Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingatani Kuti Anthu Asamangofanizira Zochita Zanga ndi za Makolo Anga?
“Bambo anga ndi mkulu wodziŵika kwambiri mu mpingo wina wa Mboni za Yehova. Ndimawapatsa ulemu, koma kungoti nthaŵi zina ndimaipidwa ndi zoti kwina kulikonse kumene ndingapite anthu azingoti ndine mwana wa mbale uje.”—Anatero Larry.a
“Poti bambo anga ndi mkulu wotchuka, poyamba ndinkangoona ngati wina aliyense ankangofuna kuti ndizichita zinthu zimene sindingakwanitse, choncho zinkandivuta kuchita zinthu bwinobwino.”—Anatero Alexander.
MUNTHU ukamakula, zimachitika ndithu kuti umalakalaka kukhala wodziimira pawekha, wotha kudzipangira dzina, kapena kuti mbiri yakoyako. Mutabadwa makolo anu anakupatsani dzina limene linawasangalatsa iwowo. Komano panopa pamene mukukula kukhala wachinyamata ndithu, mumafuna mutakhala ndi “dzina,” ndiko kuti kupanga mbiri yanuyanu.
Mfumu Solomo inalemba kuti: “Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golidi.” (Miyambo 22:1) Ngakhale pamene mudakali wamng’ono, n’kutheka kuti mungafune kuyamba kudzipangira mbiri yanuyanu.
Kufaniziridwa ndi Makolo Anu
Achinyamata ena amaona kuti anthu amafanizira zochita zawo ndi dzina la makolo awo kapena zochita za makolowo, ngati mmene ankachitira Larry ndi Alexander. Mwina makolo awo ngotchuka m’dera lawolo chifukwa cha ntchito kapena maphunziro awo. Kapenanso n’kutheka kuti ngodziŵika kwambiri mu mpingo wachikristu. Ngati ndi mmene alili makolo anu, nthaŵi zina mungamaonedi ngati maso a anthu onse amangokhala pa inu ndiponso kuti anthu amangoonetsetsa chilichonse chimene mukuchita. Zingamakuipireni kuti mumakakamizika kuchita zinthu m’njira inayake chabe chifukwa chakuti makolo anu ndi odziŵika.
Mwachitsanzo, bambo ake a Ivan ndi mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova wa m’dera la kwawo. Ivan anati: “Popeza kuti anthu ambiri ankadziŵa bambo anga ndiponso ankawalemekeza kwambiri, nthaŵi zonse ndinkangoona kuti ndiyenera kukhala mwana wopereka chitsanzo chabwino kwa ena kusukulu ndi kunyumba komwe. Ndinkaona kuti makolo ena ankanditenga kuti ndine woyenera kukhala chitsanzo cha mmene akufunira kuti ana awo azichitira zinthu. Ngakhale kuti zimenezo zinkandisangalatsa, koma zinkandiika pampanipani kwambiri pofuna kukhala chitsanzo chabwino kwa ena. Mapeto ake, nthaŵi zina ndinkachita zinthu mopitirira muyeso ndipo sindinkaona kuti ndili ndi vuto lililonse.” Alexander anati: “Ndinkaona kuti anthu ankangokhalira kuyang’ana ineyo nthaŵi zonse ndiponso kuti ngati nditangolakwitsa kenakake, anthu sakanalephera kundiloza chala.”
Larry, yemwe mawu ake tawalemba pamwamba paja, ankayesetsa kuti anthu asachite naye chidwi kwenikweni pobisa dzina la bambo ake. Iye anati: “Ndikakumana ndi anthu osandidziŵa pa mapwando enaake, ndinkangoti, ‘Muli bwanji, dzina langa ndine Larry,’ basi n’kulekera pompo, osatchula n’komwe dzina la bambo anga. Zikakhala zotheka, ndinkasaina ngakhale mafomu polemba dzina langa loyamba basi. Ndinkaopera kuti anthu andiona mwa njira inayake akadziŵa kuti bambo anga ndani. Ndinkafuna kuti anzanga azindiona ngati wina aliyense.”
Inde, n’zomveka ndithu kuti ena angamaone kuti muyenera kumachita zinthu mwapadera ngati bambo anu ali mkulu wachikristu kapena mtumiki wotumikira. Pajatu amuna amene ali ndi udindo woterewu amayenera kukhala “akuweruza bwino ana awo, ndi iwo a m’nyumba yawo ya iwo okha.” (1 Timoteo 3:5, 12) Ndiye n’zosadabwitsa kuti anthu amafuna kuti muzipereka chitsanzo chabwino! Koma kodi zimenezi zilibe pabwino paliponse? Mukaganizira kuti Paulo anasankha Mkristu wachinyamata Timoteo, mwinanso asanakwanitse zaka 20 n’komwe, kuti aziyenda naye n’kumachita naye ntchito ya utumiki, muona kuti palibe cholakwika n’kutero. (1 Atesalonika 3:1-3) Ndiye muyenera kuyesetsa kukhala chitsanzo chabwino, kaya bambo anu akhale mkulu kapena ayi.
Kugalukira N’kupanda Nzeru
Ngakhale zili choncho, achinyamata ena amayesa kuchita zinthu zoti anthu asawafanizire ndi makolo awo pochita zinthu mogalukira. Ivan anati: “Nthaŵi inayake zinkandiipira zoti ndizikhala chitsanzo chabwino kwa ena. Ndinayamba kugalukira posameta tsitsi langa kuti ndione kuti wina andidzudzula likafika pati.”
Abisalomu, mmodzi wa ana a Mfumu Davide, anachita zogalukira. Bambo ake anali munthu wotchuka pankhani ya kudzipereka kwa Yehova ndipo anthu ambiri kumtundu wa Israyeli anali kuwakonda. Pokhala mwana wa Davide, Abisalomu ankayenera kuchita zinthu mwapamwamba. Koma m’malo moti achite zinthu zomuyenerera, Abisalomu anakonda kudzipangira dzina lakelake pogalukira bambo ake. Popeza kuti Davide anachita kudzozedwa ndi Yehova kuti akhale womuimira, ndiye kuti Abisalomu ankagalukira Yehova weniweniyo. Zochita zake zinanyazitsa banja lawo ndipo zinam’pweteketsa iyeyo.—2 Samueli 15:1-15; 16:20-22; 18:9-15.
Kugalukira kungakupweteketseni inunso. Taonani zimene Baibulo limatiuza zokhudza Nehemiya. Adani ake ena anayesetsa kuti amunyengerere kuti achite zinthu zosemphana ndi zofuna za Mulungu. N’chifukwa chiyani anatero? “Kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza,” anatero Nehemiya. (Nehemiya 6:13) Kugalukira kungakuipitsireni dzina lanu, moti mwina anthu sangaiwale n’komwe zimene mungachite pogalukirapo.
Komanso china n’chakuti khalidwe lanu logalukiralo lingawakhudze anthu ena. Ndipo choopsa kwambiri n’chakuti mungawachititse makolo anu kukhala achisoni n’zachabechabe. (Miyambo 10:1) Zochita zanuzo zingachititsenso kuti achinyamata ena nawonso azichita zinthu zoipa. Ivan anati: “Khalidwe langa linasokoneza kwambiri mng’ono wanga. Kwa nthaŵi ndithu iye anasiyiratu mpingo wachikristu, n’kumachita zinthu zimene ankachita kudziŵa kuti sizogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mwayi wake, anasintha moti panopa akutumikiranso Yehova ndipo ndi wokondwa.”
Njira Yabwino
Solomo, yemwe anali mchimwene wake wa Abisalomu wa bere lina anachita zinthu mosiyana ndi mmene anachitira Abisalomuyo. Ankafunitsitsa kuphunzira zinthu modzichepetsa kuchokera kwa bambo ake a Davide. (1 Mafumu 2:1-4) M’malo moti adzitchukitse, Solomo anaganiza zokhala ndi dzina labwino kwa Mulungu. Kwa nthaŵi yonse imene anachita zimenezo, analemekezetsa banja lake ndipo anadziŵika kuti anali mmodzi wa mafumu otchuka kwambiri a Israyeli.—1 Mafumu 3:4-14.
Chitsanzo chabwino cha Solomo chikusonyeza mfundo ziŵiri zofunika kwambiri izi: Yoyamba njakuti, munthu umadzipangira mbiri yako, osati podzipatula kubanja lako, koma pophunzira zinthu zothandiza zimene banja lako limachita. Magazini yonena za achinyamata yotchedwa Adolescence inati: “Palibiretu chifukwa choti achinyamata azidzipatula kwa makolo awo paunyamata wawo pofuna kukhala ndi mbiri yawoyawo.” Pamene mukupanga mbiri yanuyanu “sikuti makolo amakulepheretsani akamakuthandizani, koma m’malo mwake amakulimbikitsani kutero,” inapitiriza motero magaziniyo.
N’zochititsa chidwi kuti Solomo weniweniyo analimbikitsa kuti: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.” (Miyambo 23:22) Zikuonekeratu kuti Solomo sankanena zimenezi polembera ana aang’ono chifukwa chakuti makolo akafika ‘pokalamba,’ nthaŵi zambiri mwanayo amakhala ali wamkulu. Nangano mfundo yeniyeni ya mawu akewo yagona pati? Yagona pakuti, ngakhale mutakula n’kufika pokhala ndi banja lanulanu, mukhozabe kupindula ndi nzeru za makolo anu. Zimenezi n’zimene Ivan anadzazizindikira. Iye anati: “Pamene ndikukula, ndimayesetsa kutsanzira zabwino zimene makolo anga ankachita, kwinaku n’kumayesetsanso kupeŵa zimene ankalakwitsa.”
Mfundo yachiŵiri yoyenera kuiganizira njakuti zimene Solomo ankafuna kwambiri sizinali zoti adzipangire mbiri yakeyake ayi, koma zinali zoti asangalatse Yehova. Inde, n’zoonadi kuti pokhala mwana wa Davide, anayenera kuchita zinthu mwapamwamba. Ndipo kudalira Yehova kunathandiza Solomo kuyendetsa bwino udindo wake. Alexander anatengera zomwezo. Iye anati: “Tsopano ndikuvomereza mfundo yakuti nthaŵi zambiri ana a akulu amafunika kuchita zinthu mwapadera. Ndinaganiza zoti mfundo imeneyi ndiziiona moyenera, ndipo ndaona kuti yandithandiza kukhala wotetezeka. Ndayamba kuona kuti mmene Yehova amandionera ndicho chinthu chofunika kwambiri. Amandidziŵa mmene ineyo ndilili pandekha osangoti kuti ndine mwana wa auje.”
Daryn, yemwe bambo ake anamaliza maphunziro ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower yophunzitsa Baibulo,b yomwe ndi sukulu imene imaphunzitsa amishonale, nayenso anaphunzira kusadandaula nazo zokhala ndi makolo otchuka. Iye anati: “Nditabatizidwa, ndinadzipereka kwa Yehova osati kwa munthu wina aliyense. Pochita zinthu zosonyeza kudzipereka kwangako mmene ndingathere, ndimakhala ndi mtendere mumtimamu podziŵa kuti Yehova amasangalala nane, ngakhale kuti nthaŵi zina sindikwanitsa kuchita zonse zimene makolo anga anachita.”
Mfumu Solomo inaona kuti: “Ngakhale mwana adziŵika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” (Miyambo 20:11) Pamapeto pake, anthu adzakukumbukirani chifukwa cha zimene mumanena ndi kuchita. Khalani munthu wachitsanzo “m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.” Ngati muli wotero, anthu azikukondani ndiponso kukulemekezani chifukwa cha mmene mulili!—1 Timoteo 4:12.
Komano kwa achinyamata ena, vuto lawo ndi kusafuna kuwafanizira ndi achimwene awo kapena achemwali awo omwe zinthu zimawayendera bwino kwambiri. Tidzafotokoza m’nkhani ina mmene mungathetsere vuto limeneli.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina ena tawasintha.
b Sukulu ya Gileadi imayendetsedwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 26]
Kugalukira kungangochititsa makolo anu kukhala achisoni ndiponso kungakuipitsireni mbiri
[Chithunzi patsamba 26]
Chitsanzo chanu chabwino chingapindulitse ena