Yehova ‘Anapulumutsa’ Anthu Ake M’nthawi za M’baibulo
“Mundifulumirire, Mulungu: Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga.”—SAL. 70:5.
1, 2. (a) Kodi ndi nthawi iti imene anthu a Mulungu amapempha kuti Iye awathandize? (b) Kodi tingafunse funso lotani, nanga yankho lake tingalipeze kuti?
MAKOLO a mtsikana wina ali kutchuthi, anamva kuti mwana wawo wapabanja wa zaka 23 wasowa mosadziwika bwino. Iwo anaganiza kuti watengedwa ndi achifwamba. Nthawi yomweyo, anabwerera kunyumba uku akupemphera kwa Yehova kuti awathandize. Mnyamata wina wa Mboni wa zaka 20, anamupeza ndi matenda opha ziwalo. Atangomva zimenezi, anayamba kupemphera kwa Yehova. Mayi wina amene sali pabanja ankavutika kupeza ntchito ndipo analibe ndalama zogulira chakudya chake ndi cha mwana wake wa zaka 12. Anapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova. Inde, atumiki a Mulungu akakumana ndi mavuto aakulu, amapemphera kwa Mulungu kuti awathandize. Kodi munapempherapo kwa Yehova zinthu zitakuvutani?
2 Mwina tingafunse kuti: Kodi Yehova angatithandizedi tikamupempha thandizo? Yankho lolimbitsa chikhulupiriro chathu likupezeka mu Salmo 70. Salmo lolimbikitsa limeneli linalembedwa ndi Davide, wolambira Yehova wokhulupirika amene anakumana ndi mavuto ambiri pamoyo wake. Wamasalmo ameneyu anauza Yehova kuti: “Mulungu: Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga.” (Sal. 70:5) Kuwerenga Salmo 70 kungatithandize kuona chifukwa chake ifenso tiyenera kupemphera kwa Yehova zinthu zikativuta ndi chikhulupiriro chakuti ‘adzatipulumutsa.’
‘Inu Ndinu Mpulumutsi’
3. (a) Kodi Davide anapempha chiyani mu Salmo 70? (b) Kodi Davide anasonyeza chikhulupiriro chotani m’Salmo 70?
3 Salmo 70 limayamba komanso limatha ndi mawu opempha thandizo kwa Mulungu. (Werengani Salmo 70:1-5.) Davide anapempha Yehova kuti ‘asachedwe’ komanso kuti ‘afulumire’ kumupulumutsa. Kuyambira vesi 2 mpaka 4, Davide anapempha zinthu zisanu ndipo zitatu zoyambirira zinali zokhudza anthu amene ankafuna kumupha. Davide anapempha Yehova kuti agonjetse adani ake ndiponso kuti awachititse manyazi. Zinthu ziwiri zotsatira zimene anapempha anazitchula m’vesi 4 ndipo zinali zokhudza anthu a Mulungu. Davide anapempha kuti anthu okonda Yehova azikhala osangalala ndiponso azitamanda Mulungu. Kumapeto kwa salmo limeneli, Davide anati kwa Yehova: “Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga.” Onani kuti Davide sananene kuti “Mukhale,” ngati kuti akum’pemphanso. Koma anati, “Inu ndinu,” kusonyeza kuti anali kum’dalira. Davide anali ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu amuthandiza.
4, 5. Kodi Salmo 70 likutiuza chiyani za Davide, ndipo tingakhale ndi chikhulupiriro chotani?
4 Kodi Salmo 70 likutiuza chiyani za Davide? Adani ake amene ankafuna kumupha atam’panikiza, Davide sanadalire mphamvu zake. Koma anadalira Yehova kuti athana ndi adani akewo panthawi ndiponso m’njira imene akufuna. (1 Sam. 26:10) Davide anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova amathandiza ndiponso amapulumutsa anthu amene amam’funafuna. (Aheb. 11:6) Davide anadziwa kuti olambira oona ali ndi zifukwa zomveka zokhalira osangalala ndiponso zotamandira Yehova pouza ena za ukulu wake.—Sal. 5:11; 35:27.
5 Monga Davide, ifenso tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ndi mthandizi ndi “mpulumutsi” wathu. Choncho, tikakumana ndi mavuto aakulu kapena tikasowa thandizo, tingapemphe Yehova kuti atithandize mwamsanga. (Sal. 71:12) Koma kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero athu? Tisanakambirane mmene Yehova angatithandizire, tiyeni tione njira zitatu zimene anapulumutsira Davide, panthawi imene ankafuna kwambiri thandizo.
Anapulumutsidwa kwa Adani
6. Kodi Davide anadziwa bwanji kuti Yehova amapulumutsa olungama?
6 Kuchokera m’nkhani za m’Baibulo zimene zinalipo panthawiyo, Davide anadziwa kuti Yehova amapulumutsa anthu olungama. Yehova atawononga anthu oipa ndi chigumula, anapulumutsa Nowa ndi banja lake loopa Mulungu. (Gen. 7:23) Yehova atawononga ndi moto anthu oipa a ku Sodomu ndi Gomora, anapulumutsa munthu wolungama Loti ndi ana ake aakazi awiri. (Gen. 19:12-26) Yehova atawononga Farao ndi magulu ake ankhondo pa nyanja yofiira, Iye anapulumutsa anthu ake. (Eks. 14:19-28) Choncho, n’zosadabwitsa kuti Davide mu Salmo lina analemekeza Yehova monga “Mulungu wa chipulumutso.”—Sal. 68:20.
7-9. (a) Kodi Davide anali ndi chifukwa chotani chokhulupirira kuti Mulungu amapulumutsa? (b) Kodi Davide ananena kuti anapulumutsidwa ndi ndani?
7 Davide analinso ndi chifukwa chomveka chokhulupirira Yehova ndi mtima wonse kuti amapulumutsa anthu ake. Iye anaona yekha kuti “manja osatha” a Yehova amapulumutsa anthu amene amam’tumikira. (Deut. 33:27) Yehova anapulumutsa Davide maulendo angapo kwa “adani” ake. (Sal. 18:17-19, 48) Tiyeni tione chitsanzo.
8 Nthawi imene akazi achiisiraeli amatamanda Davide chifukwa cha luso lake pankhondo, Mfumu Sauli anachita nsanje kwambiri moti kawiri konse anafuna kumulasa ndi mkondo. (1 Sam. 18:6-9) Maulendo onsewa Davide analewa mkondowo. Kodi Davide anapulumuka chifukwa cha luso lake pankhondo? Ayi. Baibulo limati: “Yehova anali naye.” (Werengani 1 Samueli 18:11-14.) Kenako, Sauli ataona kuti walephera zimene amafuna zoti Afilisiti aphe Davide, “Sauli anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide.”—1 Sam. 18:17-28.
9 Kodi Davide ananena kuti anapulumutsidwa ndi ndani? Timawu tapamwamba ta pa Salmo 18 timati, Davide “ananena kwa Yehova mawu a nyimbo iyi mmene Yehova anam’landitsa . . . m’dzanja la Sauli.” Davide anafotokoza maganizo ake poimba kuti: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye.” (Sal. 18:2) N’zolimbitsadi kudziwa kuti Yehova amapulumutsa anthu ake.—Sal. 35:10.
Anam’thandiza Akudwala
10, 11. Kodi n’chiyani chikutithandiza kudziwa nthawi imene Davide anadwala matenda otchulidwa mu Salmo 41?
10 Nthawi ina mfumu Davide anadwala kwambiri ndipo zimenezi zinalembedwa mu Salmo 41. Iye sankadzuka pabedi moti adani ake ena ankaona ngati kuti “sadzaukanso.” (Mavesi 7, 8) Kodi ndi liti pamene Davide anadwala kwambiri chonchi? Zimene zinatchulidwa mu Salmo limeneli zikugwirizana ndi nthawi yovuta pamoyo wa Davide pamene mwana wake Abisalomu ankafuna kumulanda ufumu.—2 Sam. 15:6, 13, 14.
11 Mwachitsanzo, Davide ananena kuti mnzake weniweni amene amadya naye anam’pandukira. (Vesi 9) Zimenezi zingatikumbutse zimene zinachitikira Davide nthawi imene Abisalomu anapanduka. Panthawi imeneyi Ahitofeli, mlangizi wodalirika wa Davide, anapanduka ndi kugwirizana ndi Abisalomu. (2 Sam. 15:31; 16:15) Apa n’kuti mfumuyi itafooka ndi matenda ndipo siimadzuka n’komwe, imadziwanso kuti inali ndi adani amene amafuna kuti ikafa achite zofuna zawo.—Vesi 5.
12, 13. (a) Kodi Davide anati chiyani posonyeza kuti anali kudalira Mulungu? (b) Kodi Mulungu anamulimbikitsa bwanji Davide?
12 Davide sanasiye kudalira ‘mpulumutsi’ wake. Ponena za mtumiki wa Mulungu aliyense amene akudwala, Davide anati: “Tsiku la tsoka Yehova adzam’pulumutsa. Yehova adzam’gwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.” (Sal. 41:1, 3) Apanso, onani kuti Davide anadalira Mulungu ponena kuti “Yehova adzam’pulumutsa.” Iye sanakayike n’komwe kuti Yehova amupulumutsa. Kodi anamupulumutsa bwanji?
13 Davide sanayembekezere kuti Yehova amuchiritsa mozizwitsa. Koma anakhulupirira ndi mtima wake wonse kuti Yehova “adzam’gwiriziza,” kapena kuti adzamuthandiza ndi kumulimbitsa pa matenda ake. Davide anafunikiradi thandizo limeneli. Kuwonjezera pa matenda amene anali nawo, analinso ndi adani amene amam’nenera zinthu zoipa. (Mavesi 5, 6) Yehova ayenera kuti anam’limbitsa Davide pom’kumbutsa mfundo zolimbikitsa. Ndipo Davide anati: “Mundigwirizize mu ungwiro wanga.” (Vesi 12) Ngakhale kuti amadwala ndiponso adani ake anali kumunenera zoipa, Davide analimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova amamuonabe kuti anali wangwiro. Kenako Davide anachira. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amasamalira odwala.—2 Akor. 1:3.
Anam’patsa Chakudya
14, 15. Kodi ndi nthawi iti imene Davide ndi anyamata ake anasowa chakudya, ndipo anathandizidwa bwanji?
14 Davide atakhala mfumu ya Isiraeli, ankadya chakudya chabwino ndipo ankaitana anthu ambiri kudzadya naye. (2 Sam. 9:10) Komabe, Davide anakhalaponso wosowa. Mwana wake Abisalomu atakonza zoukira kuti alande ufumu, Davide ndi anthu ena amene amam’thandiza mokhulupirika anathawa ku Yerusalemu ndipo analowera ku Gileadi, cha kum’mawa kwa mtsinje wa Yordano. (2 Sam. 17:22, 24) Popeza amakhala mothawathawa, Davide ndi anyamata ake anapezeka kuti analibe chakudya ndi zinthu zina. Kodi akanachipeza kuti chakudya ku malo ngati amenewa?
15 Kenako, Davide ndi anyamata ake anafika ku mzinda wa Mahanaimu. Kumeneku anapezana ndi amuna atatu olimba mtima, Sobi, Makiri, ndi Barizilai. Iwo analolera kuika moyo wawo pachiswe kuti athandize mfumu yoikidwa ndi Yehova imeneyi, popeza Abisalomu akanalanda ufumuwo, mwachionekere akanazunza anthu onse amene ankathandiza Davide. Poona mavuto a Davide ndi anyamata ake, amuna olimba mtima amenewa anawabweretsera zinthu monga makama, tirigu, barele, tirigu wokazinga, nyemba, mphodza, uchi, mafuta, ndi nkhosa. (Werengani 2 Samueli 17:27-29.) Kukhulupirika ndi kuchereza alendo kwapadera kwa amuna atatu amenewa, kunam’sangalatsa kwambiri Davide moti sanaiwale zimene anam’chitira.
16. Kodi ndani kwenikweni anapatsa Davide ndi anyamata ake chakudya?
16 Koma kodi ndi ndani kwenikweni amene anapatsa Davide ndi anyamata ake chakudya? Davide sanakayikire kuti Yehova amasamalira anthu ake. Ndithudi, Yehova angachititse atumiki ake kuthandiza okhulupirira anzawo amene akuvutika. Poganizira zimene zinachitika ku Gileadi, Davide anaona kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti amuna atatu aja awasamalire mwachikondi. Atakalamba, Davide analemba kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” (Sal. 37:25) N’zolimbikitsa zedi kudziwa kuti Yehova amasamalira atumiki ake.—Miy. 10:3.
“Yehova Amadziwa Kupulumutsa Anthu”
17. Kodi Yehova wasonyeza chiyani mobwerezabwereza?
17 Davide ndi mmodzi mwa anthu ambiri amene Yehova anawapulumutsa m’nthawi za m’Baibulo. Kuyambira m’nthawi ya Davide, Mulungu wasonyeza kambirimbiri kuti mawu amene mtumwi Petulo ananena ndi oona. Mawuwa amati: “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye m’mayesero.” (2 Pet. 2:9) Taganizirani zitsanzo zina ziwiri izi.
18. Kodi Yehova anapulumutsa bwanji anthu ake m’nthawi ya Hezekiya?
18 Gulu lankhondo lamphamvu la Asuri litaukira Yuda ndi kufuna kuwononga Yerusalemu cha m’ma 700 B.C.E., Mfumu Hezekiya anapemphera kuti: “Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse . . . kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.” (Yes. 37:20) Hezekiya sanafune kuti dzina la Mulungu liipitsidwe. Yehova anayankha pemphero lochokera pansi pamtima limeneli. Usiku umodzi wokha, mngelo mmodzi anapha asilikali a Asuri 185,000, ndipo zimenezi zinachititsa kuti atumiki a Yehova okhulupirika apulumuke.—Yes. 37:32, 36.
19. Kodi Akhristu oyambirira anapulumuka chifukwa chomvera chenjezo lotani?
19 Yesu atangotsala ndi masiku ochepa kuti aphedwe, anapereka ulosi wochenjeza ophunzira ake a ku Yudeya. (Werengani Luka 21:20-22.) Patapita zaka zambiri, Ayuda anagalukira ulamuliro wa Roma, ndipo zimenezi zinachititsa kuti asilikali a Roma azinge Yerusalemu mu 66 C.E. Asilikali otsogoleredwa ndi Seshasi Galasi amenewa anawononga khoma la kachisi; ndiyeno anabwerera mwadzidzidzi. Pozindikira kuti umenewu unali mpata woti athawe chiwonongeko chimene Yesu analosera, Akhristu okhulupirika anathawira kumapiri. Mu 70 C.E., asilikali a Roma anabweranso. Nthawi imeneyi sanabwerere mpaka anawonongeratu Yerusalemu. Akhristu amene anamvera chenjezo la Yesu anapulumuka tsoka lalikulu limeneli.—Luka 19:41-44.
20. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Yehova ‘adzatipulumutsa’?
20 Kuganizira nkhani zosonyeza kuti Yehova amathandiza anthu ake kumalimbitsa chikhulupiriro chathu. Zimene Yehova anachita m’mbuyomo zikutithandiza kuona kuti ndi bwino kum’khulupirira. Kaya tikumane ndi mavuto otani panopa kapena m’tsogolo, ifenso tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti Yehova ‘adzatipulumutsa.’ Koma kodi Yehova angatipulumutse bwanji? Nanga kodi anthu amene tawatchula koyambirira kwa nkhani ino aja, zinthu zinawayendera bwanji? Tiona zimenezi m’nkhani yotsatira.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Salmo 70 limatipatsa zifukwa zotani zokhulupirira Yehova?
• Kodi Davide analimbikitsidwa bwanji akudwala?
• Kodi tili ndi zitsanzo zotani zosonyeza kuti Yehova amapulumutsa anthu ake kwa adani awo?
[Chithunzi patsamba 6]
Yehova anayankha pemphero la Hezekiya