NW] ndipo sadzasintha”? Lumbiro limeneli ndi pangano limene Yehova anapangana ndi Yesu Kristu lakuti adzakhala Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe.—Luka 22:29.
113:3—Kodi dzina la Yehova limalemekezedwa m’njira yotani “chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake”? Apa sakunena kwenikweni za gulu la anthu olambira Mulungu tsiku lililonse. Kuchokera kum’mawa kumene dzuwa limatulukira mpaka kumadzulo kumene limalowera, kuwala kwa dzuwalo kumaunikira dziko lonse lapansi. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Ayenera kulemekezedwa padziko lonse lapansi. Zimenezi sizingatheke popanda dongosolo ndi khama. Ife Mboni za Yehova tili ndi mwayi wamtengo wapatali wolemekeza Mulungu ndi kugwira nawo ntchito yolengeza Ufumu.
116:15—Kodi ‘imfa ya okondedwa ake n’njamtengo wake pamaso pa Yehova’ m’njira yotani? Yehova amaona kuti olambira ake n’ngamtengo wapatali zedi moti sangalole kuti gulu lawo lonse life. Ngati Yehova angalole zimenezo, zingatanthauze kuti adani ake ali ndi mphamvu kuposa iyeyo. Ndiponso, sipangapezeke wotsala padziko lapansi amene angakhale ngati maziko a dziko latsopano.
119:71—Kodi kuzunzidwa kungakhale kokoma m’njira yanji? Mavuto angatiphunzitse kudalira Yehova kwambiri, kupemphera kwa iye ndi mtima wonse, ndi kuchita khama pophunzira Baibulo ndi kutsatira zimene limanena. Ndiponso, zimene timachita tikamazunzidwa zingavumbule zolakwika zina pa umunthu wathu zimene tiyenera tikonze. Tikalola mavuto kutiyenga, pamapeto pake sitingakhumudwe nawo.
119:96—Kodi mawu akuti “malekezero ake a ungwiro wonse” akutanthauza chiyani? Apa wamasalmo akulankhula za ungwiro malinga ndi maganizo aumunthu. Ayenera kuti anali kuganiza za ungwiro, kuti munthu sangathe kuumvetsa chifukwa nzeru zake zili ndi malire. Kusiyana ndi zimenezo, lamulo la Mulungu lilibe malire. Mfundo zake n’zothandiza pa zochitika zonse za m’moyo wathu.
119:164—N’chifukwa chiyani akunena za kulemekeza Mulungu “kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi”? Nambala ya zisanu ndi ziwiri imaimira kukwanira kwa chinthu. Choncho, wamasalmo akunena kuti Yehova ayenera kupatsidwa ulemu wonse.
Zimene Tikuphunzirapo:
107:27-31. Armagedo ikadzayamba, anthu amene ali ndi nzeru ya dzikoli ‘adzathedwa nzeru.’ (Chivumbulutso 16:14, 16) Nzeru ya dziko singapulumutse aliyense pa chiwonongeko. Anthu amene amayang’ana kwa Yehova kaamba ka chipulumutso ndiwo okhawo amene adzakhala ndi moyo ndi ‘kum’yamika chifukwa cha chifundo chake.’
109:30, 31; 110:5. Dzanja lamanja la msilikali limene anali kunyamulira lupanga linali losatetezeka ndi chishango, chimene anali kugwira kumanzere. Yehova mophiphiritsa ali ‘kudzanja lamanja’ la atumiki ake, kuwamenyera nkhondo. Choncho amawateteza ndi kuwathandiza, ndipo chimenechi ndi chifukwa chabwino ‘chomuyamikira kwakukulu.’
113:4-9. Yehova ndi wokwezeka kwambiri moti amachita kudzichepetsa kuti ‘apenye ndi zam’mwamba’ zomwe. Ngakhale ali wotero, iye n’ngwachifundo kwa anthu otsika, aumphawi, ndi kwa akazi osaona ana. Ambuye Mfumu Yehova ndi wodzichepetsa ndipo amafuna kuti olambira ake akhale chimodzimodzi.—Yakobo 4:6.
114:3-7. Tikamaphunzira za ntchito zodabwitsa zimene Yehova anachitira anthu ake pa Nyanja Yofiira, pa mtsinje wa Yordano, ndi pa phiri la Sinai, ziyenera kutikhudza mtima kwambiri. Anthu, amene akuimiridwa ndi “dziko lapansi,” ayenera kuchita mantha, inde, ‘kunjenjemera,’ pamaso pa Ambuye.
119:97-101. Nzeru, luntha, ndi kuzindikira zimene timapeza m’Mawu a Mulungu zimatiteteza kuti tisapwetekeke mwauzimu.
119:105. Mawu a Mulungu ndiwo nyali ya kumapazi athu m’njira yakuti amatithandiza kupirira mavuto amene tikukumana nawo panopa. Mophiphiritsa amaunikanso njira yathu, chifukwa chakuti amalosera za cholinga cha Mulungu m’tsogolo.
ODALA NGAKHALE TIKUVUTIKA
Kodi tingatani kuti tipirire ziyeso ndi kupulumuka mavuto? Masalmo 120 mpaka 134 ali ndi yankho lomveka bwino la funso limeneli. Timapulumuka mavuto ndi kukhalabe achimwemwe mwa kuyang’ana kwa Yehova kuti atithandize. Aisrayeli ayenera kuti anali kuimba Masalmo amenewa, otchedwa kuti Nyimbo Zokwerera, popita ku Yerusalemu kumapwando awo apachaka.
Masalmo 135 ndi 136 amasonyeza kuti Yehova amachita chilichonse chimene akufuna, pamene mafano alibe mphamvu iliyonse. Salmo la 136 linalembedwa m’njira yakuti oimba azilandirana, ndipo mbali yomaliza ya vesi iliyonse inkaimbidwa kuyankha mbali yoyambayo. Salmo lotsatira limasimba za chisoni chimene Ayuda anali nacho ku Babulo polakalaka kulambira Yehova ku Ziyoni. Masalmo 138 mpaka 145 ndi a Davide. Iye anafuna ‘kuyamika Yehova ndi mtima wake wonse.’ N’chifukwa chiyani anafuna zimenezo? Iye anati: “Chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwiza.” (Salmo 138:1; 139:14) M’masalmo asanu otsatira, Davide akupemphera kuti atetezedwe kwa anthu oipa, alandire zidzudzulo zachilungamo, alanditsidwe kwa ozunza, ndi kuti alangizidwe za khalidwe. Akugogomezera chimwemwe chimene anthu a Yehova ali nacho. (Salmo 144:15) Ataganizira za ukulu ndi ubwino wa Mulungu, Davide akuti: “Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera ku nthawi za nthawi.”—Salmo 145:21.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
122:3—Kodi Yerusalemu anali mudzi “woundana bwino” m’njira yotani? Malinga ndi mmene midzi yakale inalili, nyumba za m’Yerusalemu zinali zomangidwa pafupipafupi kwambiri. Mudziwu unali ngati woundana, choncho unali wosavuta kuuteteza. Ndiponso, chifukwa cha kuyandikana kwa nyumbazo, anthu okhalamo anali kudalirana kwambiri kuti athandizane ndi kutetezana. Zimenezi zikusonyeza mgwirizano wauzimu wa mafuko 12 a Israyeli akasonkhana pamodzi polambira Mulungu.
123:2—Kodi fanizo la maso a anyamata, kapena kuti akapolo, lili ndi mfundo yotani? Akapolo ndi adzakazi amayang’ana dzanja la mbuye wawo pa zifukwa ziwiri: kuti adziwe zimene mbuye wawo akufuna ndiponso kuti apeze chitetezo ndi zofunika pa moyo. N’chimodzimodzinso ife. Timayang’ana kwa Yehova kuti tidziwe chifuniro chake ndi kuti tiziyanjidwa naye.
131:1-3—Kodi Davide ‘anatontholetsa moyo wake ngati mwana wom’letsa kuyamwa amake’ m’njira yotani? Mofanana ndi mmene mwana woleka kuyamwa amapezera mpumulo ndi chisangalalo akakhala m’manja mwa amake, Davide anaphunzira kutontholetsa moyo wake “ngati mwana wom’letsa kuyamwa amake.” Anachita bwanji zimenezo? Mwa kupewa mtima wodzikuza ndi maso onyada ndiponso mwa kusafuna zinthu zimene zinali zomuposa, kapena kuti zinthu zapamwamba kwambiri. M’malo mofuna kutchuka, Davide nthawi zambiri anali kuzindikira zimene sakanatha kuchita ndipo anali wodzichepetsa. Ndi bwino ngati tingatengere mtima wake, makamaka pokalamira maudindo mu mpingo.
Zimene Tikuphunzirapo:
120:1, 2, 6, 7. Miseche ndi mawu opsetsa mtima angapweteke ena koopsa. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakonda “mtendere” ndiyo kulamulira lilime lathu.
120:3, 4. Ngati tikupirira munthu amene ali ndi “lilime lonyenga,” tisataye mtima podziwa kuti Yehova adzakonza zinthu panthawi yake. Odyera anzawo miseche adzalangidwa ndi “chimphona,” kapena kuti munthu wamphamvu. Inde, adzalandira chilango cha Yehova chonga moto chomwe akuchifanizira ndi ‘makala oyaka moto a mtengo wa tsanya.’
127:1, 2. Pa zonse zimene tikuchita, tiziyang’ana kwa Yehova kuti atitsogolere.
133:1-3. Umodzi umene anthu a Yehova ali nawo n’ngotsitsimula, n’ngwabwino, ndiponso n’ngopatsa mpumulo. Tisausokoneze mwa kupezerana zifukwa, kukangana, kapena kudandauladandaula.
137:1, 5, 6. Olambira Yehova amene anali ku ukapolo anali kum’konda kwambiri Ziyoni, amene ankaimira gulu la Mulungu. Nanga ife bwanji? Kodi timalikonda kwambiri ndi kulimamatira gulu limene Yehova akugwiritsa ntchito masiku ano?
138:2. Yehova ‘amakuzitsa mawu ake kuposa dzina lake lonse’ m’njira yakuti zonse zimene walonjeza m’dzina lake zikadzakwaniritsidwa, zidzaposeratu zonse zimene tikuziyembekezera. Inde, kutsogoloku kuli zinthu zabwino kwambiri zimene zikutidikirira.
139:1-6, 15, 16. Yehova amadziwa ntchito zathu, maganizo athu, ndi mawu athu ngakhale tisanalankhule. Amatidziwa kuchokera pamene mluza wathu unapangika, chiwalo chilichonse cha thupi chisanayambe kuonekera. Mulungu amadziwa munthu aliyense payekha ndipo izi ‘n’zotilaka ndi zodabwitsa.’ N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova samangoona mavuto amene tikukumana nawo komanso amamvetsa mmene tikuvutikira.
139:7-12. Malo alionse amene tingapiteko sam’talikira Mulungu akafuna kutilimbikitsa.
139:17, 18. Kodi ife timakonda kuphunzira za Yehova? (Miyambo 2:10) Ngati timatero, ndiye kuti tapeza chitsime chosaphwa cha chimwemwe. Malingaliro a Yehova ‘ali ochuluka koposa mchenga.’ Mpaka muyaya tidzakhalabe ndi zambiri zoti tiphunzire za iye.
139:23, 24. Tizimulola Yehova kusanthula munthu wathu wa m’kati kuti aone ngati tili ndi “mayendedwe oipa,” kapena kuti maganizo oipa, zilakolako zoipa, ndi mtima woipa, ndipo tizimulola kutithandiza kuchotsa zimenezo.
143:4-7. Kodi tingapirire bwanji ngakhale mavuto aakulu? Wamasalmo akutiuza chinsinsi chake: Tizisinkhasinkha zochita za Yehova, tizichita chidwi ndi ntchito zake, ndiponso tizipemphera kwa iye kuti atithandize.
“Haleluya”
Chilichonse mwa zigawo zinayi zoyambirira za masalmo chimamaliza ndi mawu otamanda Yehova. (Salmo 41:13; 72:19, 20; 89:52; 106:48) Chimodzimodzinso chigawo chomaliza. Pa Salmo 150:6 pamati: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya.” Zimenezi zidzatheka m’dziko latsopano la Mulungu.
Panopo tikudikirira nthawi yosangalatsa imeneyo, ndipo tili ndi chifukwa chabwino cholemekezera Mulungu woona ndi kutamanda dzina lake. Tikaganiza za chimwemwe chimene tili nacho chifukwa chodziwa Yehova ndiponso chifukwa chokhala naye ndi ubwenzi wabwino, kodi sizitilimbikitsa kum’tamanda ndi mtima woyamikira?
[Chithunzi patsamba 15]
Ntchito zodabwitsa za Yehova zimachititsa mantha
[Chithunzi patsamba 16]
Malingaliro a Yehova ‘ali ochuluka koposa mchenga’