“Yehova Ndiye Mbusa Wanga”
“Yehova ndiye Mbusa wanga. Sindidzasowa.”—MASALMO 23:1.
1, 2. Ndi ziti zomwe zinali zina za zokwaniritsa za Davide, ndipo kodi ndi masalmo angati amene iye anapanga?
TANGOLINGALIRANI chochitika ichi: Magulu ankhondo a Afilisti akuyang’anizana ndi gulu lankhondo la Israyeli. Goliati, chimphona cha Afilisti, ali wonyoza. Mwamuna wachichepere, wokonzekeretsedwa kokha ndi legeni ndi miyala, akuthamanga kukakumana naye. Mwala wolunjitsidwa bwino ukulasa chigaza cha chimphonacho ndi kupha iye. Kodi ndani amene anali mwamuna wachichepere ameneyu? Davide, mbusa yemwe anapambana chipambano chozizwitsa chimenechi ndi thandizo la Yehova Mulungu.—1 Samueli, mutu 17.
2 M’kupita kwa nthaŵi, mwamuna wachichepere ameneyu anakhala mfumu ya Israyeli, kulamulira kwa zaka 40. Iye anali katswiri pa kuseŵera mphalasa ndipo anapanga ndakatulo zambiri pansi pa kuwuziridwa kwaumulungu. Davide analembanso masalmo okongola oposa 70 omwe ali magwero a chilimbikitso chokulira ndi chitsogozo kaamba ka anthu a Yehova lerolino. Lodziŵika kwambiri la amenewa liri Salmo 23. Bwanji osatsegula Baibulo lanu ndi kutsatira pamene tikuyamba phunziro la versi ndi versi la salmo limeneli?
Yehova, Mbusa Wachikondi
3. (a) Ndi pa zochitika ziti pamene Davide anaika pa ngozi moyo wake kuti achinjirize nkhosa zake? (b) Ndi m’lingaliro lotani mmene Yehova aliri Mbusa wathu?
3 “Yehova ndiye Mbusa wanga.” (Masalmo 23:1) Monga mbusa wozoloŵera, Davide anadziŵa mmene angatsogozere, kudyetsa ndi kutetezera nkhosa. Mwachitsanzo, iye molimba mtima anatetezera nkhosa zake kuchokera ku mkango pa chochitika chimodzi ndi chimbalangondo pa chochitika china. (1 Samueli 17:34-36) Nkhosa za Davide zinakhulupirira kotheratu mbusa wawo. Koma m’chigwirizano ndi Yehova, iye iyemwini anali nkhosa. Popeza Davide anadzimva wa chisungiko m’chisamaliro chachikondi cha Mulungu, iye akananena kuti: “Yehova ndiye Mbusa wanga.” Kodi mumasangalala ndi kudzimva kumeneku kwa chisungiko pansi pa Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu? Iye ndithudi amatsogoza, kudyetsa, ndi kutetezera alambiri ake onga nkhosa lerolino. M’kuwonjezerapo, monga akulu oikidwa m’mipingo ya Mboni za Yehova, ambusa ocheperako okhulupirika, achikondi mwachangu amasamalira kaamba ka nkhosa.—1 Petro 5:1-4.
4. Kodi ndimotani mmene mkhalidwe wathu lerolino uliri wofanana ndi uja wa Israyeli m’chipululu?
4 “Sindidzasowa.” Talingalirani mosamalitsa ponena za mawu amenewo. Chifukwa cha chisamaliro chachikondi cha Yehova, kodi simukhala ndi kudzimva kotonthoza kwa bata ndi chidaliro? Kodi mumakumbukira chimene chinachitika kwa Aisrayeli pamene iwo anayendayenda m’chipululu kwa zaka 40? Nkulekelanji, popeza Mulungu anapereka kaamba ka zosowa zawo zonse zofunikira! Chiri chofananacho lerolino. Atumiki okhulupirika a Yehova sasowa kanthu. Ambiri angaimbe mawu awa owuziridwa a Davide: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba, ndipo sindinapenya wolungama wasiidwa, kapena mbumba zake zirinkupempha chakudya.” (Masalmo 37:25) Lerolino, chakudya chauzimu chochuluka chikuperekedwa kupyolera “mwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 4:4; 24:45-47) M’kuwonjezera ku misonkhano yambiri pa mlungu, tiri ndi Baibulo, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi zofalitsidwa zina zambiri. Ngakhale m’maiko mmene ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova yaletsedwa, zopereka za chakudya chauzimu zimalandiridwabe mokhazikika. Nkhosa za Yehova sizisowa kanthu!
5. Nchifukwa ninji nkhosa za Yehova lerolino ziri za mtendere ndi za mpumulo, ndipo ndi chotulukapo chotani?
5 “Andigonetsa ku busa lamsipu.” (Masalmo 23:2) Panali busa lamsipu lalikulu kuzungulira mizinda yambiri m’Israyeli wakale. Monga mmene mbusa wachikondi panthaŵiyo anatsogolera nkhosa zake ku bwalo lamsipu wabwino, lachisungiko, choteronso Yehova amasamalira kaamba ka nkhosa zake lerolino. Akutero wamasalmo kuti: “Tiri anthu a pabusa pake.” (Masalmo 79:13; 95:7) Nkhosa zenizeni zimachita bwino pamene ziri zokhutiritsidwa ndipo ziri zokhoza kupumula m’kutentha kwa tsiku. Nkhosa za Yehova lerolino ziri zamtendere ndi za mpumulo chifukwa ziri ndi chidaliro mu abusa achikulire—oyang’anira ophunzitsidwa mu mpingo ndi m’madera. Monga chotulukapo chake, nkhosa zauzimu zikuwonjezereka. Anthu ambiri amene kale anali kuchitiridwa moipa ndi abusa onyenga a Babulo Wamkulu tsopano ali achimwemwe kwambiri ndi okhutiritsidwa monga nkhosa za Yehova.
6. Ndimotani mmene Yehova ‘akutitsogolera ife ku madzi odikha’?
6 “Anditsogolera ku madzi odikha.” Mu Israyeli mbusa anayenera kutsogoza nkhosa zake ku chitsime kapena mtsinje wa madzi. Koma madzi kaŵirikaŵiri anali ovuta kupeza m’nyengo zouma. Lerolino, Yehova ‘akutitsogolera ku madzi odikha’ mwakupereka madzi a chowonadi mochuluka. (Yerekezani ndi Ezekieli 34:13, 14.) Ndipo mneneri Yesaya akupereka chiitano chodzutsa maganizo ichi: “Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi.” (Yesaya 55:1) Mwa kumwa madzi auzimu amenewa, nkhosa zimapeza chirikizo kuchokera ku ziweruzo za moto zomwe zikadza pa awo “omwe sadziŵa Mulungu ndi omwe samvera mbiri yabwino.”—2 Atesalonika 1:8; Chivumbulutso 7:16, 17.
7. Ndi liti pamene chitsitsimulo chauzimu chochokera kwa Yehova chimakhala chathandizo mwapadera, ndipo ndi pansi pa mikhalidwe yotani pamene malemba olowezedwa a Baibulo angatsimikizire kukhala a phindu lapamwamba?
7 “Atsitsimutsa moyo wanga.” (Masalmo 23:3) Pamene tatopa, tiri m’mavuto, kukhumudwitsidwa, kapena kuyang’anizana ndi chitsutso chowopsya, Yehova amatsitsimutsa ife kupyolera mwa Mawu ake. Chotero, chiri chabwino kwa Akristu kuchipanga icho chizoloŵezi kuŵerenga mbali ya Baibulo tsiku lirilonse. Kodi mumachita ichi? Ena achipeza icho kukhala chothandiza kuloweza malemba ena, monga ngati Eksodo 34:6, 7 kapena Miyambo 3:5, 6. Nchifukwa ninji ichi chiri chopindulitsa? Chabwino, ngati tsoka libuka ndipo mulibe Baibulo pafupi, malingaliro otonthoza a Malemba mwamsanga angakulimbikitseni inu. Abale ambiri omwe analamuliridwa kukhala m’jere kapena misasa ya ndende chifukwa cha kuima nji kaamba ka maprinsipulo olungama atsitsimulidwa mokulira ndi kulimbikitsidwa mwa kukumbukira malemba olowezedwa. Inde, Mawu a Mulungu angapangitse “mtima kusangalala” ndipo angapangitse “maso kuwala”!—Masalmo 19:7-10.
8. Kodi chiri chopepuka kutsatira “mabande a chilungamo,” koma kuchita tero kumatsogolera ku chiyani?
8 “Anditsogolera m’mabande a chilungamo.” Mabande a chilungamo ali ovuta kuwatsatira, koma amatsogolera ku moyo. Monga mmene Yesu ananenera: “Chipata chiri chopapatiza ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo.” (Mateyu 7:14) Mtumwi Paulo analongosola lingaliro lofananalo mwakuuza ophunzira mu Lustra, Ikoniyo, ndi Antiokeya: “Tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.” Ndipo Paulo ndithudi anadziŵa chimene anali kulankhula ponena za icho. Mwamsanga chisanachitike chimenecho, iye anali ataponyedwa miyala ku Lustra ndi kusiidwa pomulingalira kuti wafa!—Machitidwe 14:19-22.
9. (a) Ndimotani mmene Mulungu ‘amatitsogozera ife m’mabande a chilungamo’? (b) Ndi mwanjira yotani mmene Masalmo 19:14 angakhalire athandizo? (c) Ndi malemba otani omwe angatithandize ife kupewa misampha ya mkhalidwe wogonana wosalamulirika?
9 Yehova ‘amatitsogolera ife m’mabande a chilungamo’ mwa kutitsogoza ndi kutilangiza ife kupyolera m’Mawu ake ndi gulu. Koma anthu ambiri amatsatira njira yaikulu ndi yotakata “yotsogolera ku chiwonongeko.” (Mateyu 7:13) Mkhalidwe woipa wofala wa kugonana ndi kufalikira kofulumira kwa mliri wa AIDS kumasonyeza kufunika kwa Akristu kupewa mayanjano oipa. (1 Akorinto 15:33) Tiyeneranso kutenga chisamaliro kuletsa malingaliro anthu enieni kuyendayenda m’ngalande zoipa. (Masalmo 19:14) Ku mapeto amenewo, lolani ife nthaŵi zonse tigwiritsire ntchito uphungu wabwino umene Mawu a Mulungu amapereka ponena za kugonana ndi mmene tingapewere misampha yambiri ya makhalidwe oipa a chisembwere.—1 Akorinto 7:2-5; Aefeso 5:5; 1 Atesalonika 4:3-8.
10. (a) Ndi thayo lotani limene Mboni za Yehova ziri nalo m’chigwirizano ndi dzina laumulungu? (b) Nchifukwa ninji anthu a kudziko kaŵirikaŵiri amatisuliza ife? (c) Ndi pansi pa mikhalidwe iti pamene Yehova adzatithandiza ife?
10 “Chifukwa cha dzina lake.” Mboni za Yehova ziri ndi thayo lolemera la kulemekeza dzina la Mulungu ndi kusabweretsa chitonzo pa ilo. (Mateyu 6:9; Eksodo 6:3; Ezekiel 38:23) Anthu ambiri a kudziko ali ofulumira kuloza chala chopatsa mlandu pa anthu a Yehova. Ngati ichi chikuchitidwa kaamba ka kaimidwe kanthu kaamba ka maprinsipulo a baibulo oterowo onga ngati uchete kapena kupatulika kwa mwazi, chikumbumtima chathu chimakhala choyera. Koma ngati icho chichitika chifukwa cha kachitidwe kolakwa, tikakhala tisakulemekeza Yehova. (Yesaya 2:4; Machitidwe 15:28, 29; 1 Petro 4:15, 16) Chotero lolani kuti tidane ndi chimene chiri choipa. (Masalmo 97:10) Ngati tiyenera kupita pansi pa chizunzo, Yehova nthaŵi zonse adzatithandiza ndi kutichinjiriza ife chifukwa cha dzina lake.
Yehova Amachinjiriza Nkhosa Zake
11. Nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi “chigwa cha mthunzi wa imfa,” ndipo kodi ichi chingatikumbutse ife za chiyani ponena za Yesu?
11 “Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi [wozama, ‘NW’] sindidzawopa choipa.” (Masalmo 23:4) Matembenuzidwe a Isaac Leeser amaŵerenga kuti: “Inde, ngakhale ndiyenda kupyola m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzawopa choipa.” Ichi chingaitanire m’maganizo mapiri ozama kapena zigwa, zomwe zimayenda kuchokera ku mapiri a Yudeya ku mbali ya kumadzulo kwa Dead Sea. Chigwa kapena dzenje, kumene zirombo zolusa zimambisala mu mthunzi ali malo owopsya kaamba ka nkhosa. Davide anapyola zambiri za zigwa zowopsya m’moyo wake, ndi imfa iri patsogolo pake. Koma popeza kuti Mulungu anali kumtsogolera iye, iye anali ndi chidaliro ndipo sanagonjere ku mantha osalamulirika. Tiyenera kukhala ndi chidaliro chofananacho mwa Yehova. Kulozera kumeneku kuti “mthunzi wozama” kungatikumbutsenso ife za ulosi wa Yesaya: “Iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.” Mateyu analozera ku ulosi umenewo ndi kuwugwiritsira ntchito kwa Yesu Kristu, akumanena kuti: “Anthu akukhala mu mdima adawona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m’malo a mthunzi wa imfa.” Motani? Kupyolera mwa ndawala yaikulu yolalikira imene Yesu anatsogoza.—Yesaya 9:2; Mateyu 4:13-16.
12. (a) Ndimotani mmene atumiki a Yehova adzizoloweretsera ku chizunzo m’maiko ambiri, ndipo ndi chotulukapo chotani? (b) Ndimotani mmene Petro analimbikitsira Akristu oyambirira ozunzidwa?
12 Davide ‘sanawopa choipa.’ Chinthu chofananacho chiri chowona ponena za atumiki a Yehova lerolino, ngakhale kuti iwo ali achilendo m’dziko loipa iri lolamuliridwa ndi Satana. (1 Yohane 5:19) Anthu ambiri m’chenicheni amawada iwo, ndipo amazunzidwa mowopsya m’maiko ena. Koma m’maiko amenewa iwo akupitirizabe kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu, ngakhale kuti osati mowonekera monga mmene iwo mwachibadwa anachitira. Iwo amadziŵa kuti Yehova ali ndi iwo ndipo adzawachirikiza iwo. (Masalmo 27:1) Kupita patsogolo kwabwino kukupangidwa m’maiko ambiri kumene ntchito ya Ufumu iyenera kuchitidwa mobisa. M’maiko oterowo, Mboni za Yehova zimafuula mawu a salmolo: “Yehova ndi wanga; sindidzawopa. Adzandichitanji munthu?” (Masalmo 118:6) Mboni zimenezi ziri mu mkhalidwe wofanana ndi uja wa Akristu oyambirira kwa amene mtumwi Petro analemba mawu olimbikitsa awa: “Ngatinso mukamva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu. Ndipo musawope pakuwawopa iwo, kapena musadere nkhaŵa.”—1 Petro 3:14.
13. (a) Ndi kusintha kosangalatsa kotani kumene kukuwoneka pa Masalmo 23:4, ndipo nchifukwa ninji? (b) Ndimotani mmene Akristu angapewere mantha awo?
13 “Pakuti inu muli ndi ine.” Chonde dziŵani nsonga yosangalatsa kwambiri m’mawu awa. Wamasalmo wouziridwayu wasintha kuchokera ku munthu wonenedwa kupita ku womvera. M’malo mwa kulankhula za Yehova monga “iye,” Davide tsopano akugwiritsira ntchito poronauni “inu.” Nchifukwa ninji? Chifukwa liri logwirizanitsa mwathithithi. Tsoka limatibweretsa ife kufupi ndi Atate wathu wachikondi, Yehova. Ife chotero timasangalala ndi unansi wathithithi ndi iye. Kupyolera mwa njira ya pemphero ndi pembedzero, tingaitane kwa iye kaamba ka chitetezero, ndipo mwakutero kulaka mantha athu.—Yerekezani ndi Zefaniya 3:12.
14. (a) Ndi zida zotani zimene abusa anali nazo m’nthaŵi ya Davide, ndipo ndimotani mmene anazigwiritsira ntchito izo? (b) Ndimotani mmene abusa a Chikristu amachinjirizira nkhosa lerolino?
14 “Chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.” Liwu la Chihebri sheʹvet, logwiritsiridwa ntchito “chibonga,” lingasonyeze ndodo ya mbusa. Zonse ziŵiri chibonga ndi ndodo zingagwiritsiridwe ntchito kaamba ka kuchinjiriza ndi kuimira kapena kusonyeza ulamuliro. Ndithudi, zida zimenezi zingagwiritsiridwe ntchito bwino m’kumenya zosakaza zonga ngati mimbulu ndi njoka. Ndodo ya mbusa ingagwiritsiridwenso ntchito kuwongolera nkhosa m’njira yabwino kapena ngakhale kubweza nkhosa kuti zisapite kufupi ndi malo amene izo zingagweremo ndi kupwetekedwa. Lerolino, Yehova akupereka abusa okhulupirika, akulu m’mipingo, omwe amachinjiriza nkhosa ku osakaza auzimu oterowo onga ngati ampatuko. Kapena akulu angafunikire kupatsa uphungu kwa awo amene akhala ofooka m’kupezeka pa misonkhano kapena kuchoka ku mkhalidwe Wachikristu.
Phwando Lolemera Pakati pa Adani
15. (a) Ndi kusintha kwatanthauzo kotani kwa fanizo kumene kukupezeka pa Masalmo 23:5? (b) Ndi nsonga zotani zimene zikusonyeza kuti anthu a Yehova ali odyetsedwa mwauzimu, m’kusiyanitsa ndi ndani?
15 “Mundiyalikira gome pamaso panga m’kuwona kwa adani anga.” (Masalmo 23:5) Pano tiri ndi kusintha kwatanthauzo kwa fanizo, kuchokera kwa mbusa kupita kwa wochereza. Monga wochereza woolowa manja, Yehova amapereka chakudya chauzimu chochuluka kupyolera m’gulu lodzozedwa la “kapolo.” (Mateyu 24:45) Ngakhale kuti tikukhala m’dziko la udani, tikudyetsedwa bwino. Nsanja ya Olonda ikufalitsidwa m’zinenero zoposa zana kotero kuti anthu okhala m’malo akutali onga ngati South Africa, Greenland, Solomon Islands, ndi India angadyetsedwe mwauzimu. Pambali pa icho mipingo chifupifupi 55,000 kuzungulira pa dziko lonse iri ndi alankhuli apoyera ophunzitsidwa bwino ndi aphunzitsi ndi malo osokhanira abwino, kuphatikizapo mazana a Nyumba za Ufumu zatsopano. Maphunziro a Baibulo a panyumba oposa 3,000,000 akutsogozedwa kuti athandize onga nkhosa. M’kusiyanitsa, awo amene ali mu Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga, amayenda ndi njala.—Yesaya 65:13.
16. (a) M’kusiyanitsa ndi mkazi wochimwa, nchiyani chimene Mfarisi wina analephera kuchita kaamba ka Yesu? (b) Ndi mtundu wanji wa mafuta umene Yehova amapereka kwa atumiki ake okhulupirika lerolino?
16 “Mwandidzoza mutu wanga mafuta.” Mu Israyeli wakale wolandira alendo wochereza anapereka mafuta kudzoza mitu ya alendo ake. Mosangalatsa, pa chochitika china Yesu anali mlendo wa m’Farisi yemwe sanadzoze munthu wa Yesu ndi mafuta kapena kupereka madzi kusambitsa mapazi ake. Panthaŵi imeneyo, mkazi wochimwa anasambika mapazi ake ndi misozi ndi kuwadzoza iwo ndi mafuta onunkhira apadera. (Luka 7:36-38, 44-46) Koma Yehova ali wochereza woolowa manja koposa! Kwa atumiki ake okhulupirika, iye akupereka “mafuta a kukondwa” auzimu. (Yesaya 61:1-3) Inde, anthu a Yehova ndithudi akusangalala lerolino.
17. (a) ‘Chikho chosefukira’ chimasonyeza chiyani? (b) Ndimotani mmene Yehova amaperekera ‘chikho chosefukira’ kaamba ka atumiki ake lerolino?
17 “Chikho changa chasefuka.” Kalembedwe kena kali kakuti: “Chikho changa chadzaza kufika pakamwa.” (Moffatt) Ichi chimasonyeza kuchuluka kwauzimu. Ngakhale kuti kumwa mopambanitsa sikukutanthauzidwa, mawu amenewa akulingalira chikho chabwino cha vinyo. Chakudya chimenechi chiri ndi zinthu zochiritsa, monga mmene chinasonyezedwera ndi uphungu wa Paulo kwa Timoteo: “Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang’ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kaŵirikaŵiri.” (1 Timoteo 5:23) M’lingaliro lauzimu, vinyo angapangitsenso mitima yathu kusangalala. (Masalmo 104:15) Atate wathu wachikondi, Yehova, moolowa manja akupereka phwando la zinthu zabwino zauzimu kaamba ka atumiki ake okhulupirika, kuphatikizapo ‘chikho chodzazidwa bwino’ cha chimwemwe.
18. (a) Ubwino ndi chifundo cha Yehova zimasangalalidwa ndi ndani, ndipo ndimotani mmene Masalmo 103:17, 18 akusonyezera ichi? (b) Ndi chiyembekezo chowala chotani chimene chiri kutsogolo kwa awo okhulupirika kwa Yehova?
18 “Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga.” (Masalmo 23:6) Ukoma uli mbali ya chipatso cha mzimu woyera wa Yehova. (Agalatiya 5:22, 23) Ukoma wa Mulungu ndi chifundo zikusangalalidwa ndi awo omwe akuyenda m’njira yake. (Masalmo 103:17, 18) Ndi chikhulupiriro champhamvu mwa Yehova, anthu ake angayang’anizane ndi chiyeso chirichonse chimene angakumanizane nacho. Iwo nthaŵi zonse ali olandira adalitso lake ndi chisamaliro chachikondi. Ndipo kukhulupirika kufika kumapeto kukatanthauza moyo wosatha m’dziko latsopano. Ndi chiyembekezo chosangalatsa chotani nanga!
19. (a) Nchiyani chikutanthauza “kukhala m’nyumba ya Yehova”? (b) Nchiyani chimene gulu la Yehova lakhazikitsa kupititsa patsogolo kulambira kowona lerolino, ndipo nchifukwa ninji zikwi za anthu odzipereka zimawonera iwo kukhala mwaŵi kutumikira pamenepo? (c) Ndi ndaninso amene ali ogamulapo kutumikira Mulungu kosatha?
19 “Ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.” M’tsiku la Davide malo opatulika a Mulungu anali likasa, popeza kachisi anali asanamangidwe. Popeza wamasalmoyo anali ndi wochereza wosangalatsa m’malingaliro, ‘kukhala m’nyumba ya Yehova’ kunatanthauza kukhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu monga mlendo Wake. (Masalmo 15:1-5) Lerolino, nyumba imeneyo ingazindikiritsidwe ndi kachisi woyera wa Yehova, makonzedwe ake kaamba ka kulambira koyera. Mfumu Solomo anapatsidwa mwaŵi wa kumanga kachisi wa zinthu zakuthupi woyambirira, wokongoletsedwa molemera ndi golide ndi kumangidwa ku ulemerero wa Yehova. Unali mwaŵi wokulira chotani nanga kutumikira pamenepo! Ngakhale kuti kachisi woteroyo kulibenso, Mulungu ali ndi gulu loyera lofunika kumlemekeza iye ndi kupititsa patsogolo kulambira koyera. Monga njira imodzi yochitira ichi, gulu la Yehova lakhazikitsa Nyumba za Beteli m’maiko ambiri. “Beteli” imatanthauza “Nyumba ya Mulungu,” ndipo zikwi za anthu odzipereka amatumikira m’malo apakati a teokratiki amenewa. Ena a amuna ndi akazi amenewa akhala akutumikira m’njira imeneyi “kwa masiku onse,” akumathera mbali yokulira ya moyo wawo mu utumiki wa pa Beteli. Mamiliyoni ena, osati ziwalo za banja la Beteli, mofananamo agamulapo kutumikira Yehova kosatha.
20. (a) Nchifukwa ninji Salmo 23 iri mbali yowonekera ya Malemba, ndipo nchiyani chimene ilo likutithandiza ife kukulitsa? (b) Ndi mwaŵi wotani umene ukuyembekeza atumiki okhulupirika a Yehova?
20 Salmo 23 liri monga mwala wa mtengo wapatali wokhala ndi mbali zambiri zomawala ndi kuwala. Ilo limakwezeka dzina la ulemerero la Atate wathu wa kumwamba wachikondi, Yehova, ndi kuvumbula mmene iye amatsogozera, kutetezera, ndi kupereka kaamba ka nkhosa zake. Monga chotulukapo chake, anthu ake ali achimwemwe, odyetsedwa bwino mwauzimu, ndipo akuwonjezeka m’chiŵerengero mofulumira, ngakhale m’maiko mmene muli chitsutso chowawa. Masalmo 23 amatithandizanso ife kukulitsa chomangira chotentha, chathithithi ndi Mlengi wathu. Ndipo pamene tiyang’ana m’mwamba modzaza ndi nyenyezi, monga mmene anachitira Davide kaŵirikaŵiri pamene anali kuyang’anira nkhosa zake, tiri oyamikira kuti Mlengi wa chilengedwe chodabwitsa chimenechi amasamalira kaamba ka ife monga Mbusa wachikondi. Mwachikondi, iye waperekanso mwaŵi wosatha m’dziko latsopano ngati tisungilira umphumphu wathu kwa iye. Chidzakhala chosangalatsa chotani nanga panthaŵiyo kukumana ndi atumiki okhulupirika oukitsidwa oterowo a Mulungu onga Davide! Ndipo udzakhala mwaŵi wotani nanga kutumikira Yehova, Mbusa Wamkulu, kwa nthaŵi zonse!
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Ndimotani mmene Yehova akutsimikizira kukhala Mbusa wathu wachikondi?
◻ Ndi kupyolera mwa chiyani mmene Mulungu ‘akutitsogozera ife m’mabande a chilungamo’?
◻ Ndimotani mmene Yehova amachinjirizira nkhosa zake?
◻ Ndi mwanjira yotani mmene Mulungu wayalira gome kaamba ka ife pakati pa adani athu?