Pitirizani Kufunafuna Monga Chuma Chobisika
NDI ya mtengo wake chotani nanga mmene iliri miyala ya mtengo wake ya nzeru yopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo! Zokometsera zimenezi zimavumbula chifuno chaumulungu ndi kukhazikitsa ziyembekezo zosangalatsa pamaso pathu. Izo zimapereka chitonthozo ndi kutisonyeza ife mmene tingakondweretsere Mulungu. (Aroma 15:4) Miyala ya mtengo wake imeneyi imatithandizanso ife kuchita mwanzeru m’zochita zathu ndi ena. Ndithudi, nzeru yochokera kwa Mulungu imatithandiza ife kuyenda “m’njira ya moyo” ndi chikhutiritso ndi chimwemwe.—Salmo 16:11; 119:105.
Popeza kuti mapindu a nzeru ali ambiri, tiyenera kuiwona iyo kukhala ya mtengo wapatali. “Mawu onse a mkamwa mwanga alungama,” ikutero nzeru yoimiridwa monga munthu. “Mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka. Onsewo amveka ndi iye amene azindikira; Alungama kwa akupeza nzeru. Landirani mwambo wanga, si siliva ayi; Ndi nzeru kopambana ndi golidi wosankhika. Pakuti nzeru iposa ngale, Ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo.”—Miyambo 8:8-11.
Nchifukwa Ninji Kupitiriza Kufunafuna?
Kaŵirikaŵiri, kufunafuna kaamba ka zokometsera zokwiriridwa, golidi, kapena siliva kuli kosapindulitsa. Ichi sichifnikira kukhala chowona ponena za kufunafuna kaamba ka nzeru yaumulungu. Koma ndimotani mmene tingapambanire m’kufufuzaku? Chabwino, chipambano chimadalira pa ukulu wa kufunitsitsa kwathu chuma chimenechi ndi kulimbikira komwe tidzagwira ntchito kuchipeza icho. Ngati tizindikira phindu lake lowona, tidzasangalala nacho pamwamba pa zina zonse za mtengo wake. Ndiko nkomwe, “kodi kulandira nzeru sikpambana ndi golidi, Kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?”—Miyambo 16:16.
Miyambo 2:1-6 imafulumiza kuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, Ndi kusunga malamulo anga; Kutcherera makutu ako kunzeru, Kulozetsa mtima wako kukuzindikira; Ukaitananso luntha, Ndi kufuulira kuti ukazindikire; Ukaifunafuna ngati siliva, Ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; Pompo udzazindikira kuwopa Yehova Ndi kumdziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; Kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”
Popeza kuti chuma chokwiriridwa chiri chobisika, chiri choyenerera kufunafuna kaamba ka icho. Pamene akukumba, ena amapereka nsembe nthaŵi ya zosangulutsa, chakudya, ndi tulo. Koma kuyesayesa koteroko kumawonedwa kukhala kwa phindu pamene chumacho chapezedwa. Tifunikira kupanga nsembe zofananazo kuti tifunefune nzeru ya Mulungu. Monga mmene kufunafuna kaamba ka chuma chokwiriridwa kumaitanira kaamba ka kukumba kwamphamvu, choteronso kufufuza kaamba ka nzeru kumafunikira chipiriro. Sichiri chokwanira kungodutsa m’Baibulo ndi zofalitsidwa Zachikristu. Nthaŵi, kufufuza, ndi kusinkhasinkha zimafunikira kuti tipeze miyala ya mtengo wake yauzimu. Koma ndi chosangalatsa chotani nanga pamene tipeza chidziŵitso m’Malemba!—Nehemiya 8:13.
Kufunafuna Chuma Kwachipambano
Inde, chimwemwe chimatulukapo kuchokera m’kukumba m’Mawu a Mulungu ndi kupeza miyala ya mtengo wake ya nzeru. (Miyambo 3:13-18) Kufika ku mapeto amenewo, tiri anzeru ngati tipanga laibulale yabwino yaumwini kapena ya banja. Koma kodi nchiyani chimene iyenera kukhala nacho? Pambali pa dikishonale yabwino, Mboni za Yehova zimachipeza icho kukhala chothandiza kukhala ndi matembenuzidwe osiyanasiyana a Malemba, limodzi ndi zofalitsidwa za Baibulo Zachikristu, kuphatikizapo makope a chaka chirichonse a Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake, Galamukani! Ndithudi, laibulale iyenera kugwiritsiridwa ntchito moyenerera ngati idzayenera kutithandiza ife monga ofunafuna chuma.
M’kufufuza kwathu kaamba ka nzeru, tingayang’ane nkhani ndi mbali za Malemba za Watch Tower Publications Index kapena zilozero za kumbuyo kwa mabukhu a Watch Tower Society kapena mavolyumu a magazini. Izi ziri zida zokulira kaamba ka kufunafuna nzeru yaumulungu. M’chenicheni, izo ziri monga mapu yomwe ingatitsogoze ife ku “chuma chobisika” cha nzeru yaumulungu. (Miyambo 2:4) Ngati tiribe zofalitsidwa zina zofunikira kaamba ka kufufuza, izo zingakhalepo pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kumaloko.
Tsopano, tiyeni tichitire chitsanzo kufunafuna chuma kwachipambano. M’kuŵerenga kwathu kwa Baibulo, tingadabwe mmene Yudase Isikariyote anafera pambuyo pa kupereka Yesu Kristu. Mateyu 27:5 imanena kuti Yudase “anachokapo nadzipachika yekha pakhosi.” Koma Machitidwe 1:18 imanena kuti: “Anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka.” Chotero ndimotani mmene Yudase anafera? Yankho lingapezeke mwa kufufuza ndandanda kaamba ka malemba amenewa mu “Scripture Index” (Chilozero cha Lemba) ya chofalitsidwa cha Insight on the Scriptures. Imatiwuza kuti: “Mateyu akuwoneka kukhala akuchita ndi mkhalidwe wa kudzipha koyesera, pamene Machitidwe ikulongosola chotulukapo chake. Kuphatikiza zolembera ziŵirizo, chikuwoneka kuti Yudase anayesera kudzipachika yekha pa malo ena okwezeka, koma chingwecho kapena nthambi ya mtengo inathyoka kotero kuti iye anagwa pansi ndi kuphulika pa miyala pansipo. Mkhalidwe wa nthaka mozungulira Yerusalemu unapangitsa chochitika choterocho kukhala chokhulupiririka.” (Volyumu 2, tsamba 130) Ponena za Insight on the Scriptures, chonde onani tsamba 10 ya magazini ino.
Kugwiritsira ntchito concordance kumatitheketsa ife kupeza malemba a Baibulo. Ndithudi, pamene tikukambitsirana lemba, tiyenera kuzindikira za mawu ake olizungulira. Kuti tichitire chitsanzo chimenechi, tiyeni tilingalire Salmo 144:12-14. Maversi amenewa amaimira anthu ena kukhala akunena kuti: ‘Ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; Ana athu akazi ngati nsanamira za kungondya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu. Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundu mitundu; Ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwi zikwi, . . . ng’ombe zathu zikhale zosenza katundu.’ Tingalingalire kuti mawu amenewa amagwira ntchito kwa anthu a Mulungu, koma mawu ozungulira lembalo amasonyeza kuti iwo satero. Mu versi 11, wamasalmo Davide akuchonderera kaamba ka chipulumutso kuchokera kwa osalankhula chowonadi. Iwo anadzitukumula ponena za ana awo amuna, ana akazi, nkhosa zawo, ndi ng’ombe. Mogwirizana ndi versi 15, ochita zolakwa oterowo ananena kuti: “Odala anthu akuwona zotere.” Mosiyanako, ngakhale kuli tero, Davide anafuula kuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”
Miyala Yamtengo Wake Yauzimu Ichuluka!
Chimwemwe ndithudi chimatulukapo kuchokera ku zolondola za chipambano kaamba ka nzeru. Ndipo miyala ya mtengo wake yauzimu yomwe ingapezedwe kupyolera m’kufufuza imaphatikizapo mayankho okhutiritsa ku mafunso a Baibulo. Ndi mayankho otani nanga amene timapeza ngati tipitiriza kufunafuna! Mwachitsanzo, kodi Kaini anapeza kuti mkazi wake? Nsanja ya Olonda (June 1 1982) inanena kuti: “Baibulo limatiwuza ife kuti Adamu ndi Hava anali ndi ana ambiri, osati aŵiri okha [Kaini ndi Abele]. ‘Masiku ake a Adamu atabala Seti [mwana wina wamwamuna], anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana amuna ndi akazi.’ (Gen. 5:4) Pokhala ndi mawu amenewo, kodi munganene kuti Kaini anatenga kuti mkazi wake? Inde, iye ayenera kukhala anakwatira mmodzi wa alongo ake. Lerolino zimenezi zingakhale zowopsya kwa ana alionse obadwa kwa makolo apachibale kwambiri oterowo. Koma pafupi ndi chiyambi cha mbiri ya anthu, pamene anthu anali pafupi kwambiri ndi ungwiro, silinali vuto.”
Tangoyerekezani kuti tikuŵerenga bukhu la Baibulo la Miyambo. Tikumawona chomwe chanenedwa pa Miyambo 1:7, tingadabwe kuti: ‘Kodi “kuwopa Yehova” nchiyani?’ Kufufuza kungatitsogoze ife ku Nsanja ya Olonda ya May 15, 1987, yomwe inanena kuti: “Kuli mantha, ulemu wakuya, ndi kuwopa kwenikweni kwa kusamukondweretsa chifukwa timayamikira ubwino ndi kukoma mtima kwake. ‘Kuwopa Yehova’ kumatanthauza kuvomereza kuti ali Woweruza Wamkulu ndi Wamphamvuyonse, amene ali ndi kuyenera ndi mphamvu ya kubweretsa chilango kapena imfa pa osamumvera iye. Chimatanthauzanso kutumikira Mulungu mokhulupirika, kudalira mwa iye kotheratu, ndi kudana ndi chimene chiri choipa m’maso mwake.”
Pitirizani Kufunafuna!
Nsanja ya Olonda imafalitsidwa kuti ithandize ofufuza owona mtima kaamba ka nzeru kupeza miyala ya mtengo wake yauzimu. Tonsefe tifunikira nzeru ndi kumvetsetsa Mawu a Mulungu. Miyambo 4:7, 8 ikunena kuti: “Nzeru ipambana, tatenga nzeru; M’kutenga kwako konseko utenge luntha. Uilemekeze, ndipo idzakukweza; idzakutengera ulemu pamene uifungatira.”
Kokha mwa kupeza chidziŵitso m’Malemba ndi kugwiritsira ntchito nzeru molondola ndi pamene tingapeze chimwemwe chowona. Inde, ndipo kokha mwa kugwiritsira ntchito nzeru yaumulungu ndi pamene tingakondweretse Yehova Mulungu. Chotero lolani kuti chirichonse chisakuletseni inu kufunafuna nzeru monga chuma chobisika.
[Zithunzi pamasamba 4, 5]
Kufunafuna kaamba ka chuma chokwiriridwa kumaitanira kaamba ka kukumba kwamphamvu. Kodi sitiyenera kuwumirira m’kufunafuna kwathu kaamba ka nzeru yaumulungu?