Lingaliro la Baibulo
Kodi Nchiyani Chimene Chingakuthandizeni Kulimbana ndi Kupsinjika Maganizo?
KODI mukuvutitsidwa ndi kupsinjika maganizo? Ngati nditero, alipo ena ambiri. Zino ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa,” ndipo anthu a misinkhu yonse ndi a mikhalidwe yosiyanasiyana ya moyo akupsinjika maganizo. (2 Timoteo 3:1) Akatswiri ena amanena kuti oposa theka la maulendo onse opangidwa kwa dokotala amachititsidwa ndi mavuto a kupsinjika maganizo.
Komabe kupsinjika maganizo mwa iko kokha sikuli kwenikweni koipa. “Ndi iko komwe,” akutero mkulu wa chipatala cha opsinjika maganizo, “kumatipatsa chitsitsimulo, chisangalalo chokhalira moyo, nyonga yochitira zinthu. Timakondwera nako—ngati tingathe kukulamulira.”
Kumbali ina, kupsinjika maganizo kungakhale kosakaza, kowononga. Pamenepo, bwanji ngati kupsinjika maganizo kumakuvutitsani? Nawa malingaliro angapo ozikidwa pa nzeru ya Baibulo imene ingakuthandizeni kuchepetsa ziyambukiro zake zovulaza.
Peŵani Ziyembekezo Zopambanitsa
“Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima,” limatero Baibulo. (Miyambo 13:12) Pamene ziyembekezo sizikwaniritsidwa, kupsinjika maganizo kungakhale kosautsa. Zimenezi zili zotheka kuchitika pamene tiika ziyembekezo zathu pamwamba kwambiri.
Mwachitsanzo, aulutsi osatsa malonda apusitsa anthu ambiri kukhulupirira kuti chimwemwe chawo chimadalira pa kukhala ndi zinthu zakuthupi. Pamene munthu alakalaka zinthu zosafikirika kwa iye, zotulukapo zake zingakhale kupsinjika maganizo ndi kugwiritsidwa mwala. Motero Baibulo limapereka uphungu uwu: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:8) Inde, ngakhale kuti simungakhale ndi galimotolo, nyumbayo, kapena mipando imene mungakonde kukhala nayo, khutirani ndi zimene muli nazo. Ikani ziyembekezo zanu za zinthu zakuthupi pamalo achikatikati.
Ziyembekezo zopambanitsa zoloŵetsamo anthu nazonso zingachititse kupsinjika maganizo. Mwachitsanzo, pamene kuli kwakuti mwinintchito kapena woyang’anira pantchito ali woyenerera kuyembekezera mlingo wabwino wa kagwiridwe kantchito kwa awo oyang’aniridwa ndi iye, kumakhala kupusa kuyembekezera ungwiro kwa iwo. Carlos, woyang’anira ntchito m’fakitale ku Brazil, akuti: “Uyenera kulandira anthu monga momwe aliri. Ngati uyembekezera zoposa zimene angapereke, zimenezo zidzakweza mlingo wa kupsinjika maganizo, zikumachititsa aliyense kusakondwa.”—Yerekezerani ndi Yeremiya 17:5-8.
Lamulirani Kupsinjika Maganizo Kofuna Chipambano
Latin America Daily Post ikuvumbula chochititsa kupsinjika maganizo china, ikumanena kuti ‘khalidwe lokondetsa chipambano, lampikisano lili chochititsa chachikulu cha nthenda ya mtima.’ Akauntanti wina wachichepere akuulula kuti: “Kuofesi ndimakhala wodera nkhaŵa ndi wamantha kwambiri kuti ndidzavumbula chifooko chinachake. Ndimagwira ntchito zolimba ndipo ndimalefulidwa pamene ena samandithokoza.”
Ponena za zoyesayesa zoterozo za kufuna kuzindikiridwa ndi kupambana, Solomo anati: “Ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 4:4.
Choonadi nchakuti, ‘omwe athamanga msanga sapambana nthaŵi zonse m’liŵiro’ ponena za kupambana pantchito kapena kuzindikiridwa. (Mlaliki 9:11) Maria, wantchito ya m’ofesi ku Brazil, ananena motere: “Munthu angakhale ndi luso, koma mikhalidwe, ndipo mwinamwake ngakhale tsankhu, zingatsekereze kukwezedwa kwake.”—Yerekezerani ndi Mlaliki 2:21; 10:6.
Ikani ziyembekezo zanu pamalo achikatikati ndipo zindikirani zimene simukhoza kuchita. Gwirirani ntchito chisangalalo chimene ntchito yeniyeniyo imadzetsa m’malo mwa kungogwirira ntchito chipambano chokha. (Mlaliki 2:24) Ndithudi, munthu wotengeka maganizo ndi kufuna chipambano samangotaya chisangalalo chachikulu cha moyo koma angakhalenso wamantha kwambiri kwakuti amafooketsa zoyesayesa zake za kupambana. Nchifukwa chake Dr. Arnold Fox analangiza kuti: “Kufuna kukhala wopambana m’ntchito yanu kuli chonulirapo chokhumbirika, koma musalole lingaliro limodzi limenelo kulamulira moyo wanu. Ngati munyalanyaza malingaliro a chikondi, kuseka, ndi chisangalalo cha moyo, kapena ngati mutengeka maganizo kwambiri ndi kufuna chipambano moti nkuiŵala kusangalala ndi moyo, mumadzipsinja maganizo nokha.”
Zinthu Zimene Mungachite
Njira ina yolimbanirana ndi chipsinjo cha zitsenderezo za tsiku ndi tsiku ndiyo kukulitsa mzimu wa kuseka. (Mlaliki 3:4) Simutofunikira kukhala wanthabwala kuti mukhale ndi mkhalidwe wa maganizo wosangalala. “Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.”—Miyambo 17:22.
Kodi muli ndi chizoloŵezi cha kukankhira zinthu mtsogolo? M’kupita kwanthaŵi, kukankhira zinthu mtsogolo kumawonjezera kupsinjika maganizo m’malo mokuchepetsa. Baibulo limalangiza kuti: “Musakhale aulesi m’machitidwe anu.” (Aroma 12:11) Pangani ndandanda, yolembedwa kapena ya m’maganizo, ya zinthu zimene mufunikira kuchita. (Miyambo 21:5) Ndiyeno sankhani zinthu zofunikira kuyamba kuchitidwa—ndipo yambani kuzichita.
Koma bwanji ngati, mosasamala kanthu za zoyesayesa zanu zabwino koposa, simupezabe bwino kapena mukhala wopsinjikabe? Mungafunikire kupanga zoyesayesa zakhama za kusintha kalingaliridwe kanu. Musasumike malingaliro anu pa zolakwa zakale. Kutero kungawonjezere kupsinjika kwinanso pa kumene muli nako tsopano. Wafilosofi wina wa m’zaka za zana la 19 analemba kuti: “Moyo ungamvetsetsedwe mobwerera kumbuyo; koma uyenera kukhalidwa mopita kutsogolo.” Ngakhale kuti tingaphunzirire pa zolephera, machitidwe athu a tsopano lino amaumba mtsogolo mwathu.
Mfumu Davide inasonyeza mankhwala abwino koposa a kupsinjika maganizo pamene inapemphera kwa Yehova kuti: “Masautso a mtima wanga akula: munditulutse m’zondipsinja.” (Salmo 25:17) Inde, Davide anayang’ana kwa Mulungu kuti amchotsere nkhaŵa zake. Ngati mupatula nthaŵi ya kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu, nanunso mudzadzimva kukhala woyandikana ndi Mulungu. Pamene muzindikira zifuno za Mulungu, mudzasonkhezereka kuika zofuna zake patsogolo m’moyo wanu, zimene zidzakumasulani ku nkhaŵa zambiri. (Mateyu 6:31, 33) Phunzirani kudera nkhaŵa za tsiku limodzi lokha. Nkuwonjezereranji nkhaŵa za maŵa pa za lero? Yesu ananena zimenezo motere: “Musadere nkhaŵa za maŵa; pakuti maŵa adzadzidera nkhaŵa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.”—Mateyu 6:34.
Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Mawu Otsindika patsamba 32]
“Munthu angakhale ndi luso, koma mikhalidwe, ndipo mwinamwake ngakhale tsankhu, zingatsekereze kukwezedwa kwake”
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Metropolitan Museum of Art, Ndalama zopatsidwa ndi Josephine Bay Paul and C. Michael Paul Foundation, Inc., ndi Charles Ulrick and Josephine Bay Foundation, Inc., ndi Fletcher Fund, 1967.