Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu!
“Ukumbukirenso Mlengi wako . . . asanadze masiku oipa.”—MLALIKI 12:1.
1. Kodi achinyamata odzipatulira kwa Mulungu ayenera kufunitsitsa kugwiritsa ntchito motani unyamata wawo ndi mphamvu zawo?
YEHOVA amapatsa atumiki ake mphamvu yoti achitire chifuniro chake. (Yesaya 40:28-31) Amatero kwa aliyense mosasamala kanthu za msinkhu wake. Koma makamaka achinyamata odzipatulira kwa Mulungu ayenera kufunitsitsa kugwiritsa ntchito unyamata wawo ndi mphamvu zawo mwanzeru. Chotero, amamvera uphungu wa “Mlaliki,” Mfumu Solomo ya Israyeli wakale. Iye anawalimbikitsa kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.”—Mlaliki 1:1; 12:1.
2. Kodi ana a Akristu odzipatulira ayenera kuchitanji?
2 Uphungu wa Solomo wonena za kukumbukira Mlengi Wamkulu muunyamata choyamba unaperekedwa kwa anyamata ndi atsikana a mu Israyeli. Iwo anabadwira mumtundu wodzipatulira kwa Yehova. Bwanji nanga za ana a Akristu odzipatulira lerolino? Ndithudi, ayenera kukumbukira Mlengi wawo Wamkulu. Akatero, adzam’lemekeza ndi kudzipindulira.—Yesaya 48:17, 18.
Zitsanzo Zabwino Zamakedzana
3. Kodi Yosefe, Samueli, ndi Davide anapereka zitsanzo zotani?
3 Achinyamata ambiri otchulidwa m’Baibulo anapereka chitsanzo chabwino monga awo amene anakumbukira Mlengi wawo Wamkulu. Kuyambira adakali mwana wamng’ono, Yosefe mwana wa Yakobo anakumbukira Mlengi wake. Pamene mkazi wa Potifara anafuna kunyenga Yosefe kuti achite naye zachiwerewere, iye anakana kwa m’tuwagalu nati: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:9) Samueli Mlevi anakumbukira Mlengi wake osati paubwana wake pokha komanso m’moyo wake wonse. (1 Samueli 1:22-28; 2:18; 3:1-5) Mnyamatayo Davide wa ku Betelehemu anakumbukiradi Mlengi wake. Kukhulupirira kwake Mulungu kunali koonekeratu pamene anayang’anizana ndi chiphona chachifilisticho Goliyati ndi kunena kuti: “Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unaŵanyoza. Lerolino Yehova adzakupereka iwe m’dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako . . . kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo iye adzakuperekani inu m’manja athu.” Posapita nthaŵi, Goliyati anafa, ndipo Afilisti analiyala liŵiro, kuthaŵa.—1 Samueli 17:45-51.
4. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Mlengi wathu Wamkulu anakumbukiridwa ndi mtsikana wachiisrayeli wandende ku Aramu komanso ndi Mfumu Yosiya wachinyamatayo? (b) Kodi Yesu wazaka 12 zakubadwa anasonyeza motani kuti anakumbukira Mlengi wake?
4 Wachinyamata winanso amene anakumbukira Mlengi Wamkulu anali mtsikana wachiisrayeli wandende. Iye anapereka umboni wabwino kwambiri kwa mkazi wa kazembe wa gulu lankhondo la Aramu Namani mwakuti anapita kwa mneneri wa Mulungu, anachiritsidwa khate lake, nakhala wolambira Yehova. (2 Mafumu 5:1-19) Mfumu yachinyamatayo Yosiya anachirikiza molimba mtima kulambira koyera kwa Yehova. (2 Mafumu 22:1–23:25) Koma chitsanzo chabwino kwambiri cha amene anakumbukira Mlengi wake Wamkulu paubwana wake anali Yesu wa ku Nazarete. Talingalirani zimene zinachitika pamene anali ndi zaka 12 zakubadwa. Makolo ake anapita naye ku Yerusalemu kukachita Paskha. Paulendo wobwerera kwawo, anazindikira kuti Yesu panalibe; choncho anabwerera kukam’funafuna. Patsiku lachitatu, anam’peza akukambirana mafunso a m’Malemba ndi aphunzitsi apakachisi. Poyankha funso la amayi wake losonyeza kuda nkhaŵalo, Yesu anafunsa kuti: “Kuli bwanji kuti munali kundifunafuna Ine? Simunadziŵa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?” (Luka 2:49) Kunali kopindulitsa kwa Yesu kupeza chidziŵitso chofunika mwauzimu pakachisi, ‘panyumba ya Atate wake.’ Lerolino, Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ndiyo malo abwino koposa opezako chidziŵitso cholongosoka cha Mlengi wathu Wamkulu.
M’kumbukireni Yehova Tsopano Lino!
5. M’mawu anuanu, kodi mungalongosole bwanji zimene mlaliki ananena zomwe zalembedwa pa Mlaliki 12:1?
5 Wolambira Yehova ndi mtima wonse amafuna kuyamba utumiki Wake mwamsanga zedi ndi kutumikira Mulungu masiku onse a moyo wake. Komabe, kodi munthu yemwe wawononga unyamata wake pachabe chifukwa chosakumbukira Mlengi angayembekeze zotani? Mouziridwa ndi Mulungu, mlalikiyo analemba nati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.”—Mlaliki 12:1.
6. Kodi pali umboni wotani wakuti Simeoni ndi Anna okalambawo anakumbukira Mlengi wawo Wamkulu?
6 Palibe amene amasangalala ndi “masiku oipa” aukalamba. Koma anthu achikulire amene akukumbukira Mulungu n’ngachimwemwe. Mwachitsanzo, Simeoni wokalambayo ananyamula kamwanako Yesu m’manja mwake pakachisi ndi kunena monyadira kuti: “Tsopano, Ambuye, monga mwa mawu anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, chimene munakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.” (Luka 2:25-32) Anna wazaka 84 zakubadwa anakumbukiranso Mlengi wake. Nthaŵi zonse anali pakachisi ndipo analipo pamene makolo a khandalo Yesu anapita nalo kumeneko. “Iye anafikako panthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiwombolo cha Yerusalemu.”—Luka 2:36-38.
7. Kodi zinthu zili motani kwa awo amene akalambira muutumiki wa Mulungu?
7 Mboni zamakono za Yehova zimene zakalambira muutumiki wa Mulungu zingamve zopweteka ndi kulephera kuchita zinthu zina chifukwa cha ukalamba. Komabe, n’zachimwemwetu kwambiri, ndipotu timayamikira zedi utumiki wawo wokhulupirikawo! Zili ndi “chimwemwe cha Yehova,” popeza zikudziŵa kuti wasonyeza mphamvu yake yosagonjetseka padziko lapansi ndipo walonga ufumu Yesu Kristu monga Mfumu yamphamvu yakumwamba. (Nehemiya 8:10) Inoyi ndiyo nthaŵi yoti achinyamata ndi achikulire amvere chilimbikitso chakuti: “Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.”—Salmo 148:12, 13.
8, 9. (a) Kodi “masiku oipa” amakhala osapindulitsa kwa yani, ndipo n’chifukwa chiyani zimatero? (b) Kodi lemba la Mlaliki 12:2 mungalilongosole motani?
8 “Masiku oipa” a ukalamba ndi osasangalatsa, mwinanso ndi opsinja maganizo kwambiri kwa awo amene salingalira za Mlengi wawo Wamkulu ndi amenenso sadziŵa zifuno zake zaulemerero. Alibe malingaliro auzimu amene angalimbane ndi ziyeso zodza ndi ukalamba ndi masoka amene agwera mtundu wa anthu kuyambira pamene Satana anaponyedwa kuchokera kumwamba. (Chivumbulutso 12:7-12) Chotero mlaliki akutilimbikitsa kukumbukira Mlengi wathu “lisanade dzuŵa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula.” (Mlaliki 12:2) Kodi mawuŵa amatanthauzanji?
9 Solomo akuyerekeza nthaŵi yaunyamata ndi nyengo ya chilimwe ku Palestina pamene dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi zimaŵala mumlengalenga mopanda mitambo. Zinthu zimaoneka kukhala zoŵala kwambiri panthaŵi imeneyo. Koma kuukalamba, masiku a munthu amakhala ngati nthaŵi ya dzinja pamene kumakhala kozizira ndiponso kumagwa mvula, mvula yamavuto otsatizanatsatizana. (Yobu 14:1) Kungakhaledi komvetsa chisoni kwabasi kudziŵa za Mlengi koma n’kulephera kum’tumikira m’nyengo ya chilimwe ya moyo! Pamene moyo uli m’dzinja laukalamba, zinthu zimachita mdima, makamaka kwa aja amene sanagwiritse ntchito mwayi wotumikira Yehova muunyamata wawo chifukwa cholondola zinthu zopanda pake. Komabe, mosasamala kanthu za msinkhu wathu, tiyeni ‘titsate Yehova ndi mtima wathu wonse,’ monga momwe anachitira Kalebe, mnzake wokhulupirika wa mneneri Mose.—Yoswa 14:6-9.
Zotsatira za Ukalamba
10. Kodi n’chiyani chimene chimaimira (a) ‘osunga nyumba’? (b) “amuna olimba”?
10 Kenako Solomo akutchula zovuta za “tsikulo [p]omwe [o]sunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzaŵerama, akupera nadzaleka popereŵera, omwe ayang’ana pamazenera nadzadetsedwa.” (Mlaliki 12:3) “Nyumba” ikuimira thupi lamunthu. (Mateyu 12:43-45; 2 Akorinto 5:1-8) ‘Oisunga’ ake ndiwo manja, amene amateteza thupi ndi kuligaŵira zofunikira. Muukalamba manja amanjenjemera chifukwa cha kutha mphamvu, mantha, ndi kufa ziŵalo. “Amuna olimba,” imene ili miyendo, sikhalanso mizati yolimba koma imafooka ndipo imakhala yosawongoka moti okalamba poyenda amangokhwekhweretsa mapazi. Komabe, kodi simusangalala kuona okhulupirira anzathu okalambawo ali pamisonkhano yachikristu?
11. Mwaphiphiritso, kodi ‘opera’ ndi “omwe ayang’ana pamazenera” ndiwo ayani?
11 ‘Opera nadzaleka popereŵera.’ Koma motani? Mano angakhale atawola kapena kugululidwa, ndipo otsalawo, ngati atsala n’komwe, amakhala opereŵera. Kutafuna chakudya cholimba kumakhala kovuta mwinanso kumakhala kosatheka. “Omwe ayang’ana pamazenera,” maso, pamodzi ndi mphamvu yaubongo yomwe imatitheketsa kuona, zimayamba kuona mwachimbuuzi, mwinanso kuchitiratu mdima.
12. (a) Kodi “pakhomo lakunja padzatsekeka” motani? (b) Kodi mukuwaganizira bwanji olengeza Ufumu okalamba?
12 Mlaliki akupitiriza kuti: “Pakhomo lakunja padzatsekeka; potsika mawu akupera, wina nanyamuka polira mbalame, ndipo akazi onse akuimba sadzamveka bwino.” (Mlaliki 12:4) Khomo, limene lili kamwa, silitsegukanso mokwanira kapenanso silitseguka n’komwe kuti litchule zimene zili mu “nyumba,” kapena m’thupi, la okalamba amene satumikira Mulungu. Palibe chimene chimatuluka kupita “kunja” kwa anthu ena. Koma bwanji ponena za olengeza Ufumu okalamba ndi achangu? (Yobu 41:14) Angayende pang’onopang’ono kupita kunyumba ndi nyumba ndiponso ena amayankhula movutikira, komatu amalemekeza Yehova!—Salmo 113:1.
13. Kodi mlaliki akulongosola motani mavuto ena a okalamba, koma kodi choonadi n’choti bwanji ponena za Akristu okalamba?
13 Phokoso la kupera limatsika pamene chakudya chitafunidwa ndi nkhama zopanda mano. Pabedi lake wokalamba sagona tulo teniteni. Ngakhale kulira kwa mbalame kumam’dzutsa. Saimba nyimbo zambiri, komanso zimene amaimba saziimba mwamphamvu. “Akazi onse akuimba,” chimene chili chuni cha nyimbo, ‘samveka bwino.’ Nyimbo zoimbidwa ndi ena sizimveka mokwanira kwa wokalamba. Komabe, odzozedwa okalamba pamodzi ndi anzawo, omwe ena mwa iwo ndi okalambanso, amakwezabe mawu awo poimba nyimbo zotamanda Mulungu pamisonkhano yachikristu. Timasangalala zedi kukhala nawo pafupi ndi kulemekeza Yehova mumpingo!—Salmo 149:1.
14. Kodi ndi mantha otani amene amavutitsa okalamba?
14 Zinthu n’zomvetsatu chisoni kwa okalamba, makamaka aja amene anyalanyaza Mlengi! Mlaliki akuti: “Inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; mchiwu nudzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwawo kwamuyaya, akulira maliro nayendeyanda panja.” (Mlaliki 12:5) Kuti ayende penapake potsetsereka kwambiri, okalamba ambiri amaopa kugwa. Ngakhale kungoyang’ana chinachake chachitali kwambiri m’mwamba kungawachititse chizungulire. Akapita panja m’misewu yomwe muli anthu piringupiringu, mantha amaŵagwira poganiza kuti angavulale kapena kufwambidwa ndi akuba.
15. Kodi ‘mchiwu umaphuka’ motani, ndipo dzombe ‘limakoka miyendo’ motani?
15 Kwa munthu wokalamba, ‘mchiwu umaphuka,’ kusonyeza kuti tsitsi lake limamera imvi, kenako limakhala mbuu ngati matalala. Imvi zimenezo zimagwa monga maluŵa ophukira a mchiwu. Pamene ‘akoka miyendo’ yake, mwina poyenda moŵerama manja ali lende kapena atagwira m’chuuno, zigongono zitangoti njoo, iwo amaoneka ngati dzombe. Komano ngati enafe tikuoneka choncho, ena ayenera kukumbukira kuti tili m’chikhamu cha dzombe la Yehova, lamphamvu ndi laliŵiro!—Onani Nsanja ya Olonda, May 1, 1998, masamba 8-13.
16. (a) Kodi ‘kutha kwa zilakolako’ kumasonyezanji? (b) Kodi “kwawo kwamuyaya” n’kuti, ndipo ndi zizindikiro ziti zakuti akuyandikira imfa zimene zimaonekera?
16 Mawu akuti “zilakolako ndi kutha” akusonyeza kuti chilakolako cha zakudya cha munthu wokalamba chikatha, ngakhale chakudya chochititsa madyo sichim’kopa n’komwe. Zinthu ngati zimenezi zimasonyeza kuti akuyandikira “kwawo kwamuyaya,” kumanda. Kudzakhala kwawo kwamuyaya ngati sanakumbukire Mlengi wake ndipo walondola njira yoipa moti Mulungu sadzam’kumbukira pachiukiriro. Zizindikiro zakuti munthu akuyandikira imfa zimaonekera mwa mawu odandaula ndi obuula omwe amatuluka pakhomo la kamwa la munthu wokalamba.
17. Kodi “chingwe chasiliva” chimaduka motani, ndipo “mbale yagolidi” ingatanthauze chiyani?
17 Tikulimbikitsidwa kukumbukira Mlengi wathu “chingwe chasiliva chisanaduke, ngakhale mbale yagolidi isanaduke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanathyoke kuchitsime.” (Mlaliki 12:6) “Chingwe chasiliva” lingakhale fupa lamsana. Ingakhaletu imfa basi ngati njira yodabwitsa imeneyi ya mauthenga opita ku ubongo itawonongeka kwambiri. “Mbale yagolidi” ingatanthauze ubongo, umene uli m’chibade chonga mbale ndiponso ndi wolumikizana ndi fupa lamsana. Wagolidi chifukwa cha kufunika kwake, ubongo ukasiya kugwira ntchito munthuyo amafa.
18. Kodi ‘mtsuko wa kukasupe’ umaphiphiritsa chiyani, ndipo chimachitika n’chiyani ukaphwanyika?
18 ‘Mtsuko wa kukasupe’ ndiwo mtima, umene umalandira magazi ndi kuwatumizanso kuti azungulire m’thupi lonse. Paimfa, mtima umakhala ngati mtsuko wophwanyika, wosweka kukasupe chifukwa chakuti sungalandire, kusunga, ndi kukankha magazi ofunikawo kuti thupi lipeze zofunikira ndi kutsitsimulidwa. ‘Njinga yothyoka yotungira madzi kuchitsime’ imasiya kugwira ntchito, ndipo kuzungulira kwa magazi m’thupi lonse kumene kumachirikiza moyo kumaleka. Chotero Yehova anavumbulira Solomo kuti magazi amazungulira m’thupi nthaŵi yaitali kwambiri William Harvey, dokotala wa m’zaka za zana la 17 asanasonyeze kuti magazi amazungulira.
19. Kodi mawu a pa Mlaliki 12:7 amagwira ntchito motani paimfa?
19 Mlaliki anawonjezera kuti: “Fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.” (Mlaliki 12:7) “Njinga yotungira madzi” itathyoka, thupi lamunthu, lomwe poyambirira linapangidwa ndi fumbi lapansi, limabwerera kufumbiko. (Genesis 2:7; 3:19) Moyo umafa chifukwa chakuti mzimu, kapena kuti mphamvu ya moyo, yoperekedwa ndi Mulungu imabwerera ndi kukhala ndi Mlengi wathu.—Ezekieli 18:4, 20; Yakobo 2:26.
Kodi Pali Tsogolo Lotani kwa Okumbukira?
20. Kodi Mose anali kupempha chiyani pamene anapemphera monga momwe Salmo 90:12 amanenera?
20 Solomo anasonyeza bwino lomwe kufunika kwa kukumbukira Mlengi wathu Wamkulu. Ndithudi, moyo waufupi wodzaza mavuto si wokhawo umene anthu okumbukira Yehova ndi kuchita chifuniro chake ndi mtima wonse adzakhala nawo. Kaya ndi ana kapena okalamba, onse ali ndi malingaliro ofanana ndi a Mose, amene anapemphera kuti: “Mutidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.” Mneneri wodzichepetsayo wa Mulungu anafunitsitsa kuti Yehova am’dziŵitse, kapena kum’phunzitsa, iyeyo ndi Aisrayeli kusonyeza nzeru posawononga ‘masiku a zaka zawo’ ndi kuwagwiritsa ntchito m’njira imene Mulungu amaivomereza.—Salmo 90:10, 12.
21. Kuti tiwerenge masiku athu mopereka ulemerero kwa Yehova, kodi tiyenera kutani?
21 Makamaka Akristu achinyamata ayenera kutsimikiza mtima kumvera uphungu wa mlalikiyo wakuti akumbukire Mlengi. Alitu ndi mpata wabwino zedi wochita utumiki wopatulika kwa Mulungu! Komabe, mosasamala kanthu za msinkhu wathu, ngati tiphunzira kuŵerenga masiku athu mopereka ulemerero kwa Yehova mu “nthaŵi ya chimaliziro” ino, tingadzapitirizebe kuwaŵerenga kosatha. (Danieli 12:4; Yohane 17:3) Ndithudi, kuti tidzachite zimenezo, tiyenera kukumbukira Mlengi wathu Wamkulu. Tiyeneranso kukwaniritsa udindo wathu wonse kwa Mulungu.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani achinyamata akulimbikitsidwa kukumbukira Mlengi wawo?
◻ Kodi zitsanzo zina za m’Malemba za anthu amene anakumbukira Mlengi wawo Wamkulu ndi ziti?
◻ Kodi zotsatira zina za ukalamba zofotokozedwa ndi Solomo n’zotani?
◻ Kodi pali tsogolo lotani kwa awo amene akukumbukira Yehova?
[Zithunzi patsamba 15]
Davide, mtsikana wachiisrayeli wandende, Anna, ndi Simeoni anakumbukira Yehova
[Zithunzi patsamba 16]
Mboni zokalamba za Yehova zimachita utumiki wopatulika kwa Mlengi wathu Wamkulu mwachimwemwe