Musamayang’ane “Zinthu za M’mbuyo”
“Aliyense wogwira pulawo koma n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo sayenera ufumu wa Mulungu.”—LUKA 9:62.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kukumbukira mkazi wa Loti’?
Kodi tiyenera kupewa kuganizira kwambiri zinthu zitatu ziti?
Kodi tingatani kuti tiziyendera limodzi ndi gulu la Yehova?
1. Kodi Yesu anapereka chenjezo liti ndipo zimenezi zikubweretsa funso lotani?
“KUMBUKIRANI mkazi wa Loti.” (Luka 17:32) Chenjezo limeneli, lomwe linaperekedwa ndi Yesu Khristu pafupifupi zaka 2,000 m’mbuyomu, ndi lofunika kwambiri masiku ano kuposa kale lonse. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena chenjezo limeneli? Ayuda amene analipo anamvetsa mosavuta zimene ankatanthauza. Iwo ankadziwa zimene zinachitikira mkazi wa Loti. Pamene ankathawa ku Sodomu limodzi ndi anthu a m’banja lake, iye anatembenuka n’kuyang’ana kumbuyo ndipo anasanduka chipilala chamchere.—Werengani Genesis 19:17, 26.
2. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anayang’ana m’mbuyo ndipo zotsatira za kusamvera kwake zinali zotani?
2 Koma n’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anayang’ana kumbuyo? Kodi ankachita chidwi ndi zimene zinali kuchitika? Kodi iye analibe chikhulupiriro? Kodi mwina iye ankaganizira kwambiri za zinthu zimene anasiya mu Sodomu? (Luka 17:31) Kaya anayang’ana kumbuyo pa chifukwa chotani, iye anawonongedwa chifukwa cha kusamvera kwake. Tangoganizani. Iye anafa pa tsiku limene anthu oipa a ku Sodomu ndi Gomora anawonongedwa. M’pake kuti Yesu anati: “Kumbukirani mkazi wa Loti.”
3. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti mophiphiritsira sitiyenera kuyang’ana za m’mbuyo?
3 Ifenso tikukhala m’nthawi imene mophiphiritsira sitiyenera kuyang’ana za m’mbuyo. Yesu anatsindika mfundoyi polankhula ndi munthu amene ankafuna kuti akayambe watsanzikana ndi banja lake asanakhale wophunzira. Yesu anati: “Aliyense wogwira pulawo koma n’kumayang’ana zinthu za m’mbuyo sayenera ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:62) Kodi yankho limeneli likusonyeza kuti Yesu anali wokhwimitsa zinthu kapena wosaganizira ena? Ayi, chifukwa iye ankadziwa bwino cholinga cha munthuyo kuti akungofuna kuzemba udindowo. Yesu anafotokoza kuti kuzengereza koteroko kuli ngati kuyang’ana “zinthu za m’mbuyo.” Kodi pali chilichonse cholakwika ngati munthu amene akulima atayang’ana kumbuyo kwa kanthawi kochepa kapena kusiya pansi pulawo n’kutembenuka kaye? Inde, chifukwa chakuti akhoza kusokonezeka pa zimene akuchita ndipo ntchitoyo singayende.
4. Kodi tiyenera kuganizira zinthu ziti?
4 M’malo motembenuka n’kumayang’ana kumbuyo, tifunika kuyesetsa kuganizira zinthu zimene zili kutsogolo. Lemba la Miyambo 4:25 limatsimikizira mfundo imeneyi chifukwa limati: “Maso ako aziyang’ana patsogolo. Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.”
5. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyang’ana zinthu za m’mbuyo?
5 Pali chifukwa chomveka chopewera kuyang’ana zinthu za m’mbuyo. Chifukwa chake n’chakuti tili ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Tim. 3:1) Posachedwapa tidzaona osati kuwonongedwa kwa mizinda iwiri yokha koma kwa dziko lonse loipali. Kodi tingatani kuti tipewe zimene zinachitikira mkazi wa Loti? Choyamba, tiyenera kudziwa zinthu za m’mbuyo zimene tingayesedwe nazo kuti tiziziganizira. (2 Akor. 2:11) Choncho tiyeni tikambirane zinthu zimenezo ndiponso zimene zingatithandize kuti tisaziganizire.
KOMA KALE LIKANATI LIZIBWERERA!
6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthufe sitikumbukira zinthu bwinobwino?
6 Choyamba, tiyenera kupewa maganizo olakalaka zinthu zakale. Anthufe sitikumbukira zinthu bwinobwino. Mwina mosazindikira tingachepetse mavuto amene tinkakumana nawo n’kumafotokoza mokokomeza chimwemwe chimene tinkapeza, n’cholinga choti zizioneka ngati zinthu zinkatiyendera bwino pamene sizinali choncho. Maganizo amenewa ndi olakwika ndipo angachititse munthu kuganiza kuti, ‘Koma kale likanati lizibwerera!’ Komatu Baibulo limatichenjeza kuti: “Usanene kuti: ‘N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?’ Pakuti si nzeru kufunsa funso lotere.” (Mlal. 7:10) N’chifukwa chiyani maganizo amenewa ali oopsa?
7-9. (a) Kodi Aisiraeli anakumana ndi zotani ku Iguputo? (b) Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zimene Aisiraeli anaona? (c) Nanga kodi anayamba kudandaula za chiyani?
7 Taganizirani zimene zinachitikira Aisiraeli m’nthawi ya Mose. Poyamba, Aisiraeli ankaonedwa kuti ndi alendo m’dziko la Iguputo. Koma Yosefe atamwalira, Aiguputo “anawaikira akulu owayang’anira pa ntchito yawo yaukapolo, kuti aziwanyamulitsa katundu mwankhanza.” (Eks. 1:11) Anthu a Mulungu analinso pangozi moti anayamba kumawapha chifukwa chakuti Farao sankafuna kuti iwo achulukane. (Eks. 1:15, 16, 22) N’chifukwa chake Yehova anauza Mose kuti: “Ndaona nsautso ya anthu anga amene ali ku Iguputo, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Zoonadi, ndikudziwa bwino zowawa zawo.”—Eks. 3:7.
8 Tangoganizirani mmene Aisiraeli anasangalalira pamene anamasulidwa n’kumatuluka m’dziko limene anali akapolo. Iwo anaona mphamvu zodabwitsa za Yehova pamene iye anabweretsa miliri yokwana 10 pa Farao ndi anthu ake. (Werengani Ekisodo 6:1, 6, 7.) Zitatero, Aiguputo anauza Aisiraeli kuti azipita komanso anawapatsa golide ndi siliva moti Baibulo limati anthu a Mulungu “anatenga zinthu zambiri za Aiguputo.” (Eks. 12:33-36) Aisiraeli anasangalalanso kwambiri kuona Mulungu akuwononga Farao ndi asilikali ake pa Nyanja Yofiira. (Eks. 14:30, 31) Zonsezitu zinali zinthu zolimbitsa chikhulupiriro kwabasi.
9 Koma n’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli anayamba kunyinyirika ndi kudandaula patangodutsa kanthawi kochepa kuchokera pamene anapulumutsidwa mozizwitsa. Kodi iwo amadandaula za chiyani? Chakudyatu basi. Iwo sankakhutira ndi zimene Yehova ankawapatsa moti ankadandaula kuti: “Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinali kudya ku Iguputo, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu! Koma tsopano tilibe ndi mphamvu zomwe. Maso athu sakuonanso kanthu kena, koma mana basi.” (Num. 11:5, 6) Maganizo awo anasokonezeka kwambiri moti ankalakalaka kubwerera ku ukapolo. (Num. 14:2-4) Aisiraeli anayamba kuganizira zinthu za m’mbuyo ndipo izi zinakwiyitsa Yehova.—Num. 11:10.
10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli anachita?
10 Kodi ife masiku ano tikuphunzirapo chiyani? Tikakumana ndi mavuto si bwino kulakalaka zinthu za m’mbuyo, mwina zimene tinkachita tisanaphunzire choonadi zomwe zingaoneke ngati zabwino kwambiri. Si kulakwa kuganizira zinthu zimene zatichitikira m’mbuyomu kapena kukumbukira zinthu zabwino za m’mbuyo. Koma tiyenera kusamala pochita zimenezi kuti zisatisokoneze. Tikapanda kusamala tikhoza kuyamba kudandaula kwambiri ndi moyo wathu mpaka kufika pobwerera ku zinthu za m’mbuyo.—Werengani 2 Petulo 2:20-22.
ZINTHU ZIMENE TINAZISIYA
11. Kodi ena amamva bwanji akaganizira zinthu zimene anazisiya?
11 N’zomvetsa chisoni kuti ena amaganizira kwambiri zinthu zimene anazisiya n’kumaona kuti anataya mwayi. Mwina munali ndi mwayi woti mukanatha kuchita maphunziro apamwamba, kutchuka kapena kupeza chuma koma munazisiya. Abale ndi alongo athu ambiri anasiya mwayi wopeza ndalama zambiri pa zinthu monga kukhala katswiri wa zamaphunziro, zosangalatsa, masewera kapena kuchita mabizinezi akuluakulu. Panopa nthawi ikupita koma mapeto sanafikebe. Kodi mumayerekezera mmene zinthu zikanakhalira mukanati musasiye zinthu zimenezo?
12. Kodi Paulo ankaona bwanji zinthu zimene anazisiya?
12 Mtumwi Paulo anasiya zinthu zambirimbiri n’cholinga choti akhale wotsatira wa Khristu. (Afil. 3:4-6) Kodi iye ankaona bwanji zinthu zimene anazisiyazo? Iye anati: “Koma zinthu zimene zinali zaphindu kwa ine, zimenezo ndaziona kukhala zopanda phindu chifukwa cha Khristu.” N’chifukwa chiyani ankaziona choncho? Iye anapitiriza kuti: “Zoonadi, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa chakuti ndinadziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, chimene ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Chifukwa cha iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala, kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu.”a (Afil. 3:7, 8) Munthu amene wataya zinyalala sadandaulanso kuti waluza zinazake. Umu ndi mmene Paulo ankaonera zinthu zakudziko zimene anazisiya. Iye sankaonanso kuti zingamupindulitse.
13, 14. Kodi tingatsanzire bwanji Paulo?
13 N’chiyani chingatithandize ngati titayamba kulakalaka zinthu zimene tinazisiya n’kumaona ngati tinaluza mwayi winawake? Tiyenera kutsanzira Paulo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kuganizira kufunika kwa zinthu zimene tili nazo panopa. Panopa muli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo muli ndi mbiri yoti ndinu wokhulupirika kwa iye. (Aheb. 6:10) Madalitso auzimu amene tikusangalala nawo panopa ndiponso amene tikuyembekezera kudzasangalala nawo m’tsogolomu, sitingawayerekezere ndi zinthu zakuthupi zimene dzikoli lingatipatse.—Werengani Maliko 10:28-30.
14 Kenako Paulo anatchula chinthu china chimene chingatithandize kupitirizabe kukhala okhulupirika. Iye ananena kuti “ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.” (Afil. 3:13) Onani kuti Paulo anatchula zinthu ziwiri zofunika kwambiri. Choyamba, ananena kuti tiyenera kuiwala zinthu zakumbuyo. Izi zikusonyeza kuti sitiyenera kuwononga mphamvu ndiponso nthawi yathu kuganizira kwambiri zinthu zimene tinazisiya. Chachiwiri, tiyenera kukhala ngati munthu amene ali pafupi kumaliza mpikisano wothamanga. Tiyenera kuyesetsa kuti tikapeze zakutsogolo n’kuika maganizo onse pa zimenezo.
15. Kodi timapindula bwanji tikamaganizira kwambiri zitsanzo za atumiki okhulupirika a Mulungu?
15 Kusinkhasinkha zitsanzo za atumiki a Mulungu okhulupirika akale komanso a masiku ano kungatithandize kuti tisamayang’ane za m’mbuyo koma tiziganizira za m’tsogolo. Mwachitsanzo, ngati Abulahamu ndi Sara akanakhala kuti amangokumbukira za ku Uri ndiye kuti “mpata wobwerera akanakhala nawo.” (Aheb. 11:13-15) Koma iwo sanabwerere. Nayenso Mose anasiya zinthu zambiri ku Iguputo kuposa Mwisiraeli aliyense. Koma palibe paliponse pamene timawerenga zoti Mose anayamba kulakalaka zinthu zomwe anazisiyazo. Pa nkhaniyi Baibulo limanena kuti iye “anaona kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa kukhala chuma chochuluka kuposa chuma cha Iguputo, pakuti anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire.”—Aheb. 11:26.
ZINTHU ZOIPA ZIMENE ZINATICHITIKIRA M’MBUYO
16. Kodi zinthu zimene zinatichitikira kalekale zingatikhudze bwanji?
16 Sikuti zinthu zonse za m’mbuyo zimakhala zosangalatsa. Mwina timakhumudwa tikaganizira machimo amene tinachita kalekale kapena zinthu zina zimene tinalakwitsa. (Sal. 51:3) Mwina zikhoza kumatiwawa tikaganizira uphungu wopweteka umene tinapatsidwa. (Aheb. 12:11) Apo ayi zinthu zopanda chilungamo zimene wina anatichitira kapena zimene tikuganizira kuti wina anatichitira, zikhoza kusokoneza kaganizidwe kathu. (Sal. 55:2) Kodi tingatani kuti tisalole zimenezi kutichititsa kuyang’ana zinthu za m’mbuyo? Tiyeni tione zitsanzo zitatu.
17. (a) N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti iye ndi ‘munthu wochepa poyerekeza ndi wochepetsetsa wa oyera onse’? (b) N’chiyani chinathandiza Paulo kuti asiye kumangoganizira zinthu zoipa zimene anachita kumbuyo?
17 Zolakwa za m’mbuyo. Mtumwi Paulo anati iye anali ‘munthu wochepa poyerekeza ndi wochepetsetsa wa oyera onse.’ (Aef. 3:8) N’chifukwa chiyani ankadziona choncho? Iye anati: “Chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.” (1 Akor. 15:9) Mukuganiza kuti Paulo ankamva bwanji akakumana ndi anthu ena amene anawazunza m’mbuyomo? Koma m’malo molola kuti maganizo oipa amufoole, Paulo anaganizira kwambiri za mmene Mulungu anamukomera mtima. (1 Tim. 1:12-16) Izi zinamubweretsera chimwemwe chachikulu moti zinamulimbikitsa kuchita khama mu utumiki wake. Zinthu zoipa zimene Paulo anachita zinali m’gulu la zinthu zimene sankafuna kuzikumbukiranso. Ifenso tikamaganizira za chifundo cha Yehova, tidzapewa kufooledwa ndi nkhawa chifukwa choganizira zinthu zimene tinachita kale zomwe sitingazisinthe. M’malomwake tidzagwiritsa ntchito mphamvu zathu kugwira ntchito imene tapatsidwa.
18. (a) Kodi chingachitike n’chiyani ngati tayamba kuwawidwa mtima tikaganizira uphungu umene tinapatsidwa? (b) Kodi tingatsatire bwanji mawu a Solomo pa nkhani yolandira malangizo?
18 Uphungu wopweteka. Nthawi zina zikhoza kumatiwawa tikaganizira uphungu umene tinapatsidwa. Zimenezi zimakhala zopweteka komanso zofooketsa ndipo zikhoza kuchititsa munthu kutaya mtima. (Aheb. 12:5) Nthawi zina munthu ‘angapeputse’ uphungu poukana kapena ‘kutaya mtima’ atauvomereza. Zimenezi zimachititsa kuti uphunguwo usatithandize. Koma ndi bwino kutsatira mawu a Solomo akuti: “Gwira malangizo, usawataye. Uwasunge bwino chifukwa iwo ndiwo moyo wako.” (Miy. 4:13) Mofanana ndi dalaivala amene amatsatira zikwangwani za pamsewu, tiyeni tizilandira uphungu ndi kuugwiritsa ntchito n’kupitiriza kuyang’ana kutsogolo.—Miy. 4:26, 27; werengani Aheberi 12:12, 13.
19. Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Habakuku ndi Yeremiya?
19 Zinthu zopanda chilungamo zimene zinatichitikira kapena zimene tikungoganiza kuti zinatichitikira. Nthawi zina tikhoza kumva ngati mneneri Habakuku amene anafuula popempha Yehova kuti akhazikitse chilungamo. Iye sankamvetsa chifukwa chake Yehova analola zinthu zina zopanda chilungamo kuchitika. (Hab. 1:2, 3) Ndi bwino kukhala ndi chikhulupiriro chimene mneneriyu anali nacho chifukwa ananena kuti: “Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.” (Hab. 3:18) Mofanana ndi Yeremiya, timakhala ndi “mtima wodikira” n’kumakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova, yemwe ndi Mulungu wachilungamo, adzakonza zinthu zonse pa nthawi yake.—Maliro 3:19-24.
20. Tingasonyeze bwanji kuti ‘tikukumbukira mkazi wa Loti’?
20 Tikukhala m’nthawi yosangalatsa kwambiri. Pali zinthu zochititsa chidwi zimene panopa zikuchitika ndipo zina zambiri zikubwera posachedwapa. Tiyeni tonsefe tiziyendera limodzi ndi gulu la Yehova. Tiyeni tizitsatira malangizo a m’Malemba akuti tiziyang’ana za m’tsogolo osati za m’mbuyo. Tikamatero ndiye kuti ‘tikukumbukira mkazi wa Loti.’
[Mawu a M’munsi]
a Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti zinyalala amatanthauza “zinthu zimene zaperekedwa kwa agalu,” “ndowe” kapena “zonyansa za munthu.” Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti Paulo anagwiritsa ntchito mawuwa potanthauza “kukaniratu chinthu chopanda ntchito ndiponso chonyansa chimene munthu alibe nacho ntchito.”