Miyambo
12 Munthu amene amakonda malangizo* amakondanso kudziwa zinthu,+
Koma amene amadana ndi kudzudzulidwa ndi wosaganiza bwino.*+
2 Yehova amasangalala ndi munthu wabwino,
Koma munthu amene amakonza mapulani ochita zinthu zoipa, Mulungu amamuweruza kuti ndi wolakwa.+
3 Palibe munthu amene angakhale wotetezeka chifukwa chochita zoipa,+
Koma anthu olungama sadzazulidwa.
4 Mkazi wamakhalidwe abwino ndi chisoti cha ulemu kwa mwamuna wake,+
Koma mkazi wochita zinthu zochititsa manyazi ali ngati matenda amene amawoletsa mafupa a mwamunayo.+
5 Maganizo a anthu olungama ndi achilungamo,
Koma malangizo a anthu oipa ndi achinyengo.
6 Mawu a anthu oipa ali ngati msampha wakupha,*+
Koma pakamwa pa anthu owongoka mtima pamawapulumutsa.+
8 Munthu amatamandidwa chifukwa cholankhula zinthu zanzeru,+
Koma amene ali ndi mtima wopotoka adzanyozedwa.+
9 Kuli bwino kukhala munthu wamba koma nʼkukhala ndi wantchito,
Kusiyana nʼkukhala wodzikuza koma wopanda chakudya.+
10 Wolungama amasamalira ziweto zake,+
Koma munthu woipa amaganiza kuti ndi wachifundo, pamene ali wankhanza.
11 Amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+
Koma amene amafunafuna zinthu zopanda pake ndi wopanda nzeru.
12 Munthu woipa amasirira nyama imene anthu ena oipa agwira,
Koma muzu wa anthu olungama umabala zipatso.
14 Munthu amasangalala ndi zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake abwino,*+
Ndipo ntchito za manja ake zidzamupindulira.
16 Munthu wopusa amasonyeza kuti wakhumudwa nthawi yomweyo,*+
Koma munthu wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.*
18 Mawu a munthu amene amalankhula asanaganize amalasa ngati lupanga,
Koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.+
19 Milomo imene imalankhula zoona idzakhalapo mpaka kalekale,+
Koma lilime labodza lidzangokhalapo kwa kanthawi kochepa.+
20 Chinyengo chimakhala mumtima mwa anthu okonza chiwembu,
21 Palibe chopweteka chimene chidzagwere wolungama,+
Koma anthu oipa ndi amene adzakumane ndi mavuto ambiri.+
22 Yehova amanyansidwa ndi milomo yonama,+
Koma anthu amene amachita zinthu mokhulupirika amamusangalatsa.
23 Munthu wochenjera amabisa zimene akudziwa,
Koma mtima wa munthu wopusa umangolankhula zinthu zosonyeza kupusa kwake.+
26 Wolungama amafufuza malo abwino odyetserako ziweto zake,
Koma njira ya anthu oipa imawasocheretsa.