Kupindula ndi “Tirigu wa Kumwamba”
ATANGOLANDITSIDWA mozizwitsa ku Igupto, Aisrayeli anasonyeza kupanda chikhulupiriro kwakukulu mwa Mlanditsi wawo, Yehova. Chifukwa cha zimenezi, Yehova anawazunguliritsa m’chipululu cha Sinai kwa zaka 40. Nthaŵi yonseyo, Aisrayeli ndi alendo “osakanikirana” amene anawatsatira anadya ndi kumwa ‘nakhuta.’ (Eksodo 12:37, 38 NW) Salmo 78:23-25 limatiuza mmene zimenezi zinathekera: ‘[Yehova] analamulira mitambo ili m’mwamba, natsegula m’makomo a kumwamba. Ndipo anawavumbitsira mana, adye, nawapatsa tirigu wa kumwamba. Yense anadya mkate wa omveka [“amphamvu,” NW]: anawatumizira chakudya chofikira [“chowakhutitsa,” NW].’
Mose amene anadya nawo mana, anafotokoza kuti chinali chakudya chapadera. Iye analemba kuti, m’mamaŵa, “atasansuka mame adagwawo, . . . pankhope pa chipululu pali kanthu kakang’ono kamphumphu, kakang’ono ngati chipale panthaka. Ndipo pamene ana a Israyeli anakaona, anati wina ndi mnzake, N’chiyani ichi?” m’Chihebri, “man huʼ?” Mawu ameneŵa mwina ndiwo anali chiyambi cha liwu lakuti “mana,” dzina lomwe Aisrayeli anatchula chakudyacho. Mose anati: ‘Iwo anali ngati zipatso zampasa, oyera; poŵalaŵa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.’—Eksodo 16:13-15, 31, NW, mawu amtsinde.
Mana sanali chakudya chongobwera mwachilengedwe, monga ena amanenera. Mphamvu yaumulungu ndiyo inachititsa kuti aperekedwe. Mwachitsanzo, iwo sankangopezeka kumalo amodzi kapena nyengo imodzi. Akasungidwa mpaka mmaŵa, ankagwa mphutsi ndi kununkha; komabe, chakudya choŵirikiza kaŵiri chimene banja lililonse limatenga tsiku limodzi isanafike Sabata yamlungu uliwonse, sichinali kuwonongeka usiku, chotero ankadya pa Sabata—tsiku lomwe mana sanali kuoneka. Ndithudi, mana anali makonzedwe ozizwitsa.—Eksodo 16:19-30.
Kutchulidwa kwa “amphamvu,” kapena kuti “angelo,” mu Salmo 78 kukusonyeza kuti Yehova ayenera kuti anagwiritsa ntchito angelo kugwetsa mana. (Salmo 78:25, NW, mawu amtsinde) Mulimonse mmene zinalili, anthu anayenera kuyamika Mulungu chifukwa cha kukoma mtima kwake. Komabe, ambiri anasonyezanso mtima wosayamika kwa Iye amene anawalanditsa muukapolo ku Igupto. Ifenso tingapeputse zogaŵira za Yehova ngakhalenso kusayamika ngati tilephera kusinkhasinkha pa kukoma mtima kwake kwachikondi. Chotero tiyenera kukhala oyamikira kuti Yehova anaphatikiza nkhani ya kulanditsidwa kwa Aisrayeli ndi zochitika zotsatirazo kuti ‘zitilangize.’—Aroma 15:4.
Zimene Aisrayeli Anaphunzira Zipindulitsa Akristu
Pamene Yehova anapereka mana, iye anali ndi cholinga osati kungokhutiritsa zosoŵa zakuthupi za Aisrayeli pafupifupi mamiliyoni atatuwo. Anafuna kuti ‘awachepetse ndi kuwayese’ kotero kuti awayenge ndi kuwalanga kuti apindule. (Deuteronomo 8:16; Yesaya 48:17) Akanavomera kuyengedwa ndi kulangidwako, Yehova akanakondwa ‘kuwachitira chokoma potsiriza pawo’ mwa kuwapatsa mtendere, ulemerero, ndi chimwemwe m’Dziko Lolonjezedwa.
Chinthu chimodzi chofunika kwambiri chimene anayenera kudziŵa n’chakuti, “munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3) Akanakhala kuti Mulungu sanapereke mana, Aisrayeli akanafa ndi njala—mfundo imene iwo anavomereza mwamsanga. (Eksodo 16:3, 4) Aisrayeli oyamika anali kukumbutsidwa tsiku ndi tsiku za kudalira kwawo Yehova kotheratu, kotero kuti anakhala odzichepetsa. Atangofika m’Dziko Lolonjezedwa lokhala ndi zinthu zakuthupi zochuluka, kukanakhala kovuta kwa iwo kuiŵala Yehova ndi chidaliro chawo kwa iye.
Monga Aisrayeli, Akristu ayenera kukhalabe ozindikira za kudalira kwawo Mulungu pa zinthu zofunika m’moyo—zakuthupi ndi zauzimu. (Mateyu 5:3; 6:31-33) Poyankha chimodzi mwa ziyeso za Mdyerekezi, Yesu Kristu anagwira mawu a Mose opezeka pa Deuteronomo 8:3 akuti: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Inde, alambiri oona a Mulungu amadyetsedwa mwa kuŵerenga mawu a Yehova opezeka m’Mawu ake. Kuwonjezera pamenepa, chikhulupiriro chawo chimakhala cholimba pamene apeza phindu lake la mawu ameneŵa m’moyo wawo pamene akuyenda ndi Mulungu ndi kuika zinthu za Ufumu patsogolo.
Anthu opanda ungwirofe tingaiŵale kuyamikira zinthu zimene tazizoloŵera m’moyo wathu—ngakhale kuti zinthuzo zikusonyeza chisamaliro chachikondi cha Yehova. Mwachitsanzo, makonzedwe aumulungu a mana anadabwitsa ndi kusangalatsa Aisrayeli poyamba, koma patangopita nthaŵi pang’ono ambiri anadandaula. “Mtima wathu walema nawo mkate wachabe uwu,” anadandaula mopanda ulemu—kusonyeza chiyambi cha ‘kulekana ndi Mulungu wamoyo.’ (Numeri 11:6; 21:5; Ahebri 3:12) Choncho, chitsanzo chawo ‘chikutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.’—1 Akorinto 10:11.
Kodi tingalabadire motani chitsanzo chochenjeza chimenechi? Njira imodzi ndiyo kusayerekeza kulola ziphunzitso za Baibulo kapena zogaŵira zomwe timalandira kuchokera kwa kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kukhala zinthu wamba, kapena zachisawawa. (Mateyu 24:45) Tikangotero n’kuyamba kupeputsa mphatso za Yehova kapena kutopa nazo, unasi wathu ndi iye udzayamba kuzirala.
Pachifukwa chabwino, Yehova satipatsa zinthu zabwino zochititsa chidwi zatsopano mosefukira nthaŵi imodzi. M’malo mwake, amatipatsa kuunika kowonjezereka pa Mawu ake pang’onopang’ono. (Miyambo 4:18) Zimenezi zimapatsa anthu ake mpata womvetsadi zomwe akuphunzira komanso kuzichita. Yesu anatsatira chitsanzo cha Atate wake pamene ankaphunzitsa ophunzira ake oyamba. Iye analongosola Mawu a Mulungu kwa iwo “monga anakhoza kumva,” kapena kuti “kuzindikira,” monga momwe mabaibulo ena amanenera.—Marko 4:33; yerekezani ndi Yohane 16:12.
Limbitsani Chiyamikiro Chanu pa Zogaŵira za Mulungu
Yesu anagwiritsanso ntchito kubwerezabwereza. Inde, m’maganizo chabe tingamve mfundo ina mofulumira—mwachitsanzo, pulinsipulo la Baibulo—koma kuti likhazikike mumtima kuti tikhale ‘munthu wathu watsopano’ wachikristu zingatenge nthaŵi, makamaka ngati mtima wadziko ndi njira zake zakale zinazika mizu. (Aefeso 4:22-24) Zimenezo zinalidi choncho ndi ophunzira a Yesu pankhani yokhudza kuchotsa kudzikuza kuti akhale odzichepetsa. Yesu anaŵaphunzitsa za kudzichepetsa nthaŵi zingapo, nthaŵi iliyonse akumabwereza mfundo yomweyo m’njira yosiyana kuti ziŵagwire mtima, ndipo m’kupita kwa nthaŵi zinaterodi.—Mateyu 18:1-4; 23:11, 12; Luka 14:7-11; Yohane 13:5, 12-17.
Masiku ano, misonkhano yachikristu ndi zofalitsa za Watch Tower zimatsatira chitsanzo cha Yesu pa kugwiritsa ntchito kubwerezabwereza kokonzedwa bwino. Chotero tiyeni tiziyamikira zimenezi kukhala chikondi cha Mulungu kwa ife ndipo tisaleme konse ndi zomwe timalandira, monga Aisrayeli analemera ndi mana. Inde, pamene moleza mtima tidzipereka ife eni kumvera zimene Yehova amatikumbutsa nthaŵi ndi nthaŵi, tidzaona zinthu zabwino m’moyo wathu. (2 Petro 3:1) Mtima woyamikira umenewo umasonyezadi kuti ‘tikuzindikira’ Mawu a Mulungu m’mitima yathu komanso m’maganizo athu. (Mateyu 13:15, 19, 23) Pankhani imeneyi tili ndi chitsanzo chabwino cha Davide wamasalmo, amene ngakhale kuti sankalandira chakudya chauzimu chosiyanasiyana monga chimene timalandira ife lerolino, anafotokoza kuti malamulo a Yehova ‘n’ngozuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake’!—Salmo 19:10.
“Mana” Amene Amapatsa Moyo Wosatha
“Ine ndine mkate wamoyo,” Yesu anatero kwa Ayuda. “Makolo anu adadya [mana, NW] m’chipululu, ndipo adamwalira. . . . Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umenewu, adzakhala ndi moyo kosatha. . . . Mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.” (Yohane 6:48-51) Mkate weniweni kapena mana sizinapatse anthu ndipo sizingawapatse moyo wosatha. Koma amene asonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu, m’kupita kwa nthaŵi adzasangalala ndi madalitso a moyo wosatha.—Mateyu 20:28.
Ambiri amene akupindula ndi nsembe ya dipo ya Yesu adzasangalala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. “Khamu lalikulu” la amenewa—lochitidwa chithunzi ndi alendo “osakanikirana” amene anatsatira Aisrayeli paulendo wawo wotchedwa Eksodo kuchokera ku Igupto—adzapulumuka “chisautso chachikulu” chimene chikubwera kudzachotsa kuipa konse. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14; Eksodo 12:38) Ngakhale aja omwe anachitiridwa chithunzi ndi Aisrayeli enieniwo akusangalala ndi mphoto yaikulu koposa. Ponena za iwo okwana 144,000, mtumwi Paulo anafotokoza kuti iwo ndiwo Israyeli wauzimu wa Mulungu. Akamwalira mphoto yawo ndiyo chiukiriro ndi kukakhala ndi moyo kumwamba. (Agalatiya 6:16; Ahebri 3:1; Chivumbulutso 14:1) Kumeneko, Yesu adzaŵapatsa mana apadera.
Tanthauzo la “Mana Obisika”
“Kwa iye wolakika, ndidzam’patsa mana obisika,” anatero Yesu woukitsidwayo kwa Israyeli wauzimu. (Chivumbulutso 2:17) Mana obisika ophiphiritsira ameneŵa akutikumbutsa mana omwe Mulungu analamulira Mose kusunga m’mbiya yagolidi ndi kuika mu likasa lopatulika lachipangano. Likasalo linali kusungidwa m’chipinda Chopatulikitsa cha chihema. Mmenemu silinali kuoneka, linali lobisika. Popeza kuti ankasungidwa monga chikumbutso, mana ameneŵa sanawonongeke mu Likasa muja, chotero chinali chizindikiro choyenera cha kukhalapo kwa chakudya chosawonongeka. (Eksodo 16:32; Ahebri 9:3, 4, 23, 24) Popatsa a 144,000 mana obisika, Yesu akuwatsimikiza kuti adzalandira moyo wosafa ndi chisavundi monga ana auzimu a Mulungu.—Yohane 6:51; 1 Akorinto 15:54.
“Chitsime cha moyo chili ndi Inu [Yehova],” anatero wamasalmo. (Salmo 36:9) Analidi makonzedwe abwino mana—enieniwo ndiponso ophiphiritsa—akumatsimikizira choonadi chofunikacho! Mana amene Mulungu anapereka kwa Israyeli wakale, mana ophiphiritsa amene anapereka monga thupi la Yesu loperekedwa chifukwa cha ife, komanso mana obisika ophiphiritsa amene akupereka kupyolera mwa Yesu kwa a 144,000, akutikumbutsa tonsefe kudalira Mulungu kotheratu kuti tikhale ndi moyo. (Salmo 39:5, 7) Tiyeni modzichepetsa komanso nthaŵi zonse tizindikire kuti timam’dalira. Ndipo Yehova ‘adzatichitira chokoma potsiriza pathu.’—Deuteronomo 8:16.
[Zithunzi patsamba 26]
Kuti apeze moyo wosatha, anthu onse amadalira “mkate wamoyo wotsika Kumwamba”
[Chithunzi patsamba 28]
Kupezeka pa misonkhano yonse yachikristu kumasonyeza kuyamikira kwathu zikumbutso za Yehova