Kodi Mulungu Amakudziŵanidi?
“Yehova, . . . njira zanga zonse muzoloŵerana nazo.”—SALMO 139:1, 3.
1. Kodi nlofala motani lingaliro lakuti ‘ena samamvetsetsa’ nkhaŵa, mavuto, ndi zitsenderezo zimene timayang’anizana nazo?
KODI pali munthu aliyense amene amadziŵadi nkhaŵa, zitsenderezo, ndi mavuto amene mumayang’anizana nawo? Kuzungulira dziko lonse pali mamiliyoni a anthu, achichepere ndi achikulire, amene alibe banja kapena achibale amene angasamale zimene zimawachitikira. Ngakhale m’mabanja, akazi ambiri—inde, ndi amuna omwe—amaona kuti anzawo amuukwati samamvetsetsa zovuta zimene amakhala nazo. Nthaŵi zina, pokhala atathedwa nzeru, amayankha kuti: “Inu simundimvetsetsa!” Ndipo achichepere ambiri anenanso kuti palibe amene amawamvetsetsa. Komabe, pakati pa awo amene akufuna kumvetsetsedwa ndi anthu ena pali ena amene miyoyo yawo pambuyo pake yakhala yopindulitsa kwambiri. Kodi zimenezo nzotheka motani?
2. Kodi nchiyani chingatheketse alambiri a Yehova kukhala ndi moyo wokhutiritsa kwambiri?
2 Chifukwa chakuti, mosasamala kanthu kuti kaya anthu anzawo amamvetsetsa malingaliro awo kapena ayi, iwo ali ndi chidaliro chakuti Mulungu amamvetsetsa zimene akukumana nazo ndi kuti, monga atumiki ake, iwo samakhala okha m’mavuto awo. (Salmo 46:1) Ndiponso, Mawu a Mulungu pamodzi ndi chithandizo cha akulu Achikristu aluntha zimawatheketsa kuona zofunika zoposa mavuto aumwini. Malemba amawathandiza kuzindikira kuti utumiki wawo wokhulupirika ngwamtengo wapatali kwa Mulungu ndi kuti awo okhala ndi chiyembekezo mwa iye ndi m’makonzedwe amene wapanga kupyolera mwa Yesu Kristu, ali ndi mtsogolo mosungika.—Miyambo 27:11; 2 Akorinto 4:17, 18.
3, 4. (a) Kodi ndimotani mmene kuzindikira mfundo yakuti “Yehova ndiye Mulungu” ndi kuti ndiye “anatilenga” kungatithandizire kupeza chimwemwe muutumiki wake? (b) Kodi nchifukwa ninji tili ndi chidaliro chokwanira m’chisamaliro chachikondi cha Yehova?
3 Mwina mukulidziŵa bwino lemba la Salmo 100:2, limene limati: “Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.” Kodi ndiangati amene amatumikiradi Yehova mwanjira imeneyo? Zifukwa zabwino zochitira zimenezo zaperekedwa m’vesi 3, limene limatikumbutsa kuti: “Dziŵani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.” M’malemba Achihebri, iye akutchulidwa monga ʼElo·himʹ, kusonyeza ukulu wake m’mphamvu, ulemu, ndi ulemerero. Iye ali Mulungu yekha wowona. (Deuteronomo 4:39; 7:9; Yohane 17:3) Atumiki ake amafikira pakudziŵa Umulungu wake, osati chabe monga mfundo yowona imene anaphunzitsidwa koma monga chinthu chimene adzionera okha ndi chimene amachitira umboni mwakumvera, kukhulupirira, ndi kudzipereka.—1 Mbiri 28:9; Aroma 1:20.
4 Popeza kuti Yehova ali Mulungu wamoyo, wokhoza kuona ngakhale za mumtima mwathu, palibe kanthu kamene kamabisika kwa iye. Iye amadziŵa bwino lomwe zimene zikuchitika m’miyoyo yathu. Iye amamvetsetsa zimene zimachititsa mavuto amene timayang’anizana nawo limodzinso ndi kupsinjika maganizo ndi mtima kumene mavutowo angachititse. Monga Mlengi, amatidziŵa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziŵira ife eni. Iye amadziŵanso mmene angatithandizire kuchita ndi mkhalidwe wathu ndi mmene angaperekere mpumulo wokhalitsa. Iye adzatithandiza mwachikondi—mofanana ndi mbusa amene afukata pachifuwa chake mwana wa nkhosa—pamene tidalira pa iye ndi mtima wathu wonse. (Miyambo 3:5, 6; Yesaya 40:10, 11) Kuphunzira lemba la Salmo 139 kukhoza kutithandiza kwambiri kulimbitsa chidaliro chathu.
Uyo Amene Amaona Njira Zathu Zonse
5. Kodi ‘kusanthulidwa’ ndi Yehova kumatanthauzanji, ndipo kodi nchifukwa ninji zimenezo zili zofunika kwambiri?
5 Ndi chiyamikiro chachikulu, wamasalmo Davide analemba kuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziŵa.” (Salmo 139:1) Davide anali ndi chidaliro chakuti kudziŵidwa kwake ndi Yehova sikunali kwapamwamba chabe. Mulungu sanaone Davide mmene anthu angakhale anamuonera, kuona kaumbidwe ka thupi lake kokha, luso lake la kulankhula, kapena ukatswiri wake wakuimba zeze. (1 Samueli 16:7, 18) Yehova ‘anasanthula’ mtima wa Davide ndipo anatero ndi nkhaŵa yachikondi kaamba ka ubwino wake wauzimu. Ngati muli mmodzi wa atumiki odzipereka a Yehova, iye amakudziŵani bwino lomwe monga momwe anadziŵira Davide. Kodi zimenezo sizimadzutsa mwa inu malingaliro a chiyamikiro ndi mantha?
6. Kodi lemba la Salmo 139:2, 3 limasonyeza motani kuti Yehova amadziŵa kalikonse kamene timachita, ngakhale malingaliro athu onse?
6 Zochita zonse za Davide zinali pambalambanda kwa Yehova, ndipo Davide anadziŵa zimenezo. “Inu mudziŵa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga,” analemba motero wamasalmoyo. “Muzindikira lingaliro langa muli kutali. Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzoloŵerana nazo.” (Salmo 139:2, 3) Ngakhale kuti Yehova ali kumwamba, kutalitali ndi dziko lapansi, sanalephere kudziŵa zimene Davide anali kuchita kapena zimene anali kulingalira. Iye ‘anayesa,’ kapena kupenda mosamalitsa, zochita za Davide, ponse paŵiri usana ndi usiku, kuti adziŵe kuti zinali zotani.
7. (a) Mwakugwiritsira ntchito moyo wa Davide monga maziko, perekani ndemanga pazinthu zina m’miyoyo yathu zimene Mulungu amadziŵa. (b) Kodi kudziŵa zimenezi kuyenera kutiyambukira motani?
7 Pamene chikondi chake pa Mulungu ndi chidaliro m’mphamvu Yake yakupulumutsa chinasonkhezera Davide monga mnyamata kudzipereka kukamenyana ndi chimphona Chachifilisti chotchedwa Goliati, Yehova anadziŵa zimenezo. (1 Samueli 17:32-37, 45-47) Pambuyo pake, pamene chidani cha anthu chinapweteka kwambiri mtima wa Davide, pamene anavutika mtima kwambiri kotero kuti analira usiku, iye anatonthozedwa ndi chidziŵitso chakuti Yehova anamva kupembedzera kwake. (Salmo 6:6, 9; 55:2-5, 22) Mofananamo, pamene mtima wosefukira ndi chiyamikiro unachititsa Davide kusinkhasinkha ponena za Yehova m’nthaŵi ya usiku pamene anasoŵa tulo, Yehova anadziŵa bwino lomwe zimenezo. (Salmo 63:6; yerekezerani ndi Afilipi 4:8, 9.) Tsiku lina madzulo pamene Davide anali kupenyerera mkazi wa mnansi wake akusamba, Yehova anadziŵanso zimenezo, ndipo anaona zimene zinachitika pamene Davide analola chikhumbo choipa kumuiŵalitsa Mulungu, ngakhale kuti kunali kwa nyengo yaifupi. (2 Samueli 11:2-4) Pambuyo pake, pamene mneneri Natani anatumidwa kukakambitsirana ndi Davide za kuwopsa kwa tchimo lake, Yehova sanangomva mawu otuluka pakamwa pa Davide koma anaonanso mtima wolapa m’mene mawuwo anachokera. (2 Samueli 12:1-14; Salmo 51:1, 17) Kodi zimenezo siziyenera kutichititsa kulingalira mwamphamvu ponena za kumene timapita, zimene timachita, ndi zimene zili mumtima mwathu?
8. (a) Kodi ndimotani mmene ‘mawu palilime lathu’ amayambukirira kaimidwe kathu ndi Mulungu? (b) Kodi tingagonjetse bwanji kugwiritsira ntchito lilime lathu mwanjira yoipa? (Mateyu 15:18; Luka 6:45)
8 Popeza kuti Mulungu amadziŵa kalikonse kamene timachita, siziyenera kutidabwitsa kuti iye amadziŵa mmene timagwiritsirira ntchito chiŵalo cha thupi lathu ngakhale chaching’ono chonga lilime. Mfumu Davide anazindikira zimenezi, ndipo analemba kuti: “Pakuti asanafike mawu palilime langa, taonani, Yehova, muwadziŵa onse.” (Salmo 139:4) Davide anadziŵa bwino lomwe kuti awo amene akalandiridwa monga alendo m’chihema cha Yehova akakhala anthu amene sanadyere miseche anzawo ndi amene anakana kugwiritsira ntchito lilime lawo kufalitsa mphekesera zimene zikatonzetsa bwenzi lawo. Awo amene Yehova anawayanja akakhala anthu amene analankhula chowonadi ngakhale m’mitima yawo. (Salmo 15:1-3; Miyambo 6:16-19) Palibe aliyense wa ife amene akhoza kulamulira lilime lake kotheratu, koma Davide sanaganize mwamphayi kuti palibe chimene akanachita kuti awongolere mkhalidwe wake. Iye anathera nthaŵi yochuluka akumapeka ndi kuimba masalmo otamanda Yehova. Iye anazindikiranso kuti anafunikira chithandizo ndipo anachipempherera kwa Mulungu. (Salmo 19:12-14) Kodi nafenso timafunikira chisamaliro chapemphero kaamba ka mmene timagwiritsirira ntchito lilime lathu?
9. (a) Kodi malongosoledwe a pa Salmo 139:5 amasonyeza motani mmene Mulungu amadziŵira bwino mkhalidwe wathu? (b) Kodi zimenezi zimatipatsa chidaliro cha chiyani?
9 Yehova samationa kapena kuona mkhalidwe wathu mwapang’ono chabe. Iye ali ndi chithunzi chonse. Mwakugwiritsira ntchito mzinda wozingidwa monga chitsanzo, Davide analemba kuti: “Munandizinga kumbuyo ndi kumaso.” M’nkhani ya Davide, Mulungu sanali mdani womlalira; m’malomwake, iye anali mlonda womyang’anira. “Nimunaika dzanja lanu pa ine,” anawonjezera motero Davide, akumasonyeza mphamvu ndi chitetezo cha Mulungu kaamba ka mapindu osatha kwa awo amene amamkonda. Davide anavomereza kuti: “Kudziŵa ichi kundilaka ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako.” (Salmo 139:5, 6) Mulungu amadziŵa atumiki ake bwino lomwe, ndipo kotheratu, kwakuti sitikhoza kumvetsetsa mokwanira. Koma timadziŵa zokwanira kutipatsa chidaliro chakuti Yehova amatimvetsetsadi ndi kuti chithandizo chimene amapereka chidzakhala chabwino koposa.—Yesaya 48:17, 18.
Kulikonse Kumene Tili, Mulungu Akhoza Kutithandiza
10. Kodi malongosoledwe oonekera bwino a Salmo 139:7-12 amapereka chowonadi cholimbikitsa chotani?
10 Akumaona nkhaŵa yachikondi ya Yehova mwanjira ina, wamasalmoyo akupitiriza kuti: “Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathaŵira kuti kuzembera nkhope yanu?” Iye analibe chikhumbo cha kuthaŵa pamaso pa Yehova; m’malomwake, anadziŵa kuti kulikonse kumene akanakhala, Yehova akadziŵa ndipo, mwa mzimu wake woyera, akamthandiza. “Ndikakwera kumka kumwamba,” iye anapitiriza kutero, “muli komweko; kapena ndikadziyalira ku [Sheol, NW], taonani, muli komweko. Ndikadzitengera mapiko a mbanda kucha, ndi kukhala kumalekezero a nyanja; kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku; ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uŵala ngati usana: Mdima ukunga kuunika.” (Salmo 139:7-12) Kulibe malo amene tingapiteko, palibe mkhalidwe umene tingayang’anizane nawo, umene Yehova sangaone kapena kumene mzimu wake ungalephere kufikako ndi kutithandiza.
11, 12. (a) Ngakhale kuti Yona anali ataiŵala zimenezo kwakanthaŵi, kodi mphamvu ya Yehova ya kuona ndi kuthandiza inasonyezedwa motani m’chochitika cha Yona? (b) Kodi chokumana nacho cha Yona chiyenera kutipindulitsa motani?
11 Panthaŵi ina mneneri Yona anaiŵala zimenezo. Yehova anali atamtuma kukalalikira kwa anthu a ku Nineve. Pachifukwa china iye analingalira kuti sakakwanitsa kuchita ntchito imeneyo. Mwinamwake chifukwa cha kuopa mbiri yowopsa ya Asuri, Yona anachita mantha kukatumikira m’Nineve. Motero anayesa kubisala. Atafika padoko la Yopa, analipirira ulendo m’chombo chopita ku Tarisi (wolingaliridwa mofala kukhala mu Spain, wokhala pamtunda wa makilomita oposa 3,500 kumadzulo kwa Nineve). Komabe, Yehova amamuona akukwera chombo nakagona kunsi m’malo oika katundu. Mulungu anadziŵanso kumene Yona anali pambuyo poponyedwa m’nyanja, ndipo Yehova anamva Yona pamene analonjeza ali m’mimba mwa chinsomba kuti akakwaniritsa choŵinda chake. Atabwezeretsedwa kumtunda, Yona anapatsidwanso mpata wakukwaniritsa ntchito yakeyo.—Yona 1:3, 17; 2:1–3:4.
12 Kukanakhala bwino koposa chotani nanga ngati kuyambira poyamba penipenipo, Yona anadalira mzimu wa Yehova kuti ukamthandiza kukwaniritsa ntchito yake! Komabe pambuyo pake, Yona modzichepetsa analemba chokumana nacho chake, ndipo cholembedwa chimenecho chathandiza anthu ambiri chiyambire pamenepo kusonyeza chidaliro mwa Yehova chimene chinaoneka kukhala chovuta kwambiri kwa Yona kukhala nacho.—Aroma 15:4.
13. (a) Kodi ndintchito yotani imene Eliya anaikwaniritsa mokhulupirika asanathaŵe Mfumukazi Yezebeli? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova anathandizira Eliya ngakhale pamene anakafuna kobisala kunja kwa dziko la Israyeli?
13 Chokumana nacho cha Eliya chinali chosiyanapo. Iye mokhulupirika anali atapereka chilengezo cha Yehova chakuti Israyeli akakanthidwa ndi chilala monga chilango cha machimo awo. (1 Mafumu 16:30-33; 17:1) Iye anali atachilikiza kulambira kowona molimba mtima mumkangano wa pakati pa Yehova ndi Baala pa phiri la Karimeli. Ndipo anatsiriziratu kupha aneneri 450 a Baala m’chigwa cha Kisoni. Koma pamene Mfumukazi Yezebeli mwaukali analumbira kuti Eliya aphedwe, Eliya anathaŵa kuchoka m’dzikomo. (1 Mafumu 18:18-40; 19:1-4) Kodi Yehova anali naye kumthandiza m’nthaŵi zovuta zimenezo? Ndithudi. Ngati Eliya akanakwera phiri lalitali, monga ngati nkumwamba; ngati akanabisala m’phanga pansi panthaka, monga ngati ndi mu Sheol; ngati akanathaŵira kuchisumbu chakutali ndi liŵiro longa la kuunika kwa mbandakucha koŵalira padziko lapansi—dzanja la Yehova likakhala komweko kumlimbikitsa ndi kumtsogolera. (Yerekezerani ndi Aroma 8:38, 39.) Ndipo Yehova anachilikiza Eliya osati ndi chakudya chokha cha paulendo wake komanso mwa zisonyezero zozizwitsa za mphamvu Yake yogwira ntchito. Motero, atalimbikitsidwa, Eliya anayamba ntchito yake yauneneri yotsatira.—1 Mafumu 19:5-18.
14. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kolakwa kuganiza kuti Mulungu ali paliponse? (b) Kodi Yehova wachilikiza mwachikondi atumiki ake m’nthaŵi zamakono pansi pa mikhalidwe yotani? (c) Kodi zili motani kuti ngakhale ngati tikanakhala m’Sheol, Mulungu akakhala komweko?
14 Mawu aulosi a pa Salmo 139:7-12 samatanthauza kuti Mulungu ali paliponse, kuti iye mwiniyo amakhala alipodi pamalo alionse panthaŵi iliyonse. Malemba amasonyeza bwino lomwe zosiyana ndi zimenezo. (Deuteronomo 26:15; Ahebri 9:24) Komabe, atumiki ake sali osafikirika ndi iye. Zimenezo nzowona ponena za awo amene magawo awo ateokratiki awapereka kumalo akutali. Zinalinso zowona kwa Mboni zokhulupirika m’misasa yachibalo ya Nazi mkati mwa Nkhondo Yadziko II, ndiponso zinali zowona kwa amishonale amene anabindikiritsidwa mu China kumapeto kwa ma 1950 ndi kuchiyambi kwa ma 1960. Zinali zowona kwa abale ndi alongo athu okondedwa m’dziko lina Pakati pa Afirika amene anathaŵa midzi yawo mobwerezabwereza, ndipo ngakhale kutuluka m’dzikolo. Ngati kwakhala kofunikira, Yehova akhoza kufika mu Sheol mwenimwenimo, manda wamba, ndi kutulutsa okhulupirika mwachiukiriro.—Yobu 14:13-15; Luka 20:37, 38.
Uyo Amene Amatimvetsetsadi
15. (a) Kodi Yehova anayamba liti kuyang’anira kukula kwathu? (b) Kodi kuya kwa chidziŵitso cha Mulungu pa ife kunasonyezedwa motani ndi wamasalmo mwakutchula impso?
15 Mwakuuziridwa, wamasalmo akumveketsa mfundo yakuti Mulungu amatidziŵa ngakhale tisanabadwe, akumati: “Pakuti inu munalenga impso zanga; [munanditchinga m’mimba mwa amayi, NW]. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.” (Salmo 139:13, 14) Kugwirizana kwa majini ochokera kwa atate ndi amayi athu panthaŵi ya kutenga pathupi kumapanga dongosolo limene limasonkhezera kwambiri kukhoza kwathu kwakuthupi ndi kwamaganizo. Mulungu amamvetsetsa kukhoza kumeneko. M’salmo limeneli, impso zikutchulidwa mwapadera, zimene kaŵirikaŵiri zimagwiritsiridwa ntchito m’Malemba kutanthauza mikhalidwe ya mkati mwa munthu.a (Salmo 7:9; Yeremiya 17:10) Yehova amadziŵa zonsezi ponena za ife kuyambira tisanabadwe. Alinso iye amene mwachikondi analinganiza thupi la munthu mwanjira yakuti dzira lopatsidwa mphamvu ya moyo m’mimba mwa amayi litulutse chotetezera chimene ‘chimatchinga’ mluza ndi kuutetezera pamene ukukula.
16. (a) Kodi lemba la Salmo 139:15, 16 limagogomezera motani mphamvu ya Mulungu yakuona ngakhale zobisika? (b) Kodi nchifukwa ninji zimenezi ziyenera kutilimbikitsa?
16 Ndiyeno, akumagogomezera mphamvu ya Mulungu yoona ngakhale zobisika, wamasalmo akuwonjezera kuti: “Thupi langa silinabisikira inu popangidwa ine mobisika, powombedwa ine monga m’munsi mwake mwa dziko lapansi [mwachionekere ameneŵa ali mawu andakatulo otanthauza m’mimba mwa amake koma onenanso za kulengedwa kwa Adamu kuchokera kufumbi]. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziŵalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe [ziŵalo za thupi], pakalibe [chiŵalo] chimodzi cha izo.” (Salmo 139:15, 16) Nzosakaikiritsa konse zimenezo—kaya ngati anthu anzathu amatimvetsetsa kapena ayi, Yehova amatero. Kodi zimenezo ziyenera kutiyambukira motani?
17. Pamene tiona ntchito za Mulungu kukhala zodabwitsa, kodi zimenezi zimatisonkhezera kuchitanji?
17 Wolemba Salmo 139 anavomereza kuti ntchito za Mulungu zimene iye anali kulemba zinali zabwino koposa. Kodi nanunso mumalingalira motero? Chinthu chabwino koposa chimapangitsa munthu kulingalira mwakuya kapena kumchititsa chidwi kwambiri. Mwachionekere ndimmene mumaonera ntchito za Yehova za chilengedwe chakuthupi. (Yerekezerani ndi Salmo 8:3, 4, 9.) Kodi mumakhalanso ndi malingaliro oterowo pazimene wachita m’kukhazikitsa Ufumu Waumesiya, pazimene akuchita m’kupangitsa mbiri yabwino kulalikidwa padziko lonse lapansi, ndi ponena za mmene Mawu ake amasinthira makhalidwe a anthu?—Yerekezerani ndi 1 Petro 1:10-12.
18. Ngati tiona ntchito za Mulungu kukhala zochititsa mantha, kodi zidzatiyambukira motani?
18 Kodi zimateronso kwa inu kuti kusinkhasinkha pantchito za Mulungu kumakuchititsani mantha, kudzutsa mantha aulemu mwa inu, amene amakusonkhezerani maganizo mwamphamvu, amene amayambukira kwambiri umunthu wanu ndi mmene mumakhalira ndi moyo? (Yerekezerani ndi Salmo 66:5.) Ngati nditero, mtima wanu udzakusonkhezerani kuthokoza Yehova, kumtamanda, kupeza mipata yakuuza ena ponena za chifuno chake ndi zinthu zodabwitsa zimene wasungira amene amamkonda.—Salmo 145:1-3.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Insight on the Scriptures, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Voliyumu 2, tsamba 150.
Kodi Munganenenji?
◻ Kodi kudziŵa kwathu kuti “Yehova ndiye Mulungu” kumatithandiza motani kumtumikira ndi chisangalalo?
◻ Kodi miyoyo yathu iyenera kusonkhezeredwa motani podziŵa kuti Mulungu amadziŵa kalikonse kamene timachita?
◻ Kodi nchifukwa ninji mfundo yakuti Mulungu amationa nthaŵi iliyonse ili yolimbikitsa?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu ali wokhoza kutimvetsetsa mwanjira zimene munthu aliyense sangatero?
◻ Kodi nchifukwa ninji phunziro longa limeneli limatipangitsa kufuna kuthokoza Yehova?