Chidziŵitso pa Nyuzi
Kuthetsa Upandu
Mosasamala kanthu za malonjezo a andale zadziko omemeza anthu kupereka malamulo abwino pa upandu mu United States, ABA (American Bar Association) posachedwapa inavomereza kuti upandu wakhala wosalamulirika ndi kuti dongosolo la chiweruzo la zaupandu silingauthe iwo. ABA inayerekeza kuti maupandu 34 miliyoni anachitidwa mu 1986, komabe maphunziro a alamulo avumbula kuti “kokha zikwi mazana oŵerengeka anathera m’zilango za ndende,” ikusimba tero The New York Times. M’kuwonjezerapo, ABA ikudzinenera kuti unyinji waukulu wa upandu umangopita osasimbidwa ku polisi. Mosasamala kanthu za chimenechi, ndende zikudzala mopambanitsa, ndipo milandu ya upandu ikusefukira m’mabwalo a milandu. Phunzirolo linatsimikizira kuti “palibe chiyembekezo chenicheni kuti kumanga anthu kowonjezereka ndi kuika m’ndende kungakhale kodzetsa upandu,” ikulongosola tero Times.
Pamene kuli kwakuti unyinji wa anthu okwiyitsidwa ungapeze kuvomereza kumeneku kukhala kodabwitsa, ophunzira Baibulo odziŵitsidwa sakutero. Zaka mazana apita mtumwi Paulo ananeneratu kuti “masiku otsirizira” a dongosolo iri, “anthu oipa . . . adzaipa chiipire.” (2 Timoteo 3:1, 13) Ngakhale kuli tero, chimene munthu sangakhoze kuchita, Mulungu angachite. Iye amalonjeza kuti oipa “adzalikhidwa m’dziko.”—Miyambo 2:22.
Kodi ndi Thayo la Ndani?
Pamene ndege ya 103 ya Pan American World Airways inaphulika m’mlengalenga pamwamba pa Lockerbie, Scotland, December yatha, okweramo 258 onse anaphedwa. Nzika khumi ndi imodzi za ku Lockerbie nazonso zinafa pamene zidutswa za kupasukako zinagwera panyumba zoŵerengeka. Okondedwa otaika pa ngozi yodabwitsa ya m’mlengalenga analiridwa ndi achibale ndi mabwenzi mofananamo. Kodi Mulungu ali wathayo kaamba ka ngozi imeneyi?
Bishopu wa Chikatolika wina mu Scotland akuwonekera kuganizira tero. Mogwirizana ndi The New York Times, iye ananena mu ulaliki wake pa Holy Trinity Catholic Church kuti: “Atate, ngati Inu muli Mulungu wachikondi, nchifukwa ninji Inu munalola chimenechi kuchitika? Nchifukwa ninji Inu munalola chiwonongeko cha mazana a miyoyo yopanda liwongo? . . . Ndipo nchifukwa ninji Inu mukulola anthu ambiri chotero kuvutika ndi vuto la nkhanza, latsoka la kutaikiridwa achibale?”
Kodi Mulungu alidi kwenikweni wofunikira kupatsidwa mlandu kaamba ka kuvutika koteroko? Mogwirizana ndi ofufuza, umboni unapezedwa m’ngoziyo umene unaloza ku kuwononga kwa bomba la uchigawenga. Pamene anthu akumenyana wina ndi mnzake kupititsa patsogolo zikondwerero zawo zadyera, kodi Mulungu ayenera kupezedwa wa thayo kaamba ka chivulazo chimene iko kungabweretse kwa ena? Ayi! Chiyenera kuyembekezeredwa kuti anthu sakakhala otetezeredwa ku zotulukapo za chimene iwo akuchita. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Kodi nchiyaninso, ponena za minkhole yopanda liwongo la machitidwe a nkhanza ndi opanda thayo a ena, Mlaliki 9:11 imenena kuti “yense angowona zomgwera m’nthaŵi yake.” Chotero, munthu angavulale kapena ngakhale kutaya moyo wake, osati chifukwa chakuti Mulungu amafuna munthu kuvutika koma chifukwa chakuti, mwangozi, iye ali m’malo osayenera pa nthaŵi yovutayo.
Wakupha Weniweni
Akatswiri akhulupirira kwa zaka zambiri kuti anthu amene anali andewu ndipo nthaŵi zonse ofulumira anali chandamale chavhikulu cha nthenda ya mtima. Tsopano, ngakhale kuli tero, umboni watsopano ukulingalira kuti mkwiyo, osati kusakhazikika, ungakhale wakupha weniweni. Dr. Redford Williams, Jr., wa ku Duke University Medical Center, analongosola kuti kukhala wofulumira kapena wogwira ntchito mopambanitsa sikuli “kwenikweni koipa kaamba ka mtima wanu,” ikusimba tero New York Post. Williams analoza kuti “chimene chiri choipa chiri ngati inu muli ndi nkhalwe ndi ukali woipitsitsa ndipo simumasamala kuwubisa iwo pamene mukuchita ndi anthu ena.” Awo okhala pa ngozi yaikulu ya nthenda ya mtima amanenedwa kukhala “okwiya mwamsanga” ndi osakhulupirira zolinga za anzawo. “Iwo amakwiya kaŵirikaŵiri ndipo mwapoyera kusonyeza kusakondwa kwawo, m’malo mwa kukugwira iko mkati,” ikudziŵitsa tero Post.
Ziyambukiro zoipa za mkwiyo zadziŵidwa kwa nthaŵi yaitali kwa ophunzira a Baibulo. Zaka mazana apita Mfumu yanzeru Solomo analemba kuti: “Wokangaza kukwiya adzachita utsiru” ndi “munthu wozaza aputa makani.” Ngakhale kuli tero, munthu “wosakwiya msanga atonthoza makangano.” (Miyambo 14:17; 15:18) Awo amene mwanzeru amatsatira chilangizo cha Baibulo chimenechi angachepetse ngozi ya nthenda ya mtima. Mawu a Mulungu ali owona: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; Koma nsanje ivunditsa mafupa.”—Miyambo 14:30.