Chaputala 17
Kukumbukira Mokhulupirika Gulu la Yehova
1. Kodi tiyenera kulingalira za kukhulupirika kwayani, ndipo kodi Mfumu Davide ananenanji pamfundoyi?
ZAMBIRI zanenedwa lerolino ponena za kukhulupirika kwa munthu kudziko lake. Koma kodi olamulira ndi anthu a dziko lino amanena zochuluka motani ponena za kukhulupirika kwa Mulungu, amene ali Mlengi wa chigawo cha dziko limene munthuyo akukhalamo? M’nthaŵi zakale, Mfumu Davide wa Israyeli anali wolambira wokhulupirika wa Mlengi, Yehova Mulungu. Polankhula kwa Mulungu wokhulupirika ameneyu, Davide ananena mawu awa kwa iye: “Pa munthu wangwiro mukhala wangwiro.” (2 Samueli 22:26; Salmo 18:25) Kodi mawu ameneŵa amasonyeza mkhalidwe wanu kulinga kwa Mulungu?
2. Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova wakhalabe wokhulupirika kubanja laumunthu?
2 Mkhalidwe wodziŵika wa anthu lerolino ndiwo kusasonyeza nkhaŵa yaikulu ponena za kukhulupirika kwa Mulungu. Koma mosasamala kanthu za zimenezi, Yehova ali wokhulupirika kubanja laumunthu, iye sanalinyanyale. Mwana wake wokhulupirika anati: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mulungu sanasiye dziko la mtundu wa anthu kwa mdani wake wamkulu koposa, Satana, amene anali atasonkhezera makolo athu oyamba kukhala osakhulupirika kwa Mulungu. Mulungu anasonyezanso kukhulupirika kwake kubanja laumunthu mu 2370 B.C.E. mwa kusunga Nowa ndi banja lake kupulumuka chigumula cha dziko lonse chimene chinasesa otsala onse a anthu. (2 Petro 2:5) Mwanjira imeneyi, Mlengi anapereka chiyambi chatsopano kubanja laumunthu.
3. (a) Kodi nchiyani chimene chinganenedwe ponena za chiwawa lerolino, ndipo kodi Mulungu walinganiza kuchitanji za icho? (b) Kodi nchiyani chimene chiri mphotho ya kukhulupirika kwa Yehova?
3 Lerolino chiwawa padziko lonse lapansi chikuposa cha m’nthaŵi ya Nowa zaka zoposa 4 000 zapitazo. (Genesis 6:11) Motero kuli koyenerera kuti Mulungu mmodzimodziyo asese dongosolo lonse laudziko lamakono la zinthu. Iye walinganiza kuchita zimenezi, koma pakutero, sadzawononga okhulupirika ake padziko lapansi. Panthaŵiyo adzachita mogwirizana ndi Salmo 37:28: “Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake.” Mofanana ndi m’tsiku la Nowa, adzapatsa chiyambi chachilungamo m’dongosolo la zinthu latsopano lopangidwa ndi “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” (2 Petro 3:13) Mphotho ya kukhulupirika njaikulu. Njopereka moyo!
4. Kodi timadziŵa bwanji kuti mtundu wa Israyeli unali gulu lowoneka la Yehova la panthaŵiyo?
4 Mkati mwa kulamulira kwa Mfumu Davide, mtundu wa Israyeli unatsimikizira kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Davide anakhazikitsa chitsanzo cha mtundu wathunthu. Mtundu umenewo unali gulu lowoneka la Yehova. Unali anthu olinganizidwa amene anali ake mwapadera. Mosakaikira ndizo zimene zikutanthauzidwa ndi chikumbutso cha Mulungu, monga momwe chalongosoledwera mu Amosi 3:1, 2: “Tamverani mawu aŵa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israyeli, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m’dziko la Aigupto, ndi kuti, Inu nokha ndinakudziŵani mwa mabanja onse apadziko lapansi.”—Yerekezerani ndi 1 Mafumu 8:41-43.
5. (a) Mkati mwa masiku a atumwi a Yesu Kristu, kodi zoyesayesa zinapangidwa kuloŵetsa zolakwa mumpingo Wachikristu? (b) Kodi nchiyani chimene chinanenedweratu kudzachitika pambuyo pa imfa ya atumwi?
5 Mogwirizana ndi chowonadi chimenechi cha mbiri ya Baibulo, Mulungu mmodzimodzi ameneyu, Yehova, ali ndi anthu olinganizidwa, gulu lowoneka, padziko lapansi lerolino. Liri gulu limene liri la iye yekha. Komabe, zoyesayesa zinapangidwa za kuloŵetsa mphulupulu m’gulu la Mulungu ngakhale pa kuyambika kwake m’masiku a atumwi a Yesu Kristu, amene anali ochirikiza olimba aumphumphu wa mpingo Wachikristu. (1 Akorinto 15:12; 2 Timoteo 2:16-18) Pambuyo pa imfa ya mtumwi Yohane, mwachiwonekere osati nthaŵi yaitali pambuyo pa 98 C.E., kupanduka konenedweratuko kunayamba.—Machitidwe 20:30; 2 Petro 2:1, 3; 1 Timoteo 4:1.
6. (a) Kodi mpatuko unayanga nkhata kwautali wotani, ndipo ndi zotulukapo zotani? (b) Kodi magulu achipembedzo cha Dziko Lachikristu analoŵa mu ukapolo wotani, ndipo ndimafunso otani amene amabuka?
6 Mpatuko umenewo unayanga nkhata kwa zaka zoposa mazana 17, kufikira mbali yotsirizira ya zaka za zana la 19. Podzafika nthaŵiyo Dziko Lachikristu linali litagaŵanika kukhala mipatuko ya chipembedzo mazana ambiri. Kudziŵika kwa anthu owona a Mulungu kunadodometsedwa. Dziko Lachikristu linali babele wamagulu achipembedzo, aakulu ndi aang’ono, olankhula zinenero zamitundumitundu zachipembedzo zosachirikizidwa mwamphamvu m’chinenero cha chipembedzo cha Malemba ouziridwa. Kwenikweni magulu achipembedzo otero anali ataloŵetsedwa mu ukapolo ndi ulamuliro umene unali waukulu kwambiri kuposa Ulamuliro wa Babulo umene unawononga Yerusalemu. Koma kodi Babulo wakale anali wotani, ndipo kodi mkhalidwewo uyenera kukhala unali wotani kwa Ayuda okhulupirika amene adagwidwa undende?
Andende a Babulo Anakumbukira Ziyoni Mokhulupirika
7. (a) M’kulankhula kwa chipembedzo, kodi dziko la Babulo wakale linali lofanana nchiyani? (b) Kodi nchiyambukiro chotani chimene zimenezi zinali nacho pa andende Achiyuda?
7 Babulo wakale anali dziko la milungu yonyenga, imene mafano awo anali ambiri. (Danieli 5:4) Tingathe kuyerekezera chiyambukiro chimene kulambira kumeneku kwa milungu yambiri yonyenga kunali nacho pamitima ya Ayuda okhulupirika amene analambira Mulungu mmodzi wowona yekha popanda fano la mtundu uliwonse. Mmalo mwa kuyang’ana kachisi wa Yehova ndi kukongola kwake m’Yerusalemu, iwo anayang’ana tiakachisi tamilungu yonama imeneyi ndi mafano ake m’dziko lonselo la Babulo.a Ha olambira a Mulungu mmodzi wowona yekha ayenera kukhala atanyansidwa chotani nanga ndi zonsezi!
8. (a) Kodi Ayuda akapirira undende wawo kwautali wotani, ndipo ndichikhumbo chotani chimene Ayuda okhulupirika akakhala nacho? (b) Kodi ndimotani mmene Salmo 137:1-4 amalongosolera mkhalidwe wachisoni wa andende Achiyuda okhulupirika?
8 Mogwirizana ndi kunena kwa ulosi wa Yeremiya, iwo akafunikira kupirira mkhalidwe umenewu kwa zaka 70 kubwezeretsedwa kusanadze. (2 Mbiri 36:18-21; Yeremiya 25:11, 12) Mkhalidwe womvetsa chisoni wa andende Achiyuda amene anakonda Yehova ndi kukhumba kumlambira pakachisi wopatulikitsidwira kwa iye pamzinda wake wosankhidwa walongosoledwa kwa ife m’Salmo 137:1-4: “Kumitsinje ya ku Babulo, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukira Ziyoni. Pamsondodzi uli m’mwemo tinapachika mazeze athu. Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo, ndipo akutizunza anafuna tisekerere, ndi kuti, Mutiimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni. Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m’dziko lachilendo?”
9. Kodi ndimotani mmene Ababulo akawonera kuimba “nyimbo ya Yehova,” koma nchiyani chimene chinali kuyenera kuchitika pamapeto a zaka 70?
9 “Nyimbo ya Yehova” iyenera kukhala nyimbo ya anthu aufulu omlambira pakachisi wake wopatulika. Kwa Ababulo amenewo, kuimbidwa kwa “nyimbo ya Yehova” ndi Ayuda ameneŵa m’dziko limene iwo anali andende kukakhala mpata wakuti oŵagwira ndendewo atonze dzina la Yehova monga dzina la mulungu wopanda mphamvu koposa milungu ya ku Babulo. Dzina lake loyera linali litatonzedwa kale kwambiri mwa kulola kwake anthu ake kuchotsedwa m’dziko lawo limene adapatsidwa ndi Mulungu ndipo anapititsidwa kudziko la milungu yochuluka. Koma nthaŵi yakuti anthu a ku Babulo amenewo amtonze ndipo anyoze anthu a dzina lake inali kokha nthaŵi yokhala ndi polekezera—zaka 70. Pamenepo akasiya milungu yonama ya Babulo ndipo akakweza Mulungu wowona, Yehova!
Kumamatira ndi Mtima ku Gulu la Yehova
10. Kodi ndifunso lotani limene limabuka ponena za anthu a Yehova a m’zaka za zana la 20 zino amene analoŵetsedwa muukapolo wa Babulo Wamkulu?
10 Lerolino pali gulu la chipembedzo lotchedwa Babulo Wamkulu limene siliri lolekezera kudziko la Babulo woyamba koma limene liri padziko lonse lapansi. Kodi mkhalidwe wamtima wa Ayuda m’Babulo wakale unapereka chitsanzo cholungama kaamba ka anthu a Yehova a m’zaka za zana la 20 lino amene mwa chikakamizo analoŵetsedwa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu monga chilango chochokera kwa Mulungu wa Israyeli wakale?
11. (a) Kodi Ayuda okhulupirika anaiŵala kwawo? (b) Kodi ndimotani mmene wamasalmo wandendeyo anasonyezera malingaliro a andende anzake?
11 Ngakhale kuli kwakuti iwo akanakhazikika m’Babulo wakale ndi kukhala phee mosatekeseka, popeza undendewo ukakhala pafupifupi wokwanira mbadwo umodzi, kodi iwo anaiŵala dziko lawo? Wamasalmo wogwidwa ndendeyo ananena bwino pamene amalankhula malingaliro a andende anzake: “Ndikakuiŵalani, Yerusalemu, dzanja lamanja langa liiŵale luso lake. Lirime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana.”—Salmo 137:5, 6.
12. Kodi mkhalidwe wamtima wa wamasalmo wandendeyo unasonyezanji?
12 Kodi mkhalidwe wa mtima umenewo wa wandende Wachiisrayeli unasonyezanji? Ichi: Kukhulupirika kugulu lowoneka la Yehova la panthaŵiyo pamene iye anawona dziko limene Mulungu anapereka kwa anthu Ake osankhidwa liri labwinja kwa zaka 70. Inde, gulu lowoneka la Yehova linali kukhala m’mitima ya Israyeli amenewo.
13. Kodi ndimotani mmene kukhulupirika kugulu lowoneka la Yehova kunafupidwira?
13 Kukhulupirika kotero kugulu lakale lowoneka la Mulungu kunafupidwa moyenerera. Zimenezi zinachitika pamene Babulo, ulamuliro wa dziko wachitatu m’mbiri ya Baibulo, unagubuduzidwa, ndi Amedi ndi Aperisi, ulamuliro wa dziko wachinayi, unakwaniritsa chifuniro cha Mulungu wa Israyeli. Motani? Mwa kubwezeretsa Ayuda andendewo kudziko la gulu lowoneka la Yehova, limodzi ndi malangizo a kumanganso kachisi wa Mulungu wawo monga malo apakati a malikulu, Yerusalemu. (2 Mbiri 36:22, 23) Sikokha kuti kachisi wa kulambira kowona anamangidwanso koma mzinda wamalinga wa Yerusalemu anamangidwanso, kukhala mzinda kuchokera kumene Yehova analamulira monga Mfumu pa anthu ake.
14. (a) Zaka mazana angapo pambuyo pake, kodi nchiyani chimene Mesiya adanena ponena za gulu lowoneka la Yehova? (b) Kodi ndimlingaliro lotani limene Yehova analamulira kuchokera ku Yerusalemu?
14 Zaka zoposa mazana asanu ndi limodzi pambuyo pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu, Yesu anati: “Musalumbire konse, kapena kutchula kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu; kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa liri popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulu.” (Mateyu 5:34, 35) Pamene Mesiya anali padziko lapansi, kachisi womangidwanso wa Yehova anali m’Yerusalemu, ndipo, mophiphiritsira, Yehova Mulungu anachita ufumu m’Malo Opatulikitsa a kachisi ameneyo. Motero kuchokera ku Yerusalemu monga malikulu a anthu ake, Yehova anachita ufumu pagulu lake lowoneka.
Yehova Akhalabe Wokhulupirika ku Gulu Lake
15. Kodi Yesu anali kukana mbali yowoneka ya gulu la Yehova pamene anavumbula atsogoleri achipembedzo osakhulupirika a Israyeli? Longosolani.
15 Komabe, kodi ndiko kuti, Yesu anataya gulu lowoneka la Mulungu pamene anavumbula atsogoleri achipembedzo osakhulupirika a Israyeli ndi kuwadzudzula? Inde, pakuti anati: “Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Wonani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:37, 38) Pamene Yesu anakana Yerusalemu ndi “ana” ake, kodi iye mwa kutero anali kusiya Atate wake ali wopanda gulu la padziko lapansi? Ayi! Chifukwa chakuti Yesu mwiniyo anali maziko a gulu latsopano lowoneka limene Mlengi wachilengedwe chonse anali kudzamanga.
16. Panthaŵi ya imfa ya Yesu pamtengo wozunzirapo, kodi kukanidwa kwa Israyeli wakuthupi kunawoneka motani?
16 Kukanidwa kwa Israyeli wakuthupi kwenikweni kunasonyezedwa pamene, pa imfa ya Yesu pamtengo wozunzirapo, chochinga chokhuthala chimene chinalekanitsa malo Opatulikitsa ndi Opatulika m’kachisi wa Yerusalemu chinang’ambika pakati “kuchokera kumwamba kufikira pansi.” Panthaŵi imodzimodziyo “dziko linagwedezeka, ndi miyala inang’ambika.” Zimenezi zinali zochitika zozizwitsa za Mulungu amene anali kulamulira pamenepo mwanjira yophiphiritsira, kusonyeza kukana kwake mtundu wa Israyeli ndi chipembedzo chawo.—Mateyu 27:51.
17. Kodi ndimotani mmene Yesu ndi Yehova anasonyezera kukhulupirika kwa mamembala oyembekezeredwa a gulu latsopano lowoneka la Mulungu?
17 Mamembala oyembekezeredwa a gulu latsopano lowoneka limene Yehova Mulungu mwamsanga anali kudzamanga anasiyidwa kumeneko mu ufumu wa Yerusalemu. Yesu anawasiya m’chisamaliro cha Mulungu, amene anali kudzasiya mzinda wa padziko lapansi moyanja kanthu kena kabwinopo. (Yohane 17:9-15) Motero Yehova anakhalabe wokhulupirika kugulu lake, akumasonyeza chifundo chapadera kaamba ka makolo awo okhulupirika, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo ndi ana 12 a Yakobo. (Danieli 12:1) Chaputala chotsatira chidzapitirizabe ndi nkhani yathu ya kukhulupirika, yochokera pa Salmo 137.
[Mawu a M’munsi]
a Cholembedwa chozokotedwa cha ku Babulo wakale chimasimba kuti: “Onse pamodzi pali akachisi 53 m’Babulo a milungu yaikulu, malo olambirira Marduk okwanira 55, malo okwanira 300 olambirira milungu ya padziko lapansi, 600 ya milungu ya m’miyamba, maguwa ansembe 180 a mulungu wachikazi Ishtar, 180 a milungu ya Nergal ndi Adad ndi maguwa ansembe ena 12 a milungu yosiyanasiyana.”