‘Mulungu Akomera Mtima Munthu Wabwino’
YEHOVA Mulungu ndi amene analenga chinthu chilichonse cha moyo. (Salmo 36:9) Inde, “mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu.” (Machitidwe 17:28) Ndipo, kodi mitima yathu simayamikira kwambiri tikaganizira mphoto imene wapatsa anthu amene ali naye paubwenzi wapamtima? Ndithudi, “mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha.” (Aroma 6:23) N’kofunikatu kuti tifunefune kukoma mtima kwa Yehova!
Wamasalmo akutitsimikizira kuti ‘Mulungu apatsa chifundo, [kapena akomera mtima].’ (Salmo 84:11) Koma kodi amakomera mtima ndani? Anthu masiku ano nthaŵi zambiri amakomera mtima ena chifukwa cha maphunziro, chuma, khungu, fuko limene akuchokera ndi zina zotero. Kodi Mulungu amakomera mtima ndani? Mfumu Solomo ya Israyeli wakale ikuyankha kuti: “Yehova akomera mtima munthu wabwino; koma munthu wa ziwembu am’tsutsa.”—Miyambo 12:2.
Mwachionekere, Yehova amasangalala ndi munthu wabwino, wamakhalidwe abwino. Ena mwa makhalidwe a munthu wabwino ndiwo kudziletsa, kupanda tsankhu, kudzichepetsa, chifundo ndi nzeru. Maganizo ake ndi olungama, mawu ake ndi olimbikitsa, zochita zake n’zabwino ndi zopindulitsa. Mbali yoyamba ya chaputala 12 cha buku la Baibulo la Miyambo imatisonyeza mmene ubwino uyenera kukhudzira moyo wathu tsiku ndi tsiku ndiponso imafotokoza mapindu amene amakhalapo chifukwa chosonyeza khalidwe limeneli. Kupenda zimene zalembedwa pamenepa kudzatithandiza “kuzindikira ndi kuchita bwino.” (Salmo 36:3) Kugwiritsira ntchito malangizo anzeru ameneŵa kudzatithandiza kuti Mulungu atikomere mtima.
Mwambo Ndi Wofunika Kwambiri
Solomo anati: “Wokonda mwambo akonda kudziŵa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.” (Miyambo 12:1) Munthu wofuna kwambiri kuwongolera amafunitsitsa mwambo. Iye amagwiritsira ntchito mwamsanga uphungu umene amalandira pamisonkhano yachikristu kapena pokambirana ndi ena. Mawu a m’Malemba ndi zofalitsa zophunzitsa Baibulo zili ngati kachikwapu kamene kamamutsogolera kutsatira njira yabwino. Iye amafuna kudziŵa ndipo zimene wadziŵazo amazigwiritsa ntchito kuwongolera mayendedwe ake. Inde, munthu wokonda mwambo amakondanso kudziŵa.
Mwambo ndi wofunika kwambiri kwa olambira oona, makamaka kudziletsa! Tingalakelake kukhala odziŵa mwakuya Mawu a Mulungu. Tingafune kukhala ogwira mtima mu utumiki wachikristu ndi kukhala aphunzitsi abwino a Mawu a Mulungu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Koma kuti zimenezi zichitike pamafunika kudziletsa. Kudziletsa n’kofunikanso m’mbali zina za moyo. Mwachitsanzo, masiku ano zinthu zodzutsa zilakolako zoipa n’zambiri. Kodi sipamafunikira kudziletsa kuti tisayang’ane zinthu zosayenera? Ndipotu, popeza kuti “ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake” maganizo oipa angachokeredi m’kati mwenimweni mwa maganizo athu. (Genesis 8:21) Kudziletsa n’kofunika kuti tisaganizire zinthu zimenezi.
Mosiyana ndi zimenezi, munthu wakuda chidzudzulo, sakonda mwambo kapena kudziŵa. Munthu wogonjera zochita za anthu ochimwa zokana chidzudzulo, amakhala ngati nyama yosaganiza, chilombo, chimene chilibe makhalidwe abwino. Tiyenera kukaniratu maganizo ameneŵa.
‘Mizu Yomwe Singasunthidwe’
Mwachionekere, munthu wabwino sangakhale wosalungama. Chotero chilungamo n’chofunika kuti Yehova atikomere mtima. Mfumu Davide inaimba kuti: “Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzam’chinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.” (Salmo 5:12) Kusiyanitsa mmene wolungama ndi woipa alili, Solomo akuti: “Munthu sadzakhazikika ndi udyo [“kuipa,” NW], muzu wa olungama sudzasunthidwa.”—Miyambo 12:3.
Anthu oipa angaoneke ngati zinthu zikuwayendera bwino. Taganizirani zimene wamasalmo Asafu anakumana nazo. Iye akuti: “Ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka.” Chifukwa chiyani? Asafu akuyankha kuti: “Ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.” (Salmo 73:2, 3) Koma pamene analoŵa m’kachisi wa Mulungu, iye anazindikira kuti Yehova wawaika poterera. (Salmo 73:17, 18) Kupeza bwino kulikonse kumene oipa angaoneke ngati ali nako n’kwakanthaŵi. Nanga n’kuwachitiranji nsanje?
Mosiyana ndi zimenezi, iye amene Yehova am’komera mtima akhala wosasunthika. Pogwiritsira ntchito fanizo la mizu yolimba bwino ya mtengo, Solomo akuti: “Munthu wabwino ali ndi mizu yomwe singasunthidwe.” (Miyambo 12:3, The new English Bible) Mizu yosaoneka ya mtengo waukulu kwambiri, monga mtengo wotchedwa sequoia wa ku California, ingayale malo oposa mahekitala 1.5 ndipo ingapangitse mtengowo kukhala wolimba kwambiri ngakhale panthaŵi ya kusefukira kwa madzi ndiponso mkuntho. Mtengo waukulu kwambiri wa sequoia ungakhale wolimba pamene chivomezi cha mphamvu kwambiri chichitika.
Monga mizu imeneyi yomwe ili m’dothi lachonde, maganizo ndi mitima yathu ziyenera kusanthula mwakuya Mawu a Mulungu ndi kupindula ndi madzi opatsa moyo ameneŵa. Chotero chikhulupiriro chathu chimakhala chosasunthika ndi cholimba ndipo chiyembekezo chathu chimakhala chotsimikizika ndiponso chosagwedera. (Ahebri 6:19) ‘Sitidzatengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso [chonyenga].’ (Aefeso 4:14) N’zoona kuti tingavutike ndi zimene mayesero onga mkuntho abweretsa ndipo mwina ngakhalenso kuchita mantha tikamakumana ndi mavuto. Komabe, ‘mizu yathu singasunthidwe.’
“Mkazi Wodekha Ndiye Korona wa Mwamuna Wake”
Anthu ambiri amadziŵa mawu akuti, “Mwamuna aliyense yemwe zinthu zikumuyendera bwino ndiye kuti ali ndi mkazi wabwino.” Kusonyeza kufunika kwa mkazi wothandiza, Solomo akuti: “Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.” (Miyambo 12:4) Mawu akuti “wodekha” akusonyeza mbali zambiri za ubwino. Makhalidwe a mkazi wabwino, monga momwe Miyambo chaputala 31 ikuwafotokozera mwatsatanetsatane, amaphatikizapo kukhala wazintchito, wokhulupirika ndi wanzeru. Mkazi wokhala ndi makhalidwe ameneŵa ndi korona wa mwamuna wake chifukwa khalidwe lake labwino limam’pangitsa kulemekezeka ndi kukwezedwa pamaso pa anthu. Safuna kuti iye aoneke wapamwamba kapena kupikisana ndi mwamuna wake kuti azimulemekeza. M’malo mwake, iye amathandiza mwamuna wake.
Kodi ndi motani mmene mkazi angachitire zinthu mochititsa manyazi, ndipo pangakhale zotsatira zotani? Khalidwe lochititsa manyazi lingayambire pakukhala wolongolola mpaka kuchita chigololo. (Miyambo 7:10-23; 19:13) Makhalidwe otero a mkazi amangowononga mwamuna wake. Mkazi amakhala ngati “chovunditsa mafupa a mwamunayo” chifukwa choti “amamuwononga, monga nthenda yomwe imafooketsa thupi,” linatero buku lina. Buku linanso linati: “Mawu ofanana nawo amasiku ano angakhale ‘kansa,’ nthenda imene imafooketsa munthu pang’onopang’ono.” Tikukhulupirira kuti akazi achikristu adzayesetsa kuti Mulungu awakomere mtima mwa kusonyeza makhalidwe abwino a mkazi wodekha.
Maganizo Amabala Ntchito Ndipo Ntchito Zimakhala ndi Zotsatira Zake
Maganizo amabala ntchito ndipo ntchito zimakhala ndi zotsatira zake. Ndiyeno Solomo akufotokoza mmene zinthu zimasinthira kuchoka pa maganizo kufika pa zochita, akuyerekeza olungama ndi oipa. Iye akuti: “Maganizo a olungama ndi chiweruzo; koma uphungu wa oipa unyenga. Mawu a oipa abisalira mwazi; koma m’kamwa mwa olungama muwalanditsa.”—Miyambo 12:5, 6.
Maganizo a anthu abwino amakhala abwino ndipo amachita zinthu mopanda tsankhu ndi molungama. Popeza kukonda Mulungu ndi anthu anzawo n’kumene kumalimbikitsa anthu olungama, zolinga zawo zimakhala zabwino. Mosiyana ndi zimenezi, kudzikonda n’kumene kumalimbikitsa anthu oipa. Chotero, zochita zawo, njira zawo zimene amatsatira kuti apeze zolinga zawo n’zachinyengo. Zochita zawo n’zosakhulupirika. Iwo samachedwa kutchera msampha anthu osalakwa mwa kuwanamizira mwina ku khoti. Mawu awo “abisalira mwazi” chifukwa afuna kuvulaza anthu osalakwa. Anthu olungama, pokhala amadziŵa ziwembu zimenezi ndipo ali ndi nzeru zowathandiza kukhala osamala, amapeŵa msampha umenewu. Iwo angathe kuchenjeza ngakhale omwe sakudziŵa zambiri ndi kuwapulumutsa ku njira zachinyengo za anthu oipa.
Kodi n’chiyani chidzachitikira olungama ndi oipa? Solomo akuyankha kuti: “Oipa amagwa kuli zi; koma banja la olungama limaimabe.” (Miyambo 12:7) Buku lina linati banja panopa “limaimira banja la munthu ndiponso zonse zimene munthuyo amaziona kuti n’zamtengo wapatali, zimene zimamuthandiza kuti akhaledi ndi moyo.” Lingaimirenso banja ndiponso ana kapena zidzukulu za munthu wolungama. Mulimonse mmene zingakhalire, mfundo ya mwambiwu ndi yomveka: Olungama adzalimba pokumana ndi mavuto.
Munthu Wodzichepetsa Zidzamuyendera Bwino
Pogogomezera kufunika kwa kuzindikira, mfumu ya Israyeli inati: “Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake; koma wokhota mtima adzanyozedwa.” (Miyambo 12:8) Munthu wozindikira samalankhula msangamsanga koma amaganiza kaye asanalankhule ndipo amagwirizana bwino ndi ena chifukwa “nzeru yake” imam’chititsa kusankha bwino mawu ake. Pamene afunsidwa mafunso opanda pake kapena opanda maziko, munthu wozindikira amakhala “wopanda chikamwakamwa.” (Miyambo 17:27) Munthu woteroyo amatamandidwa ndipo amasangalatsa Yehova. Iye amasiyana kwambiri ndi munthu wamalingaliro opotoka ochokera mu ‘mtima wokhota.’
Inde, munthu wanzeru amatamandidwa, koma mwambi wotsatirawu ukutiphunzitsa kufunika kwa kudzichepetsa. Umati: “Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo, aposa wodzikuza, amene asoŵa zakudya.” (Miyambo 12:9) Solomo akuoneka ngati akunena kuti ndi bwino kukhala wodzichepetsa, wokhala ndi zochepa, wongokhala ndi kapolo mmodzi, kuposa kuwononga zofunika pamoyo n’cholinga choti ukhalebe ndi moyo wapamwamba. Ameneŵa ndi malangizo abwino kwambiri kwa ifeyo oti tisamagwiritse ntchito ndalama zoposa zimene timapeza.
Moyo Wauchikumbe Ukuphunzitsa Munthu Kukhala Wabwino
Mwa kugwiritsira ntchito moyo wauchikumbe, Solomo akuphunzitsa maphunziro aŵiri ponena za ubwino. Iye akuti: “Wolungama asamalira moyo wa choŵeta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.” (Miyambo 12:10) Munthu wolungama amasamalira bwino nyama zake. Iye amadziŵa zimene nyamazo zikufuna ndipo amazisamalira kuti zisangalale. Munthu woipa anganene kuti amasamalira nyama, koma samadera nkhaŵa zomwe zikufuna. Zolinga zake ndi zadyera, ndipo kusamalira kwake nyama kumadalira phindu limene angalipeze ku nyamazo. Zimene munthu woteroyo amaona kuti ndiko kusamalira bwino nyama kungakhale kuzichitira nkhanza.
Mfundo yosamalira bwino nyama ikugwiranso ntchito pa ziŵeto zimene timasunga m’nyumba. Ingakhale nkhanza yeniyeni ngati tisunga nyama m’nyumba ndiyeno n’kumazivutitsa mwa kuzinyalanyaza dala kapena kuzizunza. Ngati zachitika kuti nyama ina ikuvutika kwambiri chifukwa cha matenda kapena inavulazidwa, tingaisonyeze chifundo mwa kuipha.
Mwa kugwiritsiranso ntchito mbali ina ya moyo wauchikumbe yomwe ndi kulima, Solomo akuti: “Zakudya zikwanira wolima minda yake.” Ndithudi, kugwira ntchito molimbika kuli ndi phindu. “Koma wotsata anthu opanda pake asoŵa nzeru.” (Miyambo 12:11) Munthu wosazindikira, amene “asoŵa nzeru” amachita malonda opanda pake amene amaika moyo pangozi ngakhale kuti ali ndi phindu. Mwachionekere, m’mavesi aŵiriŵa taphunzira kuti: Tiyenera kukhala achifundo ndi azintchito.
Wolungama Amachita Bwino
Mfumu yanzeru ikuti: “Woipa akhumba chokodwa ndi amphulupulu.” (Miyambo 12:12a) Kodi woipa amachita bwanji zimenezi? Mwa kusirira phindu limene lapezedwa m’njira zoipa.
Bwanji za munthu wabwino? Munthu wotero ndi wokonda mwambo ndipo chikhulupiriro chake n’chosasunthika. Iye ndi wolungama, wanzeru ndi wodzichepetsa, wachifundo ndi wakhama. Ndipo Solomo akuti: “Koma muzu wa olungama umabala zipatso.” (Miyambo 12:12b) Baibulo la An America Translation limati: “Muzu wa olungama udzakhala kosatha.” Munthu wotero amakhala wosasunthika ndiponso wosungika. Ndithudi, ‘Mulungu akomera mtima munthu wabwino.’ Motero, tiyeni ‘tikhulupirire Yehova, ndipo tichite chokoma.’—Salmo 37:3.
[Zithunzi patsamba 31]
Monga mtengo wokula bwino, chikhulupiriro cha olungama chimakhala chosasunthika