Yehova Amawerenga ‘Tsitsi Lonse la M’mutu Mwanu’
‘Ngakhale mpheta imodzi siigwa pansi popanda Atate wanu kudziwa: komatu inu, tsitsi lonse la m’mutu mwanu amaliwerenga.’—MATEYU 10:29, 30.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani Yobu amaona kuti Mulungu wamunyanyala? (b) Kodi mawu a Yobu ankatanthauza kuti iye anali atatembenukira Yehova? Longosolani.
“NDIFUULA kwa Inu [Mulungu], koma simundiyankha; ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera. Mwasandulika kundichitira nkhalwe; ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.” Munthu amene ananena mawu amenewa anali ndi nkhawa yadzaoneni, ndipotu mpake kuti anali ndi nkhawa yoteroyo. Moyo wake unali utasokonezekeratu, ana ake anali atafa pangozi yosadziwika bwino, ndipo tsopano iyeyu anali atadwala matenda ozunza. Munthuyu dzina lake anali Yobu, ndipo nkhani yake yoliritsa inalembedwa m’Baibulo kuti tiphunzirepo kanthu.—Yobu 30:20, 21.
2 Mawu a Yobu angaoneke ngati kuti iye anali atatembenukira Mulungu, koma sizinali choncho ayi. Kwenikweni Yobu anali kungofotokoza masautso a mumtima mwake. (Yobu 6:2, 3) Iye samadziwa kuti Satana ndiye anayambitsa mavuto ake, motero anaganiza molakwa kuti Mulungu anali atamunyanyala. Panthawi ina Yobu anafika pouza Yehova kuti: “Mubisiranji nkhope yanu, ndi kundiyesa mdani wanu?”a—Yobu 13:24.
3. Kodi tikakumana ndi mavuto, ndi maganizo otani amene angatibwerere?
3 Masiku ano, anthu a Yehova ambiri amakumana ndi mavuto ochita kusowa popumira chifukwa cha nkhondo, kusokonekera kwa zinthu pa ndale kapenanso zinthu zina m’dziko, masoka achilengedwe, ukalamba, matenda, umphawi wadzaoneni, ndiponso malamulo a boma owaletsa kulambira. N’kutheka kuti inunso mukukumana ndi mavuto enaake. Nthawi zina mwina mungamaganize kuti Yehova akukuzembani. Inde, mumawadziwa bwino mawu a pa Yohane 3:16 akuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha.” Komabe, mukamavutika popanda chinachake chokulimbitsani mtima, mungathe kumadzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amandikondadi ineyo? Kodi akuona mavuto amene ndikukumana nawo? Kodi ineyo pandekha amandiganiziradi?’
4. Kodi Paulo anayenera kupirira vuto lotani losatherapo, ndipo kodi vuto langati limeneli lingatikhudze motani ifeyo?
4 Taganizirani zimene zinamuchitikira mtumwi Paulo. Iye analemba kuti: “Kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze.” Paulo anapitiriza kuti: “Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.” Yehova anamva pemphero la Paulo. Komabe, anauza Paulo kuti sathetsa vuto lakelo m’njira yozizwitsa. M’malo mwake, Paulo anayenera kudalira mphamvu za Mulungu kuti ndizo zimuthandize kuti alimbane ndi “munga m’thupi” mwake.b (2 Akorinto 12:7-9) Monga Paulo, n’kutheka kuti nanunso muli ndi vuto linalake limene silikukutherani. Ndiye mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi popeza zikuoneka kuti Yehova sanachitepo kanthu pa vuto langali ndiye kuti sakudziwa za vutoli kapena mwina sandiganizira?’ Ayi, sichoncho ngakhale pang’ono. Zimene Yesu anauza ophunzira ake atangowasankha kumene, zimagogomezera mfundo yakuti Yehova amaganizira kwambiri mtumiki wake aliyense wokhulupirika. Tiyeni tione mmene mawu ake angatilimbikitsire masiku ano.
N’chifukwa Chiyani Anati “Musamaopa”?
5, 6. (a) Kodi Yesu anathandiza bwanji atumwi kuti asachite mantha akamaganizira zimene zidzachitike m’tsogolo? (b) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti sanali kukayikira kuti Yehova amamuganizira?
5 Yesu anapatsa atumwi mphamvu zapadera, kuphatikizapo “mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.” Komabe, izi sizinasonyeze kuti atumwiwo sazikumana ndi mavuto aliwonse. Ayi ndithu, chifukwatu Yesu analongosola mwatsatanetsatane zovuta zina zimene iwo adzakumane nazo. Komabe, anawalimbikitsa kuti: “Musamawopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muwope Iye, wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.”—Mateyu 10:1, 16-22, 28.
6 Pofuna kuthandiza atumwi ake kumvetsetsa chifukwa chimene sayenera kuchitira mantha, Yesu anapereka mafanizo awiri. Iye anawauza kuti: ‘Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziwa]: komatu inu, tsitsi lonse la m’mutu mwanu amaliwerenga. Chifukwa chake musamawopa; inu mupambana mpheta zambiri.’ (Mateyu 10:29-31) Onani kuti malingana ndi mawu a Yesuwa, kuti tisachite mantha pa mavuto m’pofunika kuti tisamakayikire kuti Yehova amatiganizira ifeyo patokha. Zikuoneka kuti mtumwi Paulo sankakayikira mfundo imeneyi. Iye analemba kuti: “Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani? Iye amene sanatimana Mwana wake wa iye yekha, koma anam’pereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?” (Aroma 8:31, 32) Ngakhale mutakumana ndi mavuto aakulu motani, inunso panokha musamakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova amakuganizirani panthawi yonse imene muli wokhulupirika kwa iye. Poona mwatsatanetsatane mawu amene Yesu ananena polimbikitsa atumwi ake, titsimikizira mfundo imeneyi.
Mtengo wa Mpheta
7, 8. (a) Kodi anthu ankaziona bwanji mpheta m’nthawi ya Yesu? (b) Kodi zikuoneka kuti n’chifukwa chiyani pa Mateyu 10:29 pali mawu a Chigiriki otanthauza kuti “timpheta”?
7 Mafanizo a Yesu amasonyeza bwino mfundo yakuti Yehova amaganizira atumiki Ake onse paokhapaokha. Poyamba taganizirani fanizo la mpheta lija. M’masiku a Yesu, mpheta zinali ndiwo, koma chifukwa choti zinkawononga mbewu, kwenikweni anthu ankaziona ngati mbalame zowononga. Mpheta zinalipo zambiri ndiponso zotsika mtengo kwambiri moti ziwiri zinkagulitsidwa pa mtengo wangati umene timagulira machesi masiku ano. Ndalama zochuluka mowirikiza kawiri kuposa pamenepo ankagulira mpheta zisanu osati zinayi zokha ayi. Mpheta inayo inkangokhala ya basela basi, ngati kuti inali yosawerengeredwa n’komwe.—Luka 12:6.
8 Taganiziraninso za kukula kwa mphetazi, zomwe zinali mbalame wamba. Poyerekezera ndi mbalame zina zambiri, ngakhale mpheta yoti yakula kufika pamapeto imakhala yaing’ono kwambiri. Komatu mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “mpheta” pa Mateyu 10:29 amanena makamaka za timpheta tating’onoting’ono. Apa zikuoneka kuti Yesu ankafuna kuti atumwi ake aganizire za mbalame yaing’ono kwambiri ndiponso yotsika mtengo kwambiri.
9. Kodi chitsanzo chimene Yesu anapereka cha mpheta chili ndi mfundo yotani yogwira mtima kwambiri?
9 Chitsanzo cha mpheta chimene Yesu ananenachi chimatithandiza kumvetsa mfundo yofunika kwambiri yakuti: Zinthu zimene zimaoneka ngati zosafunika kwa anthu n’zofunika kwa Yehova Mulungu. Yesu anapitiriza kugogomezera mfundo imeneyi powonjezera kunena kuti ngakhale mpheta yaing’ono “siigwa pansi” popanda Yehova kuona.c Pamenepatu pali phunziro lomveka bwino. Ngati Yehova Mulungu amaona kambalame kakang’ono ndiponso kosawerengeredwa n’komwe kameneka, kodi angalephere bwanji kuganizira mavuto a munthu amene akum’tumikira?
10. Kodi mawu akuti ‘tsitsi lonse la m’mutu mwanu amaliwerenga’ amasonyeza mfundo yofunika yotani?
10 Kuphatikiza pa chitsanzo cha mpheta, Yesu anati: ‘Tsitsi lonse la m’mutu mwanu amaliwerenga.’ (Mateyu 10:30) Mawu achidule koma ozamawa amagogomezera kwambiri mfundo imene ili m’chitsanzo cha Yesu chija chonena za mpheta. Taganizirani izi: Anthu ambiri amakhala ndi tsitsi pafupifupi 100,000 m’mutu mwawo. Katsitsi kalikonse pakokha sikasiyana ndi tsitsi lina lonselo ndipo palibe katsitsi kalikonse kamene timachita kukaganizira pakokha. Komatu katsitsi kalikonse Yehova Mulungu amakaona ndiponso amakawerenga. Motero kodi pali chinthu chilichonse chokhudza moyo wathu chimene Yehova sangadziwe? Ndithu, Yehova amamvetsa mmene mtumwi wake aliyense payekhapayekha alili. Inde, iye amathadi ‘kuyang’ana mumtima.’—1 Samueli 16:7.
11. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova amamuganizira iyeyo payekha?
11 Davide, yemwe ankadziwa bwino mavuto, sankakayika kuti Yehova amamuganizira. Davideyo analemba kuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.” (Salmo 139:1, 2) Inunso musakayikire n’komwe kuti Yehova amakudziwani bwino. (Yeremiya 17:10) Musamafulumire kuganiza kuti Yehova sakuwerengerani inuyo panokha, podziona kuti ndinu wosafunika kwenikweni, chifukwatu n’zosatheka kuti inuyo mulephere kuonedwa ndi maso a Yehova oona zinthu zonse.
“Sungani Misozi Yanga M’nsupa Yanu”
12. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amaona mavuto onse amene anthu ake akukumana nawo?
12 Yehova sikuti amangodziwa mtumiki wake aliyense payekha komanso amadziwa bwino lomwe mavuto onse amene amakumana nawo. Mwachitsanzo, Aisrayeli akuzunzidwa kuukapolo, Yehova anauza Mose kuti: “Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m’Aigupto, ndamvanso kulira kwawo chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zawo.” (Eksodo 3:7) N’zolimbikitsatu kwambiri kudziwa kuti tikamakumana ndi chiyeso chinachake, Yehova amaona ndipo amamva tikamamufuulira kuti atithandize. Ndithu, iye sanyalanyaza mavuto amene tikukumana nawo.
13. Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti Yehova amawaganiziradi atumiki ake?
13 Timaonanso kuti Yehova amasamalira anthu amene ali paubwenzi ndi iyeyo poganizira mmene ankamvera poona Aisrayeli akuvutika. Ngakhale kuti iwo ankavutika chifukwa cha kusamva kwawo, Yesaya analemba za Yehova kuti: “M’mazunzo awo onse Iye anazunzidwa.” (Yesaya 63:9) Poti inunso ndinu mtumiki wokhulupirika wa Yehova, musakayikire n’komwe kuti zinazake zikamakupwetekani, Yehovanso zimam’pweteka. Mfundo imeneyitu iyenera kukulimbitsani mtima mukakhala pamavuto ndiponso iyenera kukupatsani mphamvu zotumikira Yehova mmene mungathere.—1 Petro 5:6, 7.
14. Kodi Davide anali pa mavuto otani pamene ankalemba Salmo 56?
14 Mfundo yakuti Mfumu Davide anali wotsimikiza mtima kwambiri kuti Yehova amamuganizira ndiponso kumumvera chisoni akakhala pamavuto imaonekera kwambiri mu Salmo 56. Davide analemba salmo limeneli pamene Mfumu Sauli ankafuna kumupha. Davide anathawira ku Gati, koma Afilisti atamudziwa iye anaopa kuti agwidwa. Davideyo analemba kuti: “Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse: pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.” Chifukwa choti moyo wake unali pachiswe, Davide anapemphera kwa Yehova. Iye anati: “Tsiku lonse atenderuza mawu anga; zolingalira zawo zonse zili pa ine kundichitira choipa.”—Salmo 56:2, 5.
15. (a) Kodi Davide ankatanthauzanji popempha Yehova kuti aike misozi yake m’nsupa kapena kuti ailembe m’buku? (b) Pamene tikukumana ndi mayesero, kodi tisakayikire mfundo yotani?
15 Kenaka, malingana ndi zimene zinalembedwa pa Salmo 56:8, Davide ananena mawu ochititsa chidwi awa: “Muwerenga kuthawathawa kwanga: sungani misozi yanga m’nsupa yanu; kodi siikhala m’buku mwanu?” Awatu ndi mawu ogwira mtima kwambiri osonyeza kuti Yehova amatiganizira kwambiri mwa chikondi chake. Tikakhala pa mavuto tingathe kum’lilira Yehova popemphera. Ngakhale Yesu, yemwe anali munthu wangwiro, anatero. (Ahebri 5:7) Davide sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova amaona zovuta zake ndiponso kuti saiwala masautso ake, kungokhala ngati kuti waika misozi yake m’nsupa kapena kuti m’thumba la chikopa ndiponso kuti wailemba m’buku.d Mwina inuyo mumaona kuti misozi yanu ingatsale pang’ono kudzadza thumba limenelo, kapena ingalembedwe m’masamba ambiri zedi a m’bukulo. Ngati mumaona choncho, khazikani mtima pansi. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”—Salmo 34:18.
Kukhala Bwenzi Lapamtima la Mulungu
16, 17. (a) Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova sanyalanyaza mavuto amene anthu ake amakumana nawo? (b) Kodi Yehova wachitapo zotani kuti anthu athe kukhala mabwenzi ake?
16 Mfundo yakuti Yehova amawerenga ‘tsitsi lonse la m’mutu mwathu’ imatithandiza kumvetsa kuti Mulungu, amene tili ndi mwayi wom’lambirayu, amaona zonse ndiponso amatiganizira. Ngakhale kuti tiyenera kudikira kaye dziko latsopano kuti zowawa ndi zosautsa zonse zidzathe, panopo Yehova akuwachitira anthu ake zinthu zinazake zodabwitsa. Davide analemba kuti: “Ubwenzi ndi Yehova n’ngwa iwo akuopa iye, ndiponso pangano lake, adzalidziwitsa kwa iwo.”—Salmo 25:14, NW.
17 Kwa anthu opanda ungwiro, zokhala ndi “ubwenzi ndi Yehova” zimaoneka ngati zosatheka. Komatu, Yehova amaitana anthu amene amamuopa kuti akhale alendo ogonera m’chihema chake. (Salmo 15:1-5) Kodi Yehova amawachitira zotani alendo akewo? Davide anati Iye amawadziwitsa pangano lake. Kutanthauza kuti Yehova amawauza zakukhosi, kuulula “chinsinsi chake” kwa aneneri, kuti adziwe zolinga zake ndiponso zimene iwo ayenera kuchita kuti moyo wawo ugwirizane ndi zolinga zakezo.—Amosi 3:7.
18. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tikhale mabwenzi ake apamtima?
18 N’zoona, zimatipatsa mphamvu kudziwa kuti anthu opanda ungwirofe tingathe kukhala mabwenzi apamtima a Wam’mwambamwamba, Yehova Mulungu. Ndipotu, iye amatilimbikitsa kuti tizichita zimenezo. Baibulo limati: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Yehova amafuna kuti tizigwirizana naye kwambiri. Kwenikweni, iye wachitapo kale kanthu kuti ubwenzi woterewu utheke. Nsembe ya dipo ya Yesu inatsegula njira yoti ifeyo tithe kukhala ndi ubwenzi ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Baibulo limati: “Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.”—1 Yohane 4:19.
19. Kodi kupirira kungalimbitse bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?
19 Ubwenzi wapamtima umenewu umalimba tikamapirira masautso osiyanasiyana. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.” (Yakobo 1:4) Kodi ndi “ntchito” yotani imene imachitika chifukwa chopirira masautso? Taganizirani za nkhani ya ‘munga wa m’thupi’ la Paulo. Kodi pankhani imeneyi kupirira kunakwaniritsa zotani? Paulo ananena izi pankhani ya masautso amene anapirira: “Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m’maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine. Chifukwa chake ndisangalala m’maufoko, m’ziwawa, m’zikakamizo, m’mazunzo, m’zipsinjiko, chifukwa cha Kristu; pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:9, 10) Paulo anaona kuti Yehova ankamupatsa mphamvu kuti athe kupirira. Nthawi zina ankamupatsa ngakhale mphamvu yoposa yachibadwa. Mphamvu imeneyi inamuthandiza kuyandikana ndi Kristu ndiponso Yehova Mulungu.—2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:11-13.
20. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti tikamakumana ndi mavuto, Yehova azitithandiza ndi kutikhazika mtima pansi?
20 Mwina Yehova walola kuti mavuto anu apitirire. Ngati zili choncho, kumbukirani lonjezo lake kwa anthu amene amamuopa lakuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Mungathe kuthandizidwa ndiponso kulimbikitsidwa m’njira imeneyi. Yehova ‘amawerenga tsitsi lonse la m’mutu mwanu.’ Iye amaona zimene mukupirira. Amamva ululu umene inuyo mukumva. Amakuganizirani zenizeni. Ndipo ‘sadzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.’—Ahebri 6:10.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu ngati amenewa ananenedwaponso ndi munthu wolungama Davide, ndiponso ana okhulupirika a Kora.—Salmo 10:1; 44:24.
b Baibulo silinena kuti “munga m’thupi” umene Paulo anali nawowu unali chiyani makamaka. N’kutheka kuti mwina unali vuto linalake, monga vuto la maso. N’kuthekanso kuti mawu akuti “munga m’thupi” ankatanthauza atumwi onyenga ndi anthu enanso amene ankatsutsa kuti Paulo anali mtumwi weniweni, n’kumalimbana ndi utumiki wake.—2 Akorinto 11:6, 13-15; Agalatiya 4:15; 6:11.
c Anthu ena ophunzira mozama amati kugwa pansi kwa mphetaku n’kutheka kuti sikukutanthauza chabe kufa kwa mphetazo. Amati mawu a Chigirikiwo angathe kutanthauza za kufika pansi kwa mbalameyo ikamatera kuti idye chakudya. Ngati tanthauzo la mawu amenewa lili limeneli, ndiye kuti Mulungu amaona ndiponso amasamalira mbalamezi pa zochitika zawo zonse za tsiku n’tsiku, osati zikangofa chabe ayi.—Mateyu 6:26.
d Kale, nsupa kwenikweni anali matumba a zikopa za nkhosa, mbuzi, ndi ng’ombe omwe ankasungiramo mkaka, batala, tchizi, kapena madzi. Zikopa zofufutidwa bwino anali kuikamo mafuta kapena vinyo.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ndi zinthu zotani zimene zingachititse munthu kuona ngati kuti Mulungu sakumuganizira?
• Kodi timaphunzirapo chiyani pa fanizo la Yesu la mpheta ndiponso la kuwerenga tsitsi la m’mutu?
• Kodi kuika misozi yathu mu “nsupa” kapena “buku” la Yehova kumatanthauza chiyani?
• Kodi tingatani kuti tikhale pa “ubwenzi ndi Yehova”?
[Chithunzi patsamba 22]
N’chifukwa chiyani Yehova sanachotsere Paulo “munga m’thupi”?
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi tingaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Yesu cha mpheta?
[Mawu a Chithunzi]
© J. Heidecker/VIREO
[Chithunzi patsamba 25]
Kuwerenga Baibulo nthawi zonse kungatithandize kusakayikira zoti Mulungu amatiganizira ifeyo patokha