“Yehova Apatsa Nzeru”
KODI ndi zochita zotani zomwe zimakudyerani nthaŵi ndi nyonga zanu? Kodi chomwe mumafunitsitsa kwambiri ndicho kudzipangira dzina labwino? Kodi m’madzipereka pa kusonkhanitsa chuma? Bwanji ponena za kuphunzira ntchito inayake mofunitsitsa kapena kukulitsa ukatswiri m’mbali imodzi kapena m’mbali zina za maphunziro? Kodi kukulitsa unansi wabwino ndi ena n’kofunika kwa inu? Kodi mumafunitsitsa kukhala wathanzi labwino?
Zonse zimene zatchulidwa pamwambazi zingaoneke kukhala zofunikadi. Koma ngakhale zili choncho, kodi n’chiyani chimene chili chofunika kopambana? Baibulo likuyankha kuti: “Nzeru ipambana, tatenga nzeru.” (Miyambo 4:7) Tsono kodi nzeru tingaipeze motani, ndipo kodi mapindu ake n’ngotani? Chaputala chachiŵiri cha buku la Baibulo la Miyambo chikupereka mayankho.
‘Tcherera Makutu Ako Kunzeru’
M’mawu a atate wachikondi, mfumu yanzeru Solomo ya Israyeli wakale inanena kuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu.”—Miyambo 2:1-5.
Kodi mukuona kuti kupeza nzeru ndi udindo wa yani? M’mavesi ameneŵa, mawu akuti “ukalandira,” “ukaitananso,” “ukaifunafuna,” akupezeka nthaŵi zitatu. Mwachionekere, ndi udindo wa aliyense wa ife kufunafuna nzeru ndi zonse zochirikiza nzeruyo, monga kuzindikira ndi luntha. Komabe, choyamba, tifunikira ‘kulandira’ ndiponso “kusunga” m’chikumbumtima mawu anzeru olembedwa m’Malemba. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuphunzira Baibulo.
Nzeru ndiyo kugwiritsa ntchito moyenera chidziŵitso chopatsidwa ndi Mulungu. Ndipotu modabwitsa zedi, nzeru imeneyi ikupezeka m’Baibulo! Inde, m’Baibulo muli mawu anzeru, monga omwe analembedwa m’mabuku a Miyambo ndi Mlaliki, ndipo n’kofunikadi kuti titchere khutu ku mawu ameneŵa. Komanso m’masamba a Baibulo, timapezamo zitsanzo zambiri zomwe zikusonyeza mapindu akugwiritsa ntchito mapulinsipulo aumulungu ndiponso mbuna zomwe wina angagwemo ngati awanyalanyaza. (Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11) Mwachitsanzo, lingalirani za nkhani ya Gehazi wadyerayo, mnyamata wa mneneri Elisa. (2 Mafumu 5:20-27) Kodi zimenezi sizimatiphunzitsa nzeru ya kupeŵa dyera? Bwanji ponena za zotsatira zomvetsa chisoni za kuchezera ‘akazi a m’dziko’ la Kanani, komwe mwana wamkazi wa Yakobo, Dina ankachita, kumenenso kunkaoneka ngati sikungadzetse ngozi iliyonse? (Genesis 34:1-31) Kodi nthaŵi zonse sitizindikira kuti n’kupusa zedi kupanga mayanjano oipa?—Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33.
Kutcherera khutu ku nzeru kumaphatikiza kupeza kuzindikira ndi kumvetsetsa. Malinga n’kunena kwa Webster’s Revised Unabridged Dictionary, kuzindikira ndi “mphamvu kapena luntha lomwe maganizo amasiyanitsira chinthu china ndi chinzake.” Kuzindikira kwaumulungu ndiko kukhoza kusiyanitsa cholondola ndi cholakwika ndiyeno kenako n’kusankha njira yoyenera. Kusiyapo ngati ‘tilozetsa mtima wathu’ ku kuzindikira kapena ngati tichita khama kuti tikupeze, tingakhalebe bwanji “m’njirayo yakumuka nayo kumoyo”? (Mateyu 7:14; yerekezani ndi Deuteronomo 30:19, 20.) Kuphunzira ndiponso kuchita zomwe Mawu a Mulungu akunena kumazindikiritsa.
Kodi ndi motani mmene ‘tingaitanire luntha,’ kukhoza kuona kugwirizana kwa mfundo za nkhani ina ndi inzake komanso ndi nkhani yonseyo? N’zoona kuti kuchuluka kwa zaka komanso zomwe takumana nazo n’zina mwa zinthu zomwe zingatithandize kukhala omvetsetsa, koma osati kwenikweni. (Yobu 12:12; 32:6-12) Wamasalmo anati: “Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu [a Yehova].” Ndipo anaimbanso kuti: “Potsegulira mawu anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.” (Salmo 119:100, 130) Yehova ndi “Nkhalamba Yakale lomwe” ndipo kuzindikira kwake n’kwakukulu kopandanso malire, kuposa kuzindikira kwa mtundu wonse wa anthu. (Danieli 7:13) Mulungu angapatse luntha munthu wosadziŵa kanthu, kum’theketsa kupita patsogolo m’mkhalidwe womwewo ngakhale omwe ali azaka zambiri. Choncho, tiyenera kukhala akhama kuphunzira ndi kutsatira Mawu a Mulungu, Baibulo.
Mawuwo akuti “ukalandira,” “ukaitananso,” “ukaifunafuna” m’ndime yoyambirira ya chaputala chachiŵiri cha Miyambo akutsatana ndi mawu akuti ‘kusunga’, ‘kufuulira,’ ‘kuipwaira.’ N’chifukwa chiyani mlembiyo anagwiritsa ntchito mawu osonyeza mphamvu zowonjezereka ameneŵa? Buku lina limati: “Munthu wanzeruyu [pano] akunena motsindika za kufunika kwa khama pofunafuna nzeru.” Inde, tiyenera kulondola nzeru mwakhama ndi mikhalidwe ina yogwirizana nayo monga kuzindikira ndi luntha.
Kodi Mudzayesetsa?
Chinthu chofunika kwambiri kuti muzichita zinthu mwanzeru ndicho kuphunzira Baibulo mwakhama. Komabe, phunziro limeneli, siliyenera kukhala kungoŵerenga kuti mupeze chidziŵitsocho ayi. Chofunika kwambiri pamene tikuphunzira Malemba ndicho kusinkhasinkha ndi cholinga pa zomwe tikuŵerengazo. Kupeza nzeru ndi kuzindikira zimaphatikiza kusinkhasinkha pa momwe tingagwiritsire ntchito zomwe tikuphunzirazo pothetsa mavuto ndi kusankha zochita. Kuti tikhale aluntha pamafunika kulingalira mmene nkhani yatsopanoyo ikugwirizanira ndi zomwe tikudziŵa kale. Ndani angatsutse kuti kuphunzira Baibulo koteroko kumafuna nthaŵi ndi kuyesetsa mwamphamvu? Nthaŵi ndi nyonga zomwe timawonongera pamenepa n’chimodzimodzi ndi zomwe zingafunike ‘pofunafuna siliva ndi popwaira chuma chobisika.’ Kodi mudzayesetsa? Kodi ‘mudzachita machaŵi’ kuti muchite zimenezo?—Aefeso 5:15, 16.
Lingalirani za chuma chochuluka chomwe tingapeze ngati moona mtima, tikumba mozama m’Baibulo. Ndithudi, ‘tidzam’dziŵadi Mulungu.’ Chidziŵitso chabwino, chokhazikika, chopatsa moyo cha Mlengi wathu! (Yohane 17:3) “Kuopa Yehova” ndi chuma chinanso chomwe tingapeze. Mantha aulemu ameneŵa n’ngamtengo wapatali zedi! Mantha abwino akuopa kusam’kondweretsa ayenera kulamulira mbali ina iliyonse ya moyo wathu, kuwonjezera tanthauzo lofunika lauzimu ku zonse zomwe timachita.—Mlaliki 12:13.
Kufunitsitsa kufufuza ndi kukumba chuma chauzimu ziyenera kukhala zamphamvu mwa ife. Kuti athandize kufufuza kwathuku, Yehova wapereka zida zokumbira zapamwamba kwambiri, zofalitsa za choonadi zapanthaŵi yake Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, komanso zofalitsa zinanso zofotokoza Baibulo. (Mateyu 24:45-47) Kuti tiphunzire Mawu ake ndi njira zake, Yehova waperekanso misonkhano yachikristu. N’kofunika kuti tizipezekapo nthaŵi zonse, kumvetsera mosamalitsa zomwe zikukambidwa, kuyesetsa kumamatira ndi kukumba mfundo zazikulu, ndiponso kuganiza mozama za ubale wathu ndi Yehova.—Ahebri 10:24, 25.
Simudzalephera
Nthaŵi zambiri, pofufuza ngale, golide, kapena siliva wobisika m’nthaka munthu amalephera kuzipeza. Zimenezi sizingachitike ngati mukufufuza chuma chauzimu. N’chifukwa chiyani tikuti sizingachitike? Solomo akutitsimikizira kuti: “Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”—Miyambo 2:6.
Mfumu Solomo inatchuka kwambiri chifukwa cha nzeru zake. (1 Mafumu 4:30-32) Malemba akusonyeza kuti iye ankadziŵa zinthu zambiri, kuphatikizapo zomera, nyama, chibadwa cha munthu, komanso Mawu a Mulungu. Iye anatchuka kumayiko ena chifukwa chosonyeza kuzindikira monga mfumu yachinyamata pamene anathetsa mkangano pakati pa akazi aŵiri amene anali kukanganirana mwana. Aliyense wa iwo anali kunena kuti ndiye mayi wa mwanayo. (1 Mafumu 3:16-28) Kodi n’chiyani chomwe chinali gwero la luso lake lapamwambalo? Solomo anapempha kwa Yehova “nzeru ndi chidziŵitso” ndi luso la ‘kuzindikira pakati pa zabwino ndi zoipa.’ Yehova anamupatsa iye zonsezi.—2 Mbiri 1:10-12; 1 Mafumu 3:9.
Ifenso tiyenera kupempherera thandizo la Yehova pamene tikuphunzira Mawu ake mwakhama. Wamasalmo anapemphera kuti: “Mundionetse njira yanu, Yehova ndidzayenda m’choonadi chanu: muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.” (Salmo 86:11) Yehova anavomereza pemphero limenelo, popeza analilemba m’Baibulo. Tili ndi chikhulupiriro kuti kupempha kwathu chithandizo chake moona mtima ndi mobwerezabwereza kuti tipeze chuma chauzimu m’Baibulo kudzayankhidwa.—Luka 18:1-8.
Solomo anasonyeza kuti: “Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika; kuti achinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake. Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.” (Miyambo 2:7-9) Chimenechitu n’chilimbikitso champhamvu zedi! Yehova samangopereka nzeru yeniyeni yokha kwa omwe akuifunafuna moona mtima komanso ndiye chikopa chotetezera kwa oongoka mtima chifukwa amasonyeza nzeru yeniyeni ndipo modzipereka amachita mogwirizana ndi miyezo yake yolungama. Tikhaletu mmodzi wa omwe Yehova akuwathandiza kuzindikira “mayendedwe onse abwino.”
Pamene “Udzakondwera ndi Kudziŵa”
Phunziro laumwini la Baibulo, chinthu chofunika kwambiri kuchita pofunafuna nzeru, silosangalatsa kwenikweni kwa anthu ambiri. Mwachitsanzo, Lawrence, wazaka 58, anati: “Nthaŵi zonse ndagwira ntchito ndi manja anga. Kuŵerenga kuti ndiphunzire n’chinthu chovuta zedi kwa ine.” Ndiponso Michael wazaka 24, yemwe ankadana ndi maphunziro kusukulu ananena kuti: “Ndinali kuchita kudzikakamiza kuti ndikhale pansi ndi kuŵerenga kuti ndiphunzire.” Komabe, chikhumbo chofuna kuphunzira chingakuzidwe.
Lingalirani zomwe Michael anachita. Iye akusimba kuti: “Ndinadzikakamiza kumaphunzira kwa theka la ola tsiku lililonse. Posapita nthaŵi ndinatha kuona zotsatirapo zake m’maganizo anga, m’ndemanga zanga pamisonkhano yachikristu, komanso m’kalankhulidwe kanga ndi ena. Tsopano ndimakhala wachidwi pamene nthaŵi yanga ya phunziro ikuyandikira, ndiponso ndimanyansidwa kwambiri ngati patachitika china chake chododometsa phunzirolo.” Inde, timayamba kusangalala ndi phunziro laumwini tikamaona mmene tikupitira patsogolo. Nayenso Lawrence anachita khama kuphunzira Baibulo ndipo, m’kupita kwa nthaŵi, anayamba kutumikira monga mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova.
Kuti phunziro laumwini likhale losangalatsa pamafunika kuchita khama nthaŵi zonse. Komanso mapindu ake n’ngaakulu. Solomo ananena kuti: “Pakuti nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza.”—Miyambo 2:10, 11.
“Kukupulumutsa ku Njira Yoipa”
Kodi ndi motani mmene nzeru, chidziŵitso, luso la kulingalira, ndi kuzindikira zidzakhalire chotetezera? “[Zidza]kupulumutsa ku njira yoipa,” akutero Solomo, “kwa anthu onena zokhota; akusiya mayendedwe olungama, akayende m’njira za mdima; omwe asangalala pochita zoipa; nakondwera ndi zokhota zoipa; amene apotoza njira zawo, nakhotetsa mayendedwe awo.”—Miyambo 2:12-15.
Inde, omwe amakondadi nzeru yeniyeni amapeŵa kuyanjana ndi wina aliyense ‘wonena zokhota,’ kutanthauza kuti, wonena zinthu zosemphana ndi zomwe zili zoona ndi zolondola. Kulingalira ndi kuzindikira zimatetezera kwa omwe amakana choonadi ndi cholinga chongofuna kuyenda m’njira zamdima, komanso kwa iwo amene ali amphulupulu omwe amasangalala pochita zoipa.—Miyambo 3:32.
Tiyeneradi kukhala oyamikira kwambiri popeza kuti nzeru yoona ndi mikhalidwe ina yabwino yolingana nayo imatitetezanso ku njira zoipa za amuna ndi akazi amikhalidwe yonyansa! Solomo ananenanso kuti mikhalidwe imeneyi “idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mawu ake; wosiya bwenzi la ubwana wake, naiŵala chipangano cha Mulungu wake; nyumba yake itsikira kuimfa, ndi mayendedwe ake kwa akufa; onse akunka kwa iye sabweranso, safika ku njira za moyo.”—Miyambo 2:16-19.
“Mkazi wachilendo,” wachigololo, akunenedwa kukhala yemwe amasiya “bwenzi la ubwana wake.” Mwamuna wa unamwali wake.a (Yerekezani ndi Malaki 2:14.) Mkaziyo waiŵala kuletsedwa kwa chigololo komwe kunali mbali ya pangano la Chilamulo. (Eksodo 20:14) Njira zake zikuloŵera ku imfa. Awo amene angayanjane ndi mkaziyo sangathenso ‘kufika ku njira za moyo,’ popeza kuti zivute zitani adzatsikira kuimfa komwe sangabwereko. Mwamuna wozindikira ndi wolingalira bwino amadziŵa za zokopa zachisembwere ndipo mwanzeru amapeŵa kukodwa m’zimenezo.
“Oongoka Mtima Adzakhala M’dziko”
Pofotokoza mwachidule cholinga cha uphungu wake wonena za nzeru, Solomo anati: “Nzeru idzakuyendetsa m’njira ya anthu abwino, kuti usunge mayendedwe a olungama.” (Miyambo 2:20) Ntchito ya nzeru n’njabwino zedi! Imatithandiza kukhala ndi moyo wachimwemwe ndi wokhutiritsa umene Mulungu amaukonda.
Lingaliraninso madalitso aakulu omwe asungidwira omwe ‘amayenda m’njira ya anthu abwino.’ Solomo anapitiriza ndikunena kuti: “Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Khalani m’gulu la anthu angwiro omwe adzakhale kosatha m’dziko latsopano lolungama la Mulungu.—2 Petro 3:13.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu lakuti “wachilendo” linali kugwiritsidwa ntchito ponena za omwe analeka kuchita zinthu mogwirizana ndi Lamulo ndipo potero akumadziika okha kutali ndi Yehova. Choncho, mkazi wachigololo, osati munthu wakudziko lina, akutchedwa “mkazi wachilendo.”
[Chithunzi patsamba 26]
Solomo anapempherera nzeru. Ifenso tiyenera kuipempherera