Yesu Khristu—Mmishonale Woposa Amishonale Onse
“Ndine nthumwi, Iyeyu anandituma ine.”—YOH. 7:29.
1, 2. Kodi mmishonale ndani, ndipo ndani amene angatchedwe Mmishonale woposa amishonale onse?
KODI mumaganiza chiyani mukangomva mawu akuti “mmishonale”? Ena amaganiza za amishonale a Matchalitchi Achikristu, amene ambiri a iwo amachita nawo zandale ndiponso zamalonda m’mayiko omwe amatumizidwa. Komabe, inu monga wa Mboni za Yehova, mosakayikira mukuganiza za amishonale amene amatumizidwa ndi Bungwe Lolamulira kuti akalalikire uthenga wabwino kumalo osiyanasiyana padziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Amishonale amenewa modzipereka amagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo kuti achite ntchito yofunika kwambiri, yothandiza anthu kuyandikira Yehova Mulungu ndi kukhala naye paubale wabwino.—Yak. 4:8.
2 M’mavesi a mu Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu mulibe mawu akuti “mmishonale” kapena “amishonale.” Koma mawu a mmunsi pa Aefeso 4:11, amati mawu a Chigiriki omwe anamasuliridwa kuti “alaliki” angamasuliridwenso kuti “amishonale.” Yehova ndi Mlaliki woposa onse, koma sitinganene kuti ndi Mmishonale woposa amishonale onse chifukwa palibe yemwe anam’tuma. Ponena za Atate ake a kumwamba, Yesu Khristu anati: “Ndine nthumwi, Iyeyu anandituma ine.” (Yoh. 7:29) Posonyeza kuti amakonda kwambiri anthu, Yehova anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi. (Yoh. 3:16) Yesu angatchedwe Mmishonale woposa amishonale onse. Chifukwa china n’chakuti anatumizidwa padziko lapansi “kudzachitira umboni choonadi.” (Yoh. 18:37) Iye anakwanitsa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo ife tikupindulabe ndi utumiki wake. Mwachitsanzo, kaya ndife amishonale kapena ayi, tingatsanzire njira zake zophunzitsira muutumiki wathu.
3. Kodi tikambirana mafunso ati?
3 Ntchito ya Yesu yolalikira za Ufumu imabweretsa mafunso monga akuti: Kodi Yesu anakumana ndi zotani padziko lapansi? N’chifukwa chiyani kaphunzitsidwe kake kanali kogwira mtima? Ndipo n’chiyani chinamuthandiza kuti achite bwino utumiki wake?
Anali ndi Mtima Wodzipereka M’dziko Lachilendo
4-6. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinasintha pamoyo wa Yesu atabwera padziko lapansi?
4 Amishonale a masiku ano ndiponso Akhristu ena amene amapita ku malo kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri, angafunike kuzolowera kukhala movutikirapo kusiyana ndi mmene anali kukhalira poyamba. Koma sitingayerekeze n’komwe ndi zimene Yesu anakumana nazo padziko lapansi atachoka kumwamba, komwe anakhala ndi Atate ake limodzi ndi angelo omwe anali kutumikira Yehova ndi zolinga zabwino. (Yobu 1:6; 2:1) Zinalidi zosiyana kwambiri pamene iye anakhala limodzi ndi anthu ochimwa m’dziko loipali. (Maliko 7:20-23) Yesu anafunika kupirira chifukwa cha mpikisano womwe unalipo ngakhale pakati pa ophunzira ake amene anali kuwakonda kwambiri. (Luka 20:46; 22:24) N’zoonadi, iye anachita bwino kwambiri pa chilichonse chimene anakumana nacho padziko lapansi.
5 Yesu sanayambe kulankhula chinenero cha anthu m’njira yozizwitsa, koma anachita kuphunzira kuyambira ali mwana. Apatu, zinthu zinasintha kwambiri chifukwa poyamba anali kutsogolera angelo kumwamba. Ali pa dziko lapansi, Yesu anali kulankhula chimodzi mwa zinenero kapena kuti “malilime a anthu.” Ndipo chinenero chimenechi chinali chosiyaniranatu ndi ‘malilime a angelo.’ (1 Akor. 13:1) Koma palibe munthu amene analankhula mawu okopa kuposa Yesu.—Luka 4:22.
6 Taganizirani zinthu zina zimene zinasintha kwambiri pamoyo wa Mwana wa Mulungu atabwera padziko lapansi. Ngakhale kuti Yesu sanatengere uchimo kwa Adamu, Iye anakhala ngati munthu, mofanana ndi amene anali kudzakhala “abale” ake, kapena kuti otsatira ake odzozedwa. (Werengani Aheberi 2:17, 18.) Pa usiku womaliza ali pa dziko lapansi, Yesu sanapemphe Atate ake a kumwamba kuti atumize “magulu ankhondo oposa 12 a angelo.” Tangoganizani za angelo amene iye anali ndi ulamuliro pa iwo, monga Mikayeli Mkulu wa Angelo. (Mat. 26:53; Yuda 9) N’zoona kuti Yesu anachita zozizwitsa, koma zimene anachita padziko lapansi zinali zochepa poyerekezera ndi zimene akanatha kuchita kumwamba.
7. Kodi Ayuda anachita chiyani ndi Chilamulo?
7 Yesu asanabwere padziko lapansi anali “Mawu,” ndipo zikuoneka kuti pamene Mulungu ankatsogolera Aisiraeli m’chipululu, iye anali Wom’lankhulira. (Yoh. 1:1; Eks. 23:20-23) Aisiraeliwo ‘analandira Chilamulo kudzera kwa angelo, koma sanachisunge.’ (Mac. 7:53; Aheb. 2:2, 3) Ndipo atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda m’zaka za zana loyamba, analephera kuzindikira cholinga chenicheni cha Chilamulo. Mwachitsanzo, taganizirani za lamulo lokhudza Sabata. (Werengani Maliko 3:4-6.) Alembi ndi Afarisi ‘ananyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.’ (Mat. 23:23) Ngakhale zinali choncho, Yesu sanataye mtima n’kusiya kulengeza choonadi.
8. N’chifukwa chiyani Yesu amatha kutithandiza?
8 Yesu anali ndi mtima wodzipereka. Iye anali kukonda anthu kwambiri ndipo anafunitsitsa kuwathandiza. Sanasiye kukhala ndi mtima wokonda kulalikira. Ndipo chifukwa chokhala wokhulupirika kwa Yehova ali pa dziko lapansi, Yesu “anakhala ndi udindo wopereka chipulumutso chamuyaya kwa onse omumvera.” Ndiponso, “popeza kuti iye mwini anavutika poyesedwa, amatha kuthandiza iwo [anthu monga ife] amene akuyesedwa.”—Aheb. 2:18; 5:8, 9.
Mphunzitsi Wophunzitsidwa Bwino
9, 10. Kodi Yesu analandira maphunziro otani asanabwere pa dziko lapansi?
9 Akhristu a masiku ano asanatumizidwe monga amishonale, Bungwe Lolamulira limakonza kuti iwo aphunzitsidwe. Kodi Yesu Khristu nayenso anaphunzitsidwa? Inde, koma sikuti anachita kupita ku sukulu za Arabi asanadzozedwe kukhala Mesiya kapena kuphunzira pa mapazi a atsogoleri otchuka a chipembedzo. (Yoh. 7:15; yerekezerani ndi Machitidwe 22:3.) Nanga n’chifukwa chiyani Yesu anali mphunzitsi wodziwa bwino ntchito yake?
10 Ngakhale kuti Yesu anaphunzitsidwa zinthu zina ndi mayi ake Mariya komanso bambo ake omulera Yosefe, iye anaphunzira zinthu zofunika kwambiri pa utumiki wake kwa Mphunzitsi wapamwamba kwambiri. Pankhani imeneyi, Yesu anati: “Sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumayo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.” (Yoh. 12:49) Onani kuti Mwanayo anapatsidwa malangizo a zimene anayenera kuphunzitsa. Asanabwere pa dziko lapansi, mosakayikira Yesu anakhala akulandira malangizo kwa Atate ake kwa nthawi yaitali. Kodi pali maphunziro amene iye akanalandira oposanso amenewa ngati?
11. Kodi Yesu anasonyeza motani mtima umene Atate ake anali nawo kwa anthu?
11 Kuyambira pamene analengedwa, Mwanayo anali pa ubale wabwino kwambiri ndi Atate ake. Nthawi yonseyo asanakhale munthu padziko lapansi, Yesu anazindikira mtima umene Mulungu anali nawo kwa anthu mwa kuona mmene Yehova anachitira ndi anthuwo. Mofanana ndi Mulungu, Mwanayo anali ndi chikondi chachikulu pa anthu. N’chifukwa chake iye, monga nzeru yolankhula ngati munthu, anati: ‘Ndinali kusekerera ndi ana a anthu.’—Miy. 8:22, 31.
12, 13. (a) Kodi Yesu anaphunzira chiyani poona mmene Atate ake anachitira ndi Aisiraeli? (b) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito motani zimene anaphunzira?
12 Maphunziro amene Mwanayo analandira, anaphatikizaponso kuona mmene Atate ake anachitira panthawi yovuta. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yehova anachitira ndi Aisiraeli opulupudza. Lemba la Nehemiya 9:28 limati: “Atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu [Yehova]; chifukwa chake munawasiya m’dzanja la adani awo amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva m’Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu.” Popeza anagwira ntchito limodzi ndi Yehova n’kuona zimene anali kuchita, Yesu nayenso anaphunzira kukhala wachifundo kwa anthu m’dera limene analalikira.—Yoh. 5:19.
13 Yesu anagwiritsa ntchito zimene anaphunzirazo pochitira chifundo ophunzira ake. Usiku wakuti mawa lake aphedwa, atumwi ake onse amene anawakonda kwambiri, “anamusiya yekha ndi kuthawa.” (Mat. 26:56; Yoh. 13:1) Mtumwi Petulo anachita kukana Khristu katatu. Ngakhale zinali choncho, Yesu anaperekabe mpata wakuti atumwi akewo abwerere kwa iye. Anati kwa Petulo: “Ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe; chotero iwenso, pamene ubwerera, ukalimbikitse abale ako.” (Luka 22:32) Isiraeli wauzimu wamangidwa bwinobwino pamaziko a “atumwi ndi aneneri,” ndipo miyala ya maziko a linga la Yerusalemu Watsopano ili ndi mayina a atumwi 12 okhulupirika a Mwanawankhosa, Yesu Khristu. Mpaka lero, Akhristu odzozedwa limodzi ndi anzawo odzipereka a “nkhosa zina,” akupita patsogolo monga gulu lolalikira za Ufumu, mothandizidwa ndi dzanja lamphamvu la Mulungu ndi utsogoleri wa Mwana wake wokondedwa.—Aef. 2:20; Yoh. 10:16; Chiv. 21:14.
Kaphunzitsidwe ka Yesu
14, 15. Kodi kaphunzitsidwe ka Yesu kanasiyana bwanji ndi ka alembi ndi Afarisi?
14 Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji zimene anaphunzira pophunzitsa otsatira ake? Tikayerekeza kaphunzitsidwe ka Yesu ndi ka atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda, timaona bwino lomwe kuti kaphunzitsidwe ka Yesu kanali kapamwamba kwambiri. Alembi ndi Afarisi ‘anasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha mwambo wawo.’ Koma zimene Yesu anali kulankhula, sizinali za m’maganizo mwake. Iye anali kuphunzitsa mawu, kapena kuti uthenga wa Mulungu. (Mat. 15:6; Yoh. 14:10) Zimenezi ndi zimene ifenso tiyenera kuchita.
15 Pali chinthu chinanso chimene chinasiyanitsa Yesu ndi atsogoleri a chipembedzo. Pofotokoza za alembi ndi Afarisi, iye anati: “Zilizonse zimene angakuuzeni, chitani ndi kuzitsatira, koma musamachite zimene iwo amachita, chifukwa iwo amangonena koma osachita.” (Mat. 23:3) Yesu anali kuchita zimene anali kuphunzitsa. Tiyeni tione chitsanzo chotsimikizira mfundo imeneyi.
16. Kodi inu mukutsimikiza bwanji kuti Yesu anatsatira zimene ananena pa Mateyo 6:19-21?
16 Yesu analimbikitsa ophunzira ake ‘kukundika chuma kumwamba.’ (Werengani Mateyo 6:19-21.) Kodi Yesuyo anatsatiradi mfundo imeneyi? Inde, n’chifukwa chake anatha kunena moona mtima za iye mwini kuti: “Nkhandwe zili nawo mapanga ndipo mbalame za m’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamiritsa mutu wake.” (Luka 9:58) Yesu sanafune zinthu zambiri pamoyo wake. Mtima wake wonse unali pa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo anasonyeza mmene moyo umakhalira wopanda nkhawa ngati munthu sakukundika chuma padziko lapansi. Yesu anasonyeza kuti ndi bwino kukundika chuma kumwamba, “kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole ndi kuba.” Kodi inu mukutsatira malangizo a Yesu okundika chuma kumwamba?
Makhalidwe a Yesu Omwe Anachititsa Kuti Anthu Amukonde
17. Kodi Yesu anali mlaliki wapadera chifukwa cha makhalidwe otani?
17 Kodi ndi makhalidwe otani amene anachititsa kuti Yesu akhale mlaliki wapadera? Mwa zina, ndi mtima umene anasonyeza kwa anthu amene anawathandiza. Makhalidwe ena a Yehova amene Yesu anatengera anali kudzichepetsa, chikondi ndi chifundo. Tiyeni tione mmene makhalidwe amenewa anakopera anthu ambiri kuti ayambe kukonda Yesu.
18. N’chifukwa chiyani tikunena kuti Yesu anali wodzichepetsa?
18 Atavomera kubwera pa dziko lapansi, Yesu “anakhuthula zonse za mwa iye n’kukhala ngati kapolo, nakhala wofanana ndi anthu.” (Afil. 2:7) Kumeneko kunali kudzichepetsadi. Ndiponso Yesu sanaderere munthu aliyense. Iye analibe mtima wakuti, ‘Pajatu ine ndinachokera kumwamba, ndiye muzindimvera.’ Mosiyana ndi amesiya onyenga, Yesu sanadzitame kapena kulengeza kwa anthu onse kuti iye ndiye Mesiya weniweni. Nthawi zina anali kuuza anthu kuti asanene kuti iye ndani kapena kuulula zimene wachita. (Mat. 12:15-21) Yesu anafuna kuti anthu asankhe okha kumutsatira malinga ndi zimene eni akewo anaona. Ophunzira ake anali odala kwambiri chifukwatu Mbuye wawo sanawayembekezere kukhala ngati angelo angwiro amene iye anakhala nawo kumwamba.
19, 20. Kodi chikondi ndi chifundo zinamulimbikitsa bwanji Yesu kuthandiza anthu?
19 Yesu Khristu anasonyezanso chikondi, lomwe ndi khalidwe lalikulu la Atate ake akumwamba. (1 Yoh. 4:8) Yesu anali kuphunzitsa anthu chifukwa chowakonda. Mwachitsanzo, taganizirani mmene anakhudzidwira mtima ndi wolamulira wachinyamata. (Werengani Maliko 10:17-22.) Yesu “anam’konda” ndipo anafuna kumuthandiza, koma wolamulira wachinyamatayo sanafune kusiya chuma chake chonse kuti akhale wotsatira wa Khristu.
20 Khalidwe lina la Yesu limene linachititsa kuti anthu amukonde linali chifundo. Mofanana ndi anthu ena onse opanda ungwiro, anthu omwe anamvetsera zimene iye anali kuphunzitsa anali olemedwa ndi mavuto. Podziwa zimenezi, Yesu anawaphunzitsa mwachifundo. Mwachitsanzo, tsiku lina Yesu ndi atumwi ake anatanganidwa kwambiri ndipo analibe nthawi ya kudya. Koma kodi Yesu anachita chiyani ataona kuti khamu la anthu lasonkhana? “Anawamvera chifundo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:34) Yesu anaona moyo womvetsa chisoni umene anthu anali nawo m’dera limene analalikira ndipo anachita khama kuwaphunzitsa ndi kuchita zozizwitsa kuti awathandize. Ena anakopeka ndi makhalidwe ake abwino, anakhudzidwa ndi mawu ake ndipo anakhala ophunzira ake.
21. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
21 Pali zinthu zinanso zambiri zimene tingaphunzire zokhudza utumiki wa Yesu padziko lapansi. Nkhani yotsatira idzafotokoza zimenezi. Kodi ndi njira zinanso ziti zimene tingatsanzire Yesu Khristu, Mmishonale woposa amishonale onse?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Yesu analandira maphunziro otani asanabwere pa dziko lapansi?
• Kodi kaphunzitsidwe ka Yesu kanali kosiyana motani ndi ka alembi ndi Afarisi?
• Kodi anthu anakonda Yesu chifukwa cha makhalidwe otani?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi Yesu anali kuphunzitsa anthu motani?