“Ndingachitenso Mantha ndi Ndani?”
“Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika, pameneponso ndidzadalira Mulungu.”—SAL. 27:3.
MALINGA NDI MALEMBA OTSATIRAWA, KODI N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI KUKHALA OLIMBA MTIMA?
1. Kodi Salimo 27 litithandiza kuyankha mafunso ati?
N’CHIYANI chikutithandiza kuchita zambiri mu utumiki ngakhale kuti m’dzikoli zinthu zikuipiraipira? N’chifukwa chiyani ifeyo timagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu kulalikira m’malo modera nkhawa za mavuto azachuma amene afala m’dzikoli? N’chiyani chingatithandize kukhala olimba mtima pamene anthu ambiri akuchita mantha ndi zam’tsogolo? Nyimbo ya Mfumu Davide yopezeka pa Salimo 27 ikuyankha mafunso amenewa.
2. Kodi munthu amatani akamachita mantha kwambiri? Koma kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?
2 Davide anayamba salimo limeneli ndi mawu akuti: “Yehova ndiye kuwala kwanga ndi chipulumutso changa. Ndingaopenso ndani? Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga. Ndingachitenso mantha ndi ndani?” (Sal. 27:1) Munthu akamachita mantha kwambiri akhoza kufooka moti sangathenso kuchita chilichonse. Koma munthu amene amaopa Yehova sachita mantha kwambiri. (1 Pet. 3:14) Aliyense amene amaona kuti Yehova ndi malo ake a chitetezo “adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.” (Miy. 1:33; 3:25) N’chifukwa chiyani tikutero?
“YEHOVA NDIYE KUWALA KWANGA NDI CHIPULUMUTSO CHANGA”
3. Kodi Yehova amakhala bwanji kuwala kwathu? Koma kodi tiyenera kuchita chiyani?
3 Mawu akuti “Yehova ndiye kuwala kwanga” amasonyeza kuti Yehova amatithandiza kuti tisakhale mu umbuli kapena mu mdima wauzimu. (Sal. 27:1) Kuwala kungathandize munthu kuona zinthu zoopsa kapena zopunthwitsa panjira koma sikungachotse zinthuzo. Tikaona zinthu zoterezi, tiyenera kuzipewa. Yehova amatithandiza kudziwa tanthauzo la zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli. Iye amatichenjeza za zoopsa za m’dziko loipali. Amatipatsa mfundo za m’Baibulo zimene zimatithandiza nthawi zonse. Koma kuti zitithandize, tiyenera kuzigwiritsa ntchito. Tikatero, timakhala anzeru kuposa adani athu ndiponso aphunzitsi athu.—Sal. 119:98, 99, 130.
4. (a) N’chifukwa chiyani Davide ananena molimba mtima kuti: “Yehova ndiye . . . chipulumutso changa”? (b) Kodi ndi liti pamene Yehova adzatipulumutsa?
4 Mawu a Davide pa Salimo 27:1 akusonyeza kuti iye ankakumbukira mmene Yehova anamupulumutsira maulendo angapo. Mwachitsanzo, Yehova anamupulumutsa “m’kamwa mwa mkango ndi m’kamwa mwa chimbalangondo.” Yehova anamuthandizanso kugonjetsa Goliati, yemwe anali chiphona. Mfumu Sauli anayesa kubaya Davide ndi mkondo maulendo angapo koma Yehova anamupulumutsa. (1 Sam. 17:37, 49, 50; 18:11, 12; 19:10) M’pake kuti Davide ananena molimba mtima kuti: “Yehova ndiye . . . chipulumutso changa.” Yehova adzakhalanso chipulumutso cha atumiki ake ngati mmene anachitira ndi Davide. Kodi adzachita zimenezi liti? Iye adzapulumutsa atumiki ake pa “chisautso chachikulu” chimene chikubwera.—Chiv. 7:14; 2 Pet. 2:9.
MUZIKUMBUKIRA NTHAWI ILIYONSE IMENE YEHOVA ANAKUTHANDIZANI
5, 6. (a) Kodi kukumbukira zochitika zam’mbuyo kungatithandize bwanji kukhala olimba mtima? (b) N’chifukwa chiyani ndi bwino kuganizira mmene Yehova anathandizira anthu ake m’mbuyomu?
5 Chinthu chofunika kwambiri chimene chingatithandize kukhala olimba mtima chili pa Salimo 27:2, 3. (Werengani.) Davide ankakumbukira nthawi zimene Yehova anamupulumutsa. (1 Sam. 17:34-37) Kukumbukira zimenezi kunamuthandiza kukhala wolimba mtima atakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Kodi inunso mumakumbukira nthawi zimene Yehova anakuthandizani? Mwachitsanzo, kodi munapempherera vuto lalikulu kwambiri kenako n’kuona kuti Yehova wakupatsani nzeru kapena mphamvu kuti mupirire vutolo? Kapena kodi mungakumbukire mmene mavuto amene ankasokoneza utumiki wanu anathera? Kodi mungakumbukire mmene khomo lalikulu la mwayi wautumiki linatsegukira? (1 Akor. 16:9) Kodi kukumbukira zimenezi kungakuthandizeni bwanji panopa? Zinthu zimenezi zimatsimikizira kuti Yehova akhoza kukuthandizani kupirira kapena kuthana ndi mavuto akulu kwambiri.—Aroma 5:3-5.
6 Kodi tingachite chiyani ngati boma lamphamvu litakonza zoti liwononge gulu lonse la Mboni za Yehova? Anthu ena ayesapo kuchita zimenezi koma alephera. Kuganizira mmene Yehova anathandizira anthu ake m’mbuyomu kungatithandize kukhala olimba mtima tikakumana ndi mavuto m’tsogolo.—Dan. 3:28.
MUZIKONDA KULAMBIRA KOONA
7, 8. (a) Malinga ndi Salimo 27:4, kodi Davide anapempha chiyani kwa Yehova? (b) Kodi kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova n’chiyani? Nanga timalambiramo bwanji?
7 Chinthu china chofunika kwambiri kuti tikhale olimba mtima ndi kukonda kulambira koona. (Werengani Salimo 27:4.) M’nthawi ya Davide, ‘nyumba ya Yehova’ inali chihema. Davide ndi amene anakonza zonse kuti mwana wake Solomo amange kachisi wokongola. Patapita zaka zambiri, Yesu ananena kuti idzafika nthawi imene anthu sadzayenera kupita kukachisi kuti alambire Yehova movomerezeka. (Yoh. 4:21-23) M’buku la Aheberi chaputala 8 mpaka 10, mtumwi Paulo anasonyeza kuti kachisi wamkulu wauzimu anayamba pamene Yesu anabatizidwa mu 29 C.E. Pa nthawi imeneyi, iye anadzipereka kuti achite chifuniro cha Yehova. (Aheb. 10:10) Kachisi wamkulu wauzimu ameneyu ndi dongosolo limene Yehova wakhazikitsa kuti ife tizimulambira m’njira yovomerezeka. Kuti Yehova avomereze kulambira kwathu, tiyenera kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Khristu. Kodi timalambira bwanji m’kachisi ameneyu? Timachita zimenezi popemphera ‘ndi mtima woona popanda kukayikira chilichonse komanso ndi chikhulupiriro.’ Timachitanso zimenezi polalikira molimba mtima ndiponso kuganizira ndi kulimbikitsa Akhristu anzathu pa misonkhano komanso pa Kulambira kwa Pabanja. (Aheb. 10:22-25) Kukonda kulambira koona kungatithandize kupitiriza kuchita zinthu zimenezi m’masiku otsiriza ovuta ano.
8 Padziko lonse, atumiki a Yehova akuchita zambiri mu utumiki. Ena akuphunzira zinenero zatsopano ndipo ena akusamukira m’madera amene mulibe ofalitsa Ufumu okwanira. Iwo ali ngati wamasalimo amene anapempha chinthu chimodzi kwa Yehova. Nawonso amafuna kuona ubwino wa Yehova ndi kuchita utumiki wopatulika zivute zitani.—Werengani Salimo 27:6.
MUZIDALIRA THANDIZO LA MULUNGU
9, 10. Kodi lemba la Salimo 27:10 limatilonjeza chiyani?
9 Davide anasonyeza kuti ankadalira kwambiri thandizo la Yehova ponena kuti: “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.” (Sal. 27:10) Koma timadziwa kuti makolo a Davide sanamusiye tikawerenga zimene zili pa 1 Samueli chaputala 22. Komabe masiku ano, anthu ambiri amakanidwa ndi achibale awo. Ambiri mwa anthu amenewa amathandizidwa ndiponso kutetezedwa mwachikondi mu mpingo wachikhristu.
10 Ngati Yehova amathandiza atumiki ake akasiyidwa, ndiye kuti akhoza kuwathandizanso pa vuto lina lililonse. Mwachitsanzo, ngati timadera nkhawa za mmene tingasamalirire banja lathu, tiyenera kukhulupirira kuti Yehova adzatithandiza. (Aheb. 13:5, 6) Iye amadziwa mavuto athu ndiponso mmene zinthu zilili pa moyo wathu.
11. Kodi anthu ena amationa bwanji chifukwa chodalira kwambiri Yehova? Perekani chitsanzo.
11 Taganizirani za mayi wina wa ku Liberia dzina lake Victoria, yemwe anali kuphunzira Baibulo. Ali pafupi kubatizidwa, mwamuna wake anamusiya ali ndi ana atatu. Ngakhale kuti analibe pokhala komanso sankagwira ntchito, sanabwerere m’mbuyo mpaka anabatizidwa. Ndiyeno tsiku lina, mwana wake wazaka 13 anatola chikwama chodzaza ndi ndalama. Iwo sanafune kuziwerenga n’komwe kuti asakopeke nazo. M’malomwake, anafufuza mwamsanga munthu amene anataya chikwamacho. Munthuyo anali msilikali ndipo anawauza kuti anthu onse akanakhala ngati Mboni za Yehova dziko likanakhala labwino ndiponso lamtendere. Victoria anasonyeza msilikaliyo kuchokera m’Baibulo kuti Yehova walonjeza dziko latsopano. Msilikaliyo anachita chidwi ndi kuona mtima kwa Victoria moti anamupatsa ndalama zambiri pomuthokoza. Popeza kuti a Mboni za Yehova amakhulupirira kwambiri kuti Yehova angawasamalire, amakhala oona mtima ndipo amalemekezedwa.
12. N’chifukwa chiyani timalolera kusiya ntchito kapena zinthu zina kuti titumikire Yehova? Perekani chitsanzo.
12 M’dziko la Sierra Leone muli wofalitsa wosabatizidwa dzina lake Thomas. Iye anayamba kuphunzitsa ku sekondale koma sanalandire malipiro pafupifupi chaka chathunthu. Kuti alandire malipirowo, anayenera kulankhula ndi woyang’anira sukuluyo, yemwe anali wansembe. Wansembeyu anafotokoza kuti zikhulupiriro za Mboni za Yehova n’zosemphana ndi malamulo a pa sukuluyo. Anauza Thomas kuti ngati akufuna ntchito asiye kukhala wa Mboni za Yehova. Koma Thomas anasiya ntchitoyo ndipo sanapatsidwe malipiro ake onse. M’malomwake, anayamba ntchito yokonza mawailesi ndi mafoni. Zitsanzo ngati zimenezi zimasonyeza kuti tikamadalira Yehova, sitichita mantha kuti tivutika. Popeza kuti Yehova analenga zonse ndipo wakhala akuteteza anthu ake, timadziwa kuti adzatisamalira.
13. N’chifukwa chiyani abale ndi alongo kumayiko osauka amalalikira mwakhama?
13 Kumayiko ambiri osauka, abale ndi alongo amalalikira mwakhama. N’chifukwa chiyani zili choncho? Ofesi ya nthambi ina inalemba kuti: “Anthu ambiri amene sali pa ntchito amakhala ndi nthawi yambiri choncho amavomera kuphunzira Baibulo. Nawonso abale amakhala ndi nthawi yambiri yolalikira. Anthu amene amakhala m’madera amene muli mavuto adzaoneni savutika kuzindikira kuti tili m’masiku otsiriza.” Kudziko lina, ofalitsa ambiri amachititsa maphunziro a Baibulo oposa atatu. Mmishonale wina, amene watumikira kumeneko zaka zoposa 12, analemba kuti: “Ofalitsa ambiri sakhala ndi zinthu zambiri zowasokoneza choncho amakhala ndi nthawi yambiri yolalikira ndiponso kuchititsa maphunziro.”
14. Kodi Mulungu adzateteza khamu lalikulu m’njira ziti?
14 Yehova walonjeza kuti adzathandiza, kuteteza ndiponso kupulumutsa gulu la anthu ake. Ndipo timadziwa kuti adzakwaniritsa lonjezo limeneli. (Sal. 37:28; 91:1-3) Anthu amene adzapulumuke “chisautso chachikulu” ayenera kukhala khamu lalikulu. (Chiv. 7:9, 14) Choncho Mulungu sadzalola anthu ake onse kuwonongedwa m’masiku otsiriza n’cholinga choti ateteze khamu lalikulu limeneli. Yehova adzawapatsa zonse zofunika kuti athe kupirira mayesero ndiponso kuteteza ubwenzi wawo ndi iye. Pa nthawi ya Aramagedo, Yehova adzapulumutsa atumiki ake.
“NDILANGIZENI, INU YEHOVA, KUTI NDIYENDE M’NJIRA YANU”
15, 16. Kodi timapindula bwanji tikamatsatira malangizo ochokera kwa Mulungu? Perekani chitsanzo.
15 Kuti tikhalebe olimba mtima, tiyenera kulangizidwa ndi Mulungu nthawi zonse. Davide anapempha Mulungu kuti: “Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende m’njira yanu. Nditsogolereni m’njira yowongoka kuti nditetezeke kwa adani anga.” (Sal. 27:11) Kodi tingalole bwanji kuti Mulungu azitilangiza? Tiyenera kumvetsera mwatcheru malangizo ochokera m’Baibulo amene timalandira m’gulu la Yehova ndiponso kuwatsatira mosazengereza. Akhristu ambiri atsatira malangizo anzeru okhudza kukhala ndi moyo wosalira zambiri ndiponso ayesetsa kuti asakhale ndi ngongole. Zimenezi zawathandiza pa nthawi ino pamene m’dzikoli muli mavuto azachuma. M’malo modzivutitsa kuti akhale ndi zinthu zapamwamba, amakhala ndi mwayi wochita zambiri mu utumiki. Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimatsatira mwamsanga zimene ndimawerenga m’Baibulo ndiponso m’mabuku ochokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru? Kodi ndimachita zimenezi ngakhale pamene ndikuona kuti n’zovuta?’—Mat. 24:45.
16 Tikamalola kuti Yehova azitilangiza ndiponso kutitsogolera pa moyo wathu, sitidzaopa chilichonse. Mpainiya wokhazikika wina wa ku United States anafunsira ntchito imene anaona kuti ingathandize kuti iye ndi banja lake azichitabe utumiki wa nthawi zonse. Koma bwana wake anamuuza kuti sizingatheke chifukwa sanapite ku yunivesite? Kodi mukanakhala inuyo, mukanadandaula kuti munasankha kuchita utumiki wa nthawi zonse m’malo mopita ku yunivesite? Patapita milungu iwiri, bwanayo anachotsedwa ntchito ndipo bwana wina anafunsa m’baleyu zolinga zake. M’baleyu anafotokoza kuti iye ndi mkazi wake ndi Mboni za Yehova ndipo amafuna kukhala ndi nthawi yambiri yolalikira. M’baleyu asanafotokoze zambiri, bwanayu anati: “Ndinaonadi kuti ndiwe wosiyana ndi anzako. Pa nthawi imene bambo anga ankadwala mwakayakaya, azimayi awiri a Mboni ankabwera kudzawawerengera Baibulo tsiku lililonse. Ndinadziuza kuti ndikadzapeza mwayi woti ndithandize wa Mboni, ndidzamuthandiza basi.” Tsiku lotsatira, m’baleyu anapatsidwa ntchito imene bwana woyamba uja anamukaniza. Tikaika patsogolo zinthu za Ufumu, Yehova amakwaniritsa lonjezo lake lakuti adzatipatsa zinthu zonse zofunika.—Mat. 6:33.
CHIKHULUPIRIRO NDI CHIYEMBEKEZO N’ZOFUNIKA KWAMBIRI
17. N’chiyani chingatithandize kuti tisamaope zam’tsogolo?
17 Davide anafotokoza kufunika kwa chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo. Iye anati: “Ngati ndikanakhala wopanda chikhulupiriro poona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo, ndikanataya chiyembekezo.” (Sal. 27:13) Moyo wathu ukanakhala wovuta kwambiri pakanapanda chiyembekezo chathu komanso tikanakhala kuti sitidziwa zinthu zimene zili m’Salimo 27. Choncho tiyeni tipitirize kupempha Yehova kuti azitipatsa mphamvu komanso kutithandiza mpaka tidzapulumuke pa Aramagedo.—Werengani Salimo 27:14.
[Chithunzi patsamba 23]
Davide anapeza mphamvu chifukwa chokumbukira mmene Yehova anamupulumutsira
[Chithunzi patsamba 25]
Kodi timaona kuti mavuto azachuma amatipatsa mwayi wochita zambiri mu utumiki?