Ekisodo
12 Tsopano Yehova anauza Mose ndi Aroni mʼdziko la Iguputo kuti: 2 “Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba pa chaka. Chaka chanu chiziyamba ndi mwezi uno.+ 3 Uzani gulu lonse la Isiraeli kuti, ‘Pa tsiku la 10 la mwezi uno mabanja onse ochokera mwa kholo limodzi adzatenge nkhosa imodziimodzi,+ banja lililonse lidzatenge nkhosa imodzi. 4 Koma ngati banja lili lalingʼono moti silingamalize kudya nkhosa yonseyo, banjalo lidzaitane banja lina loyandikana nalo kuti adzadyere limodzi mʼnyumba mwawo, mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu. Muziganizira mmene munthu aliyense amadyera kuti mudziwe kuchuluka kwa nyama imene ikufunika. 5 Nkhosa yanuyo ikhale yopanda chilema,+ yamphongo, yachaka chimodzi. Mungatenge mwana wa nkhosa kapena wa mbuzi. 6 Nkhosayo muisamalire mpaka tsiku la 14 la mwezi uno.+ Kenako banja lililonse la Aisiraeli lidzaphe nkhosa yawo madzulo kuli kachisisira.*+ 7 Adzatenge magazi nʼkuwawaza pamafelemu awiri amʼmbali mwa khomo ndi pafelemu lapamwamba pa chitseko. Adzachite zimenezi panyumba zimene adzadyeremo nkhosayo.+
8 Adzadye nyamayo usiku umenewu.+ Adzaiwotche pamoto ndipo adzaidye pamodzi ndi mikate yopanda zofufumitsa+ ndi masamba owawa.+ 9 Musadzaidye yaiwisi, yowiritsa kapena yophika ndi madzi, koma mudzadye yowotcha pamoto. Mudzawotche mutu wake pamodzi ndi ziboda ndiponso zamʼmimba. 10 Musadzasunge nyama iliyonse kuti ifike mʼmawa. Koma iliyonse yotsala kufika mʼmawa mudzaipsereze pamoto.+ 11 Kudya kwake mudzadye chonchi, mudzakhale mutamanga lamba mʼchiuno mwanu, mutavala nsapato ndiponso mutatenga ndodo mʼdzanja lanu. Muzidzadya mofulumira. Ameneyu ndi Pasika* wa Yehova. 12 Ine ndidzadutsa mʼdziko la Iguputo usiku umenewo nʼkupha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo, mwana wa munthu kapena wa chiweto.+ Ndipo ndidzapereka chiweruzo pa milungu yonse ya mu Iguputo.+ Ine ndine Yehova. 13 Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalemo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo nʼkukupitirirani, moti mliriwo sudzakugwerani nʼkukuwonongani ndikamadzalanga dziko la Iguputo.+
14 Tsiku limeneli lidzakhala chikumbutso kwa inu, ndipo muzichitira Yehova chikondwerero mʼmibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale, kuti muzichita chikondwerero chimenechi. 15 Muzidya mkate wopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ Pa tsiku loyamba muzichotsa mʼnyumba zanu ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa chifukwa aliyense wodya mkate wokhala ndi zofufumitsa, kuchokera pa tsiku loyamba kukafika pa tsiku la 7, munthu wochita zimenezi aziphedwa kuti asakhalenso mu Isiraeli. 16 Pa tsiku loyamba muzidzachita msonkhano wopatulika, ndipo pa tsiku la 7 muzidzachitanso msonkhano wina wopatulika. Masiku amenewa musamadzagwire ntchito.+ Koma chakudya choti munthu aliyense adye, chimenecho chokha muzidzaphika.
17 Muzidzachita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ chifukwa pa tsiku limeneli ndidzatulutsa makamu anu mʼdziko la Iguputo. Muzidzasunga tsiku limeneli mʼmibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 18 Mʼmwezi woyamba, tsiku la 14 la mwezi umenewo, madzulo muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa, mpaka kukafika madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo.+ 19 Kwa masiku 7 mʼnyumba zanu musamadzapezeke ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa, chifukwa aliyense amene wadya chakudya chokhala ndi zofufumitsa, kaya ndi mlendo kapena mbadwa ya Isiraeli,+ munthu ameneyo adzaphedwa kuti asakhalenso pagulu la Isiraeli.+ 20 Musamadzadye chilichonse chokhala ndi zofufumitsa. Mʼnyumba zanu zonse muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa.’”
21 Mwamsanga, Mose anaitana akulu onse a Isiraeli+ nʼkuwauza kuti: “Pitani mukasankhire mabanja anu onse ana a ziweto* nʼkuwapha kuti ikhale nsembe ya Pasika. 22 Mukatero mukatenge kamtengo ka hisope* nʼkukaviika mʼbeseni la magazi nʼkuwawaza pafelemu lapamwamba pa chitseko, ndipo ena mwa magaziwo muwawaze pamafelemu awiri amʼmbali mwa khomo. Aliyense asadzatuluke mʼnyumba yake mpaka mʼmawa. 23 Ndiyeno Yehova akamadzapita kukapha Aiguputo ndi mliri, nʼkuona magazi pamafelemu apamwamba pa zitseko zanu ndi mafelemu awiri amʼmbali mwa khomo, Yehova adzapitirira khomo limenelo ndipo sadzalola mliri wa imfa kulowa mʼnyumba zanu.+
24 Choncho muzichita chikondwerero chimenechi. Limeneli ndi lamulo kwa inu ndi kwa ana anu mpaka kalekale.+ 25 Ndipo muzidzachita mwambo umenewu+ mukadzalowa mʼdziko limene Yehova analonjeza kuti adzakupatsani. 26 Ndiyeno ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani timachita mwambo umenewu?’+ 27 mudzawauze kuti, ‘Umenewu ndi mwambo wopereka nsembe ya Pasika kwa Yehova, amene anadumpha nyumba za Aisiraeli mu Iguputo pamene ankapha Aiguputo ndi mliri, koma anapulumutsa mabanja athu.’”
Atatero, anthuwo anagwada nʼkuweramira pansi. 28 Choncho Aisiraeli anachoka nʼkukachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose ndi Aroni.+ Anachitadi zomwezo.
29 Ndiyeno pakati pa usiku, Yehova anapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo.+ Kuyambira mwana woyamba wa Farao, amene anali pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa mkaidi amene anali mʼndende, ndiponso mwana aliyense woyamba kubadwa wa nyama.+ 30 Zitatero Farao, atumiki ake onse ndi Aiguputo onse anadzuka usiku umenewo. Ndipo anthu anayamba kulira kwambiri mʼdziko lonse la Iguputo, chifukwa panalibe banja ngakhale limodzi limene linalibe maliro.+ 31 Usiku womwewo Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni+ nʼkuwauza kuti: “Nyamukani, chokani pakati pa anthu anga, inuyo ndi Aisiraeli ena onse. Pitani, katumikireni Yehova monga momwe mwanenera.+ 32 Mutengenso nkhosa ndi ngʼombe zanu monga mwanenera ndipo muzipita.+ Komanso mukandipemphere kwa Mulungu kuti andidalitse.”
33 Ndiyeno Aiguputo anayamba kuumiriza anthuwo kuti achoke mʼdzikolo mofulumira.+ Iwo anati, “chifukwa tonsefe tikungokhala ngati tafa kale!”+ 34 Choncho Aisiraeli ananyamula ufa wokanda wopanda zofufumitsa. Anaunyamulira mʼzokandiramo ufa* pamapewa awo atazikulunga mʼnsalu zawo. 35 Aisiraeli anachita zimene Mose anawauza ndipo anapempha Aiguputo zinthu zasiliva, zagolide komanso zovala.+ 36 Choncho Yehova anachititsa kuti Aiguputo akomere mtima anthu ake, moti Aiguputowo anawapatsa zinthu zonse zimene anapempha ndipo iwo anatenga zinthu zambiri za Aiguputo.+
37 Kenako Aisiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Panali amuna oyenda pansi pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+ 38 Ndipo gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana*+ linapita limodzi ndi Aisiraeliwo. Linapitanso ndi nkhosa, mbuzi komanso ngʼombe zambirimbiri. 39 Iwo anayamba kuphika mikate yozungulira yopanda zofufumitsa pogwiritsa ntchito ufa wokanda umene anachoka nawo ku Iguputo uja. Ufawo unalibe zofufumitsa chifukwa anawauza kuti achoke ku Iguputo mofulumira kwambiri moti sanathe kukonza chakudya chilichonse ponyamuka.+
40 Ndiyeno Aisiraeli amene anakhala ku Iguputo,+ anakhala mʼdziko lachilendo* zaka 430.+ 41 Zaka 430 zimenezi zitatha, pa tsiku lomwe zinathalo, gulu lonse la anthu a Yehova linatuluka mʼdziko la Iguputo. 42 Umenewu ndi usiku umene azidzakondwerera kuti Yehova anawatulutsa mʼdziko la Iguputo. Yehova anafuna kuti Aisiraeli onse, azidzachita chikondwerero chimenechi mʼmibadwo yawo yonse pokumbukira usiku umenewu.+
43 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Lamulo la Pasika ndi ili: Mlendo* asadye nawo.+ 44 Koma ngati wina ali ndi kapolo wamwamuna amene anamugula ndi ndalama, muzimudula.+ Akadulidwa nayenso angathe kudya. 45 Mlendo wobwera kudzakhala nanu ndiponso waganyu asadye nawo. 46 Muzidyera mʼnyumba imodzi. Musatuluke panja ndi nyama iliyonse komanso musaphwanye fupa lililonse la nyamayo.+ 47 Gulu lonse la Isiraeli lizichita chikondwerero chimenechi. 48 Ngati mlendo amene akukhala nanu akufuna kuchita nawo chikondwerero cha Pasika kwa Yehova, mwamuna aliyense wamʼnyumba yake adulidwe. Akatero angathe kubwera kudzachita nawo chikondwererocho, ndipo ayenera kuonedwa ngati mbadwa ya dzikolo. Koma munthu wosadulidwa asadye nawo.+ 49 Lamulo lililonse lizigwira ntchito mofanana kwa mbadwa ndi kwa mlendo wokhala pakati panu.”+
50 Choncho Aisiraeli onse anachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose ndi Aroni. Anachitadi zomwezo. 51 Pa tsiku limeneli, Yehova anatulutsa Aisiraeli onse* mʼdziko la Iguputo.