‘Zikumbutso Zanu Ndizo Zondikondweretsa’
“Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza.”—AROMA 15:4.
1. Kodi Yehova amatipatsa bwanji zikumbutso, ndipo n’chifukwa chiyani timafunikira zimenezi?
YEHOVA amapatsa anthu ake zikumbutso kuti awathandize kulimbana ndi zovuta za masiku athu ano. Zina mwa zikumbutso zimenezi zimabwera munthu akamawerenga yekha Baibulo, ndipo zina zimachokera mu nkhani kapena ndemanga zoperekedwa pa misonkhano yachikristu. Zambiri zimene timawerenga kapena kumva pa nthawi zimenezi si zachilendo kwa ife. Mosakayikira, tinamvapo zinthu ngati zimenezi m’mbuyomu. Koma popeza sitichedwa kuiwala, tifunika kupitirizabe kudzikumbutsa za zolinga, malamulo, ndi malangizo a Yehova. Tiyenera kuyamikira zikumbutso za Mulungu. Zimatilimbikitsa potikumbutsa zifukwa zomwe zinatichititsa kuyamba kukhala moyo wogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Choncho wamasalmo anaimba kwa Yehova kuti: “Mboni [“zikumbutso,” NW] zanu zomwe ndizo zondikondwetsa.”—Salmo 119:24.
2, 3. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anasunga mpaka masiku ano nkhani za moyo wa anthu otchulidwa m’Baibulo? (b) Kodi ndi nkhani ziti za m’Malemba zimene tione mu nkhani ino?
2 Ngakhale kuti Mawu a Mulungu analembedwa kalekale, ali ndi mphamvu. (Ahebri 4:12) Amatiuza nkhani zoti zinachitikadi pa moyo wa anthu otchulidwa m’Baibulo. Ngakhale kuti miyambo ndi kaganizidwe ka anthu zasintha kuchokera mu nthawi za m’Baibulo, mavuto amene timakumana nawo nthawi zambiri ndi ofanana ndi amene anthu ankakumana nawo kalelo. Nkhani zambiri zimene zasungidwa m’Baibulo kuti zitithandize zili ndi zitsanzo zokhudza mtima za anthu amene ankakonda Yehova ndipo anamutumikira mokhulupirika ngakhale anali pamavuto. Nkhani zina zimasonyeza khalidwe limene Mulungu amadana nalo. Yehova anaonetsetsa kuti nkhani za anthu zonsezi, zabwino ndi zoipa, ziikidwe m’Baibulo kuti zizitikumbutsa zinthu zofunika. Zili ngati mmene mtumwi Paulo analembera kuti: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.”—Aroma 15:4.
3 Tiyeni tione nkhani zitatu izi za m’Malemba: nkhani ya momwe Davide anachitira zinthu ndi Sauli, nkhani ya Hananiya ndi Safira, ndi nkhani ya khalidwe la Yosefe kwa mkazi wa Potifara. Iliyonse ya nkhani zimenezi ikutiphunzitsa maphunziro ofunika kwambiri.
Kukhulupirika ku Makonzedwe a Mulungu
4, 5. (a) Kodi pakati pa Mfumu Sauli ndi Davide panali kuchitika zotani? (b) Kodi Davide anatani ataona chidani cha Sauli?
4 Mfumu Sauli anakhala wosakhulupirika kwa Yehova ndiponso wosayenera kulamulira anthu Ake. Choncho Mulungu anamukana n’kuuza mneneri Samueli kuti adzoze Davide monga mfumu yam’tsogolo ya Israyeli. Davide atasonyeza luso ndi kulimba mtima monga msilikali n’kutamandidwa ndi anthu, Sauli anayamba kumuona Davide ngati wopikisana naye. Sauli anayesetsa maulendo ambiri kuti amuphe. Davide anapulumuka nthawi iliyonse chifukwa Yehova anali naye.—1 Samueli 18:6-12, 25; 19:10, 11.
5 Kwa zaka zambiri, Davide anakakamizika kukhala moyo wothawathawa. Mwayi woti aphe Sauli utapezeka, anzake a Davide anamulimbikitsa kuti atero, ndipo anati Yehova anali kupereka mdani wa Davideyo m’dzanja lake. Koma Davide anakana. Kukhulupirika kwake kwa Yehova ndi kulemekeza udindo wa Sauli monga mfumu yodzozedwa ya anthu a Mulungu, kunamuchititsa kuti achite zinthu mwanjira imeneyi. Kodi si Yehova amene anaika Sauli kuti akhale mfumu ya Israyeli? Ndi Yehova yemweyo amene akanadzamuchotsa ngati anaona kuti m’poyenera kutero. Davide anaona kuti si iyeyo amene anayenera kuchitapo kanthu. Atachita zonse zomwe akanatha panthawiyo kuti achepetseko chidani cha Sauli kwa iye, Davide anamaliza n’kunena kuti: “Yehova adzam’kantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako. Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.”—1 Samueli 24:3-15; 26:7-20.
6. Kodi n’chifukwa chiyani nkhani ya Davide ndi Sauli ili yofunika kuti tiiganizire?
6 Nkhani imeneyi ili ndi phunziro lofunika kwambiri. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani mumpingo wachikristu mumabuka mavuto enaake? Mwina n’kutheka kuti munthu wina akuchita zinthu m’njira yosayenera. Khalidwe lakelo mwina si tchimo lalikulu, koma likukuvutitsani maganizo. Kodi muyenera kutani? Chifukwa chomukonda munthuyo popeza ndi Mkristu mnzanu ndiponso chifukwa chokhulupirika kwa Yehova, mungalingalire zokalankhula naye mokoma mtima, n’cholinga choti mum’bweze. Koma bwanji ngati vutolo likupitirirabe? Mutachita zonse zomwe mungathe, mwina mungangofunika kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Zimenezo n’zimene Davide anachita.
7. Potsanzira Davide, kodi tiyenera kutani tikamachitiridwa zinthu zopanda chilungamo kapena zatsankho?
7 Mwina mukukumana ndi mavuto okhudzana ndi kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo kapena kudedwa chifukwa cha chipembedzo chanu. N’kutheka kuti pali zochepa chabe zimene mungathe kuchita pa nkhaniyo panopa, kapenanso palibe chilichonse chomwe mungachitepo. Zinthu ngati zimenezo zikhoza kukhala zovuta kwambiri kuzipirira, koma zomwe Davide anachita pochitiridwa zinthu zopanda chilungamo zikutiphunzitsa kanthu kena. Masalmo amene Davide analemba ndi mbiri yokhudza mtima ya mapemphero ake ochokera pansi pamtima opempha Mulungu kuti amuteteze kwa Sauli komanso ya kukhulupirika kwake kwa Yehova ndi nkhawa yake yoti dzina la Mulungu lilemekezedwe. (Salmo 18:1-6, 25-27, 30-32, 48-50; 57:1-11) Davide anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti Sauli anapitiriza kumuchitira zinthu zopanda chilungamo kwa zaka zambiri. Nafenso tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake kaya tikuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo, ndiponso kaya ena akuchita zotani. Tiyenera kukhulupirira kuti Yehova akudziwa bwino zomwe zikuchitika.—Salmo 86:2.
8. Kodi Mboni za Yehova ku Mozambique zinatani kukhulupirika kwawo kwa Yehova kutayesedwa?
8 Akristu a ku Mozambique ndi chitsanzo cha masiku ano cha anthu amene anamamatirabe kwa Yehova mokhulupirika pa nthawi ya mayesero. Mu 1984, midzi yawo inkaukiridwa mobwerezabwereza ndi asilikali oukira boma amene ankaba zinthu, kutentha nyumba, ndi kupha anthu. Pankaoneka kuti palibe chilichonse chomwe Akristu oonawa akanachita kuti adziteteze. Asilikaliwo anayesera kukakamiza anthu okhala m’deralo kuti alowe m’gulu lawo kapena kuti awathandize m’njira zina. Mboni za Yehova pokhala Akristu, zinaona kuti kuchita zimenezo n’kosagwirizana ndi mfundo yomwe zimayendera yosatenga nawo mbali pandale. Zitakana choncho, anazipsera mtima kwambiri. Mboni zokwana 30 zinaphedwa panthawi yovuta imeneyo, koma ngakhale pamene anali kuopsezedwa kuti aphedwa, anthu a Mulunguwa sanasiye kukhala okhulupirika.a Mofanana ndi Davide, anapirira zinthu zopanda chilungamo, koma pamapeto pake anapambana.
Chikumbutso Chotichenjeza
9, 10. (a) Kodi tingapindule bwanji ndi zitsanzo zina za m’Malemba? (b) Kodi cholakwika chinali chiyani ndi zimene Hananiya ndi Safira anachita?
9 Anthu ena otchulidwa m’Malemba amatipatsa zikumbutso zotichenjeza za khalidwe limene tiyenera kupewa. Zoonadi, m’Baibulo muli nkhani zambiri za anthu, ngakhale pakati pa atumiki a Mulungu, amene anachita zoipa ndipo zinthu sizinawayendere bwino. (1 Akorinto 10:11) Nkhani imodzi yoteroyo ndi ya Hananiya ndi Safira, mwamuna ndi mkazi wake amene anali mumpingo woyambirira wachikristu ku Yerusalemu.
10 Pambuyo pa Pentekoste wa mu 33 C.E., okhulupirira atsopano amene anatsalira ku Yerusalemu, kuti apindule pocheza ndi atumwi, anafunikira kuthandizidwa zinthu zofunika pamoyo wawo. Anthu ena mumpingomo anagulitsa katundu wawo kuti pasapezeke wosowa. (Machitidwe 2:41-45) Hananiya ndi Safira anagulitsa munda ndipo anabweretsa mbali chabe ya ndalamazo kwa atumwi, n’kuwauza kuti mphatso yawoyo inali ndalama zonse zomwe anapeza atagulitsa mundawo. N’zoona kuti Hananiya ndi Safira anali aufulu kupereka ndalama zochuluka kapena zochepa momwe akanafunira, koma cholinga chawo chinali choipa, ndipo anachita chinyengo. Ankafuna kuoneka ngati abwino kwa anthu owaona, ndiponso ankafuna kuti azioneka ngati akuchita zambiri kuposa zimene anali kuchitadi. Mtumwi Petro, mouziridwa ndi mzimu woyera, anavumbula chinyengo chawocho, ndipo Yehova anawakantha n’kufera pompo.—Machitidwe 5:1-10.
11, 12. (a) Kodi zikumbutso zina pa nkhani ya kuona mtima n’zotani? (b) Kodi timapindula bwanji chifukwa chochita zinthu moona mtima?
11 Tikafuna kubisa chilungamo pofuna kuti ena atione ngati ndife anthu abwino, nkhani ya Hananiya ndi Safira izikhala chenjezo lamphamvu kwa ife. Tikhoza kunyenga anthu anzathu, koma Yehova sitingamunamize. (Ahebri 4:13) Nthawi zambiri Malemba amatilimbikitsa kuti tizichita zinthu moona mtima ndi anzathu, chifukwa anthu abodza sadzakhala pa dziko lapansi akadzachotsapo kupanda chilungamo konse. (Miyambo 14:2; Chivumbulutso 21:8; 22:15) Ndipo chifukwa chake n’chodziwika bwino. Amene amalimbikitsa mabodza onse si winanso ayi koma Satana Mdyerekezi.—Yohane 8:44.
12 Kuchita zinthu moona mtima nthawi zonse kumatipindulitsa m’njira zambiri. Zina mwa izo ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino ndiponso kusangalala podziwa kuti ena amatikhulupirira. Nthawi zambiri, Akristu apeza ntchito kapena sanachotsedwe ntchito chifukwa chochita zinthu moona mtima. Koma phindu lofunika kwambiri n’loti kuona mtima kumatichititsa kukhala mabwenzi a Mulungu Wamphamvuyonse.—Salmo 15:1, 2.
Khalanibe Odzisunga
13. Kodi Yosefe anapezeka ali m’zochitika zotani, ndipo anatani?
13 Yosefe, mwana wa kholo lakale Yakobo, anagulitsidwa ku ukapolo ali ndi zaka 17. Kenaka anakapezeka m’nyumba ya Potifara, mmodzi mwa akuluakulu a boma ku Igupto, kumene mkazi wa Potifara, bwana wake wa Yosefe, anakopeka naye. Ankafuna kugona ndi Yosefe, amene anali mnyamata wokongola, ndipo tsiku lililonse ankamuuza kuti: “Gona ndi ine.” Yosefe anali m’dziko limene kunalibe womudziwa, kutali ndi banja lake. Akanatha kugona ndi mkaziyu popanda aliyense kudziwa. Koma tsiku lina mkazi wa Potifara atamugwira, Yosefe anathawa.—Genesis 37:2, 18-28; 39:1-12.
14, 15. (a) Kodi n’chifukwa chiyani nkhani ya Yosefe ili yofunika kuti tiiganizire? (b) Kodi n’chifukwa chiyani mkazi wina wachikristu anali woyamikira kuti anamvera zikumbutso za Mulungu?
14 Yosefe analeredwa m’banja loopa Mulungu ndipo ankadziwa kuti kugonana kwa anthu amene si okwatirana n’kulakwa. Iye anafunsa kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” N’kutheka kuti iye anazindikira zimenezi chifukwa chodziwa lamulo lomwe Mulungu anapatsa anthu mu Edene, loti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi. (Genesis 2:24) Anthu a Mulungu masiku ano angapindule poganizira momwe Yosefe anachitira zinthu panthawi imeneyo. M’madera ena, maganizo a anthu pa nkhani ya kugonana n’ngololera kwambiri moti achinyamata amene amakana kuchita chiwerewere amasekedwa ndi anzawo. Achikulire ambiri amagonana ndi munthu amene si mkazi wawo kapena mwamuna wawo. Choncho, nkhani ya Yosefe ndi chikumbutso chapanthawi yake kwa ife. Lamulo la Mulungu likadali loti kuchita dama ndi chigololo n’kuchimwa. (Ahebri 13:4) Anthu ambiri amene anagonjera thupi lawo n’kuchita chiwerewere amavomereza kuti pali zifukwa zabwino zomwe sitiyenera kuchitira zimenezi. Zina mwa zotsatirapo zake zoipa zingakhale kuchita manyazi, kuvutika chikumbumtima, kuchita nsanje, kutenga mimba, ndi kutenga matenda opatsirana pogonana. Monga momwe Malemba amatikumbutsira, munthu amene wachita chiwerewere ‘amachimwira thupi lake la iye yekha.’—1 Akorinto 5:9-12; 6:18; Miyambo 6:23-29, 32.
15 Jenny,b Mboni yosakwatiwa ya Yehova, ali ndi zifukwa zoyamikirira zikumbutso za Mulungu. Kuntchito kwawo, mwamuna wina wooneka bwino ankamufuna. Jenny atasonyeza kuti alibe chidwi, mwamunayo anawonjezera kuchita zinthu zosonyeza kuti akumufuna. Jenny anati: “Ndinayamba kuvutika kuti ndidzisungebe, chifukwa munthu umamva bwino mumtima ukaona kuti mwamuna kapena mkazi winawake akusangalala nawe.” Komabe, iye anazindikira kuti mwamunayo ankangofuna kumuwonjezera pa mndandanda wa akazi amene anagonapo nawo. Ataona kuti maganizo ake oti amukane mwamunayo ayamba kufooka, anachonderera Yehova kuti amuthandize kukhalabe wokhulupirika kwa Iye. Jenny anaona kuti zinthu zimene ankaphunzira akamafufuza m’Baibulo ndi m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo zinali ngati zikumbutso zimene zinkamupatsa mphamvu zowonjezera zoti akhalebe wolimba. Chimodzi mwa zikumbutso zimenezo inali nkhani ya Yosefe ndi mkazi wa Potifara. Iye anamaliza n’kuti: “Ndikapitirizabe kudzikumbutsa za momwe ndimakondera Yehova, palibe chifukwa choti ndiziopera kuti mwina ndingachite choipa chachikuluchi n’kumuchimwira.”
Mverani Zikumbutso za Mulungu!
16. Kodi tingapindule bwanji mwa kuwerenganso ndi kusinkhasinkha za moyo wa anthu amene anatchulidwa m’Baibulo?
16 Tonsefe tingawonjezere kuyamikira kwathu miyezo ya Yehova mwa kuyesetsa kumvetsa chifukwa chomwe anachititsira kuti nkhani zinazake zisungidwe m’Malemba kuti ifeyo tidzaziwerenge. Kodi zimatiphunzitsa chiyani? Kodi ndi makhalidwe kapena mtima wotani umene anthu otchulidwa m’Baibulo anasonyeza umene tiyenera kutsanzira kapena kupewa? M’Mawu a Mulungu timakumana ndi anthu mahandiredi ambiri. Anthu onse amene amakonda malangizo a Mulungu angachite bwino atakulitsa kufunitsitsa kwawo nzeru zopatsa moyo, kuphatikizapo maphunziro amene tingaphunzire ku zitsanzo zimene Yehova wazisunga mosamala. Magazini ino nthawi zambiri yalembapo nkhani za anthu ngati amenewo, amene moyo wawo umatiphunzitsapo kenakake. Bwanji osapatula nthawi yoti muwerengenso nkhani zimenezi?
17. Kodi zikumbutso za Yehova mumaziona bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani mumatero?
17 Tiyenera kukhala oyamikira kwambiri chifukwa cha nkhawa imene Yehova, mwa chikondi chake, amadera anthu amene akuyesetsa kuchita chifuniro chake. Ife siife anthu angwiro, monganso akazi ndi amuna otchulidwa m’Baibulo sanali angwiro. Komabe, nkhani zomwe zinalembedwa m’Baibulo za zochita zawo ndi zothandiza kwambiri kwa ife. Mwa kumvera zikumbutso za Yehova, tikhoza kupewa zolakwa zazikulu, ndipo tikhoza kutsanzira zitsanzo zabwino za anthu amene anayenda m’njira zachilungamo. Tikatero, tingathe kuvomerezana ndi wamasalmo, amene anaimba kuti: “Odala iwo akusunga [zikumbutso za Yehova], akum’funa ndi mtima wonse; moyo wanga unasamalira [zikumbutso] zanu; ndipo ndizikonda kwambiri.”—Salmo 119:2, 167.
[Mawu a M’munsi]
a Onani kabuku kakuti Mboni za Yehova m’Mozambique—Mbiri ya Kusunga Umphumphu, tsamba 30 mpaka 32.
b Tasintha dzina.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi tingaphunzire chiyani pa mtima umene Davide anaonetsa kwa Sauli?
• Kodi nkhani ya Hananiya ndi Safira ikutiphunzitsa chiyani?
• Kodi n’chifukwa chiyani nkhani ya moyo wa Yosefe ili yothandiza kwambiri masiku ano?
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi n’chifukwa chiyani Davide anakana kulola kuti Sauli aphedwe?
[Chithunzi patsamba 27]
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani ya Hananiya ndi Safira?
[Chithunzi patsamba 28]
Kodi n’chiyani chinachititsa Yosefe kukana chiwerewere?