Ana Amene Amakondwereta Mtima wa Yehova
‘Kondweretsa mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.’—MIYAMBO 27:11, NW.
1. Kodi makolo athu ndi mlengi wathu amayambukiridwa motani ndi mmene timakhalira miyoyo yathu?
KAYA mukukuzindikira kapena ayi, kumapanga kusiyana mmene mumakhalira moyo wanu. Mwachitsanzo, kumapanga kusiyana kwa makolo anu. “Mwana wanzeru akondweretsa atate,” limalongosola motero Baibulo, “koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.” (Miyambo 10:1; 23:24, 25) Koma chofunikadi kwambiri, njira imene mukhalira moyo wanu ingapangitse Mlengi wathu Yehova Mulungu kukondwera kapena chisoni: “Mwananga, khala wanzeru,” akupempha Yehova, “nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”—Miyambo 27:11.
2. Kodi ndinkhani yofunika yotani imene inadzutsidwa ndi Satana, ndipo tikulowetsedwamo motani?
2 Ndithudi, iye amene amatonza Yehova, ndiye Satana Mdyerekezi. M’munda wa Edene, Satana anadzutsa nkhani yaikulu imene inafunikira kuti Yehova ayankhe. Pamene Mdyerekezi anali wokhoza, mosavutikira, kuchititsa Hava, ndiyeno Adamu, kuswa lamulo la Mulungu, pali umboni wakuti anatokosa Yehova. Kwenikweni, iye analengeza kuti: ‘Tangondipatsani mpata ndipo ndingathe kupatutsa munthu aliyense pa kukutumikirani.’ (Yobu 1:6-12) Chotero, Yehova anapereka pempho lothutsa mtima lolembedwa pamwambapa, lakuti mwana wake Ampatse ‘yankho’ kotero kuti Iye ayankhe chitokoso cha Satana.
3. Kodi nchifukwa ninji pempho la Yehova limagwira ntchito kwakukulukulu kwa Yesu, ndiponso ndani amene akondweretsa mtima wa Mulungu?
3 Komabe, kwenikweni kodi nkwayani kumene Yehova analunjikitsako pempholi, amene anamutcha kukhala “mwananga”? Yesu Kristu ndiye mwana wa Mulungu mwapadera, pokhala Mwana wake wobadwa yekha. (Yohane 1:14) Ndiponso, kusiyapo Adamu, amene analepheretsa Mlengi wake, Yesu anali munthu yekha wangwiro amene anayenda padziko lapansi, chifukwa chake anali mwamuna yekha woyeneretsedwa kutsimikizira m’lingaliro lotheratu kuti kukhulupirika kwa Mulungu kungathe kusungidwa. (1 Akorinto 15: 45) Motero pempho la Yehova kwakukulukulu limagwira ntchito kwa Yesu. Ndipo Yesu sanagwiritse mwala Atate wake. Mwanjira yake yokhulupirika, Yesu anapereka yankho ku chitokoso chodzitamandira cha Satana chakuti anthu sakamtumikira Iye mokhulupirika poyesedwa. (Ahebri 2:14; 12:2) M’kuwonjezera, awo onse amene adzalamulira limodzi ndi Kristu kumwamba adzafunikira kukhala atapangitsa mtima wa Yehova kukondwera mwa kukhulupirika kwawo kwa Mulungu ngakhale kufikira imfa.—Chivumbulutso 2:10.
4. Posankha chimene mudzachita ndi moyo wanu, kodi ndinkhani yofunika yotani imene muyenera kuilingalira?
4 Koma bwanji za ife lerolino, kuphatikizapo achicheperenu? Kodi inu mukuphatikizidwa m’nkhaniyi yakuti kaya anthu adzakhala okhulupirika kwa Mulungu kapena ayi? Ndithudi mukuphatikizidwa! (Salmo 147:11; 148: 12, 13) Mungakhale wosakuzindikira, koma zimene mumachita ndi moyo wanu zimachirikiza kaya mbali ya Mulungu yankhaniyo kapena mbali ya Satana. Zimapangitsa Yehova kukondwera kapena Satana kukondwera. Ndithudi, chiitano cha Yehova kapena pempho lingathe kuwonedwa kukhalanso lolunjikitsidwa kwa inu mwachindunji lakuti: “Mwananga [kapena Mwana wanga wamkazi], khala wanzeru, nukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Kodi kupangitsa mtima wa Mlengi wanu kukhala wokondwera sindiko chonulirapo chokhutiritsa chimene muyenera kukhala nacho?
Chifukwa Chake Kuli Kwanzeru
5. Kodi nchifukwa ninji tiri anzeru kukondweretsa mtima wa Yehova?
5 Tamverani kuti Yehova akulimbikitsa kuti, “Khala wanzeru.” Kodi nchifukwa ninji tiri anzeru pamene tipangitsa mtima wa Yehova kukondwera? Chiri chifukwa chakuti Yehova ali Atate wachikondi amene amatifunira kokha ubwino woposa, ndipo motero chirichonse chimene amatipempha kuchita chiri kaamba ka ubwino wathu. Monga momwe Yesaya 48:17, 18 amanenera kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde anyanja.”
6. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yenova amafuna kuti musangalale ndi moyo? (b) Kodi nzotulukapo zotani zimene simungazipewe?
6 Monga kholo lachikondi, Yehova amakufunani kuti musangalale mokwanira ndi mphatso yake yamtengo wapatali ya moyo. Chifukwa chake iye amati: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku aunyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako awona.” Ndithudi, chiitanochi, sichikufunsira kuchita chinthu chokondweretsa chirichonse chimene mungakhumbe. Izi zasonyezedwa ndi chenjezo lotsatirali: “Koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.” (Mlaliki 11:9) Inde, simungathe kupewa zotulukapo za zochita zanu; Mulungu adzakuwerengerani mlandu we zimene mumachita. Lamulo la makhalidwe abwino nlotsimikizirika lakuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”—Agalatiya 6:7.
7, 8. (a) Kodi mungachotse motani mavuto ndi kupewa tsoka? (b) Kodi ndi liti pamene moyo waunyamata ndi thanzi uli wachabechabe?
7 Kaamba ka chifukwa ichi, Yehova akuwonjezera kuti: “Chotsa zopweteka [kapena zochititsa nkhawa] m’mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwachabe. (Mlaliki 11:10) Ndithudi, kuli kwanzeru kupewa zochitika zimene zidzakuchititsani kuvutika pambuyo pake. Oo, padzakhala awo amene adzanena kuti mukuluza—kuti inu ‘simunakhaledi ndi chisangalalo’ kusiyapo ngati muledzera, mumagonana ndi ambiri, kapena kuchita kanthu kena kalikonse “kosonyeza kulimba mtima.” Koma ha nkupusa chotani nanga! “Nkosakuyenerera,” analira motero wophunzira wina wachichepere pambuyo pa kuchita dama lachigololo. “Ndakhala wovutitsidwa maganizo chiyambire nthawiyo.”
8 Chotero achicheperenu, mwanzeru labadirani uphungu wa Mulungu wa kuchotsa chodetsa nkhawa chirichonse kapena kumva chisoni mu mtima mwanu, zofanana ndi zimene achichepere olondola njira ya moyo yosadera nkhawa kapena yadyera amakhala nazo. Wolemba ndakatulo wa m’zaka za zana la-17 ananena kuti: “Mbali yaikulu koposa ya anthu imagwiritsira ntchito zaka zawo zoyambirira kupanga mkhalidwe wawo womalizira wachisoni.” Ndithudi, koma nzomvetsa chisoni motani nanga! Pamene wachichepere awawanya nyonga zake zauzimu ndi maluso mwanjira imene imapangitsa zaka za pambuyo pake zaukulu kukhala zamavuto kwambiri, moyo wake waubwana ndi waunyamata zimakhaladi zachabechabe! (Miyambo 22:3) Chotero khalani wanzeru! Tsatirani uphungu wowonjezerekawo wakuti: “Ukumbukirenso mlengi wako masiku aunyamata wako.”—Mlaliki 12:1.
9. Kodi ndimapindu otani amene mudzakhala nawo mwa kukumbukira Yehova muunyamata wanu?
9 Mwa kukumbukira Yehova muunyamata wanu mudzadzipindulitsadi. Sikokha kuti mudzapewa zowawa ndi mavuto obweretsa tsoka, koma panthawi yomwe ino mudzakhala ndi moyo wachimwemwe, ndi wokondweretsa m’kutumikira Mlengi wanu Wamkulu. M’kuwonjezera, inu mwanzeru mudzakhala mukukundika chuma kumwamba chimene chidzakupindulitsani ku umuyaya wonse. (Mateyu 6:19-21) Ngati mukumbukira Yehova tsopano mwa kuchita chifuniro chake, iye adzakukumbukirani ndi kukupatsani ‘zokhumba mtima wanu,’ inde, moyo wachimwemwe, wokwanira m’Paradaiso kosatha!—Salmo 37:4; 133:3; Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi Mumalingalira Motani Ponena za Yehova
10. (a) Kodi nchifukwa ninji chosankha chanu cha kutumikira Mulungu sichingakhale kokha kuwerengera kopanda pake kwa chimene chiri nzeru? (b) Kodi ndipempho lowonjezereka lotani limene Yehova amapanga?
10 Komabe chosankha chanu cha kutumikira Yehova sichingakhale kokha kuwerengera wamba kwa kuchita mwanzeru. Satana ali mdani wochenjera kwambiri, kotero kuti ngati mulingalira kokha zimene inu mudzapindula, potsirizira pake adzakhoza kusonkhezera zikhoterero zina zadyera zokuchotsani ku kutumikira Yehova. Chotero Yehova samangokupemphani kokha kukhala wanzeru. Ayi, komanso iye amapempha kudzipatulira kwanu kwa iye. Yesu anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse.” (Mateyu 22:37) Kodi mumadziwa chimene kukonda Yehova ndi mtima wonse kumatanthauza?
11. (a) Kodi kumatanthauzanji kupereka mtima wanu kwa Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene chokumana nacho cha Yosefe chimafotokozera mwafanizo mmene chisonkhezero chamtima choyenerera chingatisonkhezerere kuchita chifuniro cha Mulungu?
11 Mtima wanu umatanthauza umunthu wanu wamkati, limodzi ndi mphamvu zanu za kuganiza, zisonkhezero zanu, makhalidwe anu, ndi malingaliro apansi pamtima. Motero kukonda Yehova ndi mtima wanu wonse kumatanthauza kuti mumamkonda kwambiri ndi kuti pa kanthu kena kalikonse m’moyo ndiko chosankha chanu cholingaliridwa kupangitsa mtima wake kukondwera mwa kumpatsa yankho la ntonzo wa Satana. Luntha lotero ndi malingaliro ozama achikondi ndi kudera nkhawa ndi Mulungu zidzakupatsani chisonkhezero champhamvu koposa cha kuchita chifuniro chake ngakhale pamene kungawonekere kukhala kosangalatsa kwambiri kuchitira mwina. Yosefe wachichepere anali kukonda Yehova motero, ndipo pamene mkazi wotchuka anampepha kuti, “Gona ndi ine,” Yosefe anayankha kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?—Genesis 39:7-9.
12. (a) Kodi mumasonyeza motani kuti mwapereka mtima wanu kwa Yehova? (b) Ngati simunapereke mtima wanu kwa Yehova, kodi ndi mafunso otani amene muyenera kusinkhasinkha?
12 Mumasonyeza kuti mumakonda Yehova ndi mtima wanu wonse pamene mupita kwa iye m’pemphero ndi kumuuza kuti mufuna kukhala wake, kuti mufuna kumtumikira kosatha. Mwanjira iyi mumadzipatulira kwa Yehova. Kodi munachita ichi? Ngati simunatero, mulekeranji? Kodi chikuletsani nchiyani? Kodi muli wamkulu mokwanira kumvetsetsa ndi kuzindikira nkhani yaikulu pakati pa Yehova ndi Satana? Ndipo kodi mumafuna kupangitsa mtima wa Yehova kukondwera? Ndithudi Satana samafuna kuti mukonde Yehova ndi mtima wanu wonse. Iye amafuna kuti mwa dyera muchite ‘zokhumba zanu’ kuti mudzikondweretse. Kodi mudzakondweretsa yani, Yehova kapena Satana? Sinkhasinkhani mfundozi mwamphamvu.
13. Ngati muli odzipatulira ndi obatizidwa, kodi ndimafunso otani amene muyenera kudzifunsa?
13 Ngati mwadzipatulira kwa Mulungu ndipo mwakusonyeza mwa ubatizo wa m’madzi, kodi njira yanu ya moyo imasonyeza kuti mtima wanu ulidi wa Mulungu? Kodi zikondwerero zanu, zikhumbo zanu, zasumikidwa pachiyani? pa kugula galimoto latsopano kodi? pa kupanga ndalama zoti mugulire zovala kapena zinthu zanu zina? Kodi nzikondwerero za yani zimene zimadza choyamba—za inu mwini kapena za Yehova? Kodi mwalabadiradi kuchiitano cha Yehova cha kupereka mtima wanu kwa iye?
14. (a) Kodi ndichuma chamtengo wapatali chotani chimene achichepere ali nacho? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kwachisoni pamene wachichepere sakumbukira Mlengi wake?
14 Pamene kuli kwakuti achikulire ali ndi chidziwitso chochulukirapo ndipo kawirikawiri nganzeru kwambiri, nawonso achichepere ali ndi chuma chamtengo wapatali chimene angagwiritsire ntchito kukondweretsa Mulungu. “Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yawo,” limatero Baibulo. (Miyambo 20:29) Chotero gwiritsirani ntchito mphamvuyo tsopano. Kumbukirani Mlengi wanu “masiku atsoka” aukalamba “asanadze,” pamene thupi limafooka ndipo ziwalo zake zimanyonyotsoka ndi kulephera kugwira ntchito bwino lomwe. Ha nkomvetsa chisoni chotani nanga kwa munthu amene walephera kukumbukira Mlengi wake mu unyamata wake ndiyeno atakalamba alibe chirichonse chimene angadzivomereze nacho kwa Mulungu! Kulidi ‘kwachabechabetu!’ (Mlaliki 12:1-8) Chifukwa chake, mwanzeru, kumbukirani mlengi wanu mudakali ndi mphamvu ndi nyonga. Pangani cholembedwa chautumiki wokhulupirika kwa Mulungu, amene adzakukumbukirani mwa chiweruzo choyanja, inde, ku moyo wosatha.—Ahebri 6:10-12; Mlaliki 12:13, 14.
Anakondweretsa Mtima wa Mulungu
15. Kodi ndizitsanzo Zabaibulo zotani zimene tiri nazo za anyamata amene anagwiritsira ntchito mphamvu yawo muutumiki wa Yehova?
15 Baibulo liri lodzala ndi zitsanzo za achichepere amene anagwiritsira ntchito “kukongola” kwawo—mphamvu yawo—muutumiki wa Mulungu. Anali “anyamata” ofulumira ndi opepuka miyendo amene anazonda dziko Lolonjezedwa. (Yoswa 6:22, 23; 2:15, 16, 23) Davide, pamene iyemwini anali kokha m’zaka zake za m’ma-20, anatumiza ‘anyamata khumi’ paulendo wokapempha chiyanjo kwa Nabala. (1 Samueli 25:4, 5) Pamene Ayuda motsogozedwa ndi bwanamkubwa Nehemiya anamanga malinga a Yerusalemu pamene anawopsedwa kuti adzaukiridwa, kodi ndani amene anachita ntchito yaupandu, ndi yamphamvu? “Gawo lina la anyamata anga,” analongosola motero Nehemiya, “anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo.” (Nehemiya 4:16) Ndipo pamene Mulungu anakantha Hananiya ndi mkazi wake Safira nafa chifukwa chakuti ananama, “anyamata” anawanyamula ndi kukawaika kumanda.—Machitidwe 5:5, 6, 10.
16. Kodi ndim’ntchito yauzimu yotani mu imene achichepere kalero anakhalamo ndi phande?
16 Ndithudi kumakondweretsa mtima wa Yehova pamene achichepere amadzipereka kaamba ka utumiki uliwonse wofunika panthawiyo. Komabe achichepere aphatikizidwa m’ntchito yauzimu imene imafuna zambiri kuposa mphamvu ndi nyonga zakuthupi. “Ndine mnyamata,” anavomereza motero Elihu. Komabe, Yehova anamgwiritsira ntchito kuwongolera Yobu. (Yobu 32:4-6) Samueli anali kokha “mwana” pamene anayamba kutumikira pa chihema cha Yehova ku Silo. (1 Samueli 2:18) Linali “buthu” limene, ngakhale linali kapolo m’nyumba ya Namani linalengeza mopanda mantha chimene mneneri wa Yehova akanachita. (2 Mafumu 5:2-4) Pamene Yehova anapatsa gawo kwa Yeremiya kukhala mneneri, Yeremiya anati: “Ndiri mwana.” (Yeremiya 1:5, 6) “Koma anyamata amene anayi”—Danieli ndi atsamwali ake atatu Achihebri—anali atumiki apadera chotani nanga a Yehova mu ukapolo wa Babulo! (Danieli chaputala 1 ndi 3) Msuwani wa Paulo, “mnyamatayo,” anachita molimba mtima m’malo mwa amalume ake. (Machitidwe 23: 16-22) Ndiyeno panali mnyamatayo Timoteo, amene kuyambira paukhanda anadziwa malemba oyera nagwiritsira ntchito unyamata wake muutumiki wa Yehova.—2 Timoteo 3:15; Afilipi 2:19-23; 1 Akorinto 3:7.
Kukondweretsa Mtima wa Mulungu Lerolino
17. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeza achichepere lerolino okondweretsa Yehova, ndipo kodi timatero?
17 Komabe saali achichepere akale okha amene anakondweretsa mtima wa Mulungu mwa utumiki wawo wokhulupirika. “Masiku otsiriza, anena Mulungu, ‘Ndidzathira chamzimu wanga pathupi lirilonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzawona masomphenya.’” (Machitidwe 2:17; Yoweli 2:28) Chotero ife tiyenera moyenerera kuyembekezera kupeza Akristu achichepere ambiri m’masiku ano omaliza amene amakondweretsa Yehova. Ndipo timatero! Pamene kuli kwakuti Mboni za chichepere siziri zosalakwa, monga momwedi palibe aliyense wa ife ali wotero, komabe ochuluka akuchita bwino kwambiri monga Akristu. Iwo amadera nkhawa ndi kukondweretsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11; 3:1, 2.
18, 19. Kodi ndintchito yotani imene ifunikira kuchitidwa lerolino, ndipo kodi nchifukwa ninji achichepere ali oyiyenerera bwino lomwe?
18 M’masiku otsiriza ano chifuniro cha Mulungu nchakuti umboni waukulu wapadziko lonse wonena za Ufumu wake uperekedwe, umene umaphatikizapo kuyesayesa kokulira. (Mateyu 24:14) Nyumba Zaufumu zolambirira zifunikira kumangidwa, kuphatikizapo nyumba zazikulu kwambiri za misonkhano yadera. M’maiko ambiri mafakitale ochuluka osindikizira mabukhu Abaibulo ali ofunika, kuphatikizapo malo okhala owonjezereka m’nyumba za Betele. Kuti malo atsopano amenewa apezeke kumafunikiritsa ntchito yomanga yakalavula gaga, ndipo monga momwe kunaliri m’nthawi ya kumanga malinga m’tsiku la Nehemiya, achichepere okhala ndi mphamvu ndi nyonga akuchita mbali yaikulu yantchitoyi.
19 Achichepere otere akuchitanso mbali yaikulu ya ntchito ya kalavula gaga yofunikayo ya kusindikiza mabukhu ofotokoza Baibulo, kuika zikuto, ndi kutumiza matani zikwi zambiri chaka chirichonse. Kwenikweni, pamalikulu a New York a Mboni za Yehova, kuphatikizapo Watchtower Farms, pali achichepere 1, 400 azaka zakubadwa 25 ndi kucheperapo. Ndipo utumiki wawo suuli wolekezera kuntchito zofunikiritsa nyonga yakuthupi mkati mwa mlungu; pamapeto a milungu amakhala ndi phande m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba ndi m’misonkhano Yachikristu m’mipingo ya kwawo. Amakondweretsa mtima wa Yehova chotani nanga!
20. (a) Kodi ndiphande lotani limene achichepere ali nalo muuminisitala waupainiya? (b) Kodi ndi mafunso otani amene achichepere amene saali muuminisitala wanthawi yonse ayenera kudzifunsa?
20 Mu United States, ogwira ntchito phewa ndi phewa limodzi ndi achichepere amenewa ndiwo ena oposa 12, 700 amsinkhu wofanana amene akutumikira monga aminisitala apainiya okhazikika. Mbali zina zadziko zoposa zikwi makumi ambiri za achichepere zikuchitanso upainiya. Ngati inu muli wachichepere amene simuli kale muuminisitala wanthawi yonse, kodi mungadzikhazikitsire chonulirapo chimene chidzaika Yehova pachiyambi m’moyo wanu, mmalo mwa mwinamwake kulinganiza kupeza ntchito yakuthupi yolipira, ndiyeno kukwatira ndi kukhala ndi banja? Kodi mukuzindikira nkhani yaikulu m’chilengedwe chonse? Kodi mukulakalakadi kuwona dzina la Mlengi wathu wamkulu likuchotseredwa mtonzo wonse? Ngati ziri choncho, pamenepo kodi sikuli koyenerera kuti muchite zothekera muutumiki wa Yehova? Ndipo kodi zimenezo sizingaphatikizepo, kwakukulukulu owonjezereka a inu, kudzipereka kuutumiki wa pa Betele kapena kukhala ndi phande m’ntchito yaupainiya?
21. (a) Kodi ndikuchiitano cha kwa Yehova chotani chimene muyenera kulabadira, ndipo motani? (b) Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro chakuti achichepere owonjezereka adzayankha chiitano cha Yehova monga momwe anachitira Yesaya?
21 Mvetserani! Yehova akuitana, inde, akukuitanani kuti mumpatse yankho pamitonzo yoipa ya Satana. Kodi mungayankhe, monga momwe anachitira Yesaya kuti: “Ndipo ndinamva mawu a Ambuye akuti, Ndizatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife?” Khalani wanzeru. Yankhani monga momwe anachitira Yesaya kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Tiri ndi chidaliro chakuti owonjezereka a achicheperenu mudzalabadira chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amalonjeza kuti: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku lachamuna chanu. . . Muli nawo mame aubwana [ndi akazi omwe] wanu.” (Salmo 110:3; 148:12, 13) Ndipo pamene mulabadira, mungathe kukhala ndi chisangalalo cha kudziwa kuti Yehova akuwona ndipo akuvomereza—kuti inu mukupangitsa mtima Wake kukondwera!
BOKOSI LOPENDA
◻ Kodi nchifukwa ninji njira mu imene tikukhaliramo moyo wathu iri yofunika kwa Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kukondweretsa mtima wa Yehova?
◻ Kodi tingasonyeze motani kuti tapereka mtima wathu kwa Yehova?
◻ Kodi ndani kalero amene anakondweretsa mtima wa Yehova, ndipo motani?
◻ Kodi ndani amene akukondweretsa mtima wa Yehova lerolino, ndipo motani?
[Mawu Otsindika patsamba 17]
Pamene achichepere aswa malamulo a Mulungu, amalipira momvetsa chisoni pambuyo pake
[Chithunzi patsamba 18]
Achichepere anakondweretsa mtima wa Mulungu mwa kuthandiza kumanga malinga a Yerusalemu