Yendani ‘M’njira Yoongoka’
“KUDZAM’KOMERA iye [wolungama]; chifukwa oterowo adzadya zipatso za machitidwe awo,” anatero mneneri Yesaya. Iye anatinso: “Njira ya wolungama ili njira yoongoka.” (Yesaya 3:10; 26:7) Inde, kuti zochita zathu zikhale zaphindu, tiyenera kuchita zolungama pamaso pa Mulungu.
Komabe, kodi tingatani kuti tiyende m’njira yoongoka? Kodi tingapindule chiyani ngati tichita zimenezo? Ndipo kodi ena angapindule motani ngati titsatira miyezo yolungama ya Mulungu? Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inayankha mafunso ameneŵa m’chaputala 10 cha buku la m’Baibulo la Miyambo. M’chaputala chimenechi, mfumuyo ikufotokoza kusiyana kwa wolungama ndi woipa. Pochita zimenezo, inagwiritsa ntchito mawu akuti “wolungama” kapena “olungama” nthaŵi 13. Mawuŵa akupezeka nthaŵi zisanu ndi zinayi m’mavesi 15 mpaka 32. Choncho, kupenda Miyambo 10:15-32 kukhala kolimbikitsa.a
Mverani Malangizo
Solomo akufotokoza kufunika kwa chilungamo. Anati: “Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphaŵi wawo uwononga osauka. Ntchito za wolungama zipatsa moyo; koma phindu la oipa lichimwitsa.”—Miyambo 10:15, 16.
Chuma chingatchinjirize kumavuto ena amene angagwe mwadzidzidzi, monga momwe tauni yam’mpanda nthaŵi zina imatchinjirizira anthu amene akukhalamo. Ndipo umphaŵi ungakhale wopweteka pakagwa vuto mwadzidzidzi. (Mlaliki 7:12) Komabe, mfumu yanzeruyo inalangizanso za ngozi zokhudza chuma ndi umphaŵi womwe. Munthu wolemera angamakhulupirire chuma chake chokha basi, n’kumaganiza kuti zinthu zamtengo wapatali zimene ali nazozo ndizo “khoma lalitali.” (Miyambo 18:11) Nayenso munthu wosauka angamaganize molakwika kuti alibe tsogolo lililonse chifukwa cha umphaŵi wakewo. Motero, onsewo amalephera kukondweretsa Mulungu.
Koma munthu amene achita zolungama, kaya ndi wosauka kapena wolemera, adzapeza moyo. Motani? Iye amakhutira ndi zomwe ali nazo. Salola kuti kulemera kwake kapena kusauka kwake kusokoneze zochita zake zabwino pamaso pa Mulungu. Zimene munthu wolungama amachita, kaya ndi wolemera kapena wosauka, zimam’bweretsera chimwemwe pakalipano ndiponso amayembekeza moyo wosatha m’tsogolo. (Yobu 42:10-13) Munthu woipa samapindula kanthu ngakhale akhale ndi chuma. Amagwiritsa ntchito chumacho kuchitira ntchito zauchimo m’malo moti achigwiritse ntchito moyenera monga chotchinjirizira ndi kuchita zimene Mulungu akufuna.
Mfumu ya Israyeli inapitiriza kuti: “Wosunga mwambo [“Amene amvera malangizo,” NW] ali m’njira ya moyo; koma wosiya chidzudzulo asochera.” (Miyambo 10:17) Katswiri wa Baibulo wina ananena kuti vesi limeneli lingakhale ndi matanthauzo aŵiri. Tanthauzo loyamba lingakhale lakuti munthu amene amvera malangizo ndi kuchita chilungamo ali panjira ya moyo, pamene wosiya chidzudzulo wasochera panjira imeneyo. Tanthauzo lachiŵiri n’lakuti “amene amamvera malangizo amaonetsa njira ya moyo [kwa ena chifukwa amapindula ndi chitsanzo chake chabwino], koma amene amakana kum’dzudzula amasocheretsa ena.” (Miyambo 10:17, New International Version) M’mbali zonse ziŵirizi, n’kofunikatu kumvera malangizo ndi kuvomera kudzudzulidwa!
Khalani ndi Chikondi M’malo mwa Udani
Kenaka Solomo anafotokoza mwambi wa mbali ziŵiri koma ganizo lake n’lofanana. Mbali yachiŵiri ikuthandizira mbali yoyamba. Akuti: “Wobisa udani ali ndi milomo yonama.” Ngati munthu amadana ndi mnzake ndiyeno n’kumabisa udaniwo mwa kulankhula mawu abwino kapena osyasyalika, ndiye kuti akuchita chinyengo—ali ndi “milomo yonama.” Pamfundo imeneyi, mfumu yanzeruyo inawonjezera kuti: “Wonena ugogodi ndiye chitsiru.” (Miyambo 10:18) Anthu ena, m’malo mobisa udani wawo, amam’nenera zabodza munthu amene akumudayo kapena kufalitsa nkhani zom’nyoza. Kumeneku n’kupusa chifukwa nkhani yabodzayo singamusinthe munthu amene akum’namizirayo. Ndiponso, munthu amene akumvetsera nkhaniyo mosamala adzalizindikira dumboli ndipo sangam’lemekezenso wabodzayo. Motero, munthu amene akufalitsa mbiri yoipayo amadzivulaza yekha.
Njira yabwino ndiyo kupeŵa chinyengo ndiponso kufalitsa nkhani zonamizira wina. Mulungu anawauza Aisrayeli kuti: “Usamamuda mbale wako mumtima mwako.” (Levitiko 19:17) Ndipo Yesu anawalangiza amene anali kumumvetsera kuti: “Kondanani nawo [ngakhale] adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:44, 45) N’kwabwinotu kwambiri kudzaza mitima yathu ndi chikondi m’malo mwa udani!
‘Khalani Chete’
Potsindika kufunika kolamulira lilime, mfumu yanzeruyo inati: “Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.”—Miyambo 10:19.
“Chitsiru chichulukitsanso mawu.” (Mlaliki 10:14) M’kamwa mwake “mutsanulira utsiru.” (Miyambo 15:2) Zimenezi sizikutanthauza kuti munthu aliyense wokonda kulankhulalankhula ndi chitsiru. Komatu, munthu wokonda kulankhula kwambiri n’kosavuta kuti afalitse miseche kapena nkhani yabodza. Kulankhula kopusa kungawononge mbiri ya munthu, kukhumudwitsa ena, kuwononga ubale, ndiponso ngakhale kuvulaza mwakuthupi. “Pochuluka mawu, uchimo susoŵapo.” (Miyambo 10:19, An American Translation) Ndiponso, n’zosasangalatsa kukhala ndi munthu amene amayankhira nkhani iliyonse. Tiyenitu tisachulutse mawu.
Kuphatikiza pa kupeŵa kunama, munthu amene amakhala chete amachita mwanzeru. Amaganiza kaye asanalankhule. Amalingalira mmene mawu akewo adzakhudzira anthu ena. Kukonda kwake miyezo ya Yehova ndiponso kufunitsitsa kwake kuti athandize anthu anzake kumam’limbikitsa kuchita zimenezo. Mawu ake amakhala achikondi ndiponso achifundo. Amasinkhasinkha mmene angalankhulire zogwira mtima ndiponso zothandiza. Mawu ake ali ngati “zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.” Nthaŵi zonse amalankhula mwaluso ndiponso moyenera.—Miyambo 25:11.
‘Dyetsani Ambiri’
Solomo anapitiriza kuti: “Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika; koma mtima wa oipa uli wachabe.” (Miyambo 10:20) Wolungama amalankhula zabwino—monga siliva wosankhika kapena woyengeka amene alibe chodetsa. N’zimenetu atumiki a Yehova akuchita pamene akufalitsa kwa ena uthenga wopulumutsa moyo umene uli m’Mawu a Mulungu. Mlangizi wawo Wamkulu, Yehova Mulungu, wawaphunzitsa ndipo ‘wawapatsa lilime la ophunzira, kuti adziŵe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema.’ (Yesaya 30:20; 50:4) Inde, lilime lawo lili ngati siliva wosankhika pamene likulankhula choonadi cha Baibulo. Mawu awo ndi amtengo wapatalitu kwambiri kwa anthu oona mtima kuposa zolinga za munthu woipa. Tiyeni tikhale ofunitsitsa kulankhula za Ufumu wa Mulungu ndi ntchito zake zodabwitsa.
Wolungama amakhala dalitso kwa anthu amene akukhala naye. Solomo anapitiriza kuti: “Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri; koma zitsiru zimafa posoŵa nzeru.”—Miyambo 10:21.
Kodi ‘wolungama amadyetsa ambiri’ motani? Liwu la Chihebri limene analigwiritsa ntchito pano limatanthauza “kuchita ubusa.” Ndiko kutsogolera ndi kudyetsa, mofanana ndi mmene mbusa wakale anali kusamalilira nkhosa zake. (1 Samueli 16:11; Salmo 23:1-3; Nyimbo ya Solomo 1:7) Munthu wolungama amatsogolera anthu kunjira yolungama ndipo zimene amalankhula zimadyetsa bwino amene akumumvetsera. Zotsatira zake n’zakuti anthuwo amakhala achimwemwe ndi okhutira, ndiponso angalandire moyo wosatha.
Nanga bwanji za chitsiru? Popeza alibe nzeru, zolinga zake n’zoipa ndipo saganiza kuti zimene akuchita zikhala ndi zotsatirapo zotani. Munthu wotero amangochita zimene akufuna basi, osadziŵa zotsatira zake. Motero, amavutika ndi zinthu zoŵaŵa zimene zimabwera chifukwa cha zochita zakezo. Wolungama amathandiza ena kuti akhale ndi moyo koma munthu wosoŵa nzeru sangakhale ndi moyo ngakhale iye mwini.
Peŵani Khalidwe Loipa
Nthaŵi zambiri, zimene munthu amakonda ndi zimene sakonda zimam’dziŵikitsa kuti iye ndi wotani. Pofotokoza mfundo imeneyi, mfumu ya Israyeli inati: “Maseŵero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa; koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.”—Miyambo 10:23.
Anthu ena amaona khalidwe loipa ngati maseŵera ndipo amachita zoipazo pofuna kungosangalala. Anthu oterowo sasamala zoti aliyense adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu, ndipo sazindikira n’komwe kuti zimene akuchitazo n’zoipa. (Aroma 14:12) Maganizo awo amapotoka kufika poganiza kuti Mulungu sakuona zolakwa zimene akuchitazo. Mwa zochita zawozo, amakhala akunena kuti: “Kulibe Mulungu.” (Salmo 14:1-3; Yesaya 29:15, 16) Kumeneko n’kupusa kwambiri!
Koma munthu wozindikira samaona khalidwe loipa kukhala maseŵera. Amadziŵa kuti Mulungu amaipidwa nalo ndipo lingawononge ubale wa munthuwe ndi Iye. N’kupusatu kuchita khalidwe loipali chifukwa limam’chotsera munthu ulemu, limathetsa mabanja, limavulaza maganizo ndi thupi, ndiponso moyo wauzimu wa munthuyo umawonongeka. N’kwanzeru kupeŵa khalidwe loipa ndi kukonda kwambiri nzeru monga mlongo wokondeka.—Miyambo 7:4.
Mangani Pamaziko Abwino
Pofotokoza kufunika koti munthu amange moyo wake pamaziko abwino, Solomo anati: “Chomwe woipa achiopa chidzam’fikira; koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa. Monga kavuluvulu angopita, momwemo woipa kuli zi; koma olungama ndiwo maziko osatha.”—Miyambo 10:24, 25.
Munthu woipa angaopseze anthu ena. Koma pamapeto pake, zimene iye amaziopa zimam’fikira. Ali ngati nyumba yosalimba imene imagwa ikawombedwa ndi mphepo yamkuntho chifukwa sanamange maziko ake pakhalidwe lolungama. Amagwa akakumana ndi mavuto. Koma wolungama ali ngati munthu amene amachita mogwirizana ndi mawu a Yesu. Iye ndiye “munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.” Yesu anati: “Ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinawomba mphepo, zinagunda panyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.” (Mateyu 7:24, 25) Munthu wotero ndi wolimba. Zimene amaganiza ndi kuchita zimachokera pa mfundo zachikhalidwe za Mulungu.
Mfumu yanzeruyo isanapitirize kufotokoza kusiyana pakati pa woipa ndi wolungama, inapereka chenjezo lalifupi koma lofunika kwambiri. Inati: “Ngati vinyo woŵaŵa m’mano, ndi utsi m’maso, momwemo waulesi kwa iwo amene amtuma.” (Miyambo 10:26) Vinyo woŵaŵa amapwetekadi m’mano. Asidi amene amakhala mu vinyo wotereyu amachititsa kuti azimveka ngati wosasa ndipo munthu angamve kupweteka m’mano. Nawonso utsi umapweteka m’maso. Motero, amene alemba ntchito munthu waulesi kapena kuuza munthu wotereyu kuwaimira m’malo mwawo, adzakhumudwa ndipo chuma chawo chidzawonongeka.
“Njira ya Yehova Ndi Linga”
Mfumu ya Israyeli inapitiriza kuti: “Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha. Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe; koma chidikiro cha oipa chidzawonongeka.”—Miyambo 10:27, 28.
Mantha aumulungu amam’tsogolera munthu wolungama ndipo amayesetsa kuti zimene akuganiza, kulankhula, ndi kuchita zikondweretse Yehova. Mulungu amam’samalira munthu woteroyo ndipo amakhutiritsa zofuna zake zolungama. Koma woipa samvera Mulungu. Nthaŵi zina zofuna zake zingaoneke ngati zikukhutiritsidwa. Komatu zimatero kwakanthaŵi chabe chifukwa munthu wotero kaŵirikaŵiri amafa msanga chifukwa cha chiwawa kapena matenda amene amabwera chifukwa cha zochita zake. Pomwalira, zonse zimene anali kuyembekezera zimathera pomwepo.—Miyambo 11:7.
“Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima; koma akuchita zoipa adzawonongeka,” anatero Solomo. (Miyambo 10:29) Njira ya Yehova pano ikutanthauza mmene Mulungu amachitira ndi anthu osati njira yamoyo imene tiyenera kuyendamo. Mose anati: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo [“chilungamo,” NW].” (Deuteronomo 32:4) Njira zolungama za Mulungu zimatetezera olungama ndi kuwononga oipa.
Ndithudi, Yehova ndi linga kwa anthu ake. “Wolungama sadzachotsedwa konse; koma oipa sadzakhalabe m’dziko. M’kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru; koma lilime lokhota lidzadulidwa. Milomo ya wolungama idziŵa zokondweretsa; koma m’kamwa mwa oipa munena zokhota.”—Miyambo 10:30-32.
Olungama zinthu zimawayenderadi bwino ndipo amadalitsidwa chifukwa choyenda m’njira yoongoka. Inde, “madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.” (Miyambo 10:22) Ndiyetu tiyeni tionetsetse kuti tikutsatira mfundo zachikhalidwe za Mulungu pamene tikuchita china chilichonse. Tisamalenso kalankhulidwe kathu ndi kugwiritsa ntchito lilime lathu kuwadyetsa anthu choonadi chopulumutsa moyo chimene chili m’Mawu a Mulungu ndi kuwatsogolera kunjira yolungama.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2001, masamba 24-7. Pamenepo tinafotokoza mwatsatanetsatane Miyambo 10:1-14.
[Chithunzi patsamba 26]
Lilime lingafanane ndi “siliva wosankhika”