Nthaŵi ya Kudikira
“Uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse. . . . Koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.”—MARKO 13:10, 13.
1. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupirira ndiponso kulimbika mtima?
TIYENERADI kupirira—pakati pa mbadwo wosakhulupirira ndi woipa! Chiyambire 1914 mbadwo wa anthu wakhala woipa, mongadi analili masiku a Yesu. Ndipo lerolino kuipa kuli padziko lonse. “Masiku otsiriza” ano, “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimene mtumwi Paulo anafotokoza zikusautsa anthu. ‘Anthu oipa ndi onyenga, akuipira chiipire.’ Ndithudi, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi, amene tsopano akuyesayesa komaliza kuwononga dziko lapansi. Koma limbikani mtima! Pali “chisautso chachikulu” chimene chikubwera chimene chidzadzetsa mpumulo wachikhalire kwa onse okonda chilungamo.—2 Timoteo 3:1-5, 13; 1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 7:14.
2. Kodi ulosi unakwaniritsidwa motani mu 1914?
2 Nzosangalatsa kuti Yehova tsopano wakhazika Ambuye Yesu Kristu pa mpando wachifumu kumwamba, kukonzekera kuchotsa adani opondereza anthu. (Chivumbulutso 11:15) Monga momwe zinalili pa kubwera koyamba kwa Mesiya, chomwechonso m’zaka za zana lino ulosi wapadera wolembedwa ndi Danieli wakwaniritsidwa. Pa Danieli 4:16, 17, 32, pamatiuza za kuimitsidwa kwa ufumu woyenera pa dziko lapansi kwa nyengo ya “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri.” Pakukwaniritsidwa kwake kwakukulu, nthaŵi zisanu ndi ziŵiri zimenezi zimakwana zaka zisanu ndi ziŵiri za m’Baibulo za ‘masiku’ 360 chimodzi, kapena zaka 2,520 zonse pamodzi.a Zinayamba mu 607 B.C.E., pamene Babulo anayamba kupondereza ufumu wa Israyeli, mpaka mu 1914 C.E., chaka chimene Yesu anakhazikidwa pa mpando wachifumu kumwamba kukhala Mfumu yoyenera pa anthu. Ndiyeno “nthaŵi zawo za anthu akunja” zinatha. (Luka 21:24) Koma amitundu akana kugonjera ku Ufumu Waumesiya ukudzawo.—Salmo 2:1-6, 10-12; 110:1, 2.
3, 4. (a) Kodi pali kufanana kotani pakati pa zochitika za m’zaka za zana loyamba ndi zija za m’nthaŵi yathu? (b) Kodi ndi mafunso otani ofunika amene angafunsidwe?
3 Pamene sabata la 70 la zaka (29-36 C.E.) linayandikira, ndiponso pamene chaka cha 1914 chinayandikira, anthu owopa Mulungu anali kuyembekezera kufika kwa Mesiya. Ndipo anafikadi! Komabe, m’nthaŵi ziŵirizo, njira imene anaonekera inasiyana ndi zimene anthu anayembekezera. Ndiponso m’nthaŵi ziŵirizo, patapita nyengo yaifupipo ya nthaŵi, “mbadwo” woipa potsirizira pake uphedwa mwa lamulo la Mulungu.—Mateyu 24:34.
4 M’nkhani yathu yoyamba, tinaona mmene unathera mbadwo woipa Wachiyuda umene unalamula kuti Yesu aphedwe. Bwanji, nanga za mbadwo wa anthu wowononga umene ngakhale tsopano umamtsutsa kapena kumnyalanyaza? Kodi chiweruzo pa mbadwo wosakhulupirira umenewu chidzaperekedwa liti?
“Dikirani”!
5. (a) Kodi pali chifukwa chabwino chotani chimene sitifunikira kudziŵira “tsiku ilo ndi nthaŵi” ya Yehova? (b) Malinga ndi kunena kwa Marko, kodi Yesu anamaliza ulosi wake ndi uphungu wabwino wotani?
5 Atalosera zochitika zotsogolera ku nthaŵi ya ‘chisautso chachikulu,’ Yesu ananenanso kuti: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:3-36; Marko 13:3-32) Sitifunikira kudziŵa nthaŵi yeniyeni ya zochitikazo. M’malo mwake, tiyenera kulimbikira kukhala odikira, tikumakulitsa chikhulupiriro cholimba, ndi kutanganidwa mu utumiki wa Yehova—osati kuŵerengera masiku. Yesu anamaliza ulosi wake waukuluwo mwa kunena kuti: “Yang’anirani, dikirani, . . . pakuti simudziŵa nthaŵi yake. . . . Dikirani . . . Chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.” (Marko 13:33-37) Ngozi ili mumdima wa dziko lamakono. Tiyenera kudikira!—Aroma 13:11-13.
6. (a) Kodi chikhulupiriro chathu chiyenera kuzikidwa pa chiyani? (b) Kodi ‘tingaŵerenge motani masiku athu’? (c) Kodi Yesu kwenikweni akutanthauzanji ndi mawuwo “mbadwo”?
6 Sitifunikira chabe kusamalira maulosi ouziridwa onena za masiku ano otsiriza a dongosolo loipa komanso tiyenera kuzika chikhulupiriro chathu makamaka pa nsembe yamtengo wake ya Kristu Yesu ndi pa malonjezo a Mulungu abwino koposa ozikidwa pa iyo. (Ahebri 6:17-19; 9:14; 1 Petro 1:18, 19; 2 Petro 1:16-19) Pokhala ofunitsitsa kuona mapeto a dongosolo loipali, anthu a Yehova nthaŵi zina ayerekeza nthaŵi pamene “chisautso chachikulu” chidzaulika, ndipo ayesa kuchita zimenezi mwa kuŵerengera zaka zake za mbadwo woyambira mu 1914. Komabe, ‘timakhala nawo mtima wanzeru’ mwa kulingalira za mmene ‘timaŵerengera masiku athu’ popereka chitamando kwa Yehova mokondwera osati mwa kuyerekeza unyinji wa zaka kapena masiku amene amapanga mbadwo umodzi. (Salmo 90:12) M’malo mopereka lamulo lopimira nthaŵi, liwulo “mbadwo” limene Yesu anagwiritsira ntchito limanena makamaka za anthu amoyo panyengo yakutiyakuti m’mbiri, ndi mikhalidwe yawo yowadziŵira.b
7. Kodi profesa wa mbiri analemba zotani ponena za “mbadwo wa 1914,” ndipo zimenezi zikugwirizana motani ndi ulosi wa Yesu?
7 Mogwirizana ndi zapamwambazi, profesa wa mbiri Robert Wohl analemba zotere m’buku lake lakuti The Generation of 1914: “Mbadwo wa m’mbiri sumadziŵika ndi nthaŵi yake . . . Sumadziŵika ndi chigawo cha madeti.” Koma ananena kuti Nkhondo Yadziko I inachititsa anthu “kumva kukhala opatukana ndi nyengo inapitayo,” ndipo anawonjezera kuti: “Amene anapulumuka nkhondoyo sanaiŵale konse kuti dziko loyamba linatha ndi kuti linanso linayamba mu August 1914.” Zimenezi nzoonadi! Zikusonyeza mfundo yake ya nkhaniyi. “Mbadwo uwu” wa anthu chiyambire 1914 waona masinthidwe owopsa. Waona dziko lapansi likudzala mwazi wa mamiliyoni. Nkhondo, kupululutsa mafuko, uchigaŵenga, upandu, ndi kusaweruzika zakhala padziko lonse. Njala, matenda, ndi makhalidwe oipa zasakaza dziko lathuli. Yesu analosera kuti: “Inunso [ophunzira ake], pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi. Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika.”—Luka 21:31, 32.
8. Kodi aneneri a Yehova akugogomezera motani kufunika kwake kwa kudikira?
8 Inde, chilakiko chonse cha Ufumu Waumesiya chili pafupi! Choncho, kodi munthu angapindule kalikonse mwa kuyang’anira masiku kapena mwa kuyerekeza zaka zake zenizeni za “mbadwo”? Kutalitali! Habakuku 2:3 amalongosola bwino kuti: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” Tsiku la Yehova la kubwezera chilango likuyandikira mofulumira nthaŵi zonse.—Yeremiya 25:31-33; Malaki 4:1.
9. Kodi ndi zochitika zotani chiyambire 1914 zimene zikusonyeza kuti nthaŵi njaifupi?
9 Pamene ulamuliro wa Ufumu wa Kristu unayamba mu 1914, Satana anaponyedwa pansi kudziko. Zimenezi zachititsa “tsoka mtunda . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Nthaŵiyo njaifupidi, poiyerekeza ndi zaka zikwi zambiri zimene Satana walamulira. Ufumuwo uli pafupi, momwemonso tsiku ndi nthaŵi ya Yehova ya kupereka chiweruzo pa mbadwo woipawu!—Miyambo 3:25; 10:24, 25.
“Mbadwo” Umene Uchoka
10. Kodi “mbadwo uwu” wakhala bwanji ngati uja wa m’tsiku la Nowa?
10 Tiyeni tipende mosamalitsa mawu a Yesu pa Mateyu 24:34, 35: “Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa. Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu anga sadzachoka ayi.” Mawu a Yesu otsatira akusonyeza kuti ‘munthu aliyense sadziŵa tsiku ilo ndi nthaŵi yake.’ Chofunika kwambiri, akusonyeza kuti tiyenera kupeŵa misampha yotizinga mu mbadwo uwu. Chotero Yesu awonjezera kuti: “Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala [kukhalapo, NW] kwake kwa Mwana wa munthu. Pakuti monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala [kukhalapo] kwake kwa Mwana munthu.” (Mateyu 24:36-39) Panopa Yesu anafanizira mbadwo wa m’tsiku lake ndi uja wa m’tsiku la Nowa.—Genesis 6:5, 9, NW; mawu amtsinde.
11. Kodi ndi kuyerekezera ‘mibadwo’ kotani kumene Yesu anachita, kumene Mateyu ndi Luka anasimba?
11 Imeneyi sinali nthaŵi yoyamba imene atumwi anamva Yesu akuyerekezera ‘mibadwo,’ pakuti masiku angapo zisanachitike zimenezo iye anati ponena za iye mwini: “Mwana wa munthu . . . ayenera athange wamva zoŵaŵa zambiri nakanizidwe ndi mbadwo uno. Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu.” (Luka 17:24-26) Motero, Mateyu chaputala 24 ndi Luka chaputala 17 akufanizira chimodzimodzi. M’tsiku la Nowa “anthu [amene] anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi” ndi amenenso anawonongedwa pa Chigumula anali “mbadwo uno.” M’tsiku la Yesu Ayuda ampatuko amene anali kumkana Yesu anali “mbadwo uno.”—Genesis 6:11, 12; 7:1.
12, 13. (a) Kodi “mbadwo uwu” umene uyenera kuchoka lerolino nchiyani? (b) Kodi anthu a Yehova tsopano akuchita motani ndi “mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka” umenewu?
12 Chotero, pakukwaniritsidwa kwake komaliza kwa ulosi wa Yesu lerolino, “mbadwo uwu” mwachionekere ndiwo anthu a pa dziko lapansi amene amaona chizindikiro cha kukhalapo kwa Kristu koma nalephera kukonza njira zawo. Mosiyana ndi amenewo, ife pokhala ophunzira a Yesu timakana kusinthidwa ndi makhalidwe a “mbadwo uwu.” Ngakhale kuti tili m’dziko, sitiyenera kukhala mbali yake, “pakuti nthaŵi yayandikira.” (Chivumbulutso 1:3; Yohane 17:16) Mtumwi Paulo akutilangiza kuti: “Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m’dziko lapansi.”—Afilipi 2:14, 15; Akolose 3:5-10; 1 Yohane 2:15-17.
13 ‘Kuonekera kwathu monga mauniko’ kumaphatikizapo osati chabe kusonyeza umunthu wabwino Wachikristu, komanso chofunika koposa, kukwaniritsa lamulo la Yesu laulosi lakuti: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Palibe munthu akhoza kunena pamene chimalizirocho chidzafika, koma tikudziŵa kuti chimaliziro cha “mbadwo uwu” wa anthu oipa chidzafika Mulungu atangokhutira kuti umboni waperekedwa “kufikira malekezero ake a dziko.”—Machitidwe 1:8.
“Tsiku Ilo ndi Nthaŵi Yake”
14. Kodi ndi chilangizo chotani chimene onse aŵiri Yesu ndi Paulo anapereka ponena za “nthaŵizo ndi nyengozo,” ndipo tiyenera kuchitapo motani?
14 Umboni wa padziko lonse utachitidwa pamlingo umene Yehova afuna, lidzakhala “tsiku ilo ndi nthaŵi yake” ya kuchotsa dongosolo la dzikoli. Sitifunikira kudziŵiratu tsiku lake. Chotero, potsanzira chitsanzo cha Yesu, mtumwi Paulo analangiza kuti: “Koma za nthaŵizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulembereni. Pakuti inu nokha mudziŵa bwino kuti tsiku la [Yehova, NW] lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi [chisungiko, NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” Taonani zimene Paulo akugogomezera: ‘Ndi pamene angonena.’ Inde, pamene padzakhala zonena za “mtendere ndi chisungiko,” chiweruzo cha Mulungu chidzaperekedwa mwadzidzidzi, pamene sakuyembekezera. Uli woyenera chotani nanga uphungu wa Paulo wakuti: “Chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire”!—1 Atesalonika 5:1-3, 6; onaninso mavesi 7-11; Machitidwe 1:7.
15, 16. (a) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuganiza kuti Armagedo ili kutali kwambiri kusiyana ndi zimene takhala tikukhulupirira? (b) Kodi ulamuliro wa Yehova udzakuzitsidwa motani patsogolopa?
15 Kodi lingaliro lathu lolondola kwambiri ponena za “mbadwo uwu” likutanthauza kuti Armagedo ili kutali kwambiri kusiyana ndi mmene tinaganizira? Ayi! Ngakhale kuti sitinalidziŵepo “tsiku ilo ndi nthaŵi yake,” Yehova Mulungu nthaŵi zonse wakhala akulidziŵa, ndipo sasintha. (Malaki 3:6) Mwachionekere, dzikoli likupitirapitira ku chiwonongeko chake chomaliza. Kudikira kuli kofunika kwambiri tsopano kuposa ndi kale lonse. Yehova wativumbulira “izi ziyenera kuchitika posachedwa,” ndipo tiyenera kuchitapo kanthu tikumazindikira kwambiri kufulumira kwake kwa nthaŵi.—Chivumbulutso 1:1; 11:18; 16:14, 16.
16 Pamene nthaŵiyo ikuyandikira, dikirani, pakuti Yehova watsala pang’ono kudzetsa tsoka pa dongosolo lonse la Satana! (Yeremiya 25:29-31) Yehova akuti: “Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.” (Ezekieli 38:23) “Tsiku la Yehova” logamula mlandu likuyandikira!—Yoweli 1:15; 2:1, 2; Amosi 5:18-20; Zefaniya 2:2, 3.
“Miyamba Yatsopano, ndi Dziko Latsopano” Zolungama
17, 18. (a) Malinga ndi kunena kwa Yesu ndi Petro, kodi “mbadwo uwu” uchoka motani? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kudikira ponena za mayendedwe ndi m’chipembedzo?
17 Yesu anati ponena za ‘zinthu zonsezi zimene zidzachitika’: “Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu anga sadzachoka ayi.” (Mateyu 24:34, 35) Mwachionekere Yesu anali kuganiza za “thambo ndi dziko lapansi”—olamulira ndi olamulidwa—a “mbadwo uwu.” Mtumwi Petro anagwiritsira ntchito mawu amodzimodziwo potchula “miyamba ndi dziko la masiku ano,” zimene “zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Ndiyeno akufotokoza mmene ‘tsiku la [Yehova, NW] lidzadzera ngati mbala; mmene miyamba [maboma] idzapita’ limodzi ndi chitaganya cha anthu oipa, kapena “dziko,” ndi ntchito zake zauchimo. Ndiyeno mtumwiyo akutilangiza kukhala ndi “mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, [pamene ti]kuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Yehova, mmenemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.” Kodi chikutsatira nchiyani? Petro akutisonyeza “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:7, 10-13.c
18 “Miyamba yatsopano” imeneyo, ulamuliro wa Ufumu wa Kristu Yesu ndi mafumu anzake, idzatsanulira madalitso pa chitaganya cha anthu olungama cha “dziko latsopano.” Kodi mukuyembekezera kukhala mbali ya chitaganya chimenecho? Ngati zili tero, ndiye kuti muli ndi chifukwa chokhalira okondwa kaamba ka mtsogolo mwanu mwabwino kwambiri!—Yesaya 65:17-19; Chivumbulutso 21:1-5.
19. Kodi ndi mwaŵi wotani umene tingakhale nawo tsopano?
19 Inde, “mbadwo” wolungama wa anthu ukusonkhanitsidwa ngakhale tsopano. Lerolino “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wodzozedwa akupereka maphunziro aumulungu mogwirizana ndi mawu a Salmo 78:1, 4: “Tamverani, anthu anga, chilamulo changa; tcherezani khutu lanu mawu a pakamwa panga . . . kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.” (Mateyu 24:45-47) Pa April 14 chaka chino, anthu oposa 12,000,000 pa dziko lonse lapansi anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu m’mipingo yoposa 75,500 m’maiko pafupifupi 230. Kodi munali pakati pawo? Muiketu chikhulupiriro chanu mwa Kristu Yesu ndi ‘kuitana pa dzina la Yehova kaamba ka chipulumutso.’—Aroma 10:10-13.
20. Popeza “yafupika nthaŵi [yotsala],” kodi tiyenera kukhala odikira motani, ndipo tikumayembekezera chiyani?
20 “Yafupika nthaŵi [yotsala, NW],” anatero mtumwi Paulo. Chotero, ndiyo nthaŵi yakudikirabe ndi kutanganidwabe m’ntchito ya Yehova, pamene tikupirira mayesero ndi maudani zimene mbadwo woipa wa anthu umadzetsa. (1 Akorinto 7:29; Mateyu 10:22; 24:13, 14) Tiyeni tikhale odikira, tikumaona zonse zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzafika pa “mbadwo uwu.” (Luka 21:31-33) Mwa kupeŵa zinthu zimenezi ndi mwa kuima ndi chivomerezo cha Mulungu pamaso pa Mwana wa munthu, tingapeze mphotho ya moyo wosatha potsirizira pake.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna kudziŵa zambiri ponena za “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri,” onani masamba 127-39, 186-9 m’buku lakuti “Let Your Kingdom Come,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Onani Voliyumu 1, tsamba 918, mu Insight on the Scriptures, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
c Onaninso masamba 152-6 ndi 180-1 m’buku la Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Mafunso Pobwereza:
◻ Pokhala taona kukwaniritsidwa kwa Danieli 4:32, kodi ife tsopano tiyenera ‘kudikira’ motani?
◻ Kodi Mauthenga Abwino a Mateyu ndi Luka amadziŵikitsa motani “mbadwo uwu”?
◻ Pamene tikuyembekezera “tsiku ilo ndi nthaŵi yake,” timaona chiyani, ndipo tiyenera kuchitapo motani?
◻ Kodi chiyembekezo cha “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” lolungama chiyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?
[Zithunzi patsamba 17]
Anthu ovutika adzapeza mpumulo pamene mbadwo uwu woipa ndi wachiwawa uchoka
[Mawu a Chithunzi]
Alexandra Boulat/Sipa Press
[Mawu a Chithunzi]
Kulamanzere ndi pansi: Luc Delahaye/Sipa Press
[Chithunzi patsamba 18]
“Miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” zaulemerero zili patsogolopa kaamba ka mafuko onse a anthu