Okonzekeretsedwa Kaamba ka Utumiki Waumishonale m’ma 1990
NYENGO yapadera ikuyambika kaamba kautumiki waumishonale. Pokhala mipata yamwaŵi ikutseguka mzigawo zatsopano zambiri, Mboni za Yehova zokhulupirika zonse nzofunitsitsa kuchita ntchito yowonjezereka yaikuludi.
Chotero chinali chikhumbo chofulumizidwa ndi changu chimene ophunzira 24 a kalasi ya 89 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower anapezeka nacho pa programu yawo yomaliza maphunziro imene inachitika pa September 9, 1990. Gulu la nthumwi zoitanidwa zoposa 5,000 ndi ziŵalo za banja la Beteli anasonkhana kaamba ka kumaliza maphunziro kwa amishonale atsopanowa, omwe anali atagawiridwa kale ku maiko khumi. Ngakhale kuti inachitikira pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova mu Mzinda wa Jersey, New Jersey, programu yonseyi inamvedwanso ndi omwe anasonkhana pa Beteli ya ku Brooklyn, Watchtower Farms, ndi pa Likulu la Maphunziro la Watchtower pa Patterson, New York.
Mosataya nthaŵi pa 10:00 mmawa, Theodore Jaracz, chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi yemwenso anali tcheyamani watsikulo, anaitanira nyimbo yotsegulira. Chotsatira, pemphero linaperekedwa ndi Arthur Worsley wa banja la Beteli la ku Brooklyn. Kenaka tcheyamani analozera ku Machitidwe 10:33, pomwe kenturiyo Korneliyo Wachiroma anati kwa Petro: “Tiri tonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.” Kunazindikiridwa kuti zochitika za m’mbiri zomwe zinkachitika m’masiku a Petro zinkatsegulira njira mbiri yabwino kuti ilengezedwe kwa anthu a mitundu yonse.
Philip D. Wilcox, wa ku Watchtower Farms, anapereka yoyamba ya nkhani zochititsa chidwi zisanu ndi ziŵiri. Poizika pa Afilipi 4:7, iye anasankha mutu wake kukhala wakuti “Lekani Mtendere wa Mulungu Ukuthandizeni m’Gawo Lanu.” Iye anati: “Yehova Mulungu ndiye Magwero a mtendere weniweni wonse. Iye amasangalala ndi mtendere kotheratu, kapena kuti mokwanira, ndipo samakanthidwapo ndi kuda nkhawa kotsendereza kulikonse, kuchititsidwa kakasi, kapena kusokonezeka maganizo. Kuwonjezera apa, pali bata ndi mtendere pamalo onse owala a Yehova pampando wake wachifumu, monga momwe zasonyezedwera ndi utawaleza wobiriŵira ngati emalodi wowonedwa ndi Yohane m’masomphenya. (Chibvumbulutso 4:2, 3) Mtendere wake umafutukulidwiranso kunja kwa anthu onse omwe adzalola kuthandizidwa nawo. Kodi mudzaulola?” Mbale Wilcox anagogomezera zithandizo zofunika ziŵiri, pemphero ndi kufunitsitsa kuyembekeza pa Yehova. (Mika 7:7; Afilipi 4:6) Iye anati, palibe chinthu chimene Mulungu wachilola chimene chingatibweretsere chivulazo chokhalirira.
Lloyd Barry, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, anatsatira ndi mutu wakuti “Dzimwetuliranibe.” Iye anayamba ndi mawu akuti, “Kuseka ndiko mankhwala abwino.” Iye anawakumbukira mawuwa chifukwa chakuti kumbuyoko mu 1955 ndiwo anali mutu wapachikuto cha kope loyamba la magazini a Galamukani! m’chinenero cha Chijapan. Koma kodi nkuseka kwamtundu wanji? Uku sindiko ‘kuseka kwa chitsiru’ kwaphokoso, ndi kopanda pake. (Mlaliki 7:6) Mmalomwake, iko ndiko kuseka kosangalala, kwaphee kwa amishonale ndi ena omwe amalabadira chiitano cha Davide cha ‘kusekerera mwa Yehova.’ (Salmo 32:11) Mbale Barry anati mosasamala kanthu za ziyeso zokakala, Yobu anamwetulirabe, pakuti anadziŵa kuti ankasunga umphumphu kwa Mulungu. Amishonale omwe ngolimba nji mosasamala kanthu ndi zokumana nazo zobweretsa chiyeso monga cha Yobu adzalandira madalitso ambiri kumapeto ake. (Yobu 29:24; 42:12) Mlankhuliyu anamaliza naati: “Khalani otanganitsikabe, khalani omwetulirabe, ndipo nanunso mudzapeza kumwetulira kosatha kwa chivomerezo cha Yehova.”
Mlankhuli wotsatira anali Richard E. Abrahamson, yemwe anasankha mutu wakuti “Kufatsa Kwanu Kuzindikirike ndi Anthu Onse,” wozikidwa pa Afilipi 4:5. Mogwirizana ndi tanthauzo la Chigiriki, liwu lakuti “kufatsa” lingatanthauze “kupirira.” Amishonale ena akhala nawo mavuto kwakukulukulu chifukwa cha kukhala okonda zinthu zapamtima pawo basi. Wina anakhumudwitsidwa ndinjira imene mmishonale mnzake ananyemera chidutswa cha tchizi pagome lodyera. Pambuyo pa zaka 22 zautumiki waumishonale, yemwe anakhumudwitsidwayo anazindikira kuti mavuto ambiri amayambira pa tinthu tating’ono kwambiri monga mmene munthu amanyemera tchizi. Mlankhuliyo analangiza kuti: “Phunzirani kugwirizana ndi masinthidwe, mofanana ndi mtengo m’mphepo yanamondwe. Kupirira kumabweretsa madalitso ambiri, monga ngati kukhala wokhoza kupirira ziyeso ndikumamatira ku chigawo cha munthuwe ndi mtendere wamaganizo.”
Milton G. Henschel, wa Bungwe Lolamulira, anafotokoza pamutu wakuti “Khomo Lalikulu Lotsogolera Kuntchito Nlotseguka.” Mbale Henschel anadziŵitsa kuti Yesu anakonda anthu, nawamverera chifundo, ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri. Ali ku Efeso mtumwi Paulo anawalembera motere Akorinto: ‘Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.’ (1 Akorinto 16:8, 9) Mosasamala kanthu za chitsutsocho, Paulo anaphunzitsa m’nyumba za sukulu ya Turano kwazaka ziŵiri, kwakuti uthenga Waufumu unamvedwa m’chigawo chonse cha Asia. (Machitidwe 19:9, 10) Khomo lotsegukalo linatsogolera ku chipambano cha kulalikira kwakeko. Mpingo wa ku Efeso unkagwirabe ntchito kumapeto kwa zaka za zana loyamba.—Chibvumbulutso 2:1-7.
Jack D. Redford, mlangizi wa Gileadi, analankhula pa mutu wakuti “Dziyeseni Nokha.” (2 Akorinto 13:5) Amishonale a Gileadi atsegula minda yatsopano ndikulimbikitsa mipingo yopangidwa kale, napirira kwambiri ndikutsutsa nyambo zimene Mdyerekezi watchera kuti awapatutse. Ndipo atsopano akugwirizana nawobe. Mwa kufotokoza zokumana nazo zochititsa nthumanzi ziŵiri, mlangiziyo anafotokoza mwafanizo mmene kuliri kofunika kuyesa chikhulupiriro cha munthuwe. Mmishonale wina anataikiridwa mwaŵi wake pamene modzitukumula ananyalanyaza uphungu wa chenjezo lonena za njira yolakwika. Mosiyana, wina anakhalabe m’gawo lake ndi chisangalalo, chinkana kuti m’miyezi yake itatu yoyambirira ali konko, anaonda kukhala mafupa okhaokha kochititsidwa ndi matenda amene anatulukaponso kuthothoka kwa tsitsi lake ndikukhala gonthi. Pambuyo pa zaka 42 iye adakali konko ndipo, kupyolera m’maphunziro a Baibulo, wathandiza anthu 156 kubatizidwa. Mbale Redford anamaliza naati: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani. Musazidye nyambo zake. Pitirizani kutsimikizira amene inuyo muli. Yehova adzakusamalirani.”
Chotsatira, mlangizi winanso, Ulysses V. Glass, analankhula pamutu wakuti ‘Nzeru Iri Ndi Odzichepetsa.’ (Miyambo 11:2) Iye anagwiritsira ntchito koloko yapadzanja yokhala ndi batili yopatsidwa mphamvu ndi dzuwa kuti afotokoze mwafanizo kuti kuunika kwa Mawu a Mulungu kungatisungebe kukhala “amphamvu.” “Koma,” iye anamveketsa kuti, “chidziŵitso chokha sichimapatsa nzeru. Kudzichepetsa kumafunikiranso kwa Mulungu.” (Mika 6:8) Kudzichepetsa kudzatitsogolera kuwopa Mulungu, ndipo ‘chiyambi cha nzeru ndicho kuwopa Yehova.’ (Miyambo 9:10) Zowona, tiyenera kuganizira chinthu china kwa ife; kudzimana kungakhale kwakupha. Yehova wapereka maluso apadera kwa ena, monga mmene anachitira pomanga guwa lansembe, koma kukhulupirika kodzichepetsa kuyenera kugwiriridwapo ntchito. “M’nyengo ya kuphunzira,” Mbale Glass anaifotokozera tero kalasiyo, “munapereka umboni wa kudalirika ndiulemu. Sonyezani kukhulupirika kofananaku mntchito yanu, ndipo Mulungu adzakudalitsani.”
Albert D. Schroeder, wa Bungwe Lolamulira, anapereka mutu wosonyezedwawo wakuti “Okonzekeretsedwa Bwino Kaamba ka Utumiki Waumishonale m’ma 1990.” Iye anayamba motere: “Ma 1990 ayamba kale ndi chiyambi chadzawoneni. Maiko ambiri a Kum’mawa kwa Yuropu agwedezedwa. Miyezi yowerengeka yapitayo Khoma la Berlin linatsegulidwa. The New York Times inali ndi mutu wakuti: ‘August 1990, Mwezi Umene Unagwedeza Dziko.’ Chotero, inu omaliza maphunziro mukukhala ndi moyo m’nthaŵi yogwedezadi. Kodi kuphunzira kwanu kwa miyezi isanu kwakukonzekeretsani kaamba ka iyo? Mosapita m’mbali, inde!” Kenaka iye anatchula mbali zina zothandiza za New World Translation of the Holy Scriptures—With References ndi mmene kuliphunzira kwapangitsira Mawu a Mulungu kukhala amoyo. Chipangizo china champhamvu chimene chakonzekeretsa ophunzira ndicho “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” yomwe tsopano inakonzedwa chatsopano mu 1990. Bukhu laposachedwapa la Mankind’s Search for God liyeneranso kukhala thandizo lamphamvu kwa amishonale. Mbale Schroeder anamaliza kuti: “Chotero, abale, muyamikireni Yehova kaamba ka maphunziro odabwitsa, amtengo wosagulika omwe mwakhala nawo—omwe ngolimba ndipo sangagwedezeke. Pitirizanibe ndi dalitso la Yehova ndikukhala ndi chidaliro chokwanira mwa iye ndi Mtsogoleri wathu wabwino, Yesu Kristu. Mawu omwe tiri nawo m’Malemba ngouziridwadi ndipo adzakulangizani ndikukutsogozani m’ntchito yaumishonale.”
Malonje ochokera kumaiko 11 anaŵerengedwa. Ophunzirawo analandira madiploma awo, ndipo mmodzi wawo anaŵerenga kalata yachiyamikiro yonka ku Bungwe Lolamulira ndi banja la Beteli.
Chigawo cha m’madzulo chinaphatikizapo phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda, lochititsidwa ndi David L. Walker, chiŵalo cha Komiti ya ku Watchtower Farms. Kenaka ophunzirawo anagwiritsira ntchito mutu wodzutsa maganizo wakuti “Mphamvu ya Pemphero Polalikira” posonyeza zokumana nazo zakumunda. Mpingo wa kumaloko unasonyeza drama yochititsa chidwi yakuti Owonjoledwa Kupititsa Patsogolo Kulambira Kowona, yozikidwa pakubwerera kwa Ezara ku Yerusalemu kukapititsa patsogolo kulambira kowona. Mbale Frederick W. Franz, pulezidenti wa Sukulu ya Gileadi, anamaliza ndi pemphero logwira mtima.
[Chithunzi patsamba 24]
Kalasi ya Omaliza Maphunziro ya 89 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera yaŵerengedwa kuyambira kutsogolo kunka kumbuyo, ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kulamanzere kunka kulamanja mumzera uliwonse. (1) Ahr, K.; Johnston, L.; Ng Ying Kin, V.; Sukkau, A.; Rodriguez, A.; Myklebust, N. (2) Ahr, H.; Verbeek, P.; Verbeek, K.; DeBolt, S.; DeBolt, S. (3) Sukkau, W.; Ayala, L.; Ayala, S.; Jenson, R.; Ng Ying Kin, J.; Myklebust, T. (4) Rodriguez, C.; Ferlisi, G.; Ferlisi, L.; Tank, J.; Jenson, K.; Tank, J.; Johnston, P.