Baibulo Linayamba Kulimbana ndi Matenda Sayansi Isanatero
Pamene Baibulo litchulidwa lerolino, anthu ambiri osadziŵa amangolinyalanyaza monga losayenerera chisamaliro chawo. Iwo amakana kutsegula maganizo awo kuti adziŵe kuti zaka zikwi zambiri zapitazo ilo linanena zinthu zimene munthu wamakono waziphunzira posachedwapa kapena zimene adzaphunzirabe. Izi ziri choncho ponena za zochitika zapadziko, boma, kupenda nyenyezi, malo otizinga, mbiri yachilengedwe, ukatswiri wopenda zamoyo, ndi ukatswiri wa malingaliro. Zirinso choncho ponena za matenda.
BAIBULO ndibukhu losimba za moyo. Palibe cholembedwa chirichonse kapena bukhu limene limakhudza mbali za moyo zochuluka motero. Pali kugwirizana pakati pa thanzi labwino ndi moyo, choncho sikuyenera kukhala kodabwitsa kuti Baibulo liri ndi malamulo amakhalidwe abwino kwambiri ochita mwachindunji ndi thanzi. Baibulo limatchula matenda ambiri, monga ngati khate, nthenda yotuluka mudzi, mbulu, ndi kudwala m’mimba.—Deuteronomo 24:8; 28:27; Luka 14:2; 1 Timoteo 5:23.
Cholinga chachikulu chimene Baibulo linalembedwera sichinali kutipatsa malangizo pa matenda akuthupi. Komabe, chidziŵitso chimene limapereka ncholongosoka mwasayansi ndipo nchopindulitsa kuchipenda. Thupi lamunthu linali lochititsa mantha kwa wamasalmo wakale, ndipo ponena za ilo analemba kuti: ‘Pakuti inu [Yehova] munalenga impso zanga; [munandilekanitsa m’mimba mwa amayi, NW]. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; Ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikira inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m’munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziŵalo zanga zonse zinalembedwa m’bukhu mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.’—Salmo 139:13-16.
Ngakhale kuti mluza umalekanitsidwa mumdima m’chibaliro, Yehova amauwona ukuumbika ndi mafupa ake akupangika. Kwa iye ‘mdima ukunga kuunika.’ (Vesi 12) Palibe chobisika kwa Yehova. Malinga nchidziŵitso cha zamankhwala, nsapo imalekanitsa mluza kwa amayi ndipo mwakutero sumakanidwa monga thupi lachilendo. Komabe, chowonadi chonenedwa ndi salmoli sichaluso la zamankhwala koma chauzimu, chakuti, Yehova amawona zonse, ngakhale mumdima wa m’chibaliro.
Kuchokera pa mphindi yakutenga pathupi, ‘ziŵalo za thupi lathu zimakhala zitalembedwa’ m’majini a selo la dzira lopatsidwa mphamvu m’chibaliro cha mayi. Ndiponso, ponena za nthaŵi mu ‘masiku akuti ziumbidwe,’ chirichonse mwadongosolo lake, imadziwidwa ndi koloko za m’thupi zimene zinalinganizidwa m’majini.
Wamasalmo Davide sanadziŵe tsatanetsatane yenseyu wa sayansi, koma Yehova, yemwe anamuuzira iye kulemba salmolo, anatero, pakuti Ndiye analenga munthu. Osuliza apamwamba amakana kuti Davide ndiye analemba zimenezi, komabe ngakhale iwo amaika nthaŵi ya kulembedwa kwa salmolo kukhala zaka mazana ambiri Kristu asanadze.
Baibulo Limagogomezera Kuchinjiriza
Tikapenda malamulo a Mulungu operekedwa kwa Israyeli kupyolera mwa Mose zaka mazana 15 Kristu asanadze, timawona kuti chigogomezero chachikulu cha Chilamulocho ponena za thanzi chinasumikidwa mowonekera bwino lomwe pa kuchinjiriza. Mwachitsanzo, pa Deuteronomo 23:13 chimati: ‘Nimukhale nacho chokumbira mwa zida zanu, ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe nacho, ndi kutembenuka ndi kufotsera chakutulukacho.’ Lamulo lakufotsera zonyansa limeneli linali muyezo wapamwamba kwambiri wa kutetezera matenda oyambukitsidwa ndi ntchentche a salmonellosis, shigellosis, typhoid, ndi matenda ena a m’mimba amene akuphabe zikwi zambiri lerolino m’madera m’mene lamulo lamakhalidwe abwino limenelo silikusungidwa.
Levitiko mutu 11 amasonyeza mfundo yakuti matenda akhoza kufalitsidwa ndi kachirombo, ndi mbeŵa, komanso kwakukulukulu, ndi madzi oipitsidwa. Madzi oterowo amatsimikiziritsa mfundo yakuti matenda amachititsidwa ndi tizirombo tosawoneka ndi maso wamba, kusonyeza kuti Baibulo liri patsogolo kwenikweni pa akatswiri onga Leeuwenhoek (1683) kapena Pasteur (zaka za zana la 19). Zirinso tero ponena za kubindikiritsa wodwala khate, kolamuliridwa m’mutu 13 wa Levitiko.
Ziletso pazakudya zolembedwa pa Levitiko 11:13-20 zinaphatikizapo zamoyo zodya zinzake, monga ngati nkhwazi, mphungu, ndi akadzidzi, ndi zamoyo zodya zonyansa, monga ngati khwangwala ndi muimba. Pokhala kuti ziri pamwamba pa ndandanda ya kudyana, izo ziri ndi ululu wochuluka m’thupi. Nyama zokhala chapansi pa ndandanda ya kudyana zimadya ululu umenewu mumlingo wochepa kwambiri, pamene kuli kwakuti zija zokhala pamwamba pa ndandanda ya kudyana zimadya ululuwo wochuluka kwabasi. Chilamulo cha Mose chinalola kudya nyama zodya masamba ndipo zosakhala pa ndandanda ya kudyana ya nyama zokhala ndi ululu. Nyama zina zoletsedwa zinali ndi tizirombo m’matupi tonga tija toyambukitsa malungo a trichinosis.
Chiletso cha Baibulo cha kugwiritsira ntchito mwazi molakwa, chophatikizidwa m’malo ambiri m’Chilamulo cha Mose, tsopano chikutsimikiziridwa kukhala chabwino m’zamankhwala pambuyo pa zaka 3,500. (Genesis 9:4; Levitiko 3:17; 7:26; 17:10-16; 19:26; Deuteronomo 12:16; 15:23) Chiletsocho chinabwerezedwa m’Malemba Achigiriki Achikristu pa Machitidwe 15:20, 29 ndi 21:25. Ochita zamankhwala akuyesayesa kuchepetsa kapena kulekeratu kugwiritsira ntchito mwazi woperekedwa ndi anthu pochiritsa impso, m’makina amene amachita ntchito ya mtima ndi mapapo pa opareshoni ya mtima, ndi m’maopareshoni wamba. Nthenda yakutupa chiŵindi m’mitundu yake yambiri, AIDS, kuyambukiridwa kwa ziŵalo za m’thupi, ndi matenda ena ambirimbiri oyambukira kupyolera m’mwazi ali zokumbutsa zomvetsa chisoni kwa anzeru akudziko amene amanyalanyaza malamulo a Mulungu.
Kuseŵera nkofunika m’kukhala ndi thanzi labwino, ndipo Baibulo limazindikira mapindu ake. Kuseŵera kwamphamvu kwa mphindi 20 katatu pamlungu kungachepetseko maupandu a mtima ndi kayendedwe ka mwazi. Kumawonjezera maselo otetezera thupi otchedwa HDL, kumakupatsani nyonga yochuluka, ndi kupangitsa thupi lanu kukhala lomasuka, ndi kukupatsani lingaliro lakumva bwino. Baibulo, pozindikira phindu la kuseŵera, limakuika pambuyo pa kukulitsa uzimu kumene kuli kofunika koposa: ‘Chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’—1 Timoteo 4:8.
Malamulo Abaibulo amakhalidwe amatumikira monga chitetezo chachikulu ku matenda opatsirana mwakugonana, amene mosakaikira adaliko komabe osadziŵidwa kapena mwinamwake osaganiziridwa konse ndi akatswiri kwa zaka mazana ambiri.—Eksodo 20:14; Aroma 1:26, 27; 1 Akorinto 6:9, 18; Agalatiya 5:19.
“Bukhu Lasayansi Lolondola Kwenikweni”
Hippocrates anali sing’anga Wachigiriki wa m’zaka za zana lachisanu ndi lachinayi B.C.E. amene anadzadziŵika monga “atate wa mankhwala,” koma zambiri zimene Baibulo limanena pamatenda zinalembedwa ndi Mose, pafupifupi zaka chikwi nthaŵiyo isanafike. Komanso ubwino wake ngwakuti, The AMA News inafalitsa kalata yochokera kwa dokotala yomwe inati: “Ofufuza zamankhwala odziŵa koposa amene tsopano akuchita ntchito yabwino kwenikweni akufika pachigamulo chakuti Baibulo liri bukhu lasayansi lolondola kwenikweni. . . . Zenizeni za moyo, kufufuza matenda, kuchiritsa, ndi mankhwala ochinjiriza zotchulidwa m’Baibulo nzopita patsogolo ndi zodalirika kuposa nthanthi za Hippocrates, zambiri zimene sizinatsimikiziridwebe, ndipo zina zopezedwa kukhala zolakwika kotheratu.”
Atasonyeza kuti malamulo aukhondo pakati pa mitundu yozinga Israyeli wakale anali otsika kwenikweni ngati analiko nkomwe, Dr. A. Rendle Short anati m’bukhu lake la The Bible and Modern Medicine: “Chotero nzodabwitsa kwambiri kuti bukhu monga Baibulo, lonenedwa kukhala lopanda sayansi, liri ndi malamulo a ukhondo, ndipo chodabwitsanso nchakuti mtundu womwe unangothaŵa kumene muukapolo, kaŵirikaŵiri womakanthidwa ndi adani ndi kutengedwa kuukapolo kwanthaŵi ndi nthaŵi, unali ndi malamulo anzeru ndi opindulitsa onena za thanzi m’mabuku ake amalamulo.”
Mavuto a Kugwirizana kwa Thupi ndi Maganizo
Baibulo latsimikizira kukhala patsogolo m’zamankhwala kuzindikira mavuto a thanzi ochita ndi kugwirizana kwa thupi ndi maganizo kalekale zisanavomerezedwe ndi antchito zamankwala. Ndiponso, kufotokoza kwa Baibulo kwa mbali imene maganizo amachita m’nthaŵi ya matenda akuthupi kukukhalabe chitsanzo chomvekera bwino. Miyambo 17:22 imati: ‘Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.’ Onani kuti mawuŵa satofunikira kuwapenda, ali mfundo yolunjika. Palibe chilangizo chouza munthu wopsinjika maganizo kuleka kuvutika nazo, monga ngati kuti zinali zosavuta motero.
Kaimidwe kabwino kamaganizo nkothandiza; kuda nkhaŵa nkoipa ndi kovulaza. ‘Nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.’ (Miyambo 12:25) Tiyenera kusinkhasinkha mawu a pa Miyambo mutu 18 vesi 14 akuti: ‘Mtima wa munthu ulimbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka?’ Lembali limapereka lingaliro lakuti kukhoza kwa munthu kupirira nthenda yakuthupi yakutiyakuti kungatheketsedwe mwakuchirikizidwa ndi mphamvu ya uzimu wake.
Katswiri wa maganizo James T. Fisher anati ponena za phindu la maganizo lopezeka Muulaliki wa Yesu wa pa Phiri: “Mukanati musonkhanitse nkhani zonse zodalirika zolembedwapo ndi akatswiri amalingaliro ndi a maganizo pankhani ya mkhalidwe wabwino wa maganizo—mukanati mudzisonkhanitse pamodzi, kuzisanthula, ndi kuchotsamo zonse zosafunikira—mukanati musankhemo kokha chidziŵitso chenicheni cha sayansi ndi kusiya mawu opanda pake, ndipo mukanati mupatse mfundo za chidziŵitso chenicheni cha sayansi zimenezi kwa akatswiri olemba ndakatulo amakono okhoza koposa kuti zilongosoledwe mwaluso, mukakhalabe ndi malongosoledwe osalunjika ndi opereŵera poyerekezera ndi Ulaliki wa pa Phiri.”—A Few Buttons Missing, tsamba 273.
Kugwirizana kwa thupi ndi maganizo kungayambukire mkhalidwe wathu wakuthupi, koma ichi mwa icho chokha sichimatanthauza kuti palibe kudwala kwakuthupi kumene kwaloŵetsedwamo. Chifukwa chake, kuli kofunika choyamba kuyesayesa kuthandiza ndi zosoŵa zakuthupi ndipo pang’ono kwenikweni kuzindikira matenda, pamene kuli kwakuti panthaŵi imodzimodzi mukumalimbikitsa kaimidwe kabwino ka maganizo ndi kulimbika mtima, zimene zidzathandiza munthuyo kupirira. Izi nzofunika kwambiri makamaka pamene sipangakhale njira yochiritsira yotsimikizirika m’dongosolo lino la zinthu.
Pambuyo pa uchimo wa Adamu, imfa inakhala chenicheni chachibadwa chosapeŵeka kwa anthu. (Aroma 5:12) Chifukwa chake, sikwabwino kaŵirikaŵiri kugwirizanitsa nthenda ya munthu ndi mkhalidwe wake wauzimu. Nkwabwino kukumbukira zimenezi pamene tikuchita ndi mavuto a anthu amene akuvutika ndi malingaliro.
Mbali ya Sing’anga
Kodi ndimotani mmene Akristu amaonera asing’anga ndi machiritsidwe amankhwala amakono? Pamene tisanthula Baibulo, timapeza kuti Malemba samachirikiza kuwakweza mopambanitsa asing’anga kapena kuwona njira zochiritsira zamakono kukhala chiyembekezo chokha chopezera thanzi labwino. M’malomwake, pali umboni wonena zosiyana. Marko akutiuza ponena za ‘munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire’ kwa zaka zambiri amene ‘anamva zoŵaŵa zambiri ndi asing’anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang’ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula.’ (Marko 5:25-29) Ngakhale kuti vuto lofala limeneli lerolino limachiritsidwa, matenda ambiri samachiritsika, ndipo matenda ochuluka osachiritsika akutulukiridwa nthaŵi zonse.
Komabe, Baibulo silimachirikiza kusuliza zimenezi mopambanitsa kumene ena amachita amene amawona kuchiritsa kwamwambo kukhala ndi phindu lochepa kapena kopandiratu lirilonse. Ena amanyalanyaza dokotala kotheratu ndi kudzidalira okha kapena kachitidwe kena kosagwiritsira ntchito mankhwala kamene kangakhale chizoloŵezi cha panthaŵiyo. Pa Akolose 4:14, kumlongosola Luka monga sing’anga “wokondedwa” mosakaikira kunasonya ku ziyeneretso zake zauzimu mmalo mwa maluso ake a mankhwala. Komabe, mwachiwonekere mwaŵi umene anakhala nawo wa kulemba mbali ya Malemba Opatulika pansi pakuuziridwa sukanapatsidwa kwa munthu amene machitidwe ake akuchiritsa anali oluluzika kapena otsutsa malemba.
Pali umboni wakuti Luka anagwiritsira mankhwala amene anali amakono m’nthaŵi yake, akugwiritsira ntchito mawu ndi maina azamankhwala amene amavumbula chisonkhezero cha Hippocrates. Ngakhale kuti Hippocrates nthaŵi zina sanali wolondola, iye anayesayesa kuyambitsa nzeru yabwino m’kachitidwe ka kuchiritsako ndipo anatsutsa kukhulupirira malaulo ndi nthanthi zachipembedzo za mankhwala. Ndiponso, fanizo lokhweka la Yesu pa Luka 5:31 lakuti, ‘Amene ali olimba safuna sing’anga; koma akudwala ndiwo,’ silikatanthauza kanthu kwenikweni ngati awo okhala ndi chidziŵitso m’mankhwala sanavomerezedwe kukhala othandiza m’matenda.
Palibe maziko Amalemba ochirikiza lingaliro lakutsutsa kotheratu kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala akupha tizirombo tamatenda m’thupi, mankhwala otetezera thupi, kapena akupha ululu ngati aperekedwa. Yeremiya 46:11 ndi 51:8 amalongosola mvunguti m’Gileadi umene uyenera kuti unali ndi mphamvu zakupha ululu ndi zotetezera thupi. Palibe Malemba alionse kapena chiphunzitso chimene chimatsutsa kumwa mankhwala.
Komabe, mankhwala ochuluka akupha tizirombo tamatenda m’thupi, alephera kugonjetsa matenda oyambukitsidwa ndi ntchentche, udzudzu, ndi nkhono—amene ali chochititsa imfa chachikulu padziko lonse. Ogwira ntchito zaumoyo atembenukira ku malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo a njira zotaira zonyansa, kutetezera madzi ogwiritsiridwa ntchito, kuchinjiriza tizirombo toyambukitsa matenda, ndi kupereka machenjezo m’zakukhudzana kwa manja ndi milomo. Posachedwapa m’ma 1970, anesi ndi adokotala ankakumbutsidwa mobwerezabwereza ndi zizindikiro zomamatizidwa pa masinki ndi makama a odwala zimene zinalembedwapo kuti: “Sambani m’Manja”—njira yaikulu yochinjirizira kufalikira kwa matenda.
Mawu Achenjezo
Awo amene amapereka malangizo pa zaumoyo—kaya akhale sing’anga, katswiri wosamalira ziŵalo za thupi, katswiri wodziŵa mankhwala a ziŵalo zathupi, kapena bwenzi wokhala ndi cholinga chabwino koma mwina wosadziŵa bwino—amakhala ndi thayo lalikulu pamene akupatsa malangizo wodwala. Ziri tero makamaka ngati malangizo amene akuwapereka ali aupandu kapena olakwika, achinyengo, kapena ochedwetsa chithandizo chimene chimagwira ntchito. Baibulo limapereka machenjezo ambiri kwa ochiritsa ndi ochiritsidwawo ponena za chinyengo ndi kukhulupirira mizimu ngati wina angathedwe nzeru m’kufunafuna kwake chithandizo. Kumbukirani Miyambo 14:15: ‘Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.’
Kodi malamulo amakhalidwe abwino ofotokozedwa m’Malemba Opatulika amathandiza kusungitsa thanzi lerolino? Monga momwe Chilamulo cha Mose chinagogomezera kuchinjiriza, lerolinonso, kuwachinjiriza matenda kwatsimikizira kukhala kofunika kwambiri kuposa kuchiritsa kwenikweniko. Mfundo yamakono ya World Health Organization m’kuyesayesa kuphunzitsa maiko osatukuka njira zamokono zochiritsira njakuti: “Kuchinjiriza kuposa kuchiritsa.”
Chomalizira, Mkristu ayenera kukhala ndi lingaliro lolemekezeka, lowona patali ponena za thanzi ndi cholinga cha kugwiritsira ntchito thanzi labwino kulemekeza Mulungu mwakupititsa patsogolo ntchito yosangalatsa ya Ufumu. Ndipo ponena za ulamuliro wa Ufumuwo, lonjezo ndi ili: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
[Chithunzi patsamba 22]
“Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika”