Chaputala 8
Kugaŵanamo ‘Chisangalalo’ cha “Kalonga wa Mtendere”
1. (a) Kodi nchifukwa ninji munthu wina anapita kudziko lakutali? (b) Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa m’fanizo la Yesu, ngakhale kuli kwakuti sichinalongosoledwe mwachindunji?
M’FANIZO la Yesu la matalente, munthu mwini matalente a siliva asanu ndi atatu sanapite kudziko lakutali paulendo wokawona malo okondweretsa. Iye anali ndi chifukwa chachikulu cha kupitira kudziko lakutali; iye anali ndi chikhumbo cha kudzipezera kanthu kena kamtengo wapatali. Iye anapita kudziko lakutali, monga momwe fanizolo likusonyezera, kukadzipezera “chisangalalo,” limodzi ndi “zinthu zambiri.” (Mateyu 25:21) Motero iye anafunikira kuyenda ulendo wautali, wofunikiritsa nthaŵi yaitali, kotero kuti apemphe kwa uyo amene akampatsa chisangalalo chimenecho.
2. (a) M’nkhani ya Yesu, kodi nchiyani chimene kupita kudziko lakutali kwa munthu wachuma kunaphiphiritsira, ndipo kodi anamka kwayani? (b) Kodi Mbuyeyo anabwerera ndi chiyani?
2 Popeza kuti munthu wachuma wa m’fanizolo amaphiphiritsira Yesu Kristu, kuyenda kwa munthuyo kudziko lakutali paulendo wautali kumaphiphiritsira Yesu kukhala akupita ku Magwero amodzi a chisangalalo chapadera chimene anali kuchilingalira. Pamenepa, kodi nkwayani, kumene anapita? Ahebri 12:2 (NW) amatiuza: “Tikuyang’anitsitsa dwii pa Mtsogoleri ndi Wokwaniritsa wa chikhulupiriro chathu, Yesu. Chifukwa cha chisangalalo chimene chinaikidwa pamaso pake iye anapirira mtengo wozunzirapo, akumanyoza manyazi, ndipo wakhala pansi pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” Inde, ndithudi, Yehova Mulungu ndiye Magwero a chisangalalo chimenecho. Kunali kwa iyeyo kumene Yesu anapitako, akumasiya ophunzira ake okhulupirika pano padziko lapansi atawaikizira “matalente” ake. Ambuye anabwerera ndi “zinthu zambiri” zimene analibe pamene anaikizira matalente a siliva asanu ndi atatu kwa akapolo ake atatu. Fanizo loyambirira loperekedwa ndi Yesu, fanizo la “ndalama khumi,” limanena molunjika kuti zimene anabwerera nazo zinali mphamvu ya “ufumu.”—Luka 19:12-15.
3. Kodi inali nthaŵi yamtundu wotani pamene Zekariya 9:9 anayamba kukwaniritsidwa m’zaka za zana loyamba C.E.?
3 Mfumuyo iri ndi chifukwa chabwino cha kusangalalira, chifukwa cha kuikidwa pampando wachifumu chatsopano, ndipo irinso ndi olambira ake okhulupirika. Tikukumbukira panyengo imene Mwana wa Mulungu anakwera pabulu kuloŵa m’Yerusalemu mokwaniritsa ulosi wa Zekariya 9:9. Ponena za kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu, kwalembedwa: “Ambirimbiri ampingowo anayala zovala zawo panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m’njiramo. Ndipo mipingo ya kumtsogolera ndi ya kumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m’dzina la Ambuye! Hosana m’Kumwambamwamba! Ndipo mmene adaloŵa m’Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu?”—Mateyu 21:4-10; wonaninso Luka 19:36-38.
4. Pambuyo pa kuikidwa pampando wachifumu monga Mfumu, kodi nchifukwa ninji Yesu Kristu anali ndi chifukwa chapadera cha kuitanira “akapolo” ake okhulupirika kuloŵa mumkhalidwe wachisangalalo?
4 Chotero, ngati, nyengoyo inali yachisangalalo pamene anangodzipereka kunzika za Yerusalemu monga wodzozedwa ndi mzimu wa Yehova kaamba ka ufumu, koposa kotani nanga mmene zikakhalira pamene kwenikweni aikidwa pampando wachifumu kukhala Mfumu pamapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914? Inalidi nthaŵi yachisangalalo kwa iye. Pamenepo, ndithudi, iye analoŵa m’chisangalalo chimene sanakhalepo nacho ndi kale lonse. Chifukwa chake, poŵerengera kugwiritsiridwa ntchito kwa zinthu, akanatha kunena kwa ophunzira amene anaŵatsimikizira kukhala “abwino ndi okhulupirika”: ‘Munali okhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakukhazikani pa zinthu zambiri; loŵani inu m’chikondwerero cha ambuye wanu.’ (Mateyu 25:21) Tsopano panali chisangalalo chatsopano chimene “akapolo” ake ovomerezedwa akagaŵanamo. Ndimphotho yotani nanga!
5. (a) Kodi mtumwi Paulo anali ‘woimira’ wa Kristu pamlingo wotani? (b) Koma kodi lerolino otsalira odzozedwa ali “oimira” a Kristu pambuyo pa chochitika chotani?
5 Mu 1919 ophunzira odzozedwa a Mfumu yolamulira, Yesu Kristu analoŵa mumkhalidwe wovomerezedwa, ndipo umenewo unagwirizanitsidwa ndi chisangalalo chawo chachikulu. Zaka mazana khumi mphambu zisanu ndi zinayi kalero mtumwi Paulo analembera okhulupirira anzake kuwauza za malo awo a ntchito okwezeka: “Chifukwa chake ndife oimira mmalo mwa Kristu.” (2 Akorinto 5:20, NW) Zimenezo zinalembedwa pamene Yesu anali kokha woloŵa nyumba wowonekera kukhala ali ndi chiyembekezo cha kulandira “ufumu wakumwamba.” (Mateyu 25:1) Motero, pamenepa, iye anafunikira kukhala padzanja lamanja la Mulungu ndi kuyembekezera pamenepo tsiku la kuikidwa kwake pampando wachifumu. Koma tsopano, chiyambire 1919, otsalira ovomerezedwa akhala ali “oimira” otumidwa ndi Iye amene kwenikweni akulamulira monga Mfumu. (Ahebri 10:12, 13) Chowonadi chimenechi chinasonyezedwa kwa Ophunzira Baibulo Amitundu Yonse pamsonkhano wa pa Cedar Point, Ohio, mu 1922.
6. Kodi zoyesayesa za pambuyo pa nkhondo za awo amene analandira “matalente” zinalunjikitsidwa pantchito yamtundu wanji choyamba?
6 Mu 1919 iwo anali atapatsidwa kale zofanana ndi “matalente” a Mfumu yolamulira, Yesu Kristu. Zimenezi zinakulitsa kuŵerengera kwawo kwa Mfumu yawo yolamulira. Kuyambira pachiyambi, zoyesayesa zawo za pambuyo pa nkhondo zinalunjikitsidwa pantchito ya “kututa,” kusonkhanitsa a kagulu ka “tirigu.” (Mateyu 13:24-30) Popeza kuti, monga momwe Yesu adanenera, kututa ndiko “mapeto a dongosolo la zinthu,” chaka cha 1919 cha pambuyo pa nkhondo chinali nthaŵi yoyenerera ya kututidwa kumeneko kwa “ana a ufumu,” ofanana ndi tirigu, otsalira odzozedwa okhulupirika kuti kuyambe.—Mateyu 13:37-39.
7. (a) Kodi ndim’nthaŵi yotani imene otuta analoŵamo ndi Mbuye wawo? (b) Kodi ndimkhalidwe wotani umene Yehova waloŵetsamo otuta, ndipo kodi ndimawu olosera otani amene iwo amawapanga kukhala awo?
7 Nthaŵi ya kututa iri nthaŵi yachisangalalo kwa otuta, amene Mbuye wa kututa akusangalala limodzi nawo chochitikacho. (Salmo 126:6) Nthaŵi ya kututa imeneyi yakhala ikulemereretsedwa kwambiri ndi umboni womakulakula wakuti Ufumu wa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914 ndi kuti Yehova anabwezeretsa mkhalidwe wolungama kwa anthu ake odzipatulira padziko lapansi. Monga kagulu, iwo akukwaniritsa mawu a Yesaya 61:10: “Ndidzakondwera kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda chachilungamo.”
Kusonkhanitsa “Khamu Lalikulu” la Ogaŵanamo “Chisangalalo”
8. Kodi ndichisangalalo chotani chimene otsalira odzozedwa sanayembekezere chimene akakhala nacho pamapeto a kusonkhanitsidwa kwa oloŵa nyumba a Ufumu?
8 Otsalira odzozedwa amene analoŵa ‘m’chisangalalo’ cha Mbuye wawo sanadziŵe kuti cha kumapeto kwa kusonkhanitsidwa kwa mamembala otsirizira a oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba kumeneko kukakhala chisangalalo china, kanthu kena kamene sanayembekezere. Kumeneku kukakhala kusonkhanitsidwa kwa kagulu ka padziko lapansi kamene kakakhala m’paradaiso wa padziko lapansi m’Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu. Kodi ndani kusiyapo anthu ochokera m’kagulu ka padziko lapansi kameneka amene akakhala oyenerera kuitanira ku chimene chikakhala kuvumbulutsidwa koyamba kwa chidziŵitso chonena za iwo?
9. Kodi kwakukulukulu ndani amene anaitanidwa kukafika pamsonkhano wa ku Washington, D.C. mu 1935, ndipo kodi ndichidziŵitso chapanthaŵi yake chotani chimene chinavumbulutsidwa kwa iwo kumeneko?
9 Chotero kunali, molabadira chiitano chofalitsidwa m’Nsanja ya Olonda Yachingelezi,a mazana ambiri a amene anali kufunafuna unansi ndi Yehova, limodzi ndi dzina lake, anafika pamsonkhano wa anthu onse wa Mboni za Yehova mu Washington, D.C., May 30 mpaka June 2, 1935. Pamsonkhano umenewo iwo anasonkhezeredwa kwambiri kumva kuti “khamu lalikulu” lowonenedweratu m’masomphenya a m’Chivumbulutso 7:9-17 linali kudzakhala gulu lapadziko lapansi.
10, 11. Kodi ndikwayani kumene zimenezi zikanatsimikizira kukhala nthaŵi ya chisangalalo chapadera kumwambako?
10 Ha ndichisangalalo chachikulu chotani nanga chimene kuchitidwa kwa msonkhano umenewo mu Washington, D.C., kuyenera kukhala kunali kwa Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova! Ha chiyenera kukhala chinalinso chisangalalo chachikulu chotani nanga kwa Mwana wake monga Mbusa Wabwino amene tsopano akayamba kusonkhanitsa “nkhosa zina” zimenezi kukhala “gulu limodzi”!—Yohane 10:16.
11 Pamene ali kutsogozedwa ndi kuwetedwa, mwa mawu ophiphiritsira, mamembala a otsalira ndi a “khamu” lowonjezerekawonjezereka la “nkhosa zina” amasanganikirana pamodzi mwamtendere ndi mwachikondi. Mtima wa ‘mbusa wawo mmodzi’ tsopano uyenera kudzala ndi chisangalalo pa kukhala ndi “gulu” lalikulu motero pafupi ndi kotsirizira kwa ‘mapeto ameneŵa a dongosolo la zinthu.’
Amithenga a “Kalonga wa Mtendere”
12, 13. (a) Kodi ndani amene aitanidwa kugaŵana ndi otsalira odzozedwa chisangalalo cha Mbuye wobwerayo, ndipo nchiyani chimene chiri chifukwa cha chimenechi? (b) Kodi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” likutumikira zinthu za “Kalonga wa Mtendere” m’malo ati antchito?
12 Onga nkhosawo amene apanga “khamu lalikulu” tsopano ali ndi mbali yaikulu ya chisangalalo cha Mbuye, Yesu Kristu. Kwakukulukulu zimenezi ziri chifukwa cha kukhala kwawo ndi mbali yokangalika m’kuloŵetsamo ofunikawo kaamba ka kukwaniritsa a “khamu lalikulu,” limene chiŵerengero chake sichinaperekedwe m’Chivumbulutso 7:9.
13 Ntchito ya kusonkhanitsa imene “nkhosa zina” zikugaŵanamo yawonjezereka pamlingo wa dziko lonse lapansi, koposa kwakukulukulu mphamvu ya chiŵerengero chomachepachepa cha otsalira odzozedwa. Moyenerera, kwakhalapo kufunika kowonjezereka kwakuti chiŵerengero chomakulakula cha “nkhosa zina” chikhale ndi phande lowonjezereka mosalekeza la kubweretsabe owonjezera a “nkhosa zina” okhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. Motero “nkhosa zina” zikutumikira monga amithenga okhulupirika a “Kalonga wa Mtendere.” Miyambo 25:13 ikuwonjenzera kuti: “Monga chisanu cha chipale chofeŵa panthaŵi yamasika, momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; atsitsimutsa moyo wa mbuye wake.”
14. (a) Kodi nkhosa zophiphiritsira za m’fanizo la Yesu pa Mateyu 25:31-46 zikulandira chiyani monga choloŵa? (b) Kodi ndimotani mmene Ufumu unakonzedwera iwo ‘kuyambira chikhazikiro cha dziko’?
14 M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, nkhosa zophiphiritsira ndiwo anthu kwa amene Mfumu Yesu Kristu amati: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pachikhazikiro chake cha dziko lapansi.” (Mateyu 25:31-46) Iwo akulandira gawo la padziko lapansi limene ufumu wakumwamba udzalamulirapo mkati mwa kulamulira kwa Kristu kwa zaka chikwi. Kuyambira panthaŵi ya Abele wokhulupirika, Yehova wakhala akukonza malo ameneŵa kaamba ka anthu okhoza kuomboledwa.—Luka 11:50, 51.
15, 16. (a) Kodi ndi “ulemu” wa mfumu wotani, monga momwe watchulidwira ndi Solomo umene Mbuye ali nawo lerolino mosasamala kanthu za kulamulira kwake pakati pa adani ake? (b) Kodi Mfumu yolamulira iri ndi “ulemu” umenewu mumpangidwe wotani lerolino? (c) Kodi opanga “ulemu” umenewu achita chiyani?
15 Mfumu yanzeru Solomo wa Israyeli wakale inalemba kuti: “Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu.” (Miyambo 14:28) Mfumu ya lerolino yolamulira, Kristu Yesu, amene ali nduna yapamwamba kwambiri kuposa Mfumu Solomo wa padziko lapansi, iri nawo ‘ulemu weniweniwo’ pamene tiwona “unyinji wa anthu.” Zimenezi ziri choncho ngakhale tsopano pamene kulamulira kwake kwa zaka chikwi kusanayambe, inde, pamene iye akulamulira pakati pa adani ake a padziko lapansi, pamene Satana Mdyerekezi ali mfumu yosawoneka yoposa anthu.—Mateyu 4:8, 9; Luka 4:5, 6.
16 “Ulemu” wa lerolino woyenerera nduna yapamwamba yokhala ndi malo antchito monga mfumu tsopano ukupezeka m’chiŵerengero chomakulakula cha ‘nkhosa zake zina’ zimene zapanga “khamu lalikulu.” Mwachisangalalo iwo akufuula mogwirizana: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wa kukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 10) Iwo apeza kale chipulumutso kuchokera ku dongosolo la zinthu loweruziridwa ku chiwonongeko, limene Satana Mdyerekezi ali “mulungu” wake. (2 Akorinto 4:4) Mwalingaliro lophiphiritsira, iwo ‘atsuka kale zovala zawo . . . m’mwazi wa Mwanawankhosa’ naziyeretsa kotero kuti awonekera ali opanda banga pamaso pa Yehova, Woweruzayo.—Chivumbulutso 7:14.
17. (a) Kodi ndikuchipulumutso chotani chimene “khamu lalikulu” likuyang’anirabe mtsogolo? (b) Kodi ndimwaŵi wotani umene adzasangalala nawo mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa “Kalonga wa Mtendere”?
17 Komabe iwo akuyang’anira mtsogolo ku chipulumutso choperekedwa ndi Mulungu chimene adzapeza pa chilakiko chachikulu cha Yehova ‘m’nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ pa Armagedo. Kugonjetsa kwake kwakukulu kumeneko kudzachititsa kulemekezedwa kwa ufumu wake wachilengedwe chonse, ndipo iwo adzakhala mboni zowona ndi maso za padziko lapansi chifukwa cha kukhala atasungidwa amoyo kupyola mapeto owopsa a dziko loipa limeneli. (Chivumbulutso 16:14; 2 Petro 3:12) Ha ndimwaŵi wamtengo wapatali chotani nanga! Ha ndichisangalalo chachikulu chotani nanga chimene pamenepo “Kalonga wa Mtendere” adzagaŵana ndi “khamu lalikulu” lopulumuka la ‘nkhosa zake zina’ zokhulupirika!
[Mawu a M’munsi]
a Tsamba 2 la kope la Nsanja ya Olonda Yachingelezi ya April 1 ndi 15, May 1 ndi 15, 1935.
[Chithunzi patsamba 71]
Mtima wa Mbusa Wabwino tsopano uyenera kukhala wodzazidwa ndi chisangalalo chifukwa cha kukhala ndi “nkhosa zina” zambiri