Moyo wa Pambuyo pa Imfa—Kodi Baibulo Limanenapo Chiyani?
“Ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”—GENESIS 3:19.
1, 2. (a) Kodi pali maganizo osiyana otani ponena za moyo wa pambuyo pa imfa? (b) Kodi tifunikira kupenda chiyani kuti tidziŵe zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za moyo?
“CHIKHULUPIRIRO chakuti kuli kuzunzika kwamuyaya n’chosagwirizana ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu amakonda zolengedwa. . . . Kukhulupirira kuti moyo [ena amati mzimu] wa munthu umakalangidwa kwamuyaya kaamba ka zochimwa zochitidwa pazaka zoŵerengeka, popanda kuupatsa mpata woti uwongolere zochimwazo kuli kosamveka,” anatero wafilosofi wina wachihindu wotchedwa Nikhilananda.
2 Mofanana ndi Nikhilananda, anthu ambiri lerolino amakayikira chiphunzitso chakuti kuli chizunzo chamuyaya. Mofananamo, ena zimawavuta kuti amvetse ziphunzitso zakuti munthu angafikire moyo wa ku Nivana kapena kukhala mbali ya chilengedwe chotizinga chachikhalire. Ngakhale pakati pa anthu amene amakhulupirira Baibulo, pali maganizo osiyanasiyana ponena za chimene moyo uli ndi chimene chimauchitikira tikamwalira. Koma kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani ponena za moyo? Kuti tipeze mayankho, m’pofunika kuti tipende tanthauzo la mawu a Chihebri ndi Chigiriki amene atembenuzidwa “moyo” m’Baibulo.
Moyo Malinga n’Kunena kwa Baibulo
3. (a) Ndi liwu liti lotembenuzidwa “moyo” m’Malemba Achihebri, ndipo tanthauzo lake lenileni n’chiyani? (b) Kodi Genesis 2:7 amatsimikiza motani kuti liwu lakuti “moyo” lingatanthauze munthu wathunthu?
3 Liwu lachihebri lotembenuzidwa “moyo” ndi neʹphesh, ndipo limapezeka nthaŵi pafupifupi 754 m’Malemba Achihebri. Kodi neʹphesh amatanthauza chiyani? Malinga n’kunena kwa The Dictionary of Bible and Religion, liwuli “kaŵirikaŵiri limatanthauza thunthu lonse la chinthu chamoyo, chamoyo chonsecho pachokha.” Ganizo limeneli timalipeza pa Genesis 2:7, pamene Baibulo likulongosola moyo kuti: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” Onani kuti munthu woyambayo ‘anakhala’ wamoyo. Ndiko kuti, Adamu sanakhale ndi mbali ina m’kati mwake yotchedwa moyo; koma iyeyo ndiye anakhala moyo—monga mmene wina amatchedwera dokotala akakhala dokotala. Pamenepo, ndiye kuti liwu lakuti “moyo,” panopo likutanthauza munthu yenseyo wathunthu.
4. Ndi liwu liti limene latembenuzidwa “moyo” m’Malemba Achigiriki, ndipo tanthauzo lenileni la liwulo n’chiyani?
4 Liwu lotembenuzidwa “moyo” (psy·kheʹ) limapezeka kwa nthaŵi zoposa zana limodzi m’Malemba Achigiriki Achikristu. Mofanana ndi neʹphesh liwuli kaŵirikaŵiri limatanthauza munthu yense wathunthu. Mwachitsanzo, taganizirani za mawu aŵa: “Moyo wanga wavutika.” (Yohane 12:27) “Panadza mantha pa anthu onse [“miyoyo yonse”, NW].” (Machitidwe 2:43) “Anthu onse [“miyoyo yonse”, NW] amvere maulamuliro aakulu.” (Aroma 13:1) “Limbikitsani amantha mtima [“miyoyo yopsinjika,” NW].” (1 Atesalonika 5:14) “Oŵerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi.” (1 Petro 3:20) Mwachionekere, psy·kheʹ, mofanana ndi neʹphesh, imatanthauza munthu yense. Malinga n’kunena kwa katswiri wina wa maphunziro Nigel Turner, liwulo “limatanthauza chimene chili munthu, munthu mwiniyo, thupi lokhala ndi rûaḥ [mzimu] umene Mulungu anauziramo. . . . Chigogomezo chili pa thunthu la chinthu.”
5. Kodi nyamanso ndi miyoyo? Fotokozani.
5 Chosangalatsanso n’chakuti, liwu lakuti “moyo” m’Baibulo silimangotanthauza anthu okha, komanso ndi nyama zomwe. Mwachitsanzo, polongosola zolengedwa za m’nyanja, Genesis 1:20 amanena kuti Mulungu analamula kuti: “Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda.” Ndipo patsiku lachiŵiri lakulenga, Mulungu anati: “Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yawo, ng’ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yawo.”—Genesis 1:24; yerekezani ndi Levitiko 24:17, 18.
6. Kodi tinganenenji za mmene Baibulo limagwiritsira ntchito liwu lakuti “moyo”?
6 Chotero, liwu lakuti “moyo” m’Baibulo limatanthauza munthu kapena nyama kapena umoyo umene munthu kapena nyama imasangalala nawo. (Onani bokosi pamwambapo.) Baibulo limafotokoza moyo m’njira yosavuta, yosasintha, yosacholoŵanitsidwa ndi mafilosofi ovuta ndi zikhulupiriro za anthu. Pokhala zili motero, funso limene limafika mwamsanga n’lakuti, Malinga n’kunena kwa Baibulo, kodi n’chiyani chimachitika ku moyo munthu akafa?
Akufa Sazindikira Kanthu
7, 8. (a) Kodi Malemba amaunikanji ponena za mkhalidwe wa akufa? (b) Perekani zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza kuti moyo ukhoza kufa.
7 Mkhalidwe wa akufa umamveketsedwa bwino pa Mlaliki 9:5, 10, pamene timaŵerenga kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda.” Choncho, imfa ndi kusakhalako. Wamasalmo analemba kuti munthu akafa, “abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:4) Akufa sazindikira kanthu, sachita china chilichonse.
8 Popereka chiweruzo kwa Adamu, Mulungu anati: “Ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Mulungu asanam’lenge Adamu kuchokera ku fumbi lapansi ndi kum’patsa moyo, Adamu kunalibe. Atafa, iye anabwerera kumkhalidwe womwewo. Chilango chake chinali imfa—osati kusamutsidwira ku malo ena. Nangano chinachitika ku moyo wake n’chiyani? Pakuti m’Baibulo liwu lakuti “moyo” kaŵirikaŵiri limangotanthauza munthu, pamene tinena kuti Adamu anafa, timatanthauza kuti moyo wotchedwa Adamu unafa. Zimenezi zingamveke zachilendo kwa munthu wokhulupirira kuti moyo sufa. Komabe, Baibulo limanena kuti: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4) Levitiko 21:1 amanena za “wakufa” (“mtembo,” The Jerusalem Bible). Ndipo Anaziri anauzidwa kusayandikira “mtembo” (“thupi lakufa,” Lamsa).—Numeri 6:6.
9. Kodi Baibulo limatanthauzanji pamene limati “potuluka moyo” wa Rakele?
9 Nanga bwanji za mawu a pa Genesis 35:18 onena za imfa yomvetsa chisoni ya Rakele, imene inachitika pobereka mwana wake wachiŵiri wamwamuna? Pamenepo timaŵerenga kuti: “Ndipo pakutsirizika iye [“potuluka moyo wake,” NW] pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini.” Kodi ndime imeneyi ikutanthauza kuti Rakele anali ndi chinthu china m’kati mwake chimene chinatuluka pa imfa yake? Kutalitali. Kumbukirani, liwu lakuti “moyo” likhoza kutanthauzanso umoyo umene munthu ali nawo. Choncho m’chochitika chimenechi “moyo” wa Rakele unangotanthauza “umoyo wake.” Ndicho chifukwa chake mabaibulo ena, m’malo monena kuti “potuluka moyo wake,” amati “umoyo wake unatsirizika” (Knox), “anapuma komalizira” (JB), ndi kuti “umoyo wake unam’chokera” (Bible in Basic English). Sakusonyeza kuti mbali inayake yosadziŵika bwino ya Rakele inapitirizabe kukhala yamoyo iye atamwalira.
10. Kodi moyo wa mwana wa mkazi wamasiye ‘unabwerera motani mwa iye’?
10 N’chimodzimodzi ndi kuukitsidwa kwa mwana wa mkazi wamasiye, wosimbidwa pa 1 Mafumu chaputala 17. Pa vesi 22, timaŵerenga kuti pamene Eliya anali kupempherera mnyamatayo, “Yehova anamva mawu a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unaloŵanso mwa iye, nakhalanso moyo.” Apanso, liwu lakuti “moyo” likutanthauza “umoyo.” N’chifukwa chake New American Standard Bible imanena kuti: “Umoyo wa mwanayo unabwereranso kwa iye ndipo anauka.” Inde, chimene chinabwereranso kwa mnyamatayo unali umoyo, osati mbali inayake imene ena amaitcha mzimu ayi. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Eliya ananena kwa mayi wa mnyamatayo kuti: “Taona, mwana wako [munthu yenseyo] ali moyo.”—1 Mafumu 17:23.
Bwanji Nanga za Mzimu?
11. N’chifukwa chiyani liwu lakuti “mzimu” silitanthauza mbali inayake imene imalekana ndi thupi pa imfa nipitiriza kukhala ndi moyo?
11 Baibulo limati munthu akamwalira, “mpweya [“mzimu,” NW] wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake.” (Salmo 146:4) Kodi zimenezi zimatanthuza kuti munthu akamwalira, mzimu umatuluka m’thupi ndi kukhalabe ndi moyo? Zimenezo sizingatheke, chifukwa wamasalmo akupitiriza kunena kuti: “Tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika” (“amasiyiratu kuganiza,” The New English Bible). Nangano pamenepa, mzimu n’chiyani, ndipo ndi motani mmene ‘umatulukira’ mwa munthu pamene amwalira?
12. Kodi mawu a Chihebri ndi Chigiriki otembenuzidwa “mzimu” m’Baibulo amatanthauzanji?
12 M’Baibulo mawu otembenuzidwa “mzimu” (Chihebri, ruʹach; Chigiriki, pneuʹma) kwenikweni amatanthauza “mpweya.” Choncho, m’malo monena kuti “mzimu wake utuluka,” Baibulo lotembenuzidwa ndi R.A. Knox limanena kuti “mpweya uchoka m’thupi mwake.” (Salmo 145:4) Koma liwu lakuti “mzimu” limatanthauza zoposa kupuma chabe. Mwachitsanzo, pofotokoza kuwonongedwa kwa miyoyo ya anthu ndi nyama panthaŵi ya Chigumula cha padziko lonse, Genesis 7:22 amati: “Zonse zimene m’mphuno zawo munali mpweya wa mzimu [Chihebri ruʹach] wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa.” Choncho “mzimu” ukhoza kutanthauza mphamvu ya moyo imene imagwira ntchito m’zamoyo zonse, anthu ndi nyama zomwe, ndipo umenewo umachirikizidwa ndi kupuma.
13. Kodi mzimu umabwerera motani kwa Mulungu munthu akamwalira?
13 Nanga tsopano Mlaliki 12:7 amatanthauzanji ponena kuti munthu akafa, ‘mzimu umabwerera kwa Mulungu amene anaupereka’? Kodi amatanthauza kuti mzimuwo umakwera ndi kudutsa m’mlengalenga mpaka kukafika kwa Mulungu? Satanthauza zimenezo m’pang’ono pomwe. Popeza kuti mzimu ndiwo mphamvu ya moyo, ‘umabwerera kwa Mulungu’ m’lingaliro lakuti chiyembekezo chilichonse cha moyo wam’tsogolo ponena za munthuyo chimatsala m’manja mwa Mulungu basi. Mulungu yekha ndiye angabwezeretse mzimuwo, kapena mphamvu ya moyo, kubwezeretsa munthuyo ku moyo. (Salmo 104:30) Koma kodi Mulungu ali ndi chifuno chochita zimenezo?
“Iye Adzauka”
14. Kodi Yesu ananenanji komanso anachita chiyani pofuna kutonthoza alongo a Lazaro atatayikidwa mlongo wawoyo?
14 M’tauni yaing’ono ya Betaniya, pafupifupi makilomita atatu kum’maŵa kwa Yerusalemu, Mariya ndi Marita anali kulira maliro a imfa yadzidzidzi ya mlongo wawo, Lazaro. Yesu anamva nawo chisoni, chifukwa ankam’konda kwambiri Lazaro pamodzi ndi alongo akewo. Kodi Yesu akanawatonthoza motani alongowo? Si mwa kuwauza zinthu zovuta kumvetsa, koma mwa kuwauza choonadi. Yesu anangoti: “Mlongo wako adzauka.” Kenako Yesu anapita kumandako, nakamuukitsa Lazaro—kubwezeretsa moyo kwa munthu wakufa masiku anayi!—Yohane 11:18-23, 38-44.
15. Kodi Marita anayankha motani pazimene Yesu ananena ndi kuchita?
15 Kodi Marita anadabwa pakumva mawu a Yesu akuti Lazaro “adzauka”? Mwachionekere sanadabwe nawo, chifukwa poyankha anati: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” Iye anali kale ndi chikhulupiriro cha kuuka. Ndiyeno Yesu anati kwa iye: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” (Yohane 11:23-25) Chozizwitsa chobwezeretsa Lazaro ku moyo chinalimbikitsa chikhulupiriro chake ndi kupangitsanso ena kukhulupirira. (Yohane 11:45) Koma kodi liwu lakuti “chiukiriro” kwenikweni limatanthauza chiyani?
16. Kodi liwu lakuti “chiukiriro” limatanthauzanji?
16 Liwulo “chiukiriro” latembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki lakuti a·naʹsta·sis, limene kwenikweni limatanthauza “kunyamukanso.” Ahebri otembenuza kuchokera m’Chigiriki atembenuza liwu lakuti a·naʹsta·sis ndi liwu lotanthauza “kuuka kwa akufa” (Chihebri, techi·yathʹ ham·me·thimʹ).a Choncho, chiukiriro chimaphatikizapo kuutsa munthu kuchokera ku mkhalidwe wopanda moyo wa imfa—kubwezeretsa umoyo wa munthu.
17. (a) N’chifukwa chiyani kuukitsa anthu sikudzakhala vuto kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu? (b) Kodi Yesu anapereka lonjezo lotani ponena za aja ali m’manda achikumbukiro?
17 Pokhala mwininzeru zonse ndi wachikumbumtima changwiro, Yehova Mulungu akhoza kuukitsa munthu mosavuta. Kukumbukira moyo wa akufawo—mikhalidwe ya umunthu wawo, mbiri yawo, ndi mbali zina zonse za chikhalidwe chawo—kwa iye si nkhani ayi. (Yobu 12:13; yerekezani ndi Yesaya 40:26.) Ndiponso, monga momwe chochitika cha Lazaro chimasonyezera, Yesu Kristu ali wofunitsitsa komanso wokhoza kuukitsa akufa. (Yerekezani ndi Luka 7:11-17; 8:40-56) Ndi iko komwe, Yesu Kristu anati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake [a Yesu], nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Inde, Yesu Kristu analonjeza kuti onse ali m’chikumbumtima cha Yehova adzaukitsidwa. Mwachionekere, malinga n’kunena kwa Baibulo, moyo umafa, ndipo mankhwala a imfa ndi kuukitsidwa. Komatu anthu amene akhalapo ndi moyo ndi kumwalira ndi mamiliyonimamiliyoni. Kodi ndayani pakati pa iwo amene ali m’chikumbumtima cha Mulungu?
18. Kodi ndani adzaukitsidwa?
18 Aja amene anatumikira Yehova m’njira yachilungamo ndiwo adzaukitsidwa. Komabe, anthu ena mamiliyoni ambiri afa popanda kusonyeza kuti angagwirizane ndi miyezo yolungama ya Yehova kapena ayi. Kumakhala koti mwina iwo sanadziŵe zofuna za Yehova kapena sanapeze nthaŵi yokwanira yoti asinthe miyoyo yawo. Enawonso ali m’chikumbumtima cha Mulungu ndipo adzaukitsidwa, pakuti Baibulo limati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15.
19. (a) Ndi masomphenya otani amene mtumwi Yohane anaona ponena za chiukiriro? (b) Kodi n’chiyani ‘chikuponyedwa m’nyanja yamoto,’ ndipo mawu amenewo amatanthauza chiyani?
19 Mtumwi Yohane anaona masomphenya ochititsa chidwi a anthu oukitsidwa ataimirira pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Polongosola zimenezo, iye analemba kuti: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali mmenemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiŵiri, ndiyo nyanja yamoto.” (Chivumbulutso 20:12-14) Tangoganizani tanthauzo la zimenezo! Akufa onse omwe ali m’chikumbumtima cha Mulungu adzamasulidwa ku Hade, kapena Shilo, manda a anthu onse. (Salmo 16:10; Machitidwe 2:31) Ndiyeno “imfa ndi Hade” zidzaponyedwa mu imene akuti “nyanja yamoto,” yophiphiritsa chiwonongeko chotheratu. Manda a anthu onse sadzakhalaponso.
Chiyembekezo Chapadera!
20. Kodi mamiliyoni a anthu amene tsopano ngakufa poukitsidwa adzapeza mikhalidwe yotani?
20 Pamene mamiliyoni aukitsidwa, sadzafikira padziko lapululu. (Yesaya 45:18) Iwo adzauka ndi kupeza malo okongoletsedwa bwino komanso nyumba, zovala, ndi chakudya chochuluka zitakonzedwera iwo. (Salmo 67:6; 72:16; Yesaya 65:21, 22) Nanga ndani adzakonzekera zonsezo? Mwachionekere, anthu adzayamba kukhala m’dziko latsopano chiukiriro cha padziko lapansi chisanayambe. Koma kodi ndani amenewo?
21, 22. Kodi awo okhala mu “masiku otsiriza” ali ndi chiyembekezo chotani chapadera?
21 Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumasonyeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo ili la zinthu.b (2 Timoteo 3:1) Posachedwa pompa, Yehova Mulungu adzaloŵerera pankhani za anthu ndipo adzasesa kuipa konse padziko lapansi. (Salmo 37:10, 11; Miyambo 2:21, 22) Panthaŵiyo, n’chiyani chidzachitika kwa aja amene akutumikira Mulungu mokhulupirika?
22 Yehova sadzawononga olungama pamodzi ndi oipa. (Salmo 145:20) Sanayambe wachitapo chinthu choterocho, ndipo sadzachichita pochotsa zoipa zonse padziko lapansi. (Yerekezani ndi Genesis 18:22, 23, 26.) Ndi iko komwe, buku lomalizira la m’Baibulo limalankhula za “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” akutuluka “m’chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:9-14) Inde, namtindi wa anthu adzapulumuka chisautso chachikulu mmene mudzathere dziko loipa lilipoli, ndipo adzaloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Mmenemo, mtundu wa anthu omvera adzapindula pamlingo wachikwanekwane ndi makonzedwe odabwitsa a Mulungu omasula mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa. (Chivumbulutso 22:1, 2) Pachifukwa chimenecho, “khamu lalikulu” silidzafunikira kulaŵa imfa. Ha, chikomerenji chiyembekezo chodabwitsa chimenecho!
Moyo Wopanda Imfa
23, 24. Kodi muyenera kuchitanji ngati mukufuna kudzasangalala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi?
23 Kodi tikhoza kudalira chiyembekezo chodabwitsa chimenecho? Kulekeranji! Yesu Kristu mwiniyo anasonyeza kuti kukakhala nthaŵi pamene anthu adzakhala ndi moyo osafa. Nthaŵi pang’ono asanaukitse bwenzi lake Lazaro, Yesu anauza Marita kuti: “Yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.”—Yohane 11:26.
24 Kodi inuyo mukufuna kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi? Kodi mukukhumba kudzaonanso okondedwa anu? “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.” (1 Yohane 2:17) Ino ndiyo nthaŵi yoti tiphunzire chifuniro cha Mulungu nitikhale otsimikiza mtima kukhala moyo wathu mogwirizana nacho. Mukatero, inuyo limodzi ndi mamiliyoni ena omwe anayamba kale kuchita chifuniro cha Mulungu, mudzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso pom’pano padziko lapansi.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti liwu lakuti “chiukiriro” silipezeka m’Malemba Achihebri, chiyembekezo cha chiukiriro n’chomveketsedwa bwino pa Yobu 14:13, Danieli 12:13, ndi Hoseya 13:14.
b Onani Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 98-107.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi tanthauzo lenileni n’chiyani la mawu a m’zinenero zoyambirira otembenuzidwa “moyo”?
◻ Kodi chimachitika ku moyo pa imfa n’chiyani?
◻ Malinga n’kunena kwa Baibulo, kodi mankhwala a imfa n’chiyani?
◻ Kodi n’chiyembekezo chapadera chotani chimene okhulupirika lerolino ali nacho?
[Bokosi patsamba 15]
“Moyo” Umatanthauzanso Umoyo wa Cholengedwa
Nthaŵi zina, liwu lakuti “moyo” limatanthauza umoyo umene munthu kapena nyama ikusangalala nawo. Zimenezi sizikusintha tanthauzo la m’Baibulo lakuti moyo ndiye munthu kapena nyama. Mwachitsanzo: Timanena kuti winawake ali wamoyo, kutanthauza kuti ndi munthu wamoyo. Tinganenenso kuti iye ali ndi moyo. Mofananamo, munthu wamoyo ndi moyo umene. Komabe, pamene kuli kwakuti ndi wamoyo, “moyo” ukhozanso kunenedwa monga chinthu chimene munthu ali nacho.
Mwachitsanzo, Mulungu anauza Mose kuti: “Adafa anthu onse amene anafuna moyo wako.” Mwachionekere, adani a Mose ankafuna kuwononga moyo wake. (Eksodo 4:19; yerekezani ndi Yoswa 9:24; Miyambo 12:10.) Yesu anagwiritsa ntchito liwulo m’njira yofanana pamene anati: ‘Mwana wa munthu anadzapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28; yerekezani ndi 10:28.) Ponsepo, liwulo “moyo” limatanthauza “umoyo wa cholengedwa.”
[Zithunzi patsamba 15]
Yonseyi ndi miyoyo
[Mawu a Chithunzi]
Hummingbird: U.S. Fish and Wildlife Service, Washington, D.C./Dean Biggins
[Chithunzi patsamba 17]
Yesu anaonetsa kuti mankhwala a imfa ndi chiukiriro
[Chithunzi patsamba 18]
“Yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.”—Yohane 11:26