Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi nchifukwa ninji New World Translation imamasulira liwu Lachihebri lakuti ʽa·rumʹ pa Genesis 3:1 monga “kuchenjera” popeza kuti matembenuzidwe ena a Baibulo amati “chinyengo” kapena “kungwala”?
Lemba limenelo limaŵerengedwa motere: “Tsopano njoka inatsimikizira kukhala yochenjera pa zirombo zakuthengo zonse zimene Yehova Mulungu anazipanga. Chotero inayamba kunena kwa mkaziyo: ‘Kodi Mulungu ananenadi kuti musadye ku mtengo uliwonse wa m’mundamu?’”
Pa Miyambo 12:23 ndi malo ena, New World Translation imamasulira liwu Lachihebri lakuti ʽa·rumʹ kukhala “luntha,” limene liri tanthauzo lenileni limodzi la liwulo pamene ligwiritsiridwa ntchito kwa anthu. Koma monga momwe ziriri ndi mawu ena ambiri, ʽa·rumʹ iri ndi matanthauzo ambiri. Mwachitsanzo, Benjamin Davidson akulongosola ʽa·rumʹ motere: “I. ukamberembere, chinyengo, upalu.—II. luso, kuchenjera.”—The Analytical Hebrew and Chaldee Lexicon.
Nangano, kodi nchifukwa ninji New World Translation ikusankha tanthauzo lachiŵirilo lakuti “kuchenjera” pa Genesis 3:1? Chosankha chimenecho n’chogwirizana ndi matembenuzidwe ena. Mwachitsanzo, pamene Genesis 3:1 anatembenuzidwa m’Chigiriki m’mamasulidwe a Septuagint a m’zaka za zana lachitatu B.C.E., liwu lakuti phroʹni·mos linagwiritsiridwa ntchito—liwu limodzimodzilo lagwiritsiridwanso ntchito pambuyo pake pa Mateyu 10:16: “Muyenera kukhala ochenjera monga njoka ndi ofatsa monga nkhunda.”—Today’s English Version.
Katswiri Wachihebri Ludwig Koehler pothirira ndemanga kumbuyoko mu 1945 anati: “Njoka njamanyazi. Ichi chingalongosoledwe bwino kwambiri m’Chigiriki ndi liwu lakuti phronimos, popeza kuti ndimanyazi kapena kuchenjera kumeneku njoka imasonyeza kukhala ndi kuchita phrenes.” Phreʹnes panopa akutanthauza mtundu wa nzeru zachilengedwe zimene zinyama zina zimasonyezanso.—Yerekezerani ndi Miyambo 30:24.
Komabe, pali chifukwa china chachikulu chogwiritsirira ntchito liwu lakuti “kuchenjera” mmalo mwa “luntha” kapena “kungwala” pa Genesis 3:1. Kuitcha njoka kukhala yongwala panopa, isanalongosoledwe kukhala ikunyenga Hava kulowa m’chimo, kungatsogolere aŵerengi ambiri kutsimikizira kuti Baibulo likusonyeza njokayo payokha kukhala ikugwira ntchito kupanga chiŵembuchi mwa kungwala kwake kwachilendo. Kumasulira koteroko kungapange cholembedwachi kungokhala nthano—ndipo nthano yopusadi.
Mosemphana ndi ichi, Baibulo limaphunzitsa kuti panali winawake woposa njoka yongwala amene ankagwira ntchito m’munda wa Edeniwo. Chibvumbulutso 12:9 chikuzindikiritsa mowonekera Satana Mdyerekezi ndi “njoka yokalambayo.” Iye ndiye anali wosawonekayo, mphamvu yoposa yaumunthu yosonkhezera chokwawa wamba mofanana ndi mmene katswiri wopangitsa zinyama kuwoneka ngati ndizo zikulankhula amapangira matsenga ake. Kuchenjera kwachilengedwe kwa njoka kunaipangitsa kukhala chosankha chabwino cha wonyengayo. Pamene iyo sinachite manyazi nichokapo mochenjera monga momwe mwachilengedwe iriri koma mmalo mwake inatsegula pakamwa pake niyamba kulankhula ndi Hava, iyo inakoka chisamaliro cha Hava mokhutiritsa kwabasi.
Mawu ouziridwa a Mulungu sali nthano, ndipo mwakumasulira molongosoka, New World Translation imatithandiza kuyamikira nsongayi.—2 Timoteo 3:16.
◼ Popeza kuti Mboni za Yehova zimadziŵa Kuti akufa sadziŵa kanthu, kodi nchifukwa ninji zimalingalira kukhala kofunika kupezeka pamaliro a akhulupiriri anzawo?
Chidziŵitso cholongosoka chochokera m’Baibulo chonena za mkhalidwe wa akufa chimachinjiriza Mboni za Yehova ku malingaliro olakwika omwe amatulukapo mkhalidwe wopanda nzeru pamaliro. Chimawapatsanso chifukwa chakupezekera pamaliro Achikristu.
Mawu a Mulungu amasonyeza momvekera bwino kuti pamene munthu wamwalira, iye samapitiriza kukhalako monga moyo wosakhoza kufa. (Mlaliki 9:5) Pambuyo pa imfa, thupi limabwerera kufumbi, kaya mwakuola kwa nthaŵi zonse kapena mwakutenthedwa. Womwalirayo sakhalanso ndimoyo; iye adzakhalanso ndimoyo kokha ngati Mulungu adzamuukitsa kutsogoloku.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Chotero, Mboni za Yehova sizimatsatira miyambo yamaliro imene njozikidwa pa chikhulupiriro chakuti munthu wakufayo adali ndi moyo wosakhoza kufa, umene umapitiriza kukhala ndimoyo kwinakwake. Iwo samakhalamo ndi phande m’madzoma, oimba nyimbo mofuula kapena kulira kuti achititse mantha “mizimu,” osatinso mwambo wa kuchezera usiku wonse kulonda mtembowo kapena kumva chisoni mopambanitsa kuti akondweretse wakufayo.
Komabe, ichi sichikutanthauza kuti anthu a Mulungu samalira. Imfa ya wachibale kapena bwenzi lapamtima nchokumana nacho chomvetsa chisoni, ngakhale kwa alambiri owona amene ali ndi chidziŵitso cholongosoka chonena za akufa. Mwachitsanzo, pamene Yakobo anaganiza kuti chirombo cholusa chinapha Yosefe, kholo limenelo ‘linamlirira mwana wake masiku ambiri.’ Timaŵerenga kuti ‘ana amuna ake onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze.’ (Genesis 37:33-35) Pamene Yakobo wokhulupirikayo anamwalira, Yosefe ‘anauza akapolo ake asing’anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi,’ ndipo ‘Aaigupto anamlira iye masiku makumi asanu ndi aŵiri.’ Pamene kuli kwakuti banja la Yakobo silinali ndi malingaliro onyenga a Aigupto ponena za akufa, mwachiwonekere iwo anayambukiridwa ndi imfa ya Yakobo. ‘Mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake’ anafuna kuti Yakobo aikidwe moyenera, ndipo ngakhale akunja anawona kuti iwo ankalira.—Genesis 50:1-11.
Zitsanzo zina zambiri za Baibulo zingasonyezedwe zonena za mmene atumiki a Yehova anayambukiridwadi ndi imfa ya wolambira mnzawo kapena wachibale ndipo motero analira moyenera.a Pamene Yesu anali ndi achibale ochita chisoni a Lazaro, Yesu sanakhale wosayambukiridwa mosawonekera kapena kukondwera mosayenerera. Ngakhale kuti anali ndi chidaliro m’mphamvu ya chiukiriro, Yesu analira. (Yohane 11:33-35) Yesu iyemwiniyo atamwalira, ophunzira ake analira, ngakhale kuti adawauza kuti akaphedwa ndi kuukitsidwanso ku moyo.—Mateyu 16:21, 28; Yohane 16:17-28; 20:11.
Atumiki a Mulungu lerolino akhoza ndipo amamva chisoni chimene imfa imabweretsa. Komabe, kumvetsetsa kwawo Baibulo kumathandiza kuchepetsa kapena kulinganiza kulira kwawo, mogwirizana ndi 1 Atesalonika 4:13, 14: ‘Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye iwo akugona mwa Yesu.’
Nangano, bwanji ponena za kupezeka pamaliro Achikristu (kapena nkhani yachikumbutso ya wokhulupirira)? Pali zifukwa za m’Baibulo zimene Mboni zimaganiza kuti n’chopindulitsa kukhala ndi nkhaniyo ndikupezekako.
Kumbukirani kuti pamene chinawoneka kwa Yakobo kuti mwana wake wamwalira, ‘ana amuna ake onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze.’ (Genesis 37:35) M’maiko ambiri kumakhala kwamwambo kwa achibale kusonkhana pamaliro. Ichi chimapereka nthaŵi kwa ena, amene sangakhale anali kuyanjana nawo mwathithithi ndipo chotero sayambukiridwa mwamaganizo, kupereka mawu opepesa ndi chitonthozo. Lazaro atamwalira ‘ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wawo.’ (Yohane 11:19) Ichi chimayambukiranso Akristu amene amafuna kukhala okhoza ‘kutonthoza iwo okhala m’nsautso iriyonse.’—2 Akorinto 1:4.
Oyang’anira Achikristu, ngakhale kuti angakhale otanganitsidwa koposa, ayenera kutsogolera m’kupereka chitonthozo ku gulu. Iwo amakumbukira kuti chitsanzo chawo Yesu, Mbusa Wabwino, anatumidwa ‘kudzamanga osweka mtima ndikutonthoza mtima wa onse amene akulira maliro.’ (Yesaya 61:1, 2; Yohane 10:14) Yesu sanapereke chitonthozo choterocho kokha pamene kunali koyenera. Iye anali wofunitsitsa kuchita chirichonse chimene akanatha kukhala ndi anamalira achibale a Lazaro—kukhalamo ndi phande m’chisoni chawo.—Yohane 11:11, 17, 33.
Ngakhale Akristu amene sangakhale okhoza kunena zambiri kwa anamalira pamaliro angachite bwino mwakungopezekapo. Ziŵalo zabanja lolira zingapeze chitonthozo ku kupezekapo kwachisoni kwa ambiri—achichepere ndi achikulire—ochokera mu mpingo Wachikristu. Kumbukirani kuvomereza kwa Ayuda ena pamene Yesu anapita kwa alongo ochita chisoni a Lazaro: “Taonani, anamkondadi!” (Yohane 11:36) Achibale osakhulupirira, anansi, kapena mabwenzi amalonda opezeka pamaliro Achikristu akondweretsedwa ndi chiŵerengero chachikulu cha Mboni zopezekapo ndipo motero akhala ovomereza kwambiri ku chowonadi Chabaibulo choperekedwa.
Mkhalidwe wa Mboni pamene zikupezekapo uyenera kuyenerana ndi malowo. Ngakhale kuti amadziŵa kuti womwalirayo sakuvutika, ndipo ali ndi chidaliro chakuti chiukiriro chikuyembekezera okhulupirika onse, iwo amalabadira uphungu uwu: ‘Mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina.’ (Mlaliki 3:4) Maliro kapena utumiki wachikumbutso sinthaŵi yakulankhula kofuula kapena kwachiphwete. Iyo ndinthaŵi yakumva chifundo, mogwirizana ndi chilangizo ichi: ‘Kondwani nawo iwo akukondwera; lirani nawo akulira.’—Aroma 12:15.
Pali chifukwa chinanso chimene Mboni za Yehova zimapezekera pamaliro. Mawu a Mulungu amati: “Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo. . . . Mtima wa anzeru uli m’nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m’nyumba ya kuseka.”—Mlaliki 7:2-4.
Pamene kuli kwakuti Mboni za Yehova ziri ndi chifukwa cha chiyembekezo, mawu amenewo anauziridwa ndi kulembedwa m’Baibulo kaamba ka phindu lathu. Maliro angayerekezedwe ndi “nyumba ya maliro.” Pamene tikupezekapo, malingaliro athu angachoke pa zodera nkhaŵa zathu kapena machitachita anthaŵi zonse ndi kusumika pa kufupika kwa moyo. Kaya kupyolera mwa matenda kapena ‘zotigwera m’nthaŵi yake’ zina, imfa ingakanthe aliyense wa ife ndipo mwamsanga kutichotsapo, pakuti ‘munthu sadziwiratu mphindi yake.’ (Mlaliki 9:11, 12) Makolo amene akupezeka pamaliro Achikristu ndi ana awo angapeze kuti ichi chingatsogolere ku kukambirana chimene imfa iridi, kufunikira kwathu dipo, ndi nzeru ya kutumikira “Mulungu wakuukitsa akufa.”—2 Akorinto 1:9; Mlaliki 12:1, 13.
Mboni za Yehova sizimalingalira maliro kukhala nsembe, koma zimazindikira kuti zochitika zachisoni zimenezi zimapereka nthaŵi yakupereka chitonthozo. Mwakupezekapo, Akristu angapereke umboni wa chikondi ndi ulemu zimene anali nazo kwa Mkristu mnzawoyo. Ndipo angasonkhezeredwe kulingalira mosamalitsa za tanthauzo la moyo, ponena za mmene ayenera kumagwiritsira ntchito moyo wawo pamaso pa Mulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Genesis 23:2, 19; Numeri 20:29; Deuteronomo 34:7, 8; 2 Samueli 1:11, 12; 3:31-34; 13:32-37; 18:33; 2 Mbiri 35:24, 25; Yobu 1:18-20; Salmo 35:14; Yeremiya 9:1; Luka 7:12, 13; 8:49-52; Machitidwe 8:2; 9:39.